44 YOHANE M’BATIZI
‘Palibe Wamkulu Kuposa Iyeyu’
PANALI patadutsa zaka zambiri Yehova asanatumize mneneri kuti akalangize anthu ake. Koma kenako anatuma munthu wina dzina lake Yohane kuti akauze anthu uthenga wake. Yohane ankakhala yekhayekha m’chipululu cha Yudeya chomwe chinali chopanda zomera komanso chamiyala. M’chipululuchi munali njoka, zinkhanira, nyama zikuluzikulu zoopsa komanso achifwamba. Yohane anali wolimba mtima moti ankakhala kumeneko komanso ankauza anthu uthenga wamphamvu wochokera kwa Yehova.
Makolo ake anali Zekariya ndi Elizabeti. Iwo ayenera kuti anamuuza zimene mngelo wa Yehova ananena zokhudza iyeyo. Choncho n’kutheka kuti Yohane ayenera kuti ankadziwa kuti ayenera kukhala mneneri wakhama ngati Eliya, Mnaziri ngati Samueli komanso kalambulabwalo wa munthu wina wamkulu kuposa iyeyo. Ali ndi zaka 30, Yohane akanatha kukhala wansembe ngati bambo ake. Koma m’malomwake ankauza anthu kuti ayenera kulapa machimo awo. Iye anadzakhala “mawu a winawake amene akufuula mʼchipululu” yemwe mneneri Yesaya ananeneratu. Yohane ankalalikira ndi mtima wonse za “Ufumu wakumwamba” moti anthu ambiri ankabwera kuchokera m’matauni ndi mizinda kuti adzamve uthenga wake. Mogwirizana ndi malangizo amene Mulungu anamupatsa, iye ankabatiza m’madzi anthu amene alapa machimo awo. Asaduki ndi Afarisi atapita kukamuona, Yohane anawauza molimba mtima kuti iwo sankatsatira malamulo a Mulungu moyenera.
Yohane sankadziona kuti ndi wapamwamba kuposa ena chifukwa cha utumiki wakewu. M’malomwake anali wodzichepetsa ndipo ankalalikira kuti iye ndi kalambulabwalo wa munthu wina wamkulu amene akubwera pambuyo pake. Yohane ananena kuti iye sanali woyenera ngakhale kumasula nsapato za munthu ameneyo. Ndiyeno atabatiza Yesu, Yohane anamva mawu a Yehova akuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa ndipo amandisangalatsa kwambiri.” Pa nthawi ina, pambuyo poti Yesu wayesedwa ndi Satana, Yohane ananena mokweza mawu kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!”
Yohane anasonyezanso kudzichepetsa pamene anauza ophunzira ake kuti ayambe kutsatira Yesu. Ambiri mwa iwo anachitadi zimenezi. Wina anali Andireya yemwe anali mchimwene wake wa Petulo ndipo wina ayenera kuti anali Yohane mwana wa Zebedayo. Anthu awiriwa anadzakhala atumwi a Khristu. Kwa kanthawi ndithu, Yesu ndi Yohane ankachita utumiki wofanana. Onse ankalimbikitsa anthu kuti abatizidwe posonyeza kuti alapa machimo awo. Yohane atauzidwa kuti ophunzira a Yesu akubatiza anthu ambiri kuposa iyeyo, sanakhumudwe. M’malomwake iye anadzichepetsa n’kunena kuti, “Iyeyo akuyenera kumawonjezereka, koma ine ndikuyenera kumacheperachepera.”
Uthenga umene Yohane ankalalikira molimba mtima unkakwiyitsa anthu achinyengo komanso olamulira amphamvu koma unkalimbikitsa anthu amene ankayembekezera Mesiya
Yohane ankafotokoza molimba mtima uthenga wodzudzula olamulira amphamvu. Mwachitsanzo, Herode Antipa anali wolamulira yemwe analowa Chiyuda ndipo ankati ndi wokhulupirika. Koma iye analanda mkazi wa mchimwene wake. Yohane analimba mtima n’kumudzudzula kuti akuchita chiwerewere. Chifukwa cha zimenezi, Herode anatsekera Yohane m’ndende. Koma mkazi wake Herodiya ankaona kuti zimenezi n’zosakwanira moti ankafuna kuti Yohane aphedwe.
Yohane ali m’ndende ankafunika kulimbikitsidwa. Choncho anatuma ophunzira ake awiri kukafunsa Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?” Yesu anamutumizira uthenga wolimbikitsa wakuti: “Amene anali ndi vuto losaona akuona, . . . ndipo amene anali ndi vuto losamva akumva. Akufa akuukitsidwa.” Ngakhale kuti Yohane anali mneneri ngati Eliya, iye sanapatsidwe mphamvu zochita zodabwitsa. Ali m’ndendemo, analimbikitsidwa kumva kuti anali kalambulabwalo wa Yesu amene ankachita ntchito zambiri zodabwitsa.
Pasanapite nthawi yaitali, Herodiya anapeza njira yoti aphere Yohane. Mwana wake anavinira Herode ndipo Herodeyo, anamuuza kuti apemphe chilichonse chimene angafune. Herodiya anauza mtsikanayo kuti akapemphe mutu wa Yohane M’batizi. Herode sankafuna kupha Yohane koma sanalimbe mtima n’kukana zimene anapemphedwazi. Yohane anakhala wolimba mtima kwa moyo wake wonse.
Ponena za Yohane, Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, pa anthu onse, palibe wamkulu kuposa Yohane.” Palibe munthu aliyense, kaya mneneri Mose kapena Eliya, amene anakhala ndi mwayi wokhala ‘winawake wofuula mʼchipululu,’ komanso kalambulabwalo wa Mesiya. Ndipo kulimba mtima kwa Yohane kumalimbikitsabe Akhristu mpaka pano.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yohane M’batizi anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi chibale cha Yohane M’batizi ndi Yesu chinali chotani? (w10 9/1 15 ¶4-6)
2. Kodi katswiri wa mbiri yakale dzina lake Flavius Josephus anasonyeza bwanji kuti Yohane M’batizi analiko? (mrt nkhani 14) A
Chithunzi A: Iyi ndi ndalama ya Herode Antipa yomwe inatuluka mu 30 C.E. Analembapo kuti: “Herode Wolamulira Chigawo”
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yohane anali “ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya”? (Luka 1:17; it “Mzimu” ¶60-wcgr) B
Chithunzi B
4. N’chiyani chikusonyeza kuti Yohane sanaukitsidwe n’kupita kumwamba? (Mat. 11:11; ijwbq nkhani 178 ¶4)
Phunzirani Zambiri
Ngakhale kuti Yohane anakwaniritsa ulosi komanso anali kalambulabwalo wa Mesiya, anali wodzichepetsa. (Yoh. 1:26, 27) Kodi tikuphunzira chiyani kwa iye?
Yohane ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo maganizo ake onse anali pa kuchita chifuniro cha Mulungu. (Mat. 3:4) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala moyo wosalira zambiri masiku ano? C
Chithunzi C
Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yohane M’batizi?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzafunsa chiyani Yohane M’batizi akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onani zimene zinathandiza Yohane kuti azipirira mosangalala komanso moleza mtima.
“Yohane M’batizi Chitsanzo Chabwino pa Nkhani Yokhalabe Wosangalala” (w19.08 29-31)
Kodi chitsanzo cha Yohane chingatithandize bwanji kupirira mavuto azachuma, kuzunzidwa komanso kukhumudwitsidwa?