51 BARANABA
“Mwana Wotonthoza”
SAULO wa ku Tariso atabwerera ku Yerusalemu pambuyo pa zaka zitatu, anayamba kufufuza Akhristu kumeneko. (Agal. 1:15-19) Iye ankawaona kuti ndi abale ndi alongo ake koma iwo ankamuopabe kuti ndi munthu wozunza. Zikuoneka kuti ambiri sankadziwa kuti iye wasinthiratu. Koma munthu wina anasonyeza kulimba mtima komanso chifundo ndipo anamuthandiza. Munthu ameneyu anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Baranaba.
Akhristu a ku Yerusalemu ankaopa kuthandiza Saulo wa ku Tariso koma Baranaba analimba mtima n’kumuthandiza
Dzina loyamba limene Baranaba amadziwika nalo m’Baibulo ndi lakuti Yosefe. Pa nthawi ya Pentekosite mu 33 C.E., Yosefe anagulitsa munda wake n’kupereka ndalamazo kuti zithandizire Akhristu amene ankavutika. Iye ankadziwika kuti anali wokoma mtima komanso ankafunitsitsa kuthandiza ena, choncho atumwi anamupatsa dzina lakuti Baranaba limene limatanthauza kuti “Mwana Wotonthoza.” Kenako cha m’ma 36 C.E., iye analimba mtima n’kumulandira bwino Saulo. Baibulo limanena kuti: “Baranaba anamuthandiza popita naye kwa atumwi.”
Kungochokera pa nthawi imeneyo, Saulo ndi Baranaba ankagwirizana kwambiri. Saulo ankalalikira mwakhama ku Yerusalemu, zomwe zinachititsa kuti Ayuda ena azifuna kumupha. Choncho abale a ku Yerusalemu anamutumiza ku Tariso komwe anabadwira. Patapita zaka 9, Baranaba anatumizidwa ku Antiokeya wa ku Siriya kuti akalimbikitse Akhristu atsopano. Baibulo limanena kuti “anali munthu wabwino komanso wa chikhulupiriro cholimba. Iye ankatsogoleredwa kwambiri ndi mzimu woyera.” Anthu ambiri ku Antiokeya ankamvetsera uthenga wabwino moti Baranaba ankafunika munthu woti amuthandize. Baranaba anapita ku Tariso kukafufuza Saulo uja. Anthu awiriwa ankagwira mwakhama ntchito yolalikira. Iwo anathandizanso kuti anthu asonkhanitse katundu wokathandizira Akhristu omwe ankavutika.
Saulo, yemwe anadzayamba kudziwika kuti Paulo, anapita ndi Baranaba ku ulendo waumishonale. Iwo ankafunika kulimba mtima kuti agwire ntchitoyi. Ali ku Ikoniyo, Ayuda otsutsa ankafuna kuwapha powagenda ndi miyala choncho anachoka n’kupita ku Lusitara. Poyamba anthu akumeneko ankaganiza kuti iwo ndi milungu. Koma anthu otsutsa anabwera kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo ndipo ananena zinthu zabodza zokhudza Paulo ndi Baranaba. Choncho anthu anayamba kugenda Paulo ndipo anamusiya kunja kwa mzinda poganiza kuti wafa. Akhristu a ku Lusitara atabwera pamene panali Paulo, iye anadzuka n’kuyamba kuyenda kupita mumzinda. Baranaba anasangalala kwambiri kuona kuti Paulo ali moyo. Kenako anthu awiriwa anachoka bwinobwino mumzindawo. Koma pasanapite nthawi yaitali, iwo anabwerera ku Lusitara kuti akalimbikitse Akhristu kumeneko. Apatu anasonyeza kulimba mtima kwambiri.
Paulo ndi Baranaba anachita zambiri potumikira Yehova koma anakumananso ndi mavuto. Pa nthawi ina iwo anasemphana maganizo. Pa ulendo wawo wachiwiri, Baranaba ankafuna kutenga msuweni wake dzina lake Maliko. Koma Paulo sanagwirizane nazo chifukwa chakuti pa ulendo woyamba, Malikoyo anawasiya panjira. Ndiye palibe amene ankafuna kutsatira maganizo a mnzake. Baibulo limanena kuti “zitatero anakangana koopsa mpaka anasiyana.”
Baranaba ankafunika kusonyeza kulimba mtima m’njira inanso. Nthawi zina tikasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzathu, zimakhala zosavuta kupitiriza kumukwiyira, kulankhula zoipa zokhudza munthuyo kapena kusiya kusonkhana. Ndiye pamafunika kulimba mtima kuti tisachite zimenezi koma m’malomwake tiyesetse kukhala pa mtendere ndi Mulungu komanso Akhristu anzathu.
N’zodziwikiratu kuti anthu awiriwa sanalole kuti zimenezi ziwalepheretse kutumikira Yehova. Baranaba ndi Maliko anapita ku Kupuro kumene anakapitiriza kuphunzitsa anthu. Pomwe Paulo anapitiriza ulendo wake ndi Sila ndipo anachita zinthu zambiri m’dzina la Yehova.
Kodi anthu awiriwa anasungirana zifukwa? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti patapita nthawi, Paulo analemba zinthu zabwino zokhudza Baranaba m’makalata ake ouziridwa. Mwachitsanzo, m’kalata ina, Paulo ananena kuti Baranaba nayenso ankagwira ntchito kuti azipeza ndalama zomuthandizira pa utumiki wake. (1 Akor. 9:6) M’kalata inanso analemba zinthu zabwino zokhudza Maliko “msuweni wa Baranaba.” (Akol. 4:10, 11) N’zoona kuti Paulo ndi Baranaba anasiya kuyendera limodzi koma ankagwirizanabe. N’zosachita kufunsa kuti Baranaba anapitiriza kukhala mogwirizana ndi dzina lake komanso ankalimbikitsa anthu ena ndi uthenga wabwino. Ndipo pamene ankagwira ntchito ndi Maliko, yemwe anali wachinyamata, n’zodziwikiratu kuti ankapitiriza kumuphunzitsa. M’mutu wotsatira, tidzakambirana za kulimba mtima kwa Maliko.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Baranaba anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Alevi sankalandira malo awoawo ngati cholowa. Ndiye zinatheka bwanji kuti Baranaba yemwe anali Mlevi akhale ndi munda wake? (Num. 18:20) (Mac. 4:36, 37; w98 4/15 20 ¶4, mawu a m’munsi-wcgr)
2. N’chifukwa chiyani Baranaba ankatchedwa mtumwi? (Mac. 14:14; it “Baranaba” ¶3-wcgr)
3. Ku Kupuro, Baranaba ndi Paulo analalikira kwa munthu wina dzina lake Serigio Paulo. Kodi Luka ananena zoona pamene analemba kuti Serigio Paulo anali “bwanamkubwa”? (Mac. 13:7, 12; it “Kupuro” ¶7-wcgr) A
Bank of Cyprus Cultural Foundation Collection
Chithunzi A: Ndalama ya mu ulamuliro wa Kalaudiyo, amene anali mfumu pa nthawi imene Baranaba ndi Paulo anapita ku Kupuro. Ikusonyeza kuti wolamulira pachilumba ankatchedwa “bwanamkubwa”
4. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti anthu a ku Lusitara anapereka nsembe polandira Paulo ndi Baranaba? (bt 97, bokosi)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi tingatsanzire bwanji Baranaba pa nkhani ya kuwolowa manja?
Zikuoneka kuti Baranaba ndi amene ankatsogolera pa ulendo woyamba waumishonale. Kenako Paulo anayamba kudziwika kwambiri kuposa iyeyo. Koma zikuoneka kuti Baranaba sanamuchitire nsanje. Kodi ifeyo tingamutsanzire pa zochitika ziti? B
Chithunzi B
Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Baranaba pa moyo wanu?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
N’chifukwa chiyani mukuyamikira mukaganizira zoti Baranaba anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Kodi kugwirizana kwa Paulo ndi Baranaba kukusonyeza bwanji kuti anthu osiyana akhoza kugwira ntchito limodzi bwinobwino?
“Kodi Mumathetsa Kusamvana N’kukhazikitsa Mtendere?” (w17.06 16-20)
Muvidiyo yotsatirayi, onani mmene abale masiku ano amathetsera kusamvana ngati mmene Paulo ndi Baranaba anachitira.