Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg tsamba 246-255
  • “Tikhale Olimba Mtima”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tikhale Olimba Mtima”
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunika kwa Pemphero
  • “Limbani Mtima”
  • ‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Mukhoza Kukhala Olimba Mtima Kwambiri
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Khalani Olimba Mtima!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • ‘Khalani Olimba Mtima Kwambiri Ndipo Muchite Zinthu Mwamphamvu’
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg tsamba 246-255

MAWU OMALIZA

“Tikhale Olimba Mtima”

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

1. Kodi tingaphunzirenso chiyani pa nkhani ya kulimba mtima?

PAMENE tamaliza kuphunzira bukuli, kodi palinso zina zimene tinganene zokhudza kulimba mtima? Inde zilipo. Choyamba, dziwani kuti Baibulo limanena zambiri zokhudza nkhani yofunika imeneyi kuposa zimene tingakambirane m’buku limodzi. Chachiwiri, tingafunike kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti tipindule kwambiri ndi nkhani za m’Baibulo zokhudza kulimba mtima.

2. Kodi ndi atumiki a Mulungu ena ati amene anasonyeza kulimba mtima?

2 Kodi pali anthu enanso otchulidwa m’Baibulo omwe mukuwaganizira amene anasonyeza kulimba mtima kupatula amene takambirana m’bukuli? Mwina mungaganizire za ena mwa aneneri odziwika bwino otchulidwa m’Malemba a Chiheberi monga Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Yona komanso Malaki. N’zosachita kufunsa kuti mtumwi Paulo ankanena za anthu ngati amenewa pamene analemba kuti ena “anakumana ndi mayesero chifukwa ananyozedwa komanso kukwapulidwa. Kuwonjezera pamenepo anamangidwa ndiponso kutsekeredwa mʼndende.” Analembanso kuti ena “ankasowa zinthu, ankazunzidwa komanso ankakumana ndi mavuto ena” ndipo enanso anaphedwa. (Aheb. 11:​36, 37) Komabe anapitiriza kutumikira Yehova molimba mtima.

3-4. Kodi azimayi awiri omwe mayina awo sanatchulidwe anathandiza bwanji kupulumutsa Davide pa nthawi yovuta?

3 M’Baibulo muli anthu ambiri amene anachita zinthu molimba mtima omwe mayina awo sanatchulidwe. Taganizirani za azimayi awiri a nthawi ya Mfumu Davide. Azimayiwa anathandiza Davide pamene mwana wake Abisalomu ankafuna kumupha. Abisalomu anali wonyada komanso woipa ndipo ankafuna kulanda ufumu wa bambo ake zomwe zinachititsa kuti bambo akewo athawe ku Yerusalemu. Davide anapempha Zadoki, yemwe anali wansembe wolimba mtima, kuti abwerere ku Yerusalemu n’cholinga choti azimuuza mapulani a Abisalomu. ‘Wantchito wina wamkazi’ anaika moyo wake pa ngozi n’kufotokozera atumiki okhulupirika awiri a Davide uthenga wochokera kwa Zadoki. Anthu awiriwa ananyamuka kuti akapereke uthengawu kwa Davide koma munthu wina anawaona ndipo anakauza Abisalomu. Zitatero anthuwa anachita zinthu mwanzeru ndipo anabisala m’chitsime. Ndiyeno mkazi wina, yemwe sanatchulidwenso dzina, amene anali mkazi wa mwiniwake wa chitsimecho, anatenga chinsalu nʼkuchiyala pamwamba pa chitsimepo, kenako anaunjikapo tirigu. Anthu otumidwa ndi Abisalomu atabwera kudzawafufuza, mayiyu anawalozera kwina. Zimene azimayi olimba mtima amenewa anachita, zinathandiza kuti mfumu yosankhidwa ndi Yehova itetezedwe.—2 Sam. 15:​23-37; 17:​8-22.

Zithunzi: Akazi awiri omwe sanatchulidwe mayina amene anasonyeza kulimba mtima poteteza Mfumu Davide. 1. Wantchito wamkazi akulankhula ndi atumiki awiri a Davide. 2. Mayi amene anabisa atumiki a Davide m’chitsime, akuganizira pamene azibambo awiri akuchoka panyumba pake.

Wantchito wamkazi wolimba mtima komanso mayi wolimba mtima amene anakwatiwa ndi mwini chitsime.

4 Kunena zoona, m’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anasonyeza kulimba mtima. Limatchula za amuna ndi akazi amene anachita zinthu molimba mtima n’kukhala kumbali ya Yehova. Ena anatchulidwa mayina ndipo ena sanatchulidwe, ena anali olemera pomwe ena anali osauka, enanso anali otchuka pamene ena sanali otchuka. Nkhani za anthu amenewa zingatithandize masiku ano.

Kufunika kwa Pemphero

5-7. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti akhale wolimba mtima pamene ankatsutsidwa kwambiri?

5 Kodi tingatsanzire bwanji anthu olimba mtima otchulidwa m’Baibulo? Tiyenera kudziwa kuti anthu amenewa sanali olimba mtima mwachibadwa. Komanso sankatumikira Yehova chifukwa cha mphamvu zawo. Ndiye kodi n’chiyani chinawathandiza kuti azichita zinthu molimba mtima?

6 Taganizirani zimene zinathandiza mtumwi Paulo kuti akhale wolimba mtima. Paulo ndi Sila ali ku Filipi, gulu la anthu linawaukira, kuwavula zovala, kuwamenya ndi ndodo ndipo kenako anawatsekera m’ndende atawamanga mapazi awo m’matangadza. (Mac. 16:​12, 19-24) Atawatulutsa m’ndendemo, kodi Paulo anachita mantha? Popeza iye anali munthu ngati ife tomwe anangoyenera kuchita mantha. Komabe Paulo ankafunika kuchita utumiki umene Yehova anamupatsa. Iye anafunika kukalalikira mumzinda wa Tesalonika. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apeze mphamvu komanso akhale wolimba mtima?

7 Patapita nthawi iye analemba kuti: “Ngakhale kuti poyamba tinavutika komanso kuchitiridwa zachipongwe ku Filipi, monga mmene mukudziwira, tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu pa nthawi imene anthu ankatitsutsa kwambiri.” (1 Ates. 2:2) Paulo ankadziwa kuti ankafunika kukhala wolimba mtima kuti akwanitse kuchita zimene Mulungu ankafuna. Koma iye sanakhale wolimba mtima payekha. M’malomwake analimba mtima “mothandizidwa ndi Mulungu wathu.” Paulo anapempha Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima ndipo anamuthandizadi.

8. Mofanana ndi Paulo, kodi nafenso tingatani kuti tikhale olimba mtima?

8 Nafenso tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize kukhala olimba mtima. Musamadziderere n’kumaganiza kuti simungakhale munthu wolimba mtima. M’malomwake muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima.—Mac. 4:29.

9. N’chifukwa chiyani ndi bwino kupempha Atate wathu kuti atiwonjezere chikhulupiriro?

9 Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kukhala ndi chikhulupiriro. Chikhulupiriro ndi limodzi mwa makhalidwe amene timakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova. (Agal. 5:​22, 23) Ndipo ndi chimodzinso mwa zida zankhondo zauzimu zimene Mkhristu aliyense amafunikira. (Aef. 6:16) Chikhulupiriro cha Akhristu ndi champhamvu kwambiri moti Baibulo limanena kuti ‘chimagonjetsa dziko.’ (1 Yoh. 5:4) Kukhulupirira Yehova n’kumene kungatithandize kuti tikhale olimba mtima. Mukamakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzakuthandizani pamene mufunika kuchita zinthu molimba mtima, m’pamenenso mumakhala olimba mtima kwambiri. Choncho mofanana ndi atumwi a Yesu tiyenera kupempha kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”—Luka 17:5.

“Limbani Mtima”

10-11. Pamene Paulo ankalembera Akhristu a Chiheberi, n’chifukwa chiyani anatsindika kufunika kokhala wolimba mtima?

10 Pamene Paulo ankalembera kalata Akhristu a Chiheberi ku Yerusalemu ndi madera apafupi ndi mzindawu, ankadziwa kuti pasanapite nthawi yaitali iwo akumana ndi mavuto aakulu. Yesu ananena kuti mzindawu udzawonongedwa ndipo nthawi yoti zimenezi zichitike inali itatsala pang’ono kukwana. (Luka 19:​41-44; 21:​20-24) Ndiye kodi Paulo anawakumbutsa bwanji kufunika kokhala olimba mtima? Tiyeni tionenso zimene ananena, zomwe zatchulidwanso m’Mawu Oyamba a bukuli. Iye anawakumbutsa lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pangʼono.” Kodi lonjezo limeneli likanawathandiza bwanji? Iye ananenanso kuti: “Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”—Aheb. 13:​5, 6.

11 Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza tsatanetsatane wokhudza mmene Yerusalemu anawonongedwera mu 70 C.E., sitikayikira kuti Akhristu okhulupirika amumzindawu anatsatira malangizo ouziridwa a Paulo. Iwo analimba mtima n’kumvera mawu a Yesu akuti ‘adzayambe kuthawira kumapiri’ ndipo anachita zimenezi pa nthawi yoyenera.—Luka 21:​20, 21.

12. (a) Kodi mungatani kuti mukhale olimba mtima mukakumana ndi mavuto? (b) Kodi anthu ena asonyeza bwanji kulimba mtima m’masiku otsiriza ano, nanga inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani? (Onani bokosi lakuti, “Tsanzirani Kulimba Mtima Kwawo.”)

12 Inunso Yehova angakuthandizeni kukhala olimba mtima mukakumana ndi mavuto panopa kapenanso m’tsogolomu. (Ezek. 38:​1, 2, 10-12; Mat. 24:21) Nthawi zonse muzikumbukira kuti Yehova anatilonjeza kuti adzatiteteza. (Ezek. 38:​19-23; 2 Ates. 3:3) Iye sadzasiya anthu amene amamukonda komanso kumukhulupirira. Zimene Yehova anauza Yoswa zikugwiranso ntchito kwa inuyo. Inunso akukuuzani kuti mukhale ‘olimba mtima kwambiri ndipo muchite zinthu mwamphamvu.’ (Yos. 1:​7, 9, 18) Komanso musamaiwale mawu a Yesu akuti: “Limbani mtima.” Iye sadzalephera kukwaniritsa lonjezo lake loti adzakutumizirani mzimu woyera wa Yehova womwe udzakuthandizeni kukhala olimba mtima mukamakumana ndi vuto lililonse. (Yoh. 14:26; 15:​26, 27; 16:33) Choncho mukhoza ‘kukhala olimba mtima’ ndithu.

Zithunzi: Abale ndi alongo akusonyeza kulimba mtima pamene akukumana ndi mayesero. 1. Mtsikana wa Mboni ali m’kalasi ndipo akumwetulira atatenga kope komanso kabuku kakuti “Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?” 2. Bambo ndi mayi ali kumsasa kumene athawira ndipo akumwetulira atagwira mwana wawo. 3. M’bale wachinyamata ali m’ndende ndipo akumwetulira.

Kaya zinthu zili bwanji, Yehova amalonjeza kuti adzatipatsa mzimu woyera kuti utithandize kukhala olimba mtima n’kumapirira mavuto alionse.

Tsanzirani Kulimba Mtima Kwawo

Martin ndi Gertrud Poetzinger

Martin ndi Gertrud Poetzinger.

Martin ndi Gertrud atakwatirana ankachitira limodzi utumiki wa nthawi zonse. Koma atangokhala m’banja miyezi itatu ndi hafu, chipani cha Nazi chomwe chinkatsogoleredwa ndi Adolf Hitler chinawasiyanitsa. Martin anamangidwa mu 1936 ndipo anapita naye kundende ya ku Dachau. Kenako nayenso Gertrud anamangidwa. Iwo sanaonane kwa zaka 9 ndipo kwa nthawi yonseyi palibe amene ankadziwa ngati mnzake ali moyo. Koma onse anatsimikiza mtima kuti sasiya kukhala okhulupirika. Martin anamusamutsira kundende ina yozunzirako anthu yoipa kwambiri yotchedwa Mauthausen ndipo ankamuzunza koopsa. Gertrud anaweruzidwa kuti akakhale kundende m’chipinda chayekha kwa zaka zitatu ndi hafu. Zaka zimenezi zitatha anapititsidwa kundende yozunzirako anthu yotchedwa Ravensbrück komwe anakhalako zaka 4. Nkhondo itatha, iye anazindikira kuti Martin adakali moyo. Choncho anakapempha mkulu wa asilikali kuti Martin atulutsidwe kundende. Izi zinathandiza kuti a Mboni enanso 100 omwe ankazunzidwa kwambiri kundende ya Mauthausen amasulidwe. Martin ndi Gertrud atakumana, anayambanso kuchitira limodzi utumiki wa nthawi zonse. Kenako anapita ku Brooklyn, New York, ndipo Martin ankatumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Nthawi zambiri iye ankauza abale ndi alongo ake kuti: “Kulimba mtima ndi chuma chamtengo wapatali kwambiri.” Onse anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika komanso mosangalala mpaka pamene anamwalira.

“Kulimba mtima ndi chuma chamtengo wapatali kwambiri”—M. Poetzinger

Valentina Garnovskaya

Valentina Garnovskaya.

Valentina ankakhala ku Belarus pamene anakumana koyamba ndi wa Mboni mu 1945. Pa nthawiyo anali ndi zaka pafupifupi 20. Zimene anaphunzira kuchokera m’Baibulo pa nthawi imeneyo komanso maulendo awiri otsatira zinamusangalatsa. Koma kenako sanakumanenso ndi wa Mboniyo. Popeza a Mboni ankaletsedwa m’dzikoli, zinali zovuta kuwapeza. Koma iye analimba mtima n’kumauza anthu ena zimene anaphunzira. Chifukwa cha zimenezi, Valentina anamangidwa n’kuweruzidwa kuti akakhale kundende zaka 8. Atatulutsidwa mu 1953, anayambiranso kuuza ena choonadi cha m’Baibulo. Choncho anamangidwanso ndipo anaweruzidwa kuti akakhale kundende zaka 10. Kundende ina anakumana ndi alongo angapo. Alongowo anali ndi Baibulo lomwe linali buku loletsedwa. Mmodzi mwa alongowa anamusonyeza Valentina Baibulo. Aka kanali koyamba kuti aonenso Baibulo kuchokera pamene anasiyana ndi wa Mboni uja zaka zambiri m’mbuyomo. Valentina atamasulidwa mu 1967, anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Iye anapitiriza kulalikira mwakhama mpaka pamene anamangidwanso mu 1969 n’kuuzidwa kuti akakhala kundende zaka zitatu. Koma iye anapitiriza kulalikira uthenga wabwino. Pamene ankamwalira mu 2001, anali atathandiza anthu 44 kuphunzira choonadi. Pofotokoza za moyo wake, iye anati: “Sindinakhalepo ndi malo angaanga okhala. Ndipo katundu wanga yense ankangokwana m’chikwama chimodzi. Koma ndinkatumikira Yehova mosangalala komanso ndinkakhala wokhutira.”

“Sindinakhalepo ndi malo angaanga okhala. Ndipo katundu wanga yense ankangokwana m’chikwama chimodzi. Koma ndinkatumikira Yehova mosangalala komanso ndinkakhala wokhutira.”—V. Garnovskaya

Alfredo Fernández

Alfredo Fernández.

Alfredo atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20, anaitanidwa kuti akakhale msilikali ku Argentina. Chifukwa choti ankakhulupirira kuti Akhristu sayenera kumenya nawo nkhondo, iye anakana kulowa usilikali komanso kuvala yunifomu ya asilikali. Iye anamangidwa ndipo kundendeko asilikali ankamuzunza kwambiri. Mwachitsanzo, nthawi zina ankayerekezera kuti akupita kukamupha. Koma iye anapitiriza kuwerenga Baibulo n’kumalemba notsi za zimene waphunzira. Pa nthawi ya mlandu wake, woweruza anamuuza kuti akhoza kumumasula ngati atangovala yunifomu ya asilikali popita kukhotiko. Koma iye anakana molimba mtima. Choncho anabwerera naye kundende. Chifukwa choti ankamuzunza, anayamba kudwala kwambiri. Dokotala wa kundendeko amene ankamuthandiza anamuuza kuti ulendo wotsatira adzamuona ali m’bokosi. Alfredo atazindikira kuti watsala pang’ono kumwalira, analembera anthu am’banja lake kalata. Iye anayamba ndi mawu akuti: “Okondedwa abale anga. Sindinkafuna kukulemberani kalata ngati imeneyi. Koma mmene zilili panopa, sindingachitire mwina.” Anawayamikira chifukwa chomulimbikitsa pa nthawi yomwe anali m’ndende. Analemba kuti: “Ndikuyamikira kwambiri Mulungu wachikondi Yehova pondilola kuti ndikhale m’banja ngati limeneli. . . . Ndikudziwa kuti mumva chisoni kwambiri mukamawerenga kalatayi. Koma ndikungopempha kuti musalole kuti chisoni chikufooketseni. Pitirizani kukhala olimba mtima. Lolani kuti Yehova akutonthozeni kudzera m’Baibulo. . . . Musaiwale kuti imfa si mathero a zonse. Ndikukhulupirira kuti mukamakumbukira kuti ndinakhalabe wokhulupirika kwa Yehova, inunso mukhalabe wokhulupirika.” Alfredo anakhala wokhulupirika kwa moyo wake wonse ndipo anamwalira mu 1982 ali ndi zaka 21.

“Ndikungopempha kuti musalole kuti chisoni chikufooketseni. Pitirizani kukhala olimba mtima.”—A. Fernández

Karen Oehm

Karen ndi Rainer Oehm.

Kuyambira ali mwana, Karen ankatumikira Yehova ndipo anali munthu wansangala. Iye ankakonda kwambiri upainiya ndipo kenako anatumikira ku Beteli ya ku United States limodzi ndi mwamuna wake, Rainer. Koma ali ndi zaka za m’ma 50, anayamba kudwala matenda osachiritsika. Matendawa amachititsa kuti pakapita nthawi munthu azilephera kulankhula komanso kuyenda mpaka amafa. Kungoyambira pamene anadziwa za vuto lakeli, Karen anasankha kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi ndipo asamangokhalira kudandaula. Ankakonda kuphunzira payekha komanso kulalikira. Ankayesetsanso kusintha zinthu pa moyo wake kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili. Atayamba kuvutika kulankhula, anaphunzira kugwiritsa ntchito kompyuta yomwe inkamuthandiza kulemba mawu poyendetsa maso pasikirini ya pakompyutapo. Njira imeneyi inali yovuta koma inkamuthandiza kuti azilemba zokayankha kumisonkhano komanso azilalikira polemba makalata. Mlongo wina yemwe anali mmodzi wa manesi ake ananena kuti: “Sanadandaulepo kuti, ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zikundichitikira?’ Kutatsala mawiki awiri kuti amwalire, iye analembera kalata mayi wina amene ndinamulalikirapo ndipo anamaliza ndi mawu akuti, ‘Ukakhumudwa ndi zinazake, utha kumandifotokozera.’” Nesi wina ananena kuti: “Atapezeka ndi matendewa, sanalire. Anali ndi zifukwa zambiri zomuchititsa kukhumudwa, koma ankakhulupirira kwambiri zoti akufa adzauka moti sankakhumudwa. Iye ankadziwa kuti Yehova adzamuukitsa ali wathanzi komanso wangwiro.” Karen atayamba kudwala, mchemwali wake amene anabadwa naye mapasa anamufunsa kuti: “Umatha bwanji kukhalabe wolimba chonchi?” Karen anangoyankha kuti: “Yehova amatipatsa mphamvu zimene tikufunikira.” Yehova anamupatsadi mphamvu Karen mpaka pamene anamwalira. Atamwalira, mwamuna wake anapereka kwa achibale ndi anzake makalata amene Karen analemba pofuna kuwayamikira, kuwatonthoza komanso kuwalimbikitsa.

“Yehova amatipatsa mphamvu zimene tikufunikira.”—K. Oehm

13. Kodi n’chiyani chimakuthandizani kukhalabe olimba mtima masiku ano?

13 Yerekezerani kuti padziko lonse pali mtendere, tikulandira anthu omwe anamwalira amene Yehova akuwakumbukira, komanso takumana ndi anthu olimba mtima amene takambirana m’bukuli ndiponso ena ambiri. Kodi mukuganiza kuti pali aliyense mwa anthuwo yemwe adzanong’oneze bondo kuti ankatumikira Yehova molimba mtima m’dziko la Satanali, mwina mpaka kufika pophedwa? Ayi ndithu. Nanga bwanji inuyo? Mukamadzagwira ntchito ndi anthuwa kuthandiza kuti dzikoli likhalenso Paradaiso, kodi mudzanong’oneza bondo kuti simunachite bwino kusonyeza kulimba mtima komanso kukonda Yehova m’masiku otsiriza ano? Ayinso. Choncho tsimikizani mtima kuti mupitirizabe kukhala olimba mtima mpaka mapeto. Mukatero, mudzasangalala mpaka kalekale kuti munachita zimenezi.

Abale, alongo komanso ana akusangalala m’Paradaiso. Ena akudyetsa nyamalikiti, ena akuyang’ana mphaka wam’tchire, ena akupanga piza, ena akucheza pomwe ena akuimba.
    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena