Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 46 tsamba 208-tsamba 211
  • “Ambuye Ndawaona Ine!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ambuye Ndawaona Ine!”
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Analimba Mtima N’kuvomera
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • “Wachita Zimene Akanatha”
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 46 tsamba 208-tsamba 211

46 MARIYA WA KU MAGADALA

“Ambuye Ndawaona Ine!”

Losindikizidwa
Losindikizidwa

MARIYA wa ku Magadala anakumana ndi mavuto aakulu. Ziwanda zinkamuvutitsa, kumuopseza komanso kuchititsa kuti moyo wake ukhale wovuta kwambiri. Koma zinthu zinasintha pa moyo wake atakumana ndi Yesu. Baibulo limanena kuti Yesu “anamutulutsa ziwanda 7.” Mariya anayamikira kwambiri zimenezi ndipo molimba mtima anasankha kuti akhale wotsatira wa Yesu n’kumamuthandiza mmene angathere.

Iye anatchula Yesu, Ambuye wake wokondedwa, ndi mawu aulemu kwambiri akuti Rabboni omwe amatanthauza “Mphunzitsi.” Yesu ndi atumwi ake 12 ankayenda m’madera osiyanasiyana n’kumaphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu. Mariya anaona kuti anthuwa anasiya ntchito zawo kuti azigwira ntchito yofunikayi. Ndiye kodi iye ankawathandiza bwanji?

Poyamba moyo wa Mariya unali wovuta kwambiri koma kenako anadzipereka kuti azithandiza Yesu ndi otsatira ake

Mariya anali mmodzi mwa azimayi “amene ankatumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.” Azimayi amenewa ankagwiritsa ntchito ndalama zawo pothandiza Yesu ndi atumwi ake. N’kutheka kuti onse pamodzi analipo ophunzira 20, amuna ndi akazi amene ‘ankayenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi.’ Mogwirizana ndi chikhalidwe chawo, zinali zachilendo kuti azimayi aziyenda ndi mtsogoleri wachipembedzo, choncho azimayiwa ayenera kuti ankanyozedwa. Koma Mariya ndi anzakewo sankadandaula ndi zimenezi ndipo ankaona kuti zimene ankachitazo zinali zofunika kwambiri. Iwo analimba mtima n’kumathandiza Yesu posatengera kuti anthu aziganiza zotani.

Mariya ayenera kuti anamva chisoni kwambiri pamene Yesu anamangidwa pamwambo wa Pasika usiku wina ku Yerusalemu. Iye ankaimbidwa mlandu wabodza wakuti ananyoza Mulungu ndipo anaweruzidwa kuti aphedwe pamtengo wozunzikirapo. Koma Mariya anakhalabe wolimba mtima. Iye ndi azimayi ena, kuphatikizapo mayi a Yesu, anapita nawo kumalo amene Yesu anaphedwera. Ndipo anapitiriza kumusonyeza chikondi, kumuthandiza komanso anakhalabe okhulupirika kwa iye. Pa nthawi imene Yesu ankazunzika kwambiri, ankaona azimayi okhulupirikawa. Iwo anaona Yesu akukhalabe wokhulupirika mpaka kumaliza zonse zimene Atate wake anamutuma. Mariya analipo mpaka pamene Yesu ankatsirizika.

Mariya wa ku Magadala akutonthoza mayi a Yesu ndipo onse akuona Yesu akuvutika pamtengo wozunzikirapo. Atsogoleri achipembedzo a Chiyuda akuwayang’anitsitsa, asilikali a Chiroma aima chapafupi ndipo anthu ena omwe aima chapatali akulira.

Azimayi olimba mtimawa anamulira Yesu ndipo sanaope asilikali a Chiroma komanso atsogoleri achipembedzo a Chiyuda. Koma Mariya wa ku Magadala anali wofunitsitsa kuchitiranso Ambuye wake wokondedwayo chinthu china. Iye anasamalira thupi la Yesu. Nyengo ya ku Yudeya inali yotentha kwambiri ndipo thupi silinkachedwa kuwonongeka. Choncho pofuna kuti athe kumulira bwinobwino munthu amene wamwalira, anthu ankapaka thupi lake mafuta onunkhira komanso zonunkhiritsa zina asanaliike m’manda. Mariya anachita zimenezi Yesu atangoikidwa m’manda. Tsiku la Sabata litangotha, Mariya ndi azimayi ena anagula zinthu zimenezi ndipo analawirira m’mawa n’kupita kumanda a Yesu kuti akapake thupi lake.

N’kutheka kuti Mariya ndi amene anali woyambirira kufika kumandako koma anadabwa kwambiri kuona kuti mandawo anali otsegula ndipo munalibe chilichonse. Zitatero anathamanga kukadziwitsa Petulo ndi Yohane. Atabwereranso kumandako anapeza azimayi ena aja atapita. Mariya anasuzumira m’mandamo “ndipo anaona angelo awiri amene anavala zoyera atakhala pamene panali mtembo wa Yesu.” Atalankhula nawo kwakanthawi, anatembenuka ndipo anaona bambo wina amene ankamuganizira kuti ndi wosamalira mundawo. Bamboyo anamufunsa kuti: “Mayi iwe, nʼchifukwa chiyani ukulira?” Iye anafunsa komwe kunali mtembo wa Yesu kenako anati: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika ndipo ine ndikamutenga.” Mariya sanaime kaye kuti aganizire ngati akanakwanitsadi kunyamula mtembo wa Yesu. Ankangoona kuti akuyenera kuchita zonse zimene angathe.

Mwachisoni Mariya anatembenuka, koma anamva bambo uja akumuitana kuti, “Mariya!” Nthawi yomweyo anamuzindikira ndipo anakuwa kuti “Rabboni!” n’kumugwira. Koma Yesu sanalole kuti apitirize kumugwira chifukwa ankafuna kumupatsa ntchito yofunika kwambiri. Anamuuza kuti: “Pita kwa abale anga.” Yesu anamutuma kuti akauze atumwi ake uthenga wofunika kwambiri wakuti Mbuye wawo waukitsidwa. Mariya anapita nthawi yomweyo. Poyamba atumwiwo sanamukhulupirire. Baibulo limati: “Kwa iwo, zimene ankawauzazo zinkaoneka ngati zopanda pake.” Koma zimenezi sizinamufooketse ndipo palibenso chilichonse chimene chinamufooketsa. Iye anapitirizabe kuuza anthu uthenga wabwinowu molimba mtima.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Mateyu 27:​55, 56

  • Maliko 16:​1, 2

  • Luka 8:​1-3; 24:​1-11

  • Yohane 19:25; 20:​1, 2, 11-18

Funso lokambirana:

Kodi Mariya wa ku Magadala anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi Mariya wa ku Magadala ndi azimayi ena ayenera kuti ankathandiza Yesu ndi atumwi ake m’njira ziti? (ijwia nkhani 6 ¶5-6) A

    Mariya wa ku Magadala akupereka moni kwa Yesu ndi atumwi ake awiri omwe akulowa m’nyumba mwake. Azimayi ena akuphika buledi komanso kusoka zovala mosangalala.

    Chithunzi A

  2. 2. N’chifukwa chiyani Mariya poyamba sanamuzindikire Yesu ataukitsidwa? (ijwia nkhani 6 ¶16)

  3. 3. N’chifukwa chiyani Yesu anauza Mariya wa ku Magadala kuti asamukangamire? (w08 4/15 32 ¶6)

  4. 4. Atumwi ankaganiza kuti zimene Mariya wa ku Magadala ankanena zoti Yesu waukitsidwa ndi “zopanda pake.” N’kutheka kuti n’chiyani chinawachititsa kuti aziganiza choncho? (Luka 24:11; w12 9/1 10 ¶4-5)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Mariya wa ku Magadala ankagwira ntchito zooneka ngati zonyozeka pothandiza ena. Kodi tingamutsanzire bwanji? B

    Alongo atatu akugawira abale chakudya mosangalala pamalo a zomangamanga.

    Chithunzi B

  • Kodi tingatsanzire bwanji Mariya wa ku Magadala ngati anthu ena sakukhulupirira uthenga wa m’Baibulo umene timalalikira? (Luka 24:​10, 11)

  • Kodi inuyo mungatsanzire bwanji Mariya wa ku Magadala pa nkhani ya kulimba mtima?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi mukumva bwanji mukaganizira zoti Mariya wa ku Magadala ayenera kuti ali m’gulu la anthu omwe anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba, ndipo n’chifukwa chiyani mukumva choncho?

Phunzirani Zambiri

Yerekezerani zinthu zabodza zokhudza Mariya wa ku Magadala ndi mfundo zoona zopezeka m’Baibulo.

“Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?” (ijwbq nkhani 172)

Kodi tiyenera kumawaona bwanji azimayi tikaganizira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi Mariya wa ku Magadala komanso azimayi ena?

“Akazi a Chikhristu Ayenera Kupatsidwa Ulemu” (w95 7/15 15-18 ¶3-8-wcgr)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena