47 MARIYA, MCHEMWALI WAKE WA LAZARO
“Wachita Zimene Akanatha”
MARIYA anakhudzidwa kwambiri ndi kukoma mtima kwa Yesu Khristu. Yesu anali atamuchitira zambiri iyeyo, mchemwali wake Marita komanso mchimwene wawo wokondedwa Lazaro. Yesu anali atakhala nawo kunyumba kwawo ku Betaniya maulendo angapo n’kumawaphunzitsa zokhudza iyeyo komanso Yehova. Yesu ankakonda kwambiri Mariya, Marita komanso Lazaro. Ndipo Lazaro atamwalira, Yesu anamuukitsa.
Mariya ankafuna kuchitira Ambuye wake Yesu chinthu chapadera. Iye anaganiza zomupatsa mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Mphatso yake inali mafuta onunkhira a “nado weniweni, okwera mtengo kwambiri, okwana magalamu 327” ndipo anali m’botolo la alabasitala. Nthawi imeneyo, munthu ankafunika kugwira ntchito pafupifupi chaka chonse kuti apeze ndalama zokwanira kugula mafuta onunkhira okwana m’botolo laling’ono limeneli. Baibulo silifotokoza kuti Mariya anapeza bwanji mafuta onunkhirawa komanso kuti anawapeza liti. Koma ayenera kuti anali odula kwambiri pa zinthu zonse zimene iye anali nazo.
Mariya ankafunitsitsa kupatsa Yesu mphatso yamtengo wapatali ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti anthu ena amunyoze
Tsiku lina Yesu akudya chakudya kunyumba ya munthu wina ku Betaniya, Mariya anaganiza zopereka mphatso yake ija. Iye anafika pamene panali Yesu, n’kutsegula botolo lija mochita kuliswa kenako anathira mafutawo pamutu pa Yesu ndiponso m’mapazi ake. Atamaliza kumuthira mafutawo, anachotsa mpango womwe anavala kumutu kwake ndipo anayamba kupukuta mapazi a Yesu pogwiritsa ntchito tsitsi lake. Malinga ndi chikhalidwe chawo, ena akanaona kuti zinali zosayenera kuti Mariya avule mpango kumutu kwake. Koma Mariya ankaona kuti chofunika kwambiri ndi kulemekeza Ambuye wake ndipo anadzichepetsa n’kuchita zimenezi.
M’nyumba monsemu munadzaza kafungo konunkhira ka mafutawo. Koma anthu ena sanasangalale nazo. Mwachitsanzo, Yudasi Isikariyoti anakwiya ndi zimene Mariya anachitazi moti anachititsa kuti atumwi enanso ayambe kuona ngati Mariya wachita zolakwika. Yudasi ananena kuti: “Nʼchifukwa chiyani mafuta onunkhirawa sanagulitsidwe madinari 300 nʼkupereka ndalamazo kwa anthu osauka?” Kodi mukuganiza kuti Mariya anamva bwanji? Iye ankakonda kwambiri Yesu ndipo anapereka mphatso yapaderayi ndi mtima wake wonse. Koma m’malo momuyamikira, atumwi a Yesuwa anakwiya nazo kwambiri. Mariya ayenera kuti anachita manyazi. Koma Yesu anamuikira kumbuyo.
Yesu anauza anthuwo kuti: “Musiyeni.” Atanena mawu amenewa, atumwiwo ayenera kuti anakhala chete. Kenako Yesu ananena kuti, “Iyetu wandichitira zinthu zabwino.” Ndipo anafotokoza kuti Mariya anasonyeza chikondi pomuchitira zimenezi. Mariya sankadziwa kuti Yesu watsala pang’ono kuikidwa m’manda ndipo kumudzoza mafuta onunkhirawa kunali kukonzekera mwambo womvetsa chisoni umenewo. Yesu anafotokoza mwachidule zimene Mariya anachitazi ndi mawu osaiwalika akuti: “Wachita zimene akanatha.” Kenako anawonjezera kuti: “Ndithu ndikukuuzani, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe padziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzamukumbukira.” Yesu anaona kuti zimene Mariya anachitazi zinasonyeza kuti anali wolimba mtima komanso wachikondi. Mariya anafunika kuyamikiridwa chifukwa cha mtima wopatsa umene anasonyezawu, osati kuimbidwa mlandu.
Zitatero, palibe aliyense amene analankhulanso chilichonse chotsutsana ndi zimene Mariya anachita. Kenako Yudasi anachoka n’kukayamba kukonza zoti apereke Yesu. Mariya ayenera kuti anayamikira zimene Yesu anachita pomuikira kumbuyo ndipo ankaziganizirabe. Patadutsa masiku ochepa, zimene Yesu ananena zokhudza kuikidwa kwake m’manda, zinachitikadi ndipo Mariya ayenera kuti anamvetsa bwino zimene Yesu ankatanthauza. Mogwirizana ndi zimene ananeneratu, Yesu anamangidwa, kuimbidwa milandu yabodza, kuweruzidwa kuti ndi wolakwa, kuphedwa ndiponso kuikidwa m’manda. Mariya anali wokoma mtima komanso wachikondi. Choncho ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona Yesu akuvutika komanso kuphedwa. Pa nthawi yovuta imeneyi, ayenera kuti ankalimbikitsidwa akaganizira zimene Yesu anamuuza zija.
Pa tsiku lachitatu kuchokera pamene Yesu anaphedwa, panachitika chinthu chapadera. Ambuye Yesu anaukitsidwa. Pasanapite nthawi yaitali, Yesu anaonekera kwa otsatira ake oposa 500. N’kutheka kuti pa nthawiyi ndi pamene anawalamula kuti azilalikira uthenga wabwino kwa “anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:19, 20) Paja iye ananena kuti “uthenga wabwino” umenewu uzidzaphatikizapo nkhani yonena kuti Mariya anamusonyeza kudzichepetsa komanso chikondi. N’zosachita kufunsa kuti Mariya sankanong’oneza bondo akaganizira kuti analimba mtima n’kupereka kwa Ambuye wake zonse zimene akanatha. Ayenera kuti pa moyo wake wonse ankakumbukirabe kuti Yesu anamuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwake pamene ananena mawu akuti, “Wachita zimene akanatha.”
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Mariya, mchemwali wake wa Lazaro, anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza makhalidwe a Mariya ndi mchemwali wake Marita? (Luka 10:39, 40; Yoh. 11:20; ia 173 ¶5-6; 176 ¶17) A
Chithunzi A
2. Kodi Yesu ankasiyana bwanji ndi aphunzitsi ena pa nkhani yophunzitsa akazi? (w99 9/1 30 ¶1-4-wcgr)
3. N’chifukwa chiyani mafuta amene Mariya anadzoza Yesu anali amtengo wapatali kwambiri? (“mafuta onunkhira okwera mtengo” mfundo yothandiza pophunzira pa Mat. 26:7, nwtsty-wcgr) B
Indian nard: © Haijie Lu, licensed under CC BY-NC 4.0. Source; dried jatamansi: wasanajai/stock.adobe.com; alabaster jar: © The Trustees of the British Museum. Licensed under CC BY-NC-SA 4.0. Source
Chithunzi B: Botolo la mafuta onunkhira a alabasitala. Duwa komanso mizu ya Nardostachys jatamansi. Mwina chomera chimenechi ndi chimene ankagwiritsa ntchito popanga mafuta amene Mariya anathira Yesu
4. Kodi zimene Mariya anachita pothira Yesu mafuta, osati m’mutu mokha komanso mapazi, zinasonyeza chiyani? (w10 11/1 6 ¶4, mawu a m’munsi)
Zomwe Tikuphunzirapo
Yesu ananena kuti ‘Mariya anasankha chinthu chabwino kwambiri,’ kutanthauza kuti anaika zinthu zauzimu pamalo oyamba. (Luka 10:42) Kodi tingamutsanzire bwanji masiku ano? C
Chithunzi C
Yesu anayamikira Mariya chifukwa ‘anachita zimene akanatha.’ Kodi zimenezi zikutiphunzitsa kuti Yehova amaona kuti chofunika ndi chiyani pa zimene timachita? (Maliko 12:29, 30; 14:8)
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Mariya m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira kuti Mariya, mchemwali wake wa Lazaro, ali m’gulu la anthu omwe akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Mariya, Marita ndi Yesu pa nkhani yosankha anthu ocheza nawo?
Yesu anayamikira mphatso yodula ya Mariya komanso anayamikira tindalama tiwiri timene mayi wamasiye anapereka. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yesu?
“Kodi Mumayamikira?” (w99 4/15 16 ¶3-7-wcgr)