52 MALIKO
“Amandithandiza”
YOHANE MALIKO anasonyeza kulimba mtima ngakhale pamene anali wachinyamata. Pa nthawiyo Yesu Khristu anali atangomangidwa n’kutengedwa ndi anthu onyamula zida. Atumwi onse anali atathawa. Ndiyeno Baibulo limanena za “mnyamata wina” amene analimba mtima n’kumatsatirabe Yesu ndipo anthu atamuona ankafuna kumugwira. Koma iye anangowasiyira chovala chake n’kuthawa ali maliseche kapena kuti atangovala chovala chamkati. Buku la Maliko lokha ndi limene limanena za nkhaniyi, choncho ambiri amaganiza kuti mnyamatayo anali Maliko yemweyo.
Maliko ankakhala ku Yerusalemu. Iye ayenera kuti ankakhala limodzi ndi mayi ake ndipo zikuoneka kuti mayi akewo anali olemera. Yesu atamwalira, mpingo unkasonkhana kunyumba kwawo. Mtumwi Petulo atamasulidwa ndi mngelo kundende, anapita kunyumba imeneyi usiku. N’zosakayikitsa kuti Maliko ankadziwana ndi atumwi komanso ophunzira ena a Yesu. Iye ayenera kuti anaphunzira kulimba mtima kuchokera kwa anthu amenewa.
Cha m’ma 46 C.E., Baranaba, yemwe anali msuweni wa Maliko anapita ku Yerusalemu ndi mtumwi Paulo ndipo anachita chidwi kwambiri ndi mnyamatayu. Pamene anthuwa ankabwerera ku Antiokeya, Maliko anapita nawo. Patatha pafupifupi chaka chimodzi, Paulo ndi Baranaba anapempha Maliko kuti ayende nawo pa ulendo waumishonale. Iye analimba mtima n’kuvomera kuti apite n’cholinga choti azikatumikira amishonalewa.
Pa nthawiyo, kuyenda ulendo kunali kovuta komanso koopsa. Paja Paulo anadzalemba kuti pa maulendo ake anakumana ndi zoopsa ‘mʼmitsinje, kuchokera kwa achifwamba, mumzinda, mʼchipululu komanso panyanja.’ (2 Akor. 11:26) Popeza Maliko anali mtumiki wa anthu awiri omwe ankalemekezedwa kwambiri mumpingo, iye anali wokonzeka kuchita chilichonse chimene anamupempha. Kodi ntchito imeneyi inali yovuta? Baibulo silinena chilichonse. Limangonena kuti Maliko anawasiya anthu awiriwa ku Pamfuliya ndipo anabwerera kwawo ku Yerusalemu. Zimene anachitazi ziyenera kuti zinakhumudwitsa anthuwa, koma makamaka Paulo.
Pambuyo poyenda ulendo wautaliwu, Paulo ndi Baranaba anaganiza zopitanso ku ulendo wina. Baranaba ankafuna kupereka mwayi winanso kwa Maliko kuti ayende naye. Koma Paulo sanagwirizane nazo. N’kutheka kuti ankaona kuti Maliko ndi wosadalirika. Paulo ndi Baranaba anasemphana maganizo moti Baibulo limati “anakangana koopsa.” Baranaba anatenga Maliko n’kupita naye ku Kupuro kumene anakapitiriza kulalikira. Ndipo Paulo anapeza munthu wina n’kupitiriza naye ulendo wake.
Zimenezi ziyenera kuti zinakhumudwitsa Maliko. Tikutero chifukwa chakuti iye anakhumudwitsa Paulo amene ankamulemekeza kwambiri komanso anachititsa kuti anthu amene ankagwirizana asiyane. Kodi Maliko ankangokhalira kudziimba mlandu, kukwiya kapena kusunga zifukwa? Ayi ndithu.
Utumiki wa Maliko unaima kwa kanthawi koma iye sanangokhalabe wokhumudwa
Maliko ankachita zomwe angathe pothandiza Akhristu anzake. Cha mu 60 mpaka 61 C.E., Paulo anali pa ukaidi wosachoka pakhomo ku Roma. Iye analemba kalata ndipo m’kalatayo anatchulamo Maliko yemwe anali naye limodzi. Ponena za Maliko, iye anati: “Amandilimbikitsa kwambiri.” Ndiyeno cha m’ma 62 ndi 64 C.E., Maliko anatchulidwanso m’kalata imene Petulo analemba. Zikuoneka kuti Maliko anayenda ulendo wautali wopita ku Babulo kukakhala ndi mtumwi wachikulireyu. Petulo anatchula Maliko kuti “mwana wanga.” Maliko ayenera kuti ankamulimbikitsa kwambiri Petulo. Petuloyo ayenera kuti anamufotokozera Maliko zinthu zambiri zomwe zinachitika pamene ankayenda ndi Yesu Khristu. Zikuoneka kuti Maliko analemba Uthenga Wabwino wodziwika ndi dzina lake ali ku Roma ndipo umasonyeza kuti analembamo zinthu zimene Petuloyo anaona ndi maso.
Mtumwi Paulo anatchula Maliko komaliza m’kalata yake yopita kwa Timoteyo. Pa nthawiyi, Paulo analinso kundende ndipo anapempha Timoteyo kuti apite kukamuona limodzi ndi Maliko. N’chifukwa chiyani anapempha kuti Maliko apite nawo? Paulo anati: “Chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.” N’zosachita kufunsa kuti anthu awiriwa ankafunitsitsa kupita kwa Paulo komanso kukamulimbikitsa pa masiku omaliza a moyo wake. Ngakhale kuti Maliko anakumana ndi zinthu zambiri zokhumudwitsa, iye analimba mtima n’kumapitiriza kutumikira Mulungu. Izi zinachititsa kuti azithandiza abale ake komanso kuti Yehova Mulungu azimukonda kwambiri.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Maliko anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chiyani chikusonyeza kuti Maliko ankachokera m’banja lolemera? (w10 3/15 6 ¶6–7 ¶1)
2. Kodi n’kutheka kuti Maliko ankagwira ntchito ziti potumikira Baranaba ndi Paulo? (Mac. 13:5; w10 3/15 7 ¶5)
3. Kodi Maliko anayenda malo ati? (w10 3/15 8 ¶6-8) A
Chithunzi A: Mizinda ina imene Maliko ayenera kuti anapitako
4. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti mu Uthenga Wabwino wa Maliko muli zinthu zimene Petulo anaona ndi maso. (w08 2/1 26 ¶1)
Zomwe Tikuphunzirapo
Maliko satchulidwa kuti mtumwi kapena mneneri. Komabe ankatumikira ena modzichepetsa. Kodi ifenso tingatumikire bwanji anthu ena masiku ano?
Pa nthawi ina Maliko anataya mwayi wotumikira ndi Paulo, koma iye anakhalabe wokhulupirika. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Maliko ngati nafenso utumiki wathu watha? B
Chithunzi B
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Maliko m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
N’chifukwa chiyani mumayamikira mukaganizira kuti Maliko anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Kodi Uthenga Wabwino wa Maliko ndi wapadera m’njira ziti?
Gwiritsani ntchito chitsanzo cha Maliko pophunzitsa ana anu ubwino wopitirizabe kutumikira Yehova ngakhale titakumana ndi mavuto.