Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 4/15 tsamba 5-7
  • Mbali Yatsopano ya Nzeru ya Umulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbali Yatsopano ya Nzeru ya Umulungu
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chinsinsi Chopatulika Chifutukulika
  • Kuomboledwa ndi Dipo
  • Chipangano Chatsopanondi Chilengedwe Chatsopano
  • Dziko Lapansi la Paradaiso
  • Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’
    Yandikirani Yehova
  • Makonzedwe Okwaniritsira Cholinga cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Yesu Amapulumutsa Motani?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 4/15 tsamba 5-7

Mbali Yatsopano ya Nzeru ya Umulungu

“NDIPO Mulungu anati kwa Mose: ‘INE NDINE YEMWE NDIRI INE.’ Ndipo anatinso: ‘Ukatero ndi ana a Israyeli, “INE NDINE WANDITUMA KWA INU.”’” (Eksodo 3:14) Yehova analongosola kwa Mose kuti ngakhale chisanachitike chimenechi atumiki ake sanamvetsetse kufunika kwenikweni kwa dzina lake. Iye ali Mulungu wachifuno ndiponthawi zonse amakwaniritsa chifuno chake. Ngati mikhalidwe ilola, iye angasinthe njira zake za kachitidwe ka zinthu kuti akwaniritse chifuno chake. Iye ali wanzeru yotero!

Satana iye mwini sanayamikire chimene dzina la Mulungu linatanthauza. Mwachiwonekere, iye anadziwa za mtengo wa moyo m’munda wa Edene. Ngati iye akanatsogoza Adamu ndi Hava ku iwo, chimenecho chikanawoneka monga kuika Yehova panyanga za tsoka: kaya kusunga mawu ake kuti chimo likatanthauza imfa yawo kapena kusunga mawu ake ponena za mtengo wa moyo. (Genesis 2:9; 3: 1-6) Mu chochitika chirichonse, Satana anayenera kukhumudwitsidwa.

Mulungu tsopano anayamba kuwonetsera nzeru yake yosayembekezeredwa kwa ana ake auzimu ndipo kumbuyoko yosavumbulutsidwa kwa iwo. (Yerekezani ndi Aefeso 3:10.) Iye anayamba kuwonetsa ndandanda yazolankhulidwa ndi zochitika zomwe kwa nthawi yaitali mosangalatsa zidzawonetsa nzeru yake yaikulu ndi kuthekera kwake kwakukwaniritsa chifuno chake chosatha, chomwe chinali kukhala ndi dziko lapansi lodzaza ndi anthu achimwemwe, omvera omwe angakhale ndi moyo kosatha mu Paradaiso. (Genesis 1:27, 28) Nthaŵi ndi nthaŵi Mulungu akathetsa zoyesayesa za Satana za kusokoneza.

Chinsinsi Chopatulika Chifutukulika

Mwamsanga kutapangika kuukira koyamba, Mulungu anachitapo kanthu. Iye anazenga mlandu anthu awiri ochimwawo ndi kumamatira ku chilango chake cha imfa kaamba ka kusamvera. Bwanji ponena za kudya kuchokera ku mtengo wa moyo kwa Adamu ndi Hava? “Ndipo anati Yehova Mulungu: ‘tawonani munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa; ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,—’ Yehova Mulungu anamtulutsa iye m’munda wa Edene.”​—Genesis 3:17-23.

Panthawi imeneyi Mulungu anatenganso ntchito ya Mlaliki, kapena Wolengeza wa mbiri yabwino. Iye ananena ulosi wake woyambirira: “Ndipo Yehova Mulungu anati kwa njokayo, . . . ‘Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.’ ” (Genesis 3:14, 15) Zaka mazana pambuyo pake mtumWi Paulo analongosola: “Pakuti cholengedwacho [anthu] chagonjetsedwa ku utsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa ndi chiyembekezo.”​—Aroma 8:20.

Inde, kuyambira pamenepo popanda chirikizo munthu adzapita ku imfa yacholowa kuchokera kwa Adamu, koma Mulungu anali kulengeza chifuno chake cha kupulumutsa mbadwa zomvera za Adamu. Komabe, kodi nchiyani chimene chinali “maziko a chiyembekezo”? Kodi ndimotani mmene iye akanapulumutsira anthu ndipo ndi kumamatirabe ku chilango chake cha imfa. kaamba ka chimo? Ichi chinayenera kukhala nzeru yobisika ya Mulungu; iyo inaphatikizamo “chinsinsi chopatulika chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo.” (Akolose 1:26; 1 Akorinto 2:7, 8) Ngakhale kuti okhulupirika a nthawi yakale sanamvetsetse chinsinsicho, iwo anali ndi chiyembekezo chakuti mwanjira ina yake Mulungu adzawapulumutsa iwo. Nchifukwa ninji? Ngakhale angelo anali ofunitsitsa kuphunzira ndimotani mmene Yehova adzakwaniritsira chifuno chake! (l Petro 1:10-12) Kodi mukumvetsetsa chinsinsi chopatulika chimenecho?

Kuomboledwa ndi Dipo

Mkupita kwanthawi mkati mwa zaka mazana, Yehova anawonjezera chidziwitso ku lonjezo lake loyambirira. Kwa Abrahamu wokhulupirika iye analonjeza mbewu kupyolera mwa imene madalitso kaamba ka anthu onse omvera adzabwera. (Genesis 22:15-18) Kudzera mwa Yakobo iye anavumbulutsa kuti mbewu imeneyo idzakhala mfumu yochokera ku fuko la Yuda. (Genesis 49:10) Kufika panthawi imeneyo anthu aumulungu anakhulupirira mu chiukiriro cha akufa, ngakhale kuti sanamvetsetse mokwanira kuti ichi chikachitika motani. (Yobu 14:14, 15; Ahebri 11:19) Pomalizira, Mulungu analonjeza Davide kuti Mfumu ikudzayo, kapena Mesiya, adzakhala wochokera ku fuko la Davide ndipo adzalamulira kunthawi yosatha.​—2 Samueli 7:16.

Aneneri onse anawonjezera zidutswa za kumvetsetsa ku chinsinsi chopatulika, koma anthu sanawone chinthu chokwanira. Kenaka, nthawi ya kuwonekera Mesiya inafika, ndipo kenaka, pomalizira, nzeru imeneyi yobisika ya Mulungu inakhala yomvekera bwino kwambiri. lyo inazikidwa pa Yesu Kristu ndi pachopereka chake cha moyo wangwiro monga dipo loyenerera kaamba ka mtundu wa anthu. Ndi chimenecho monga maziko, mbali yotsatira ya chifuno cholemekezeka cha Yehova kudzera mu Ufumu chinapitirira. Kodi mukumvetsetsa dipolo?

Mu Aroma mutu 5 ndi 6, Paulo akupereka kulongosola kwabwino kwa ilo. Pa Aroma 5:12 iye akulongosola uchimo wathu wa cholowa ndi imfa. Iye akupitiriza kusonyeza ndimotani mmene chotulukapo cha chimo la munthu mmodzi wangwiro Adamu ndi cholanda cha moyo kaamba ka mbadwa zake chingalinganizidwire ndi moyo wa munthu wina wangwiro. Umenewo unatsimikizira kukhala moyo wa “munthuyo, Kristu Yesu.” (Maversi 15-21; onaninso 1 Timoteo 2:5, 6. ) Kodi ndimotani mmene Yesu akanaperekera dipo limeneli? Chifukwa iye anali Mwana wa Mulungu, Yesu anali “woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa wosiyana ndi ochimwa.” (Ahebri 7:26; Luka 1:32, 33) Sitifunikira kuyesera kulongosola tsatanetsane wa majini akubadwa kwa Yesu. Mngelo Gabrieli anatsimikizira mayi wa Yesu, Mariya, ndi ife, kuti palibechiri chonse chosatheka ndi Mulungu. (Luka 1:37) Chotero Yesu, ngakhale kuti anabadwa kuchokera ku mbadwa ya chikazi yochokera kwa Adamu, anali Mwana wa Mulungu​—mchenicheni munthu wangwiro. Mwazi wake, kapena moyo, unali wamtengo wapatali kuposa mwazi wa nyama zosawerengeka zomwe zinaperekedwa nsembe ndi ansembe a Aroni a Israyeli pakachisi mu Yerusalemu. Iye anali “Mwanawankhosa wa Mulungu amene amachotsa machimo ake a dziko lapansi.”​—Yohane 1:29; 3:16.

Kodi Mulungu akanapanga makonzedwe amenewo kudzera mwa Yesu ndi kukhalabe wolungama? Ngati Mulungu anaukitsa Mwana wake ku moyo patsiku lachitatu, kodi nchiyani chimene chinachitika ku dipo? Paulo akutitsimikizira ife kuti Mulungu ali wolungama. Tsatirani kulingalira kwake: “Koma ndi chifundo chake iwo apangidwa olungama kwaulere [icho kukhala chaufulu], mwa chipulumutso chopezedwa kudzera mwa Kristu Yesu. Popeza Mulungu anamuwonetsa iye poyera kufa monga nsembe ya chigwirizanitso yotengedwa kudzera mwa chikhulupiriro. Ichi chinali kaamba ka kuyeretsa chilungamo chake (popeza Mulungu m’kulekerera kwake analekerera machimo otchulidwa kale lomwe)​—kuti awonetse chilungamo chake mnyengo yatsopano, ndi kuti awonetsere kuti iye ndi wolungama, ndi kuti amapanga awo amene asonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kukhalanso olungama.” (Aroma 3:24-26, An American Translation) Tsopano, kodi nchiyani chimene ichi chimatanthauza? Icho chimatanthauza kuti Yesu, monga wangwiro, munthu wa nyama ndi mwazi, anafadi monga munthu ndi kukhalabe wakufa monga munthu kwanthawi yosatha. Iye anafa “kamodzi kokha kwatha, podzipereka yekha.” (Ahebri 7:27) Chotero dipolo lidakali kugwira ntchito. Yesu anafa mthupi; patsiku lachitatu iye “anapatsidwa moyo mumzimu.”​—1 Petro 3:18.

Chipangano Chatsopanondi Chilengedwe Chatsopano

Tsopano tikuwona mbali yowonekera kwambiri ya chinsinsi chopatulika. Kukhala kwa Yesu wokhulupirika kufikira imfa kumuyeneretsa iye kukhala Wansembe Wamkulu wa Yehova ndi Mfumu. Ndi mwazi wake wokhetsedwa iye akupangitsa chipangano chatsopano kukhala chogwira ntchito. Chipangano chatsopano chimenechi chiyenera kuturutsa oyanjana nawo akumwamba omwe adzalamulira limodzi ndi Yesu monga mafumu ndi ansembe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:4, 6) Ichi chimaphatikizamo mtundu watsopano, “chilengedwe chatsopano,” ndipo chimenecho mowona chiri chinachake!​—Agalatiya 6:15, 16.

Lingalirani: Mulungu kudzera mwa Kristu Yesu akusankha chiwerengero choimira kuchokera mwa mtundu wa anthu, ponse pawiri amuna ndi akazi. Iye mwalamulo angawalalikire iwo kukhala olungama ndi kuwaitana iwo kukhala ana auzimu. Mu nthawi yake Mulungu pambuyo pa imfa yawo, iye amawaukitsira iwo kumwamba ndi kuwapatsa moyo wosakhoza kufa, monga momwe iye anafupira Yesu. (1 Petro 1:3, 4) Ndi chidaliro chotani chimene iye ali nacho mu “chilengedwe chake chatsopano” ndi kumvera kwawo kwa iye! Liri yankho lotani kwa uyo amene mwabodza anawatsutsa iwo pamaso pa Yehova! (Chivumbulutso 12:10) Ngakhale adzakhala osakhoza kufa limodzi ndi Yesu Kristu, iwo sadzakhala osamvera kwa Yehova. Koma zimenezo sindizo zokha.

Dziko Lapansi la Paradaiso

Kristu Yesu, limodzi ndi mafumu anzake ndi ansembe akumwamba, adzawona ku icho kuti chifuno cha Yehova kaamba ka munthu ndi dziko lapansi mokwanira chidzakwaniritsidwa mkati mwa Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi. Kugwiritsira ntchito mapindu a dipo, Yesu adzaukitsa akufa ndipo, adzabweretsa ku umunthu wangwiro okhulupirika pakati pawo ndi opulumuka mapeto a dongosolo iri loipa la zinthu. Panthawi imodzimodziyo, dziko lapansi lidzapangidwa kukhala paradaiso. Onse amene adzakana kuyesayesa komalizira kwa Satana kuwawononga iwo adzapatsidwa moyo wangwiro wa umunthu wosatha. Satana limodzi ndi khamu lake loipa adzawonongedwa kosatha. Mtendere ndi umodzi udzakhalapo mu chilengedwe chonse, mokwanira kuyeretsa ulamuliro wa Yehova ndi lamulo lake mwachikondi. Ponse pawiri angelo ndi anthu adzakhala atasonyeza chikondi chawo chomvera kaamba ka Mlengi wawo ndi Mulungu.​—Chivumbulutso, mutu 20.

Tsopano tingamvetsetse bwino chinsinsi chopatulika. Tsopano tikuwona nzeru ya Yehova yomwe imapambana angakhale mapangidwe a chilengedwe chake cha dziko la mitengo ndi zinyama. Tiri ndi chifukwa chabwino chakufuulira: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake. . . chifukwa zinthu zonse zichokera kwa iye, zichitika mwa iye, ndi kufikira kwa iye. Kwa iyeyu ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.”​—Aroma 11:33-36.

Chithunzi patsamba 7]

Zotulukapo za chimo limodzi ndi munthu mmodzi wangwiro Adamu ndi kulandidwa kwa moyo wake kungalinganizidwe Motani? Ndi moyo wa munthu wina wangwiro, uja wa Yesu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena