Sukulu Yatsopano Yodzatsegulidwa!
Nkhani iyi iri ndi mbali ya mawu othera a tcheyamani pa kumaliza maphunziro kwa kalasi ya Gileadi ya 82.
KUYAMBIRA pa chiyambi chake mu February 1943, Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower yaphunzitsa aminisitala odzipereka oposa pa 6, 000 a Mboni za Yehova kaamba ka ntchito ya umisbonale. Mkati mwa zaka zoposa 40 zimene amishonale amenewa akhala akutumizdwa, maiko ambiri atsegulidwa kulandira umboni wokwanira ponena za Ufumu. Mkuyang’ana mmbuyo pa zimene Yehova wakwaniritsa, anthu a Mulungu mowonadi amasangalala kuwona kukwaniritsidwa kwa ulosi wodziwika kwambiri.
Pa Yesaya mutu 49, maversi 9-12, mneneriyo ananeneratu za kumasulidwa kwa anthu olungama amene anali kusungidwa monga akapolo achipembedzo mu “Babulo Wamkulu. Kupyolera mwa mtumiki wake wodzozedwa pa dziko lapansi, kuyitana kolamulira kwa Yehova kwachitidwa: “Nena kwa iwo amene ali omangidwa, [Tulukani!, NW] kwa iwo amene ali mumdima, ‘dziwonetseni nokha! iwo adzadya mnjira . . . iwo sadzakhala ndi njala pena ludzu; ngakhale thukuta pena dzuwa silidzawatentha; pakuti iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe amadzi adzawatsogolera . . . Tawonani! awa adzachokera kutali.” Kodi pakhala kuyankha? Inde pakhala! Owona mtima zana za zikwi abwera, kuchokera kumbali zonse, kudziwonetsera iwo eni kukhala a njala kaamba ka chowonadi, kukhumba kudyetsedwa ndi kusangalatsidwa ndi mawu a Mulungu, kufunafuna kuwomboledwa mwauzimu kuchokera ku ‘’Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:5) Tsopano iwo ali mkati mwa gulu la pa dziko lapansi la gulu lake la Ufumu, kudya pa chakudya chauzimu chochuluka.
Chiwonjezeko Chowonekera
Mkati mwa mu ma-1940, maiko mu Latin America ndi kudera la ku Caribbean anali pakati pa oyambirira kupindula kuchokera kwa amishonale a ku Gileadi. Munali ofalitsa ochepa kwambiri mmalo amenewa, chomwe chinapereka chitokoso chenicheni ku kupereka umboni wokwanira wa Ufumu. Mwachitsanzo, Puerto Rico inali ndi ofalitsa 25 okha mu 1944. Costa Rica inali ndi 181. Mexico inali ndi ofalitsa 2, 431 mu 1944 pamene omaliza maphunziro oyambirira a Gileadi anafika. Koma pamene anthu a njala yauzimu anabwera kutuluka mu mdima wa chipembedzo ndi kudziwonetsera iwo eni kukhala ofuna Ufumu wa Mulungu, iwo analalikira mwachangu, ndipo ena analembetsa mu ntchito yaupainiya. Amuna anafikira kaamba ka mathayo. Chotulukapo chake? Lerolino, Puerto Rico yachitira ripoti atumiki okangalika 21, 943, kuwirikiza nthawi zinayi monga mmene analiri mmaiko 12 ochitira ripoti mu gawo la Caribbean mu 1947. Costa Rica iri ndi ofalitsa ochuluka tsopano kuposa amene analimo mu Central America yonse mu zaka 40 zapita. Mu January wa chaka chino, Mexico inachitira ripoti chiwerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa oposa 206, 000, chomwe chiri chifupifupi chiwerengero cha ofalitsa onse amene anali kulalikira m’dziko lonse zaka 40 zapita.
Mu South America chakhala chofanafanako. Pamene amishonale anatumizidwa choyamba ku Argentina mu 1947, kunali ofalitsa 790. Lerolino kuli aminisitala okangalika 63, 613, kuchulukitsa nthaŵi 26 chiŵrerengero cholalikira mu maiko 12 osiyanasiyana mu South America zaka 40 zapitazo. Ndipo bwanji ponena za Brazil? Pamene amishonale oyambirira anatumizidwa kumeneko mu 1945, ofantsa 394 okha anali kuchita ntchito ya umboni. Koma iwo anapilira, ndipo Brazil tsopano yapitirira chiŵrerengero cha ofalitsa 200,000. Chimenecho chiri choposa kuchulukitsa nthawi 80 chiŵrerengero cha amene anali okangalika mu South America monse mu 1947. Maiko ena ku mbali imeneyi ya dziko achitiranso ripoti ziwonjezeko zowonekera.
Kutembenukira ku Far East, nakonso tikuwona chitsimikiziro chozizwitsa cha madalitso a Yehova pamene uthenga womasula wa chowonadi cha Ufumu unatheketsa zikwi kutuluka mu mdima. Pamene amishonale oyambirira anagawiridwa ku Japan mu 1949, ofalitsa asanu ndi atatu okha anali kuchitira ripoti Mu maiko asanu ndi atatu aku Asia ochitira ripoti ntchito zaka 40 zapitazo, kunali chiwonkhetso cha atumiki okangalika 475. Lerolino, kuli 116, 272 mu Japan mokha
Mu South Pacific munali nthambi ziwiri zokha kufika mu 1959. Ndi chithandizo cha ofalitsa ochokera ku Australia amene anapita kukatumikira kumene kusowa kunali kokulira, ndi zoyesayesa za ofalitsa ena a mpingo ndi amishonale ochepa, zikwi za anthu zafikiridwa ndi mbiri yabwino mu madera a zisumbu zosiyanasiyana. Kuli tsopano nthambi zowonjezereka zisanu ndi imodzi mu mbali imeneyo ya munda.
Mbiri ya kukula kwa mu Africa irinso yosangalatsa. Maiko 17 ochitira ripoti mu 1947 anali ndi chiwonkhetso cha ofalitsa 24, 896. Koma ndi thandizo la amishonale lakubukitsa mbiri yabwino mwachangu, mazana a zikwi mwamsanga anadziwonetsera iwo eni kukhala akufunafuna Yehova ndi chilungamo chake. Lerolino, mu Nigeria mokha, chifupifupi mboni 130, 000 zikulalikira mwachangu utnenga wa Ufumu.
Palibe chikaikiro chakuti mawu omasula a chowonadi a Yehova akukwaniritsa chimene iye afuna. Ndipo akukula ndi chipambano chenicheni cha chimene iye anawatumizira. (Yesaya 55:10, 11) Tsopano popeza kuti kututa kwakukulu kukusonkhanitsidwa, mawu amodzimodziwo akutitsimikizira kuti Yehova adzautsa abusa ophunzira ochuluka. (Yerekezani ndi Yeremiya 23:4. )Bungwe Lolamulira liri lozindikira mwachangu za kufunika komakulakula kwa amuna oyeneretsedwa kusamalira kaamba ka mathayo a m’munda ndiponso ndi a mu nthambi zosiyanasiyana za Sosaite. Masitepe atengedwa kuthandiza kufikiritsa chosowa chimenechi.
Sukulu ya Maphunziro a Utumiki
Inu omaliza maphunziro a kalasi ya Gileadi ya 82, limodzinso ndi onse amene munalipo kaamba ka chochitika chomangirira koposa chimenechi, mudzakhala achimwemwe kudziwa kuti mu chirimwe cha 1987 sukulu yatsopano idzatsegulidwa. Sukulu ya Maphunziro a Utumiki imeneyi, monga mmene idzatchedwera, idzakhala mbali ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, chotero kutheketsa abale ochokera ku maiko ena kupezekapo. Kalasi loyambirira likuyembekezeredwa kuyamba chifupifupi pa October 1 wa chaka chino mu mzinda wa Pittsburgh, Pennsylvania, U. S. A. , malo apakati oyambirira akukula koyambirira kwa Sosaite. Kutsatira kumaliza kwa kalasi loyamba, makalasi ena adzatsogozedwa pa nthawi yokhazikika mu mbali zosiyanasiyana za United States.
Ziyeneretso zotsimikizirika za mmalemba ziyenera kufikiridwa ndi awo amene adzalembetsedwa. Kuphunzitsako kudzaperekedwa poyamba kwa akulu osakwatira ndi atumiki otumikira osakwatira omwe ali ndi umoyo wabwino. Ngati ena ali apainiya, icho chiri chabwino koposa. Awo oyitanidwa kukapezeka ku sukuluyo ayenera kukhala ofunitsitsa kutumikira kutsatira kuphunzitsidwa kwawo, kulikonse kumene kuli kusowa mu munda wa dziko lonse. Ichi chidzaitanira ku kukhala ndi mzimu wa Yesaya, yemwe anadzipereka iyemwini mofunitsitsa, akumati: “Ndine pano! munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Inu omaliza maphunziro a kalasi la 82, ndi amishonale ena amene akutumikira kale mu maiko oposa zana, mungayang’ane kutsogolo mu nthawi yake kukhala ndi abale ena ophunzitsidwa akumagwira ntchito limodzinanu.
Njira yophunzitsira yatsopano yakonzekeredwa kaamba ka sukulu ya maphunziro a Utumiki. Sukuluyo yakhazikitsidwa ndi cholinga chofuna kuphunzitsa abale oyeneretsedwa omwe ali ndi chizolowezi china cha gulu monga akulu kapena atumiki otumikira mu mpingo.
Kufunika kwa Kupita Patsogolo.
Kutsatira tsiku la phwando la Pentekoste mu 33 C.E., mpingo wa Chikristu unali wokangalika kwambiri mkubukitsa mbiri yabwino mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse ndi mu Samariya, ndipo kenaka pambuyo pake, ku maiko ena apadziko lapansi. (Machitidwe 1:8) Chifupifupi mu chaka ena 60 C.E. mtumwi Paulo, yemwe anatsogolera ntchito za kulengeza pakati pa amitundu, analemba ku Akolose, akumati: “Chiyembekezo chimene mudachimva kale mu mawu authenga wabwino umene udafikira kwa inu monganso ku dziko lonse lapansi umabala zipatso numakula.”Kenaka, iye anawonjezera kuti akhulupiriri anzake amenewo ‘asasunthike kulekana nacho chiyembekezo cha uthenga wabwino umene adaumva, wolalikidwa ku cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.—Akolose 1:5, 6, 23.
Mu nthawi ina yochepera, Akristu ena oyambirira anabukitsa mbiri yabwino kutali ndi mofalikira. Yehova anapereka chiwonjezeko, ndi chiwerengero cha ophunzira chikumachuluka kwambiri. Ichi chinayitanira kaamba ka amuna oyeneretsedwa kwambiri kuphunzitsa mu mpingo ndi kuweta nkhosa. Mmodzi wa oyang’anira achichepere amene anapatsidwa thayo loterolo anali Timoteo. Kodi ndi chiyani chimene mtumwi Paulo anamufulumiza Timoteo kuchita? Sipanayenera kukhala kulekerera mkuphunzitsidwa kwake: “Ngati ukumbutsa abale zinthu izi udzakhala mtumiki wabwino wa Kristu Yesu, woleredwa mmawu a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata . . .ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo.” (1 Timoteo 4:6-8) Ichi chikakhala chofunika kwambiri kuposa kumamatira pa zikondwerero zina za umwini kapena zolondola, kuphatikizapo ngakhale chizolowezi chathupi ndi kuphunzira. Kuti akwaniritse utumiki wake mokwanira, Timoteo anayenera kupereka chisamaliro kwa iye mwini ndi chiphunzitso chake.
Inu omaliza maphunziro a kalasi iri la Gileadi mwalandira kuphunzitsidwa kaamba ka ntchito yanu ya umishonale. Mphatso zabwino zauzimu zaperekedwa kwa inu ndi oyang’anira oyeneretsedwa kuphunzitsa. Tsopano pali programu ina yabwino ya kuphunzitsa kaamba ka amuna oyeneretsedwa okhala ndi chizolowezi china mkusa malira kaamba ka mathayo a mpingo. Iwo adzakhala akuphunzitsa ndi kupembedza Mulungu mchiyang’aniro, komwe kudzawathandiza iwo kusunga kayang’anidwe kabwino ndi kuwakonzekeretsa iwo kulunjikitsa chidwi chawo pa zimene Paulo mowonjezereka analemba kwa Timoteo: “Munthu asapeputse ubwana wako, komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, mmawu, mmayendedwe, mchikondi, mchikhulupiriro, mkuyera mtima . . . usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza. Izi uzisamalitse, mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse.”—1 Timoteo 4:12, 13, 15.
Mofanana ndi Timoteo, abale osankhidwa kusamalira mathayo a mu mpingo lerolino, kuphatikizapo amuna achichepere, ayenera kuzindikira kuti iyi iri nthawi yoyenerera ndi yofulumira kaamba ka iwo kupanga kupita patsogolo kwawo kuwonekera. Mwakuchita tero, iwo adzapereka chitsimilkiziro mnjira yochokera mu mtima cha kufikira kayimidwe ka umulungu ndi cha kukhala ndi kayimidwe kenikeni kakusamalira kaamba ka zikondwerero zauzimu, chotero kukhala oyenerera kaamba ka mwawi woonjezereka wa utumiki.—Afilipi 2:20, 21.
Mchiyang’aniro cha kusowa komwe kulipo pa nthawi ino m’kukwaniritsa kwa chifuno cha umulungu, uli mwawi kugwiritsiridwa ntchito ndi Yehova kulikonse mkati mwa gulu lake. Tiri oyamikira chotani nanga kwa iye monga Mbusa wathu Wamkulu ndi kwa Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, kaamba ka mphatso yatsopano yapanthawi yake ya gulu, Sukulu ya Maphunziro a Utumiki!