49 PETULO
Anadzakhala Thanthwe
YESU atangokumana ndi Simoni anamupatsa dzina latsopano. Iye anati: “Iwe ndiwe Simoni mwana wa Yohane, dzina lako likhala Kefa.” Zikuoneka kuti dzina lakuti “Kefa” lomwe m’Chigiriki ndi “Petulo,” limatanthauza “Mwala.” N’chifukwa chiyani Yesu anamupatsa dzina limeneli? Mwala umakhala wolimba ndipo umagwiritsidwa ntchito pomanga nyumba. Zikuoneka kuti ponena zimenezi Yesu ankatanthauza kuti Petulo adzakhala ngati mwala.
Kodi Petulo ankachitadi zinthu ngati mwala? Mogwirizana ndi zimene tinaphunzira m’Mutu 45, si nthawi zonse pamene Petulo ankachita zinthu ngati mwala. Petulo ankakayikira zinthu zina ndipo nthawi zina ankachita zinthu chifukwa cha mantha. Ngakhale zinali choncho, Yesu ankamukhulupirirabe. Iye sankakayikira kuti pakapita nthawi Petulo adzasintha n’kukhala munthu wolimba mtima. Kodi ndi zimene zinachitikadi?
Khristu ataphedwa n’kuukitsidwa, anapatsa atumwi ake ntchito yofunika kwambiri. Petulo anali wofunitsitsa kugwira ntchitoyi. Anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Pachikondwerero china ku Yerusalemu, iye anaimirira pagulu la anthu omwe anasonkhana ndipo analankhula molimba mtima kuti iwo ndi amene anapha Mesiya. Chifukwa cha zimenezi, ambiri mwa anthuwa “anavutika kwambiri mumtima” ndipo analapa. Kenako anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu.
Kodi n’chiyani chinathandiza Petulo kukhala munthu wa chikhulupiriro cholimba komanso wolimba mtima ngati mmene Yesu ananenera?
Pa moyo wake wonse, Petulo ankagwira mwakhama ntchito yolalikira ndipo ankaiona kuti ndi yofunika kwambiri. Yesu anamupatsa “makiyi a Ufumu” posonyeza kuti ankamudalira. Anamupatsa udindo woti athandize magulu atatu a anthu kuti akhale ndi mwayi wodzalamulira ndi Yesu kumwamba. Choncho Petulo analalikira molimba mtima komanso mosakondera kwa Ayuda kenako kwa Asamariya ndipo pomaliza, kwa anthu a mitundu ina. Ankapita kukalalikira kumadera akutali ndipo nthawi zina ankayenda ndi mkazi wake kukalimbikitsa Akhristu anzawo. Komanso anasamukira kutali ku Babulo n’kumakalalikira.
Kwa zaka zambiri, Petulo akamagwira ntchitoyi ankakumana ndi mavuto ambiri komanso kupirira akamatsutsidwa. Iye ndi atumwi anzake anaikidwa m’ndende maulendo angapo. Pa nthawi ina, atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda anawalamula kuti asiye kulalikira. Koma Petulo anawayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” Ngakhale kuti anamenyedwa, iwo sanasiye kulalikira za Ufumu wa Mulungu ndi Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu imene Yehova anaisankha.
Anthu amene ankadana ndi Akhristu anayamba kuzunza kwambiri Akhristuwo. Munkhani yapita ija, tinaona kuti Sitefano anaphedwa. Patadutsa pafupifupi zaka 10, mtumwi Yakobo yemwe anali mnzake wa Petulo nayenso anaphedwa chifukwa cha zimene ankakhulupirira. Herode yemwe anachititsa kuti Yakobo aphedwe ataona kuti Ayuda asangalala ndi zimenezi, analamula kuti Petulo amangidwe. Petulo anamangidwa ndi unyolo n’kutsekeredwa m’ndende ndipo asilikali ankamulondera. N’kutheka kuti pa nthawiyi iye ankaganizira zomwe Yesu anamuuza m’mbuyomo kuti adzamangidwa kenako n’kuphedwa.
Mwadzidzidzi mngelo anafika m’ndendemo pakati pa usiku. Anadzutsa Petulo, kumumasula unyolo uja kenako n’kumutulutsa m’ndendemo. Zitatero anadutsa naye pamene panali asilikali apageti, kudutsa pageti lalikulu la ndendeyo n’kukafika mumsewu. Ndiye kodi Petulo anatani? M’malo mothawira kutali, iye anapita kunyumba ina komwe ankadziwa kuti abale ndi alongo asonkhana kuti alambire Yehova ndiponso kupemphera. Petulo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ataona abale ndi alongo akewa.
Petulo sanaiwale zimene Ambuye wake anamuuza kuti, “Ukalimbikitse abale ako” komanso kuti, “Dyetsa ana a nkhosa anga.” (Luka 22:32; Yoh. 21:17) Iye ankalalikira molimba mtima komanso kulimbikitsa anthu a Mulungu kulikonse komwe wapita. Komatu iye sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Pa nthawi ina, chifukwa choopa anzake anasankha zinthu molakwika ndipo mtumwi wina anamudzudzula. Koma Petulo anadzichepetsa n’kuphunzirapo kanthu pa zomwe analakwitsazo moti anapitiriza kulimbikitsa abale ndi alongo ake. Analemba makalata awiri ouziridwa omwe anaikidwa m’Baibulo. Atatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, Petulo anamangidwanso n’kuikidwa m’ndende komaliza ndipo anaphedwa. Pa nthawi yonseyi, iye anasonyezabe chikhulupiriro komanso kulimba mtima. Apa n’zoonekeratu kuti anakhaladi “thanthwe.”
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Petulo anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti pambuyo poti Yesu waphedwa n’kuukitsidwa?
Zoti Mufufuze
1. Yesu anapereka “makiyi a Ufumu” kwa Petulo. Kodi iye anawagwiritsa ntchito bwanji? (Mat. 16:18, 19; ijwbq nkhani 124 ¶1-5) A
Chithunzi A: Petulo analalikira uthenga wa Ufumu kwa Ayuda ku Yerusalemu, kwa Asamariya ku Samariya komanso kwa anthu amitundu ina ku Kaisareya
2. Kodi timadziwa bwanji kuti Petulo analibe tsankho ngakhale asanapite kwa Koneliyo yemwe sanali Myuda? (Mac. 10:5-7, 23; bt 69 ¶1, mawu a m’munsi) B
Chithunzi B: Pamene panali mzinda wakale wa Yopa
3. Kodi timadziwa bwanji kuti Petulo anatsatira malangizo omwe Paulo anamupatsa? (w17.04 26-27 ¶15-17)
4. N’chifukwa chiyani Petulo anasamukira ku Babulo? (it “Kutengedwa Kupita ku Ukapolo” ¶24-wgcr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Petulo analankhula molimba mtima koma mwaulemu ku gulu la anthu ku Yerusalemu. Kodi ndi pa nthawi iti imene nafenso timafunika kuchita zinthu molimba mtima komanso mwaulemu?
Ngakhale kuti Petulo anali ndi udindo waukulu mumpingo, anatsatira malangizo a Paulo. Kodi tingamutsanzire bwanji? C
Chithunzi C
Mogwirizana ndi zomwe taphunzira munkhaniyi, kodi tingasonyeze kulimba mtima ngati Petulo m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira zoti Petulo anasankhidwa kukalamulira ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Kodi chitsanzo cha Petulo chingatithandize bwanji kudalira Yehova komanso kuthetsa mantha?
Gwiritsani ntchito ‘zoti muchitezi’ kuti muphunzire zambiri zokhudza nkhani yopezeka pa Machitidwe chaputala 10.
“Mulungu Alibe Tsankho” (Nkhani zapawebusaiti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo”)