45 PETULO
“Ndine Munthu Wochimwa”
PETULO anali msodzi wakhama ndipo ankagwira ntchitoyi limodzi ndi anthu am’banja lake. Iye anali wolimba mtima kwambiri. Petulo sankachedwa kunena maganizo ake ndiponso kuchita zimene akuona kuti n’zofunika. Tsiku lina mchimwene wake Andireya anamuuza mosangalala kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.” Pasanapite nthawi Petulo anakhala wotsatira wa Yesu.
Patadutsa miyezi ingapo, Yesu anapita ku Kaperenao kumene Petulo ankakhala. Petulo anali atagwira ntchito yosodza usiku wonse koma osapha nsomba. Yesu anamuuza kuti apalasire ngalawa kwakuya n’kuponya maukonde. Petulo ankakayikira zoti angaphe nsomba chifukwa nthawi zambiri, masana asodzi sankapha nsomba. Iye anati: “Ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse.” Komabe anachita zomwe anauzidwazo. Pasanapite nthawi yaitali anagwira nsomba zambiri moti ngalawa ziwiri zinadzaza n’kuyamba kumira. Petulo anachita mantha ndipo anagwada pamaso pa Yesu n’kumuuza kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano chifukwa ndine munthu wochimwa.” Iye ankadziona kuti ndi wochimwa kwambiri moti sakuyenera kukhala ndi Mwana wa Mulungu amene ankachita zodabwitsa. Koma Yesu anamulimbikitsa pomuuza kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”
Yesu anaona makhalidwe abwino amene Petulo anali nawo ndipo patapita nthawi anamusankha kuti akhale mmodzi mwa atumwi ake 12. Petulo anasonyeza kulimba mtima m’njira zambiri. Mwachitsanzo, Yesu akanena zinthu zovuta kumvetsa, ophunzira ena ankaopa kufunsa, koma iye ankalankhula n’kumupempha kuti afotokoze bwinobwino. Komanso Yesu akuyenda pamadzi, Petulo analimba mtima n’kupempha kuti nayenso ayende nawo.
Nthawi zambiri Petulo ankafulumira kulankhula. Choncho akadzudzulidwa, ankafunika kulimba mtima kuti akhalebe wokhulupirika
Petulo anasonyeza kulimba mtima m’njira inanso. Munthu akadzudzulidwa amafunika kulimba mtima ndi kudzichepetsa kuti adzifufuze moona mtima, kuvomereza zimene walakwitsa kenako n’kukonza zolakwikazo. Petulo ankachita zimenezi mobwerezabwereza. Mwachitsanzo, Yesu ataneneratu za imfa yake, Petulo analakwitsa n’kumudzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye.” Yesu anamudzudzula mwamphamvu chifukwa cholankhula zinthu zosemphana ndi chifuniro cha Mulungu ngati zimene akanalankhula Satana. Zitatero, Petulo anadzichepetsa n’kulandira malangizowo.
Pa usiku wake womaliza, Yesu ankafuna kuphunzitsa atumwi ake kufunika kwa kudzichepetsa. Choncho anayamba kuwasambitsa mapazi ngati mmene kapolo angachitire. Koma Petulo anakana n’kunena kuti: “Ndithu, sizitheka kuti musambitse mapazi anga.” Zitatero Yesu anamudzudzula. Ndiye m’malo mongovomera, anapitirira malire n’kuuza Yesu kuti amusambitsenso manja ndi mutu womwe. Atatero Yesu anamudzudzulanso. Patapita nthawi, Yesu ananena kuti atumwi ake onse adzamuthawa. Koma Petulo ananena kuti ngakhale atumwi onse atamuthawa Yesuyo, iye sangamuthawe. Yesu anayankha kuti usiku umenewo Petulo amukana katatu.
Patangopita maola ochepa, asilikali anabwera n’kudzagwira Yesu. Petulo analimba mtima n’kumawatsatira chapatali. Asilikaliwo anapita ndi Yesu kunyumba ya mkulu wa ansembe komwe anthu ankamunenera zachipongwe komanso kumuimba mlandu wabodza. Pa nthawiyi, Petulo anali m’bwalo la nyumbayi. Ndiyeno anthu ena anazindikira kuti Petulo anali mmodzi wa ophunzira a Yesu. Koma mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, Petulo anamukana katatu.
Pa nthawi imeneyo, anthu anatuluka ndi Yesu m’nyumbamo ndipo iye anayang’ana Petulo. Petulo anamva chisoni kwambiri ndi zimene anachitazi moti “anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.” Patapita maola angapo Yesu anaphedwa mwankhaza ndipo Petulo ayenera kuti zinamupweteka kwambiri mumtima. Koma sanalole kuti afooke chifukwa cha zimene analakwitsazi. Iye anatsimikiza mtima kuti apitiriza kutumikira Mulungu. Ndiye kodi anatani? Iye anapita kukakumana ndi atumwi anzake. Kenako Yesu ataukitsidwa, anaonekera kwa Petulo, Petuloyo ali yekha. Baibulo silinena zimene anakambirana pa nthawiyo, koma zikuoneka kuti Petulo analimbikitsidwa kwambiri chifukwa Yesu anamukhululukira.
Patapita mawiki angapo, Yesu anakumana ndi atumwi ake pa nyanja ya Galileya ndipo anapereka mphatso yapadera kwa Petulo. Paja Petulo anakana Yesu katatu. Choncho Yesu anamupatsanso mwayi maulendo atatu woti asonyeze kuti amakonda Mbuye wakeyu. Kenako Yesu anapatsa Petulo udindo wofunika kwambiri. Anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” Monga tionere m’Mutu 49, Petulo anachitadi zimenezi molimba mtima kwambiri.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Malinga ndi nkhaniyi, kodi Petulo anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi Petulo ankachita zinthu ziti pa ntchito yake yausodzi? (it “Kusaka Nyama Komanso Kupha Nsomba” ¶6-7-wcgr) A
Chithunzi A
2. N’chifukwa chiyani Yesu anapatsa Simoni dzina lakuti Kefa (Petulo)? (“Iwe ndiwe Simoni,” mfundo yothandiza kuphunzira pa Yohane 1:42, nwtsty-wcgr)
3. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza Petulo ndi Andireya kuti ndikusandutsani “asodzi a anthu”? (Mat. 4:18-20; w16.05 9 ¶3-4) B
Chithunzi B
4. Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba anafunsa Petulo kuti: “Kodi umandikonda ine kuposa izi?” Kodi n’kutheka kuti Yesu ankatanthauza chiyani? (“kodi umandikonda ine kuposa izi?” mfundo yothandiza pophunzira pa Yoh. 21:15, nwtsty-wcgr)
Phunzirani Zambiri
Kodi tikuphunzira chiyani kwa Petulo pa nkhani yopitiriza kutumikira Yehova ngakhale kuti timalakwitsa zinthu zina mobwerezabwereza? C
Chithunzi C
Kodi kuganizira mmene Yehova ndi Yesu anakhululukira Petulo kungakuthandizeni bwanji?
Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kumene Petulo anasonyeza komwe kwafotokozedwa munkhaniyi?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndi zinthu ziti zokhudza Petulo zomwe mwaphunzira munkhaniyi zimene zikukusangalatsani mukaganizira zoti iye adzalamulira ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Kodi makolo angagwiritse ntchito bwanji chitsanzo cha Petulo pophunzitsa ana awo zokhudza chifundo cha Yehova?
Onani mmene Petulo anasonyezera kukhulupirika anthu ambiri atasiya kutsatira Yesu.