Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 22 tsamba 106-tsamba 109
  • Anafunika Kulimba Mtima Kuti Akhalebe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anafunika Kulimba Mtima Kuti Akhalebe
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Jonatani Anachita Zinthu Mothandizidwa ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Ogwirizana Pansi pa Mbendera ya Chikondi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Muzikhala Okhulupirika kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 22 tsamba 106-tsamba 109

22 YONATANI

Anafunika Kulimba Mtima Kuti Akhalebe Wokhulupirika

Losindikizidwa
Losindikizidwa

AMUNA awiri ankakwera mofulumira phiri lokhala ndi miyala yambiri komanso zigwembe. Analinso atanyamula zida zankhondo. Ankapita kukalimbana ndi gulu lalikulu la Afilisiti. Yemwe ankatsogolera anali Yonatani, mwana wa Sauli, mfumu yoyamba ya Aisiraeli. Wina anali mnyamata wake yemwe ankamunyamulira zida ndipo anali atalimbikitsidwa ndi mawu a Yonatani akuti: “Palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.” Pasanapite nthawi, Yehova anasonyeza kuti mawu a Yonataniwa ndi oona. Ndipo amuna awiriwo anapha asilikali pafupifupi 20. Zimenezi zinathandiza kuti Aisiraeli aphe Afilisiti ambiri.

Nkhaniyi imasonyeza kuti Yonatani anali wolimba mtima. Komatu si nthawi yokhayi pomwe anasonyeza kulimba mtima. Iye anali wokhulupirika ndipo kuti munthu akhale wokhulupirika amafunikanso kulimba mtima. Yonatani anali mwana wokhulupirika wa Sauli. Koma m’kupita kwa nthawi Sauli anayamba kuchita zinthu zoipa ndipo anasiya kumvera Yehova. Yonatani anafunika kulimba mtima kuti akhale wokhulupirika kwa Yehova osati kwa Sauli.

Patapita zaka zambiri, mwina Yonatani ali ndi zaka pafupifupi 50, anakhala mnzake wa Davide yemwe anali wamng’ono kwa iye. Apa n’kuti Davide atangopha kumene Goliyati yemwe anali chimphona cha Afilisiti. N’zosakayikitsa kuti Sauli ndi anthu ena onse anadabwa kwambiri ndipo ankatamanda Davide. Ndiye kodi Yonatani anamva bwanji? Iye sanamuchitire nsanje Davide. M’malomwake anamupatsa zida zake zomenyera nkhondo kuphatikizapo uta. Imeneyi inali mphatso yapadera chifukwa Yonatani anali ndi luso logwiritsa ntchito uta. Ngakhale kuti Yonatani anali wamkulu kuposa Davide ndi zaka 30, analonjezana kuti akhala mabwenzi ndipo panalibe munthu amene akanawalekanitsa.

Yonatani ankafunika kukhala wokhulupirika kwa Mulungu, kuposa mmene akanakhalira wokhulupirika kwa bambo ake

Nayenso Sauli poyamba ankakonda Davide. Koma pasanapite nthawi, chikondi chake chinachepa ndipo anayamba kumuchitira nsanje. Ndipo ankayembekezera kuti Yonatani nayenso azidana ndi Davide. Koma Yonatani anakhalabe wokhulupirika kwa mnzakeyu ngakhale kuti Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu m’malo mwa iyeyo. Sauli atanena kuti akufuna kupha Davide, Yonatani anakhalabe kumbali ya mnzakeyu. Pamenepatu anasonyeza kulimba mtima. Ngakhale kuti pa nthawiyi Sauli anali wachikulire, anali adakali msilikali wamphamvu. Nthawi ina Yonatani akulankhula zabwino zokhudza Davide, Sauli ankafuna kupha mwana wakeyu ndi mkondo. Ngakhale kuti mkondowo sunamubaye, Yonatani anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi. Iye anapita kwa Davide n’kukamuuza kuti Sauli akufuna kupha Davideyo. Ndipo Yonatani anapempha Davide kuti ngati chinachake chitamuchitikira adzasamalire anthu am’banja lake.

Mfumu Sauli waimirira moopseza kutsogolo kwa Yonatani yemwe wakhala pa tebulo la chakudya ndipo akumuikira kumbuyo Davide. Abineri ndi anthu ena omwe ali pamenepo akuyang’ana mwankhawa.

Sauli anachititsa kuti Davide azikhala moyo wothawathawa. Mfumu Sauli ankagwiritsa ntchito asilikali ake kusaka Davide ndipo zimenezi zinachititsa kuti Davideyo azibisala m’malo osiyanasiyana. Ndiye kodi Yonatani ankathandiza nawo kuchita zimenezi? Baibulo silinena kuti ankathandiza nawo, choncho tikukhulupirira kuti sanachite nawo zimenezi. Pa nthawi ina, Yonatani anadziwa kumene Davide ankabisala ndipo anapita kukamuona. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Ankafuna ‘kumuthandiza kuti apeze mphamvu kuchokera kwa Yehova.’ Anauza Davide kuti: “Usachite mantha, chifukwa Sauli bambo anga sakupeza, moti iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.” Kenako anasiyana koma kameneka kanali komaliza kuonana.

Pasanapite nthawi, Yonatani anapita ndi bambo ake kukamenyana ndi Afilisiti omwe anali adani a Aisiraeli. Koma pa nthawiyi n’kuti Sauli atayamba mpatuko ndipo ankakhulupirira zamizimu. Yehova anasiya kudalitsa Sauli. Kunkhondoko Sauli anavulala kwambiri ndipo kenako anadzipha. Komanso ana ake atatu, kuphatikizapo Yonatani, anaphedwa pankhondoyo.

Davide anamva chisoni kwambiri. Anaimba nyimbo yolira komanso yosonyeza mmene ankamukondera mnzake wapamtimayu. Iye anatchula nyimboyo kuti “Uta,” mwina pokumbukira mphatso imene Yonatani anamupatsa zaka zingapo m’mbuyomo. Davide analemba kuti: “Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe mchimwene wanga Yonatani. Ndinkakukonda kwambiri.” Iye anasunga lonjezo limene anapangana ndi mnzakeyo. Atakhala mfumu, anafufuza ngati panali aliyense wam’banja la Yonatani ndipo anapeza Mefiboseti yemwe anali wolumala. Davide anatenga Mefiboseti kuti azikhala pafupi ndi Yerusalemu ndipo anamusamalira kwa moyo wake wonse.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • 1 Samueli 13:​2, 19-23; 14:​1-15; 16:21; 18:​1-9; 19:​4-6; 20:​1-42; 23:​16-18; 28:​6-8; 31:​1-6

  • 2 Samueli 1:​17-27; 9:​1-7

Funso lokambirana:

Kodi Yonatani anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi Afilisiti anali ndani? (w95 2/1 31-wcgr)

  2. 2. Kodi mawu akuti “pimu” akusonyeza bwanji kuti nkhani ya m’Baibuloyi ndi yolondola? (w05 3/15 29) A

    Munthu wina wanyamula kamwala ka pimu m’manja mwake.

    Chithunzi A: Kamwala ka pimu

  1. 3. N’chifukwa chiyani zinali zovuta kudutsa pamalo owolokera a ku Mikimasi? Nanga n’chiyani chinathandiza Yonatani kuti adutse pamalowa? (it “Mikimasi” ¶4-wcgr) B

Todd Bolen/BiblePlaces.com

Chithunzi B: N’kutheka kuti malo awa, ndi pamene panali malo owolokera a ku Mikimasi

Chithunzi B: N’kutheka kuti malo awa, ndi pamene panali malo owolokera a ku Mikimasi

Todd Bolen/BiblePlaces.com

  1. 4. Kodi Davide anachita chiyani pokwaniritsa lonjezo lake loti adzasamalira anthu am’banja la Yonatani? (it “Mefiboseti” Na. 2 ¶1-wcgr)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Yonatani anakhala wokhulupirika kwa Yehova osati kwa Sauli. Kodi nafenso tingakumane ndi zinthu ziti zomwe tingafunike kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova osati kwa wina aliyense? C

    Mlongo wina akuganizira mozama pamene mwamuna wake wagwada paguwa lansembe la Buda m’nyumba mwawo.

    Chithunzi C

  • Kodi nkhani ya Yonatani ndi Davide ikukuphunzitsani chiyani zokhudza . . .

    • anzathu?

    • kudzichepetsa?

    • kukhulupirika?

  • Kodi mungatsanzire Yonatani pa nkhani ya kulimba mtima m’njira zinanso ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yonatani akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

N’chiyani chinathandiza kuti Yonatani ndi Davide azigwirizana kwambiri, nanga ifeyo tingatani kuti tikhale ndi anzathu otero?

“Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chenicheni” (w21.01 20-25)

Thandizani ana anu kuti adziwe zimene akuphunzirapo pa zimene zinachitika pa moyo wa Yonatani.

“Yonatani” (Khadi la munthu wotchulidwa m’Baibulo)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena