54 MTUMWI YOHANE
Analimba Mtima pa Nthawi Yovuta
MTUMWI YOHANE analemba kuti: “Ino ndi nthawi yakumapeto.” Pa nthawi yomwe anali wachikulire ankadziwa kuti atumwi onse atsala pang’ono kutha. Ndipo zaka zambiri m’mbuyomo, Yesu komanso mtumwi Paulo anali atachenjeza kuti kudzabwera anthu ampatuko. Atumwi ndi amene ankalepheretsa kuti mpatuko usafalikire. Koma pambuyo poti onse amwalira, aphunzitsi abodza anayamba kusokoneza mpingo. (Mat. 7:15; Mac. 20:29, 30; 2 Ates. 2:6, 7) Zikuoneka kuti Yohane ndi amene anali mtumwi womaliza kulepheretsa kuti mpatuko usafalikire kwambiri. Mukuganiza kuti iye ankamva bwanji pa nthawi yovutayi, pomwe mpatuko unkayamba kufalikira m’mipingo? Komabe Yohane sanachite mantha kapena kutaya mtima.
N’chiyani chinathandiza Yohane kuti akhalebe wokhulupirika pamene ankazunzidwa, kuikidwa m’ndende komanso pamene mpatuko unayamba?
Pamene Yohane anali ndi zaka mwina 90, ankachitabe khama pa nkhani ‘yolankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.’ Chifukwa cha zimenezi, anakhala mkaidi pachilumba cha Patimo. Chilumbachi chinali m’nyanja ya Ejani ndipo chinali chamiyala komanso chopanda mitengo. Ndiye kodi n’chiyani chinathandiza Yohane kuti asataye mtima? Iye ayenera kuti ankakumbukira lonjezo la Yesu lakuti: “Dziwani kuti ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mat. 28:20.
Pa nthawiyi, n’kuti patatha zaka 60 kuchokera pamene Yesu ananena mawu amenewa. Koma tsopano Yohane anasangalala kuona komanso kumva Yesu akumulankhula m’njira yapadera kwambiri. Yesu anaonetsa Yohane masomphenya a zinthu zam’tsogolo. Masomphenyawo anali onena za “tsiku la Ambuye” pamene anthu a Mulungu padziko lonse lapansi azidzamulambira m’njira yoyenera komanso mogwirizana. Masomphenyawa anasonyezanso kuti Khristu adzathandiza otsatira ake kuti akhalebe okhulupirika pamene akukumana ndi mavuto aakulu.
Yesu anaonetsa Yohane masomphenyawa pogwiritsa ntchito “zizindikiro.” Zinthu zambiri zimene Yohane anaona zinali zovuta kuzimvetsa. Koma zimene anamvetsa ndi zakuti: Yehova ndi Yesu adzaonetsetsa kuti anthu amene akufalitsa mpatukowo asawonongeretu zinthu m’mipingo. M’tsiku la Ambuye anthu a Mulungu zinthu zizidzawayendera bwino ndipo azidzasangalala ndi madalitso ambiri. Satana adzagonjetsedwa pa nkhondo yakumwamba n’kuponyedwa padziko lapansi. Kenako adzawonongedwa moti sadzakhalakonso. Yohane ayenera kuti analimba mtima ataona masomphenyawa ndipo analemba “zonse zimene anaona.”
Moyo wapachilumba cha Patimo unali wovuta, koma Yohane sanafooke. Domitani anali mfumu ya Aroma komanso ankadana kwambiri ndi Chikhristu. Choncho iye atamwalira, Yohane anamasulidwa. Patapita nthawi, Yohane anachoka pachilumbapo ndipo mwina anapita ku Efeso. Ali ndi zaka pafupifupi 100, Yehova anamupatsa ntchito ina yovuta kwambiri.
Yohane anauziridwa kulemba Uthenga Wabwino womaliza womwe ndi wa nambala 4. Iye ayenera kuti ankadziwa kuti zimene alembezo zifika mofulumira kumipingo ndipo zithandiza anthu ambiri kukhala olimba mtima komanso okhulupirika. Anthu odana ndi Chikhristu akanadana naye kwambiri. Koma zimenezi sizinachititse kuti asagwire ntchito yakeyi.
Panali patadutsa zaka 70 kuchokera pamene Yohane ankayenda ndi Yesu. Komabe mothandizidwa ndi mzimu woyera, iye anakumbukira zonse bwinobwino moti analemba nkhani yogwira mtima yonena za moyo wa Yesu. Ndipotu zambiri mwa zinthu zimene analemba sizipezeka m’Mauthenga Abwino atatu ena aja. Mwachitsanzo, Yohane yekha ndi amene analemba zokhudza kuukitsidwa kwa Lazaro komanso zoti atsogoleri achipembedzo ankafuna kuphanso Lazaroyo pambuyo poti waukitsidwa. (Yoh. 11:1-46; 12:10) Yohane anafotokozanso mwatsatanetsatane zimene Yesu anauza ophunzira ake komanso pemphero limene anawapempherera usiku umene anaperekedwa. Imeneyitu inali mphatso yapadera kwambiri yopita kwa Akhristu onse.
Chapanthawi yomweyi, Yohane analembanso makalata atatu ouziridwa opita kwa Akhristu anzake. Iye analemba mopanda mantha za mpatuko womwe unkayamba kufalikira. Anachenjezanso Akhristu kuti azipewa kugwirizana ndi ampatuko ndipo asamawapatse ngakhale moni. Makalata atatu a Yohane amafotokozanso kwambiri za chikondi ndi chiyembekezo. Yohane analemba kuti, “Mulungu ndi chikondi.” Ndipo m’makalata akewa mtumwiyu anasonyeza khalidwe limeneli pamene ankalimbikitsa Akhristu anzake komanso kupereka malangizo. Analembanso kuti ankasangalala kwambiri kuona ana ake auzimu “akuyendabe m’choonadi.” Ambiri a iwo ayenera kuti analimbikitsidwa ndipo anapitiriza kuchita zimenezi.
Akhristu masiku ano sangakumane ndi vuto la mpatuko ngati mmene zinalili pa nthawi ya Yohane. N’zoona kuti mpatuko ulipo, koma sungasokoneze kwambiri mipingo ngati mmene unachitira Yohane atamwalira. (Yes. 54:17; Mac. 3:21) Komabe nafenso tingakumane ndi mavuto ena monga kuzunzidwa kapena kuikidwa m’ndende. Zikatero, tiyenera kutengera chitsanzo cha Yohane. Tiyeni tipitirize kuyenda ndi Mulungu molimba mtima, zivute zitani.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yohane anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chiyani chikusonyeza kuti Yohane anali wolimba mtima? (bt 33, bokosi ¶3-4)
2. N’chifukwa chiyani Yohane ananenedwa kuti anali ‘wosaphunzira komanso munthu wamba’? (Mac. 4:13; w08 5/15 30 ¶6)
3. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Yohane adzakhalabe ndi moyo mpaka iye adzabwere? (mfundo yothandiza pophunzira pa Yohane 21:22, nwtsty-wcgr)
4. N’chiyani chikutitsimikizira kuti Yohane ndi amene analemba Uthenga Wabwino wa Yohane? (it “Uthenga wabwino wa Yohane” ¶2-8-wcgr) A
Fondation Martin Bodmer, Cologny (Genève)
Chithunzi A: Mpukutu wa m’ma 200 C.E. ndipo uli ndi mutu wakuti “Uthenga Wabwino wa Yohane”
Zomwe Tikuphunzirapo
Yohane analemba zokhudza nsembe ya Yesu kapena ubwino wake maulendo oposa 100. Kodi ifeyo tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe ya Yesu?
Yohane ayenera kuti anali ndi zaka za m’ma 90 pamene anauziridwa kulemba mabuku 5 a m’Baibulo. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amawaona bwanji anthu achikulire? B
Chithunzi B
Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yohane?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
N’chifukwa chiyani mumayamikira mukaganizira kuti Yohane anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Kodi abale ndi alongo achikulire masiku ano angasonyeze bwanji kulimba mtima ngati mmene Yohane anachitira?
Yohane analemba kwambiri zokhudza chikondi. Onani zimene tingaphunzire pa zimene analemba komanso chitsanzo chake
“Zimene Tingaphunzire Kwa ‘Wophunzira Amene Yesu Anali Kumukonda Kwambiri’” (w21.01 8-13)