53 PAULO
“Musadandaule”
YESU anamusonyeza Saulo wa ku Tariso “mavuto onse amene adzakumane nawo” pogwira ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu. Kodi zimene Yesu ananenazi zinachitikadi? Patapita zaka 20 Saulo, yemwe anadzayamba kudziwika kuti mtumwi Paulo, analemba kalata yachiwiri yopita kwa Akorinto. Pofika nthawi imeneyi anali ‘atamenyedwa kosawerengeka ndiponso anabwerera lokumbakumba.’ Komanso katatu konse anapulumuka ngalawa itasweka, ndipo pa ulendo wina anakhala masana onse komanso usiku ali panyanja. Koma pa nthawi ina ngalawa inadzamuswekeranso.
Paulo anakhala m’ndende ya Aroma ku Kaisareya kwa zaka zoposa ziwiri. Pa nthawi imeneyi bwanamkubwa ankayembekezera kuti amupatsa chiphuphu koma sanam’patse. Bwanamkubwayo atalowedwa m’malo ndi wina, Paulo anachita apilo kuti akaonekere kwa Kaisara. Choncho Paulo anakwezedwa mungalawa yopita ku Roma. Ulendo wochoka ku Kaisareya kupita ku Roma unali woposa makilomita 3,000 komanso wovuta. Pa ulendowu Paulo anapita ndi anzake awiri, Arisitako komanso Luka, yemwe anali dokotala.—Akol. 4:14.
Atafika ku Mura ku Asia Minor, mtsogoleri wa asilikali dzina lake Yuliyo anakweza akaidi onse mungalawa ya ku Iguputo yonyamula chakudya yopita ku Italy. Anthuwo atangokwera ngalawayo n’kunyamuka, chimphepo chinayamba kusokoneza ulendowo. Luka analemba kawiri kuti ngalawayo inkayenda “movutikira.” Ataima pamalo otchedwa Madoko Okoma, Paulo anaona kuti ndi bwino akhalebe pomwepo mpaka nyengo yozizira ithe, kuti asakumane ndi mavuto aakulu.
Mtumwiyu analimba mtima n’kufotokoza maganizo ake. Anauza Yuliyo kuti ngati atapitiriza ulendowo ‘adzawonongetsa zambiri.’ Koma Yuliyo anamvera malangizo a anthu ena n’kupitiriza ulendowo. Iye ayenera kuti anadzanong’oneza bondo ndi zimene anachitazi. Luka analemba kuti mphepo yamphamvu inkawomba ngalawayo moti inayamba kulowera kwina. Mphepoyo inakula ndipo kwa masiku ambiri ‘inkawakankha mwamphamvu.’ Pofuna kuti ngalawayo ipepuke, anthu anayamba kutaya katundu m’madzi. Kwa masiku angapo aliyense sanadye ndipo mphepoyo inapitirira kwa mawiki awiri. Luka analemba kuti: “Tinayamba kukayikira zoti tipulumuka.”
Paulo ali mkaidi anathandiza kupulumutsa miyoyo ya anthu amene anakwera nawo ngalawa pa nthawi yomwe kunali chimphepo
Zinkaoneka kuti palibe chabwino. Koma Paulo anawalimbitsa mtima anthuwo ponena kuti: “Musadandaule chifukwa palibe amene ataye moyo wake, koma ngalawa yokhayi iwonongeka.” Pamene anthu ena ankafuna kuchoka m’ngalawamo kuthawira m’kaboti kakang’ono, Paulo anawauza kuti akhalebe m’ngalawamo kuti apulumuke. Choncho asilikali anadula zingwe za kaboti kakang’onoko kuti anthu asakweremo.
Chakum’bandakucha Paulo anauza anthuwo kuti tsopano angathe kudya mmene akufunira. Anawauzanso kuti: “Ngakhale tsitsi limodzi lamʼmutu mwanu siliwonongeka.” Anthuwo asanayambe kudya, Paulo anapemphera kwa Yehova. Kenako onse anadya chakudyacho ndipo tirigu amene anatsala anamutayira m’madzi. Zimene Paulo analankhula komanso kuchita zinathandiza anthuwo moti “onse analimba mtima.” Mmene kunkacha, ngalawayo inali itayandikira kumtunda koma kenako kutsogolo kwake kunakanirira pansi. Mafunde ankaiwomba kwambiri moti inayamba kusweka. Koma zimene Paulo ananena zija zinachitikadi. “Onse anafika kumtunda ali bwinobwino.”
Kenako anazindikira kuti ali pachilumba cha Melita. Pasanapite nthawi, Paulo ndi anzake aja anayamba kulalikira. Moti kumeneko, Mulungu anathandizanso Paulo kuchita zodabwitsa. Anthu ambiri apachilumbachi anamvetsera uthenga wawo komanso anawachitira zinthu zabwino zambiri.
Paulo sanasiye kuchita zinthu molimba mtima. Kenako anakafika ku Roma nyengo yozizira itatha. Kwa zaka ziwiri anali pa ukaidi wosachoka panyumba ndipo ankalonderedwa ndi msilikali. Koma pa nthawiyi, Paulo ankalalikirabe komanso ankalemba makalata omwe anadzakhala mbali ya Baibulo. Atamasulidwa, anapitiriza kulalikira mwaufulu. Patapita nthawi, anamangidwanso ku Roma komweko ndipo aka kanali komaliza. Zikuoneka kuti patapita nthawi, Aroma anapha munthu wokhulupirika ndi wolimba mtimayu. Komabe Paulo sankaopa imfa. Iye anali atanena kuti imfa ndi “mdani womaliza” ndipo ankadziwa kuti Yehova adzaithetsa. (1 Akor. 15:26) Pa nthawi yoyenera, Yehova anamupatsa mphoto. Mphoto yake ndi yokhala ndi moyo kumwamba mpaka kalekale monga mfumu komanso wansembe limodzi ndi Yesu Khristu.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Paulo anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti pa nthawi iyi ya moyo wake?
Zoti Mufufuze
1. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Saulo ankakonda kugwiritsa ntchito dzina lake la Chiroma lakuti Paulo? (w08 3/1 12 ¶4-5)
2. Kuchokera pamene Paulo anabwerera ku Tariso kufika pamene anapita ku Antiokeya panadutsa zaka 9 ndipo zaka zimenezi zimatchedwa “zaka zosatchulidwa” za Paulo. Kodi n’kutheka kuti anakumana ndi mavuto ati pa nthawi imeneyi? (w00 7/15 26-27, bokosi ¶3-4-wcgr)
3. Kodi Paulo anachita bwino kuuza anthu kuti asapitirize kaye ulendo wopita ku Italy? (Mac. 27:9, 10; wp17.5 9 ¶3-4) A
Chithunzi A: Ngalawa yonyamula katundu ya m’nthawi ya atumwi yofanana ndi imene anakwera Paulo popita ku Mura
4. N’chifukwa chiyani anthu a ku Melita ananena kuti Paulo ndi “wopha anthu”? (Mac. 28:4; w15 10/1 9 ¶5-6)
Zomwe Tikuphunzirapo
Paulo anauza anthu amene anali nawo m’ngalawa kuti Mulungu awathandiza moti ‘ngakhale tsitsi limodzi lamʼmutu mwawo siliwonongeka.’ (Mac. 27:22, 34) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu yochita chiyani, nanga zikukuthandizani kuti muziiona bwanji ntchito yolalikira?
Paulo atapemphera anthu amene anali m’ngalawa “analimba mtima.” (Mac. 27:35, 36) Kodi ndi pa nthawi iti imene mapemphero athu akhoza kulimbikitsa anthu ena? B
Chithunzi B
Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kumene Paulo anasonyeza munkhaniyi?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
N’chifukwa chiyani mumayamikira mukaganizira kuti Paulo anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Onani ubwino wa maulendo apanyanja munthawi ya atumwi komanso mmene maulendowa anathandizira kuti Chikhristu chifike m’madera ambiri.
‘Zoopsa Panyanja’ (w99 3/15 29-31-wcgr)
Kodi akulu okhulupirika amatsanzira bwanji Paulo pa nkhani ya kupirira komanso kudzimana?
Muzitsanzira Anthu Amene Anadalitsidwa Chifukwa cha Kuleza Mtima—Paulo (3:22)