Mafunso Ochokera kwa Owerenga
◼ Kodi chiri choyenerera kaambaka Mkristu kulola kupendedwa kwathupi pa mbale wake?
Baibulo silimapereka ndemanga yachindunji ponena za kupendedwa kwathupi, koma pali malingaliro ena a Baibulo ogwirizana amene Mkristu angawalingalire. Kenaka pali chosankha chaumwini chomwe chingachitidwe mu kuwunikira malemba oterowo ndi tsatanetsatane wa mkhalidwe wopatsidwawo.
Kupenda thupi kuli kutumbula (kucheka pakati) kwakufufuza mtembo ndi cholinga chofuna kudziwa chomwe chapangitsa imfa. Kungaperekenso chidziwitso ponena za zotulukapo kapena mkhalidwe wamatenda. Kawonedwe ka zipembedzo zina ka kupenda thupi kwakhudza ziphunzitso zopanda malemba. Mwachitsanzo, encyclopedia ya Chikatolika ikunena kuti: ‘Thupi la wakufa liyenera kusamalidwa ndi ulemu waukulu monga nyumba ya moyo wake wakale. . . ilo liri lotsimikizirika kudzaukitsidwa ku moyo wake, mkati mwa chiukiliro, ku moyo wosatha. . . pangakhale nthawi pakati pa imfa ya chipatala ndi kunyamuka kwa moyo.” Komabe, Baibulo limasonyeza kuti pamene munthu (chinthu chamoyo) afa, iye amakhala munthu wakufa. (Genesis 2:7; 7:21-23; Levitiko 21:1, 11) Bwanji ponena za thupi lake? Ponena za zonse ziWiri “ana a anthu“ ndi “zinyama,“ timaWerenga: “Onse achokera m’pfumbi ndi onse abwereranso kupfumbi.” (Mlaliki 3:18-20) M’chiukiliro, Mulungu sadzaukitsa thupi limene mkupita kwanthawi linakhala lapfumbi, koma iye adzapereka thupi monga mmene chidzamukondweretsa iye.—Onani 1 Akorinto 15:38, 47, 48.
Mbali ina ya kayang’anidwe ka Baibulo ka akufa ingalingaliridwe m’chigwirizano ndi kupenda thupi. Mulungu analamulira Aisrayeli: “Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; ine ndine Yehova.” (Levitiko 19:28; Deutronomo 14:1, 2; Yeremiya 47:5; Mika 5:1) Inde, anthu a Mulungu sayenera kutsanzira mitundu yowazinga mkuchekacheka minofu yawo monga chizindikilo cha chisoni pa wakufa osatinso kaamba ka zifukwa zabodza za chipembedzo. Lamulo limeneli lingakhalenso linalimbikitsa Aisrayeli kusonyeza ulemu wawo kaamba ka matupi awo monga zolengedwa za Mulungu.—Masalmo 100:3; 139:14; Yobu 10:8.
Akristu mofananamo ayenera kusonyeza ulemu kaamba ka miyoyo yawo ndi matupi awo, amenawapereka kwa Mulungu (Aroma 12:1) Ena afika pa nsonga yakuti kayang’anidwe ka ulemu kameneka ka thupi kayenera kuwongolera maganizo awo ponena za kupenda thupi. Iwo aganiza kuti kokha ngati panali chifukwa china chotsendereza, iwo sangavomereze kuti thupi la mnansi wawo wokondedwa lichekedwe pambuyo pakufa. Iwo angakhale atadziwa kuti mmalo ena mwazi wotengedwa kuchokera kwa munthu wakufa wakhala ukugwiritsidwa ntchito mu kupereka mwazi kapena zifuno zina, za zimene iwo sangafune kukhala mbali a
Nchifukwa ninji, nanga, Akristu ena amavomereza kupenda thupi? Iwo amazindikira kuti Baibulo mwachindunji silimapereka ndemanga panjira ya kachitidwe ka zinthu ka using’anga kameneka. Iwo angakhalenso atazindikira kuti Aisrayeli mu Aigupto analola asing’anga a chiAigupto kukonza mitembo ya Yakobo ndi Yosefe, imene mwachiwonekere inaphatikizamo kutumbula kwa using’anga kuchotsa ziwalo za mkati. (Genesis 50:2, 3, 26) Mnkhani zina lerolino, lamulo la m’dziko limafuna kuti kupenda kwathupi kuchitidwe. Mwachitsanzo, ngati wachichepere, munthu waumoyo wabwino afa popanda chifukwa chenicheni, kumutumbula munthu woteroyo kungakhale kwa lamulo. Mwachiwonekere, pamene lamulo lilamulira kupenda thupi, Mkristu ayenera kusunga m’maganizo uphungu wakuti “kumvera maulumaliro a akulu.”—Aroma 13:1, 7; Mateyu 22:21.
Ngakhale ponena za munthu amene anali pansi pa chisamaliro cha sing’anga ndipo mwakutero kumene chopangitsa cha imfa chiri chodziwika, kupenda thupi kungapereke chidziwitso chothandiza. Ana opulumuka angafune kudziwa chifukwa chenicheni kotero kuti awonjezere chidziwitso ponena za mbiri ya using’anga ya banja lawo. Chidziwitso choterocho chingakhudze njira yamoyo ya mtsogolo mwawo kapena mankhwala. Pali zifukwa zinanso, zimene ena amavomerezera kupenda thupilo. Ripoti lakutumbulidwa lotsimikiziridwa ndi kuphunzira minofu lingathandize banja kuyenerera kaamba ka mapindu a opulumuka, monga ngati kupereka chitsimikiziro chanthenda ya mapapo akuda yogwirizanitsidwa ndi kugwira ntchito mu migodi ya malasha. Ena aganiza kuti kupenda thupi kungawonjezere mtendere wawo wa maganizo mwakuwathandiza iwo kumvetsetsa nchiyani chimene chinapangitsa kapena nchiyani chimene sichinapangitse imfa ya wokondedwa wawo. Anthu akunja kwa banja angalowetsedwemonso. Anansi angaganize kuti moyenerera kuvomereza kupenda thupi lakufa kungathandize sing’anga kumvetsetsa mkhalidwe wamatenda, ndipo mwakutero kukhala wokonzekeretsedwa kuthandiza ena.
Chotero, chiri choyenerera kaamba ka Akristu kusonyeza ulemu kaamba ka matupi awo, koma pali zinthu zina zomwe iwo angazilingalire mkugamulapo kuti kaya avomereze kupenda thupi mu mi khalidwe ina yapadera.
Mawu a M’munsi
a Ponena za kuthekera kwa kugwiritsira ntchito ziwalo za thupi la munthu kaamba ka zolinga za kuika ziwalo, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1980, tsamba 31, Chingelezi.