Kuyang’ana M’mbuyo Kuposa Zaka 93 Zakukhala ndi Moyo
Monga Yalongosoledwa ndi Frederick W. Franz
PA September 12, 1893, mwana wamwamuna anabadwa mu Covington, Kentucky, yomwe iri kudera la kum’mwera loyang’anizana ndi mtsinje wa Cincinnati, Ohio. Atate wake wachimwemwe, Edward Frederick Franz, ndi mayi wake wosangalala, Ida Louise née Krueger, anamutcha mwana wawo wamwamuna Frederick William Franz.
Pamenepo panali pachiyambi pa zaka zanga 93 zakukhala ndimoyo. Atate wanga, yemwe anabadwira mu Germany, anadzinenera kukhala wa Tchalitchi cha Lutheran ndipo chotero anandipangitsa ine kubatizidwa mwa kuika manja okhala ndi madzi a wansembe pamphumi panga. Chiphaso cha ubatizo chinadzazidwa, ndipo chinaikidwa mu thabwa lokonzedwa bwino ndi kupachikidwa pakhoma m’nyumba yathu, limodzi ndi ziphaso za ubatizo wa abale anga achikulire awiri, Albert Edward ndi Herman Frederick. Kokha zaka 20 pambuyo pake ndinaphunzira kuti kachitidwe ka chipembedzo kameneka sikanali ka m’malemba.
Panali pamene tinasamukira ku Greenup Street kumene ndinawona kwa nthawi yoyamba ngolo yosakokedwa ndi kavalo, galimoto lopanda denga la mipando iwiri, likuyendetsedwa kukwera msewu. Zaka zambiri pambuyo pake ndinayenera kuwona ndege kwa nthawi yoyamba. Kenaka tinakhala pafupi ndi Krieger’s Bakery, kumene atate anga anagwira ntchito usiku monga wophika mkate. Iwo ankabwera kunyumba m’mawa ndi kugona. Kenaka masana anali kukhala waufulu kuwononga nthawi ina ndi anyamatafe.
Pamene ndinafika pa msinkhu wopita ku sukulu, ndinatumizidwa choyamba ku sukulu yotsogozedwa ndi achipembedzo ndi misonkhano ya chipembedzo ya St. Joseph’s Roman Catholic Church, popeza inali pafupi ndi misewu ya 12th ndi Greenup. Ndimakumbukirabe kalasi ya ku sukulu. Pa nthawi ina “mbale” wachipembedzo akumachita monga mphunzitsi anandipangitsa ine kukaima kutsogolo kwa kalasi ndi kuwongola chikhato changa chofutukulidwa kulandira zikoti zingapo ndi rula ya 12 inchi chifukwa chakusamvera kumbali yanga.
Ndimakumbukiranso ndikupita mu kachipinda kopanda magetsi kolapira ka mu tchalitchi, ku malankhula kwa wolapitsa kumbuyo kwa kachipinda ndi kumanena pe mphero lolowezedwa ndi kulapa kuti ndi nali mnyamata woipa chotani nanga. Pambuyo pa chimenecho, ndinapita pansi kuguwa ndi kugwada pamene wansembe anaika chidutswa chamkate mkamwa mwanga, chotero kundipatsa ine Mgonero monga ndinaphunzitsidwa ndi tchalitchi, pamene anali kusunga vinyo kuti amwe iye mwini pambuyo pake. Ichi chinali chiyambi cha maphunziro anga achipembedzo ndi ulemu wanga kaamba ka Mulungu womwe ukakula mu zaka zinali nkudza.
Pambuyo pa kumaliza kwanga chaka mu sukulu yotsogozedwa ndi achipembedzo mu 1899, banja langa linasamukira ku tsidya lina la Mtsinje wa Ohio ku Cincinnati, ku 17 Mary Street (tsopano wotchedwa East 15th Street). Panthawiyi ndinatumizidwa ku sukulu yophunzira anthu onse ndipo ndinaikidwa mu kalasi la chitatu. Ndinatsimikizira kukhala wophunzira wosamvetsera kwenikweni, kotero kuti ndimakumbukira kuti, panthawi ina, wophunzira amene anali kumanja kwa desiki yanga ndi ine tinatumizidwa ku ofesi ya mphunzitsi wamkulu chifukwa chakhalidwe lathu loipa. Kumeneko Mphunzitsi Wamkulu Fitzsimmons anatipangitsa ife tonse kuwerama ndi kukhudza nsonga ya nsapato zathu ndi zala zathu pamene iye anali kutikwapula ife zikoti kumsana kwathu. Monga mmene mungayembekezere, ndinalephera mayeso.
Koma atate wanga sanali wofunitsitsa kuti ndiwononge zaka ziwiri mu kalasi imodzimodziyo. Chotero pamene chigawo china cha sukulu chinayamba, iwo ananditumiza ine ku sukulu ya ku Liberty Street, ku ofesi ya mphunzitsi wamkulu wa pa sukulupo, A Logan. Iwo anafunsa A Logan kundilowetsa ine mu kalasi lachinayi. A Logan anawoneka kukhala achifundo kulinga kwa ine, ndipo anati: “Chabwino, tiyeni tiwone zimene mwamuna wachichepereyo amadziwa.” Pambuyo pakuya nkha mafunso angapo ovuta kwambiri kuchitsimikizo chake chokwaniritsa, iye ananena: “Chabwino, chikuwoneka kuti iye wayeneretsedwa kaamba ka kalasi lachinayi.” Mu njira imeneyi, iye mwaumwini anandikweza ine kupita ku kalasi lokulirapo kuposa limene ndinalephera mayesolo. Kuyambira panthawi imeneyo ndinakhazikika ndi kuzigwiritsira ine mwini mosamalitsa kuntchito yanga ya ku sukulu, ndipo kuyambira pamenepo sindinalepherenso nkomwe mayeso
Mbali ya chipembedzo ya umoyo wanga wachichepere inasinthanso. Mwanjira ina yake, oimira a Second Presbyterian Church of Cincinnati anakumanizana ndi mayi wanga, ndipo analingalira kutumiza Albert, Herman, ndi ine ku sukulu ya pa Sande ya tchalitchi chimenecho. Panthawi imeneyo, a Fisher anali mtsogoleri wamkulu wa sukulu ya pa Sande, ndipo Bessie O’Barr wachichepere anakhala mphunzitsi wanga wa sukulu ya Sande. Mu njira imeneyi, ndinakhala wozolowerana ndi mawu ouziridwa Baibulo Loyera. Ndinali woyamikira chotani nanga pamene mphunzitsi wanga wa Sande sukulu anandipatsa ine kope laumwini la Baibulo Loyera monga mphatso ya Krisimasi!
Ndinagamulapo kupanga icho chikakamizo m’moyo wanga kuwerenga mbali ya Baibulo tsiku liri lonse. Ichi chinatulukapo mu kukhala kwanga wozolewerana bwino ndi bukhu loyera limenelo. Ndipo chotulukapo chake chabwino chinandipangitsa ine kusakhala wophatikizidwa mkulankhula koipa ndi khalidwe loipa la anzanga a mu kalasi. Chinali chosadabwitsa kuti anandiwona ine kukhala wosiyana.
Sukulu Yapamwamba ndi Koleji
Pambuyo pakumaliza maphunziro a kalasi yachitatu pa sukulu ya pulaimale mu 1907, makolo anga anandilola ine kupitiriza maphunziro anga ndi kulowa mu Sukulu Yapamwamba ya Woodward, kumene Albert, mbale wanga wamkulu kwambiri, anapezekako kwa chaka chimodzi. Mofanana ndi iye, ndinalingalira za kutenga phunziro la zaluso. Chotero ndinatenga phunziro la Chilatin—phunziro limene ndinalilondola kufikira zaka zisanu ndi ziwiri zotsatira.
Kenaka inabwera nthawi yomaliza maphunziro mu ngululu ya mu chaka cha 1911. Ndinasankhidwa kukhala mtsogoleri wa Sukulu Yapamwamba ya Woodward pa masewero okondwerera kumaliza maphunziro omwe anayenera kuchitidwa pa bwalo lalikulu kwambiri la misonkhano la mu Cincinnati, Music Hall.
Panthawiyo, masukulu onse atatu apamwamba a mu Cincinnati—Sukulu Yapamwamba ya Woodward, Sukulu Yapamwamba ya Hughes, ndi Sukulu Yapamwamba ya Walnut Hills—anakumana pamodzi kaamba ka masewero akumaliza maphunziro. Akulu a sukulu zapamwambazo anakhala pa pulatiformu yaikulu akumayang’ana ku bwalo la msonkhano lodzaza ndi anthu. Mawu otsegulira anaperekedwa kwa mtsogoleri wa Sukulu Yapamwamba ya Woodward. Mutu umene ndinasankha kaamba ka chochitikacho unali wakuti “Sukulu ndi kukhala Nzika Alankhuli atatu onse anawomberedwa m’manja mosangalatsa kwambiri. Panthawiyi ndinali mu chaka changa cha 18 chamoyo
Makolo anga anandilola ine kupitiriza ntchito yanga ya maphunziro, chotero ndinalowa mu University ya Cincinnati, kutenga maphunziro a liberal arts. Panthawiyi ndinali nditalingalira za kudzakhala wolalikira wa Presbyterian
Ku kupitirizidwa kwa phunziro la Chilatin, ndinawonjezerako phunziro la Chigriki. Linali dalitso lotani kuphunzira Baibulo la Chigriki pansi pa Profesa Arthur Kinsella! Pansi pa Dr. Joseph Harry, mlembi wantchito ina ya Chigriki, ndinaphunziranso luso la Chigriki. Ndinadziwa kuti ngati ndinafuna kukhala wansembe wa chiPresbyterian, ndinayenera kukhala ndi lamulo la Baibulo la Chigriki. Chotero mopsya mtima ndinadzigwiritsira ntchito ine mwini ndi kupambana mayeso.
M’kuwonjezera ku kuphunzira Chigriki ndi Chilatin ku sukulu, ndinasangalatsidwanso ndi kuphunzira Chispanish, chomwe ndinachipeza kukhala chofananako ndi Chilatin. Ndinazindikira zochepa panthawiyo kuti ndi mochulukira chotani mmene ndidzakhalira wokhoza kugwiritsira ntchito Chispanish mu uminisitala wanga Wachikristu.
Nsonga yapamwamba mu moyo wanga wamaphunziro inali pamene Dr. Lyon, prezidenti wa yuniversiteyo, analengeza kwa msonkhano wa ana asukulu mu bwalo la msonkhanolo kuti ndinali nditasankhidwa kupita ku Ohio State University kukatenga mayeso opikisana ndi ena kuti ndikalandire mphatso ya Cecil Rhodes Scholarship kundiyeneretsa kaamba ka kulowetsedwa ku Oxford University mu England. Mmodzi wa wopikisana nawo anga anandipambana ine mchigwirizano ndi masewera apa bwalo, koma chifukwa cha magredi anga ofananako, iwo anafuna kunditumiza, limodzi ndi iye, ku Oxford University. Ndinayamikira kuti ndinafika ku muyezo wofikira zoyenerera kaamba ka kupeza chiphaso cha maphunziro, ndipo machibadwa, ichi chikanakhala choyamikiridwa kwambiri.
“Ichi ndi Chowonadi!”
Timakumbukira kuti panthawi ina Yesu Kristu ananena kwa ophunzira ake: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Chaka chimodzi pambuyo pake, mu 1913, mbale wanga Albert anapeza “chowonadi” mu Chicago. Kodi ndimotani mmene Albert anapezera “chowonadi”?
Usiku wina pa Loweruka lina lake mu ngululu ya 1913, Albert anapita kukagona msanga ku chipinda chogonamo cha mu YMCA kumene anali kukhala pamene anali kugwira ntchito mu Chicago. Pambuyo pake, mnzake wokhala naye mu chipinda chimodzi analowa mu chipindamo akumalongolosa vuto. Iye anaitanidwa usiku umenewo ku nyumba ya a Hindman ndi akazi awo, ndipo mwana wawo wamkazi Nora anayenera kukhala ndi bwenzi lake lachikazi kunyumbako. Asungwana awiri akakhala ambiri koposa kwa mnzake wogona naye mchipinda chimodzi wa Albert kuwasamalira iye yekha. Ndi changu, Albert anapita ku chochitikacho. Mkati mwa chochitika cha madzulowo, wogona naye m’chipinda chimodzi wa Albert anali kutchuka ndi akazi achichepere awiriwo. Koma a Hindman ndi akazi awo anamamatira pa Albert, kumusonyeza iye ku ziphunzitso za Watch Tower Bible and Tract Society.
Albert kenaka ananditumizira ine kabukhu kokhala ndi mutu wakuti Where Are the Dead? (Kodi Akufa Ali Kuti?) kolembedwa ndi dokotala wa ku Scotland, John Edgar, chiwalo cha Mpingo wa Glasgow wa International Bible Students. Poyamba, ndinakaika kabukhuko pambali. Kenaka madzulo ena, pamene ndinali ndi nthawi yochepera ndisanapite kukaimba, ndinayamba kuliwerenga iro. Ndinalipeza iro kukhala losangalatsa kotero kuti sindinathe kuliika pansi. Ndinapitirizabe kuwerenga iro pamene ndinali kuyenda kwa mtunda wa mailo imodzi kukafika ku tchalitchi cha Presbyterian. Popeza chitseko cha tchalitchi chinali chidakali chotseka, ndinakhala pa masitepi amiyala yozizira ndi kupitirizabe kuwerenga. Mtsogoleri wa kwaya anafika ndipo, kuwona mmene ndinaliri womwerekera mu chimene ndinali kuwerenga, anati: “Chimenecho chiyenera kukhala china chake chosangalatsa.” Ndinayankha: “Icho chiridi!”
Popeza kuti ndinasangalala kwambiri ndi chowonadi chimene ndinali kuphunzira, lingaliro linabwera kwa ine lakumufunsa mlaliki, Dr. Watson, zimene iye anaganiza ponena za kabukhuko. Chotero madzulo amenewo, ndinakapereka kabukhuko ndi kufunsa: “Dr. Watson, kodi nchiyani chomwe mumadziwa ponena za ichi?”
Iye anatenga kabukhuko, kukatsegula, ndipo kenaka ndi kumwetulira kosasonyeza ulemu: “Oh, limenelo linayenera kukhala lina la zinthu za Russell. Kodi nchiyani chimene iye amadziwa ponena za phunziro lonena za chifuno cha munthu padziko lapansi?”Ndinakhumudwitsidwadi kwambiri ndi kawonedwe kake konyodola. Pamene ndinakatenga kabukhuko ndinatembenukira kumbali, ndinalingalira kwa ine mwini: “Sindisamala kanthu ponena za zimene iye amaganiza ponena za ichi. Ichi ndi CHOWONADI!”
Pasanapite nthawi yaitali, paumodzi wa maulendo ake ku mudzi, Albert anandibweretsera ine mavoliyumu atatu oyamba a Studies in the Scriptures, olembedwa ndi Charles Taze Russell. Albert anandiyanjanitsanso ine ndi mpingo wa kumaloko wa Ophunzira Baibulo, omwe amasonkhana pafupi ndi tchalitchi cha Presbyterian. Ndinali wosangalatsidwa ndi zimene ndinali kuphunzira ndipo mwamsanga ndinalingalira kuti nthawi inabwera kaamba ka ine kudula mayanjano anga ndi Tchalitchi cha Presbyterian.
Chotero pambuyo pake, pamene Albert anatichezeranso ife kachiwiri, tinapita kumaphunziro a Dr. Watson pa Sande usiku wina. Pambuyo pake, Albert ndi ine tinapita kumene iye amapatsana chanza ndi ansembe omwe anali kuchoka. Ndinanena kwa iye: “Dr. Watson, Ine ndikuchisiya tchalitchi.”
Iye anati: “Ndinadziwa za chimenecho! Ndinadziwa za chimenecho! Kungoyambira panthawi imene ndinakuwona iwe ukuwerenga zinthu za Russell. Munthu amene uja, Russell, sindingamulole iye kulowa mkati mwachitseko changa!” Iye kenaka anawonjezera: “Fred kodi siukuganiza kuti chingakhale bwino ngati utalowa mu chipinda changa chopatulika ndi kupemphera pamodzi?” Ndinamuuza iye: “Ayi, Dr. Watson, ndasintha maganizo anga.”
Ndi chimenecho, Albert ndi ine tinatulukamo mu tchalitchi. Linali lingaliro la ulemerero lotani nanga kumasulidwa kuchokera ku ukapolo ku njira ya chipembedzo yomwe inali kuphunzitsa zinthu zonyenga! Chinali chosangalatsa chotani nanga kutengedwa mu mpingo wa Ophunzira Baibulo a Dziko Lonse, amene anali omvera kotero ku Mawu a Mulungu! Pa April 5, 1914, mu Chicago, Illinois, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga—monga mmene tinkatchulira kudzipereka—mwa ubatizo wa m’madzi.
Sindinakhalepo wachisoni kuti, mwamsanga zisanapangidwe zilengezo zopangidwa ndi olamulira a maphunziro ponena za zotulukapo za mayeso kaamba ka Cecil Rhodes Scholarship, ndinalemba kalata kwa olamulira ndi kuwachenjeza iwo kuti ndinali nditataya chikondwerero mu Oxford University scholarship ndipo kuti iwo ayenera kusandiika ine pandandanda ya opikisana. Ichi ndinachita ngakhale kuti mphunzitsi wanga wamkulu wa Chigriki pa yuniversite, Dr. Joseph Harry, anali atandidziwitsa kale kuti ndinali nditasankhidwa kaamba ka kulandira iyo.
Miyezi iwiri pambuyo pake, kapena pa June 28, 1914 kuphedwa kwa Archduke Ferdinand wa ku Austria-Hungary ndi mkazi wake kunachitika pa Sarajevo mu Bosnia. Patsiku lomwelo, Ophunzira Baibulo a Dziko Lonse anali ndi tsiku lawo lachitatu la msonkhano wawo pa Memorial Hall, Columbus, Ohio. Mwezi umodzi wokha pambuyo pake, kapena pa July 28, 1914, nkhondo yoyamba ya dziko ya mbiri yonse ya mtundu wa munthu inaulika. Ife Ophunzira Baibulo tinali kuyembekezera kuti mapeto a Nthawi za Amitundu za zaka 2, 520 adzafika pa October 1, chaka chimenecho.
Ndi chilolezo cha atate wanga, ndinachoka pa University ya Cincinnati mu May 1914, kokha milungu ingapo lisanathe gawo langa lachitatu kumeneko monga wachichepere wa mu kalasi yam’munsi. Mwamsanga ndinapanga makonzedwe ndi Watch Tower Bible and Tract Society kukhala koputala, kapena mpainiya, monga mmene minisitala wanthawi zonse amatchulidwira lerolino. Panthawi imeneyo ndinali mokangalika wogwirizana ndi Mpingo wa Cincinnati wa Ophunzira Baibulo a Dziko Lonse.
Pambuyo pake ndinakhala mkulu mu Mpingo wa Cincinnati. Chotero pamene United States of America inalowa mu Nkhondo ya Dziko ya I kumbali ya Maiko Ogwirizana, ndipo amuna achichepere anali kukakamizidwa kupita ku nkhondo, ndinapatulidwa monga m’minisitala wa uthenga wabwino.
Kumudziwa Mbale Russell
Pakati pa zochitika za m’moyo wanga zomwe zinachitika kumbuyoku zomwe ndimayang’ana ndi chisangalalo zinali nthawi pamene ndinasangalala kukumana ndi prezidenti woyamba wa Sosaite, Charles Taze Russell. Poyamba ndinakhala woyanjana naye mwaumwini tsiku limodzi lisanafike tsiku lowonetsa mbali yoyamba ya Zithunzithunzi za Chilengedwe pa Music Hall pa Sande, January 4, 1914. Loweruka limenelo mkulu wa Mpingo wa Cincinnati anakumana nane kunja kwa Music Hall ndikunena kuti: “Ndikukuuza kuti, Mbale Russell ali mkatimo, ngati upita kumbuyo kwa pulatifomu udzamuwona iye.” Mofunitsitsa kwambiri ndinalowa mkati ndipo kenaka ndinadzipeza ine mwini ndikulankhulana naye mwachindunji. Iye anabwera kudzayendera makonzedwe kaamba ka kuperekedwa koyamba kwa chitsanzo cha Zithunzithunzi za Chilengedwe.
Kenaka mu 1916 iye anali kulunzanitsa ulendo wa pa sitima ya panjanji mu Cincinnati ndipo anali ndi maora angapo omwe anakhalapo. Mlongo wina ndi ine, pamene tinauuzidwa za icho, tinathamangira ku malo oima sitima ya panjanji, kumene tinamupeza iye limodzi ndi mlembi wake. Iye anali atabweretsa chakudya chamasana limodzi naye, ndipo pamene nthawi ya chakudya chamasana inafika, iye anachigawana icho ndi ife.
Pamene tinamaliza kudya chakudya chamasana, iye anatifunsa ife ngati wina wake anali ndi funso lochokera mu Baibulo. Ndinafunsa ponena za kuyenerera kwa kuukitsidwa kwa Adamu pokhala kuti iye anali wochimwa mwadala, wosalapa. Ndi kumwetuliram’maso, mwake iye anayankha: “Mbale, ukufunsa funso ndi kuliyankha panthawi imodzimodziyo. Tsopano, kodi nchiyani chimene chinali funso lako?”
Bukhu la “The Finished Mystery”
Pa Lachiwiri, October 31, 1916, Charles Taze Russell anamwalira, asanatulutse voliyumu yachisanu ndi chitfriri yandandanda yake ya Studies in the Scriptures. Pamene anali pa kama yake ya imfa, mu sitima pamene anali kubwerera kuchokera ku California, anafunsidwa ndi mlembi wake ponena za voliyumu yachisanu ndi chiwiri, iye anayankha: “Wina wake adzayenera kulemba iyo.”
Mchaka chotsatira, 1917, voliyumu yachisanu ndi chiwiri inawoneka monga ndemanga pa mabukhu aulosi a Ezekieli ndi Chivumbulutso, limodzi ndi kulongosola kosangalatsa kwa Bukhu la Nyimbo ya Solomo. Sosaite inakonzekera kugawira kosangalatsa kwa bukhu latsopanolo. Mofananamo, iwo anatumiza makatoni a voliyumu ya chisanu ndi chiwiri imeneyi kwa ena mu mipingo kuzungulira mu United States monse. Makatoni ambiri anatumizidwa ku nyumba yanga pa 1810 Baymiller Street, Cincinnati, Ohio, ndi kusungidwa pamene ndinali kudikira malangizo owonjezereka ponena za ndimotani mmene za mkatimo zinayenera kugawiridwa.
Panali masamba asanu ndi atatu a The Finished Mystery omwe anali ndi mawu otsutsa omwe ananenedwa ndi akulu a boma ponena za nkhondo. Pansi pa kufulumizidwa ndi magulu achipembedzo a Chipembedzo cha Dziko, Katolika ndi a Protesitanti, boma la United States linadzutsa zitsutso, chotero masamba 247-54 anachotsedwamo. Pambuyo pake, pamene The Finished Mystery linagawidwa kwa anthu, malongosoledwe anapangidwa kwa iwo ponena za nchifukwa ninji masamba amenewa anali kusowa. Boma la United States silinakhutiritsidwe ndi kachitidwe kameneka, ndipo pansi pa kufulumizidwa kowonjezereka ndi magulu a chipembedzo a mdzikolo, ilo linaletsa voliyumu yonse yachisanu ndi chiwiri ya Studies in the Scriptures.
Ndimakumbukira kuti m’mawa mwina pa Sande ndinali kugwira ntchito pa chitseko chakumbuyo cha nyumba yathu. Amuna ena anayenda kufika kunyumba, ndipo mtsogoleri wawo anatembenuza kolala ya khoti yake, kundisonyeza ine baji yake ya chitsulo ndikulamulira kulowa m’nyumbamo. Chotero ndinaloledwa kuwalola iwo mkati ndi kuwasonyeza makatoni omwe anali ndi makope a The Finished Mystery. Pambuyo pa masiku ochepa, iwo anatumiza galimoto ndi kuwatenga mabukhu onse.
Pambuyo pake ndinamva kuti Joseph F. Rutherford, prezidenti wachiwiri wa Watch Tower Society, ndi anzake ena asanu ndi awiri omwe anali kutumikira pamalikulu ku Brooklyn molakwa anaimbidwa mlandu wa kulowerera mu zoyesayesa za nkhondo za United States. Iwo anagamulidwa kutumikira zaka 20 ku Atlanta Federal Penitentiary pa ulionse wa milandu inayi, zigamulozo, ngakhale kuli tero, zinayenera kuchitidwa pantnawi ina. Nkhondo inatha pa November 11, 1918, ndipo kena ka pa March 25, 1919, Mbale Rutheiford ndi anzake anamasulidwa kwakanthawi. Iwo kenaka anamasulidwa kotheratu. Bukhu la The Finished Mystery linachotsedwanso pansi pa chiletso ndi kulamuliridwa kuti liyambe kugawiridwa mwaufulu kachiwirinso.
Chinali chosangalatsa kwambiri chotani nanga kwa ife pamene Sosaite inakonzekeretsanso kaamba ka msonkhano wathu woyamba wapambuyo pa nkhondo pa Cedar Point, pa nsonga ya kachisumbu pafupi ndi Sandusky, Ohio, pa September 1-8, 1919. Unali mwawi wosangalatsa kwambiri kaamba ka ine kupezeka pa msonkhano umenewu.
Kuitanidwa kupita ku Betele
Mu chaka chotsatiracho mu 1920, Prezidenti Rutherford anavomereza chiitano chokapereka nkhani yapoyera kwa khamu mu Cincinnati, Ohio. Ndinali kupanga ntchito yanga ya ukoputala panthawiyo, ndipo Mbale Rutherford anandiitana ine kukamulembera iye kalata kufunsira kaamba ka utumiki pa malikulu a Betele ya ku Brooklyn.
Ndinatumiza kalatayo, ndipo pambuyo pa kulandira yankho labwino, ndinakwera sitima ulendo wa ku Mzinda wa New York. Lachiwiri madzulo, June 1, 1920, ndinafika kumeneko ndipo ndinalandiridwa ndi Leo Pelle, bwenzi langa lakale kuchokera ku Louisville, Kentucky, ndipo iye ananditsogolera ku nyumbaya Betele. Tsiku lotsatira, Lachitatu, ndinagawiridwa kukhala chipinda chimodzi ndi HugoRiemer ndi Clarence Beatty mu chipinda chakumwamba kwadenga, kukhala wanambala102 mu banja la Brooklyn Betele.
Sosaite inali itakhazikitsa malo ake osindikizira oyamba pa 35 Myrtle Avenue, amene pansi pake panakhazikitsidwa kaamba ka makina athu osindikizira oyamba, omwe tinawatcha Battleship chifukwa cha msinkhu wake. Tinali kusindikiza magazini atsopano a Sosaite okhala ndi mutu wakuti The Golden Age—kenaka otchedwa Consolation ndipo tsopano Galamukani! Pamene magaziniwo anali kutuluka pansi ndipo anali kuyendetsedwa pa mawaya pa thabwa lozondoka, ndinawasonkhanitsa iwo pamodzi, kuwagwedeza iwo ndi kuwaunjika pamodzi kaamba ka kuwadula ndi kusamaliridwa.
Loweruka m’mawa, pamene makina osindikizira sanali kutulutsa magazini, unyinji wa abalefe tinali kukuta magazini mu pepala la khaki lokhala ndi maina ndi makeyala a anthu olembetsa. Kenaka tinali kuwatseka iwo kaamba ka kusamaliridwa ndi positi ofesi. Ndinapitiriza kuchita ntchito imeneyi kwa miyezi ingapo kufikira pamene Donald Haslett, ye mwe anali kutumikira pa Desiki la Makoputala, anachoka kukakwatira Mabel Catel. Kenaka ndinasamutsidwa kuchokera ku 35 Myrtle Avenue kupita ku ofesi ya Sosaite ku 124 Columbia Heights kukatumikira pa Desiki yaMakoputala.
Ndiponso, monga chiwalo cha Mpingo wa New York, ndinagawiridwa kukatsogoza phunziro la bukhu pa nyumba ya banja la a Afterman mu dera la ku Ridgewood mu Brooklyn.
Mwawi wa Wailesi ndi Misonkhano
Ndinapitiriza kutumikira pa Desiki ya Makoputala kufika mu 1926. Panthawiyo, Watch Tower Bible and Tract Society inali itakhazikitsa pa Staten Island nyumba yake ya wailesi yoyamba, WBBR. Mmenemo munali mu 1924. Ndinali ndi mwawi wachimwemwe wa kutumikira pa maprogramu a Sosaite, osati kokha kupereka nkhani komanso kupereka nyimbo, ndipo ngakhale kuimba mandolin ndi kugwirizana kwa piano; Kuwonjezerapo, ndinaimba tenala yachiwiri pa gulu lathu loimba la amuna la mu WBBR. Ngakhale kuli tero, Mbale Rutherford, monga prezidenti wa Sosaite, anali mlankhuli wowonetsedwa pa WBBR ndipo anali ndi khamu lalikulu la amvetseri.
Munali mu chaka cha 1922 pamene msonkhano wa Watch Tower Bible and Tract Society unapangidwa kwanthawi yachiŵiri pa Cedar Point, Ohio. Pamenepa tinafulumizidwa mwaphamvu ndi Mbale Rutherford “kulengeza, kulengeza, kulengeza Mfumu ndi ufumuwake.”
Umodzi wa mwaŵi wanga wamtengo wapatali kwambiri mu zaka za mu ma 20 unali kutumikira ndi Mbale Rutherford pa msonkhano wa mitundu yonse mu London, England, mu 1926. Kumeneko iye anapereka nkhani yapoyera mu Royal Albert Hall mu London pamaso pa amvetseri ochuluka pambuyo pa kuimba kwanga nyimbo mchigwirizano ndi organi yotchuka ya mu holoyo.
Usiku wotsatirapowo iye analankhula kwa amvetseri a Chiyuda pa “Palestine kaamba ka Ayuda—Chifukwa ninji?” ndipo ndinaimba nyimbo kuchokera mu Handel’s Messiah, “Chitonthozo Kwa Inu, Anthu Anga.” Zikwi za Ayuda zinapezekapo pa msonkhano wapadera umenewo. Panthawiyo, molakwika tinali kugwiritsira ntchito maulosi a mu Malemba a Chihebri kwa Ayuda akuthupi, odulidwa. Koma mu 1932 Yehova natsegula maso athu kuwona kuti maulosi amenewo anali kugwiritsidwa ntchito kwa Israyeli wauzimu.
Ndipo chinali chosangalatsa chotani nanga kwa ine kukhalapo pa msonkhano wa Columbus, Ohio, mu 1931 pamene Mbale Rutherford anapereka ‘dzina latsopano’ Mboni za Yehova, ndipo tonse a ife tinalitenga ilo mwathumanzi! Mwamsanga pambuyo pake, mipingo yonse ya anthu a Yehova kuzungulira dziko lonse inatenga ‘dzina latsopano’ limenelo.—Yerekezani ndi Yesaya 62:2.
Lachisanu, May 31, 1935, inandipeza ine ndikutumikira monga wotsogoza gulu loyimba mu dzenje pansi pa pulatiformu ku imene Mbale Rutherford anapereka nkhani yake yosangalatsa pa Chivumbulutso 7:9-17, molondola kutilongosolera ife umembala wa “khamu lalikulu” losonyezedwa pamenepo. Limene limatchedwanso gulu la Yonadabu mwapadera linaitanidwa kupezekapo, ndipo chifukwa chake kuchokera pamenepo chinakhala chodziwika pamene Mbale Rutherford anasonyeza kuti“gulu lalikulu” (King James Version), kapena“khamu lalikulu,” linayenera kupangidwa ndi “nkhosa zina” za “mbusa wabwino” Yesu Kristu. (Yohane 10:14, 16, KJ) Chinali chochitika chosangalatsa. Chinali chosangalatsa mtima chotani nanga kwa ine pamene tsiku lotsatira, Loweruka, June 1, anthu opezeka pa msonkhano 840 anamizidwa m’madzi kuchitira chizindikiro kudzipereka kwawo kwa Mulungu kudzera mwa Kristu ndi chiyembekezo cha dziko lapansi la paradaiso! Kuyambira pamenepo kupita mtsogolo, chiŵerengero cha nkhosazina” za Kristu chinapitirizabe kupitirira kutalitali, chiŵerengero chomachepa cha “kagulu ka nkhosa” ka ophunzira onga nkhosa odzozedwa ndi mzimu a Mbusa Wabwino, Yesu Kristu.—Luka 12:32.
Komabe, pamene Nkhondo ya Dziko ya II inaulika mu 1939, chinawoneka ngati kuti ichi chinatanthauza kutha kwa kusonkhanitsa kwa “khamu lalikulu.” Ndimakumbukira Mbale Rutherford akunena kwa ine tsiku lina: “Chabwino, Fred, chikuwoneka ngati kuti ‘gulu lalikulu silidzakhala lalikulu. Tinazindikira zochepa ponena za kusonkhanitsa kwakukulu komwe kunali kutsogolo.
Sosaite inayambitsa makina oulutsira okhoza kunyamula mu 1934, ndipo kujambulidwa kwa maphunziro a Prezidenti Rutherford kunagwiritsidwa ntchito kuyambitsa mabukhu a Baibulo. Pamene zojambulidwa zake zotembenuzidwa mu Chispanish zinatuluka, ndinamamatira pa kuzigwiritsira ntchito izo mu kufikira anthu olankhula Chispanish pafupi ndi fakitare yathu pa 117 Adams Street. Kenaka, mwa maulendo obwereza, ndinathandiza anthu okondwerera kuphunzira chowonadicha Baibulo, ndipo kudzera mwanjira imeneyi kenaka ndinapatsidwa mwaŵri wa kukhazikitsa mpingo woyamba wa anthu olankhula Chispanish mu Brooklyn. Ndakhala ndi Mpingo wa Brooklyn Spanish, woyambirira, kuyambira pamene unakhazikitsidwa.
Masinthidwe mu Uprezidenti wa Sosaite
Pa imfa ya Mbale Rutherford pa January 8, 1942, Nathan H. Knorr anamulowa mmalo iye ku uprezidenti wa Sosaite. Mosasamala kanthu za ukali wa nkhondo ya dziko yachiŵiri nkhani yake yapoyera mu chilimwe cha 1942 pa mutu wakuti “Mtendere—Kodi Ungakhalitse?” unabweza kayang’anidwe kathu kaamba ka mtsogolo mwaposachedwa. Mwamsanga pambuyo pake, Mbale Knorr anatsegula Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower pa Kingdom Farm Lolemba, February 1, 1943, ndi ophunzira zana akupanga kalasi loyamba. Ndinali ndi mwaˆri wa kutumikira pa programu kaamba ka nthawi ya kuperekedwa. Mbale Eduardo Keller, Maxwell G. Friend, Victor Blackwell, ndi Albert D. Schroeder anatumikira monga aphunzitsi.
Mu nkhani yotsegulira, Mbale Knorr anatichenjeza ife kuti Sosaite inali ndi ndalama zokwanira kutsogoza sukuluyo kwa zaka zisanu. Koma tawonani, lerolino Yehova Mulungu Wamphamvu yonse waipanga sukuluyo kugwira ntchito kuwirikiza nthawi zisanu ndi zinayi za utali umenewo!
Unali mwaŵi wosangalatsa kwambiri kugwirizana ndi Nathan H. Knorr. Ndinazindikira zochepa kuti pamene iye anabatizidwa pambuyo pa kupereka kwanga nkhani ya ubatizo pa July 4, 1923, m’mphepete mwa Little Lehigh River kunja kwa mudzi wake wa Allentown, Pennsylvania, kuti iye adzakhala prezidenti wachitatu wa Watch Tower Bible and Tract Society.
Pansi pa uprezidenti wa Mbale Knorr, ndinayenda mokulira, kulankhula ku misonkhano yaikulu ya abale kuzungulira padziko lapansi—kuphatikizapo Latin America ndi Australia—kuwalimbikitsa iwo kukhalabe okhulupirika. Pa chimodzi cha chochitika chotero, mu 1955, pamene panali chiletso pa ntchito ya Mboni za Yehova mu Spain, ndinatumikira msonkhano wachinsinsi mu nkhalango kunja kwa Barcelona. Kusonkhana kwathu kwa abale a Chispanish kunazunguliridwa ndi apolisi a chinsinsi okhala ndi zida, ndipo amuna anatengedwa mumagalimoto kupita ku malikulu a polisi. Kumeneko tinasungidwa ndi kufunsidwa. Popeza ndinali nzika ya Chiamerica, ndinanamizira kuti sindidziwa Chispanish. Ndiponso. alongo awiri anali atathawa ndi kudziwitsa American Consulate ponena za kumangidwa kwanga, ndipo iwo, pambuyo pake, analankhulana ndi apolisi. Kukhumba kupewa chochitika chadziko lonse ndi kusaulutsidwa, iwo kenaka anatibweza ife alendo, ndipo pa mbuyo pake, abale enawo. Pambuyo pake, unyinji wa ife tinasonkhana pamodzi ku nyumba ya Mbale Serrano ndipo tinasangalala mokulira pa chipulumutso cha Yehova kwa anthu ake. Mu 1970 Spain inapereka kuzindikirika kwalamulo kwa Mboni za Yehova. Lerolino tiri ndi ofesi ya nthambi pafupi ndi Madrid, ndipo chaka chapita gulu mu Spain linaphatikizamo ofalitsa a Ufumu oposa 65, 000, ndi mipingo kuzungulira mu dzikolo.
Pa Jun 8, 1977, Nathan H. Knorr anamwalira, kumaliza ntchito yake ya padziko lapansi, ndipo ine ndinalowa m’malo mwake mu ofesi ya uprezidenti wa Sosaite. Mbale Knorr anatumikira kwa zaka zoposa 35 mu uprezidenti, utali woposa aliyense wa awiri a maprezidenti oyambirira a Sosaite, Russell ndi Rutherford. Monga chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndagawiridwa kutumikira ku Publishing Committee ndi ku Writing Committee ya Bungwe Lolamulira.
Uli mwaŵi waukulu ndi chisangalatso kupitiriza kutumikira mu maofesi a Sosaite pa 25 Columbia Heights. Ichi chimaitanira pa kuyenda kokhazikika pa tsiku la ntchito pakati pa maofesi ndi nyumba ya Betele—masewero akuthupi abwino kwambiri kaamba ka thupi lomakula. Ngakhale kuti ndiri ndi zaka 93 zakubadwa ndipo maso anga sapenya bwino kwenikweni, ndiri wosangalala kwambiri kuti Yehova wandidalitsa ine ndi umoyo wabwino, kotero kuti sindinaphonyeko tsiku limodzi la ntchito chifukwa chakudwala kwa zaka 66 pa Betele, ndipo ndidakali wokhoza kutumikira nthawi zonse. Icho chakhaladi chiyanjo chaumulungu kwa ine kukhala pano kuyambira 1920 ndi kuwona kukula ndi kufutukuka kwa gulu pa malikulu ku Brooklyn ndi kuzungulira dziko lonse lapansi.
Ndi chidaliro chotheratu mwa Wolamulira Wadziko Lonse, Yehova Mulungu ndi Mkulu wa Nkhondo wake, Yesu Kristu, yemwe ali pamwamba pa khamu la aserafi, akerubi, ndi angelo oyera akumwamba, ndimayang’ana kutsogolo, panthawi ino ya kulemba kwanga, limodzi ndi mamiliyoni a Mboni zinzanga, kuchimene Baibulo linasonyeza kuti chidakali kutsogolo: kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, dziko la chipembedzo chonyenga, ndi nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse pa Armagedo, yothera muchipambano cha zipambano kumbali ya Wolamulira Wadziko Lonse, Yehova Mulungu, yemwe ali “kuchokera kunthawi zosatha kunka kunthawi zosatha.” Haleluya!—Masalmo 90:2, Byington.
[Chithunzi patsamba 23]
[Chithunzi patsamba 24]
Pakati Mmunsilimodzi ndi ogwira nawo ntchito a pa Betele 1920
[Chithunzi patsamba 25]
Ndi N. H. Knorr 1961
[Chithunzi patsamba 26]
Akupangitsa msonkhano mu Japan 1978