Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 7/1 tsamba 14-15
  • Mkazi Wanzeru Apeŵa Tsoka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkazi Wanzeru Apeŵa Tsoka
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Thandizo Lomwe Sanaliyamikire
  • Nzeru ya Abigayeli
  • Zimene Tikuphunzirapo
  • Anachita Zinthu Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Anachita Zinthu Mwanzeru
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Abigayeli ndi Davide
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • “Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 7/1 tsamba 14-15

Anachita Chifuniro cha Yehova

Mkazi Wanzeru Apeŵa Tsoka

ABIGAYELI anali mkazi wanzeru wokwatiwa ndi Nabala, mwamuna woipa. Abigayeli anali “wanzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola.” Koma Nabala anali “waphunzo ndi woipa machitidwe ake.” (1 Samueli 25:3) Zomwe zinachitikira mwamuna ndi mkazi wake osayeneranawo zinasiya maina awo atalembedwa kosatha m’mbiri ya Baibulo. Tiyeni tione mmene zinachitikira.

Thandizo Lomwe Sanaliyamikire

Zimenezo zinachitika m’zaka za zana la 11 B.C.E. Panthaŵiyo Davide anali atadzozedwa kukhala mfumu yamtsogolo ya Israyeli, koma m’malo molamulira, iye anali kungothaŵathaŵa. Saulo, yemwe anali kulamulira monga mfumu, anafuna kwambiri kumupha. Choncho, Davide anakakamizika kumathaŵathaŵa. Iyeyo ndi anyamata ake 600 m’kupita kwa nthaŵi anapeza pobisala m’chipululu cha Parana, kummwera kwa Yuda kulinga ku chipululu cha Sinai.​—1 Samueli 23:13; 25:1.

Ali kumeneko, anakumana ndi abusa, antchito a mwamuna wina dzina lake Nabala. Munthu wachuma ameneyu, mbadwa ya Kalebi, anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000 ndipo amasenga nkhosa zake ku Karimeli, mudzi wa kummwera kwa Hebroni pamtunda ngati makilomita 40 kuchokera ku Parana.a Davide ndi anyamata ake anathandiza abusa a Nabala kulinda nkhosa zawo kuti mbala zomayendayenda m’chipululu monsemo zisabe.​—1 Samueli 25:14-16.

Ku Karimeli, anali atayamba kusenga nkhosa. Nthaŵi imeneyo inali ya chikondwerero, mofanana ndi nthaŵi ya mlimi ya kututa. Inalinso nthaŵi yopatsa mooloŵa manja, pamene eni nkhosa anali kufupa aja amene anawagwirira ntchito. Choncho Davide sanali kudzikuza pamene anatumiza anyamata khumi ku mudzi wa Karimeli kukapempha Nabala chakudya monga malipiro a ntchito imene anaichita pankhosa zake.​—1 Samueli 25:4-9.

Yankho la Nabala silinali labwino ayi. “Davide ndani?” anafunsa monyodola. Ndiyeno, posonyeza kuti Davide ndi anyamata ake sanali kanthu koma akapolo othaŵa basi, anafunsa nati: “Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziŵa kumene afumira?” Davide atamva zimenezi, anati kwa anyamata ake: “Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake.” Anthu monga 400 anakonzekera nkhondo.​—1 Samueli 25:10-13.

Nzeru ya Abigayeli

Abigayeli, mkazi wa Nabala, anamva za mwano womwe mwamuna wake ananena. Mwina uku sikunali kuyamba kuloŵapo ndi kukhala wakuchita mtendere m’malo mwa Nabala. Kaya zinalidi choncho kaya, koma Abigayeli sanazengereze. Popanda kuuza Nabala, anatenga chakudya​—kuphatikizapo nkhosa zisanu ndi zakudya zina zochuluka​—napita nazo kukakumana ndi Davide kuchipululu.​—1 Samueli 25:18-20.

Ndipo Abigayeli poona Davide, anafulumira kugwada pamaso pake. “Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa,” anamchonderera. “Mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.” Anawonjeza mawu nati: ‘[Mlandu wa Nabala] musadodome nawo, kapena kusauka nawo mtima mbuye wanga.’ Liwu lachihebri panopa lotembenuzidwa kuti “kudodoma” limatanthauza kuvutika chikumbumtima. Choncho Abigayeli anachenjeza Davide kuti asathamangire kuchita zoti nkudzachita nazo chisoni pambuyo pake.​—1 Samueli 25:23-31.

Davide anamvera Abigayeli. “Kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi,” anatero kwa iye. “Ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi.”​—1 Samueli 25:32-34.

Zimene Tikuphunzirapo

Nkhani imeneyi ya m’Baibulo ikusonyeza kuti si kulakwa ayi ngati mkazi woopa Mulungu waganiza zochita kanthu kena koyenera kamene kali kofunika. Abigayeli anachita zimene Nabala mwamuna wake sanafune, koma Baibulo silimuimba mlandu. M’malo mwake, limamtama kuti anali mkazi wanzeru ndi wochenjera. Mwa kudziganizira yekha zochitapo pangozi inali kudzayo, Abigayeli anapulumutsa moyo wa anthu ambiri.

Ngakhale kuti nthaŵi zonse mkazi ayenera kusonyeza mzimu wogonjera poopa Mulungu, iye moyenera angakane zimene mwamuna wake afuna ngati zingaswe mapulinsipulo olungama. Zoona, ayenera kuyesetsa kukhala ndi “mzimu wofatsa ndi wachete” ndipo sayenera kuchita zinthu payekha chabe chifukwa cha njiru, kunyada, kapena kupanduka. (1 Petro 3:4) Komabe, mkazi woopa Mulungu sayenera kukakamizika kuchita chilichonse chimene akudziŵa kuti si chanzeru ayi kapena chimene chingaswe mapulinsipulo a Baibulo. Inde, nkhani ya Abigayeli ikupereka chifukwa cholimba chotsutsira aja amene amaumirira kunena kuti Baibulo limaonetsa kuti akazi ndi akapolo.

Ndiponso nkhani imeneyi ikutiphunzitsa kudziletsa. Nthaŵi zina, Davide anasonyeza kwambiri mkhalidwe umenewu. Mwachitsanzo, anakana kupha Mfumu Sauli yemwe anafuna kumlanga, ngakhale kuti anali ndi mwaŵi wochita zimenezo ndipo imfa ya Sauli ikanampatsa mtendere Davide. (1 Samueli 24:2-7) Kusiyana ndi zimenezo, pamene Nabala anamnyoza, Davide anaiŵala nalumbira kumbwezera choipa. Limeneli ndi chenjezo lomveka kwa Akristu, amene amayesetsa ‘kusabwezera munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa.’ Pamikhalidwe yonse, ayenera kutsata uphungu wa Paulo wakuti: “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo.”​—Aroma 12:17-19.

[Mawu a M’munsi]

a Akuti chipululu cha Parana chimafika ndi kumpoto komwe ku Beereseba. Dera limeneli la dzikolo linali ndi msipu wambiri ndithu.

[Chithunzi patsamba 15]

Abigayeli abweretsa mphatso kwa Davide

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena