24 ABIGAYELI
Ankafunika Kulimbana Ndi Amuna Awiri Okwiya
PA NTHAWI ina, zinthu sizinali bwino kwa Abigayeli chifukwa amuna awiri anali atakwiya. Mmodzi wa amunawo anali Nabala, mwamuna wake wa Abigayeli yemwe anali wankhanza komanso wopanda nzeru. Wina anali Davide, munthu wabwino, mtumiki wa Yehova wokhulupirika komanso mfumu ya Aisiraeli ya m’tsogolo. Nabala anachita chinthu china chomwe chinakwiyitsa kwambiri Davide. Zimenezi zinaika pangozi moyo wa anthu onse am’banja la Nabala. Abigayeli anali mkazi wokongola komanso wanzeru koma apa ankafunika kulimba mtima kuti athane ndi vutoli.
Abigayeli anamva kuchokera kwa wantchito wake zokhudza zimene mwamuna wake anachitira Davide. Wantchitoyo anauza Abigayeli kuti Davide akubwera ndi asilikali ake 400 kudzawononga “anthu onse am’nyumba yawo.” N’chifukwa chiyani ankafuna kuchita zimenezi? Davide anapempha chakudya kwa Nabala. Ndipo zimenezi zinali zomveka chifukwa Davide ndi anyamata ake ankateteza abusa a Nabala ndi nkhosa zawo. Davide anateteza mokhulupirika dziko la Isiraeli ndi anthu ake kwa adani. Ngakhale kuti Mfumu Sauli inkadana naye popanda chifukwa, inachititsa kuti Davideyo azikhala moyo wothawathawa. Ndiyeno pa nthawiyi, Davide anatuma anyamata ake kuti akapemphe chakudya kwa Nabala, koma Nabala anawalalatira ndipo anatchula Davide kuti ndi kapolo wothawa mbuye wake.
Wantchito wa Nabala anadziwa kuti sizithandiza ngati atauza Nabala nkhaniyi. Anauza Abigayeli kuti: “Abwana athu ndi munthu wopanda pake ndipo palibe amene angalankhule nawo.” Koma ankadziwa kuti Abigayeli amumvetsera ndipo achita zinthu mwanzeru. Ndiye kodi Abigayeli anatani?
Abigayeli sanatekeseke kwambiri koma ankafunika kuchita zinthu mwachangu. Anakonza chakudya chambiri kuti akachipereke ngati mphatso kwa Davide ndi anyamata ake. Anaika chakudyacho pabulu ndipo anapempha antchito ake kuti atsogole nacho ndipo iye ankawatsatira pabulu wake. Koma Nabala sanamuuze chilichonse chifukwa mwina ankaopa kuti amukaniza kukakumana ndi Davide.
Abigayeli analimba mtima n’kukakumana ndi Davide ndi asilikali ake omwe anakwiya chifukwa cha zinthu zopusa zimene mwamuna wake anachita
Pamene Abigayeli ankatsika phiri, anakumana ndi Davide ndi anyamata ake. Nthawi yomweyo anatsika pabulu paja, n’kupita kukakumana ndi Davide yemwe pa nthawiyo anali atakwiya. Anagwada kutsogolo kwa Davide n’kumuchonderera kuti amulole kuti alankhule. Davide ataona kudzichepetsa kwake, anamumvetsera.
Abigayeli analankhula ngati kuti wolakwa anali iyeyo ndipo anavomereza kuti Davide ankayeneradi kukwiyira mwamuna wake chifukwa anachita zinthu mopanda nzeru. Kenako anapempha Davide kuti akhulupirire kwambiri Yehova Mulungu. Iye sankafuna kuti Davide apalamule mlandu wa magazi kenako n’kumavutika ndi chikumbumtima chifukwa chopha anthu osalakwa. Ananenanso kuti nthawi zonse Yehova azidzasankha munthu wam’banja la Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli ndipo adzapulumutsa Davideyo kwa adani ake onse. Apatu n’zowonekeratu kuti Abigayeli ankadziwa kuti Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu yotsatira.
Davide atamva mawu ake okoma mtima komanso anzeruwa, mtima wake unakhala pansi. Iye anati: “Atamandike Yehova Mulungu wa Aisiraeli amene wakutumiza kudzakumana ndi ine lero.” Davide anayamikira Abigayeli chifukwa chochita zinthu moganiza bwino ndipo anadzichepetsa n’kuvomereza malangizo anzeru amene anam’patsa. Iye anati: “Ndamvera mawu ako.”
Koma Nabala sankadziwa chilichonse. Usiku umenewo anachita phwando ndipo anali “ataledzereratu.” Abigayeli anadikira mpaka m’mawa mowa utamuthera. Koma monga mwa nthawi zonse, Nabala anali wankhanza komanso wopanda nzeru. Ngakhale zinali choncho, anamuuzabe zonse zimene anachita. Mwina Abigayeli ankayembekezera kuti amukalipira komanso kumumenya koma sanachite zimenezi. Chifukwa chiyani? Chifukwa “mtima wake unaferatu ndipo anauma ngati mwala.” Patapita masiku pafupifupi 10, “Yehova anapha Nabala.” Choncho Mulungu anamulanga chifukwa chochitira zoipa Davide mtumiki wake. Yehova anadalitsanso Abigayeli pomupulumutsa kwa mwamuna wankhanzayo.
Yehova anadalitsa Abigayeli m’njira zinanso. Davide atamva kuti Nabala wamwalira, anapempha Abigayeli kuti akhale mkazi wake ndipo iye anavomera. Patapita nthawi, Davide anakhaladi mfumu poyamba ya Ayuda kenako ya Aisiraeli onse. Ndipo Abigayeli anamuberekera mwana wamwamuna. Pa nthawi ina Abigayeli anatengedwa ndi a Amaleki, koma mwamuna wake yemwe anali wachikondi komanso wolimba mtima anapita kukam’pulumutsa.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Abigayeli anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinapangitsa kuti Abigayeli akwatiwe ndi Nabala? (ia 77 ¶6)
2. Fotokozani zimene zinkachitika pa nthawi yometa ubweya wa nkhosa, pamene Davide anatuma anyamata ake kuti akapemphe chakudya kwa Nabala. (w97 7/1 14 ¶4-wcgr) A
Chithunzi A: Anthu ankachita phwando pa nthawi yometa ubweya wa nkhosa
Chithunzi A: Anthu ankachita phwando pa nthawi yometa ubweya wa nkhosa
3. N’chifukwa chiyani Nabala ankafunika kuyamikira zimene asilikali a Davide anamuchitira? (ia 77-78 ¶9-10) B
Hanan Isachar/Alamy Stock Photo
Chithunzi B: Dera lozungulira Karimeli linali lamiyala komanso zigwembe
4. Kodi Abigayeli ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Mulungu ‘adzakulunga moyo wa Davide m’phukusi la moyo kuti utetezeke’? (1 Sam. 25:29; it “Moyo” ¶45-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi amuna okwatira akuphunzira chiyani kwa Davide yemwe anamvera Abigayeli? C
Chithunzi C
Kodi alongo amene amuna awo si Mboni angaphunzire chiyani kwa Abigayeli?
Kodi mungatsanzire bwanji Abigayeli pa nkhani ya kulimba mtima?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Abigayeli akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi Mkhristu angatani kuti alimbitse banja lake ndi mwamuna kapena mkazi amene samatumikira Yehova?
Abigayeli anathandiza Davide kuti abweze mkwiyo wake. Ganizirani njira zimene zingakuthandizeni kuti mubweze mkwiyo anthu ena akakukhumudwitsani.
“Kuzindikira Kumachititsa Munthu Kubweza Mkwiyo” (w14 12/1 12-13)