Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/1 tsamba 30-31
  • Mu New Zealand—Tsiku Loyenera Kukumbukira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mu New Zealand—Tsiku Loyenera Kukumbukira
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubale Wachikristu
  • Maziko Okhazikitsidwa ndi Mboni Zokhulupirika
  • Dalitso la Yehova
  • Inali Yoyamba Zaka 100 Zapitazo
    Galamukani!—2001
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/1 tsamba 30-31

Lipoti la Olengeza Ufumu

Mu New Zealand​—Tsiku Loyenera Kukumbukira

“IFE TIRI osangalatsidwa kotheratu pokhala ndi inu. Sitidzaiwala ichi nkomwe!”

“M’mayanjano anga onse ateokratiki, sindinakhalepo nkomwe ndi chokumana nacho chofanana ndi ichi.”

“Chinawoneka ngati kuti tinali kusangalala ndi tsiku mu dongosolo la kachitidwe ka zinthu katsopano“

Izo zinali zina za ndemanga za nthumwi ku programu ya kupereka malikulu a nthambi ya Watch Tower Bible and Tract Society mu New Zealand, November 29, 1986. Kodi nchifukwa ninji anthu amenewo anasonkhezeredwa motero? Chifukwa ilo mowonadi linali tsiku lokumbukirika. Tiyeni tigawane ndi inu zina za zifukwa zake.

Choyamba, zipangizo zokongola zomwe zinali kuperekedwa zinalipanga tsikulo kukhala lokumbukirika. John E. Barr, wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, analongosola Nyumba ya Ufumu yongomangidwa chatsopanoyo ndi malo ophatikizidwako a nthambi monga “okoma, okongola, osangalatsa . . . Ntchito yotsirizidwayi imawunikira chisamaliro chosamalitsa ku tsatanetsatane, ku kukongola. Ikuwoneka kukhala yogwirizana.”

Ubale Wachikristu

Kenaka, chinali chokumbukirika kuwonera limodzi anthu akale ambiri, Mboni zomwe zakhala zikutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambirimbiri. M’chenicheni, awa anapanga unyinji waukulu pakati pa alendo oitanidwa 658. Pamene iwo anakumana ndi mabwenzi awo akale, ambiri a amene sanawawonepo kwa zaka makumi ochuluka, iwo anadzimva monga Paulo, pamene, pambuyo paulendo wautali, iye anakumana ndi abale kuchokera ku Roma: “Pamene Paulo anawona [abale ake], anayamika Mulungu nalimbika mtima.” (Machitidwe 28:15) Kuchitira umboni zitsanzo zoterozo za kukhulupirika kopirira​—ena amene analipo mosasamala kanthu za umoyo wovutika​—anali magwero achilimbikitso ndi chiyamikiro.

Tsikulo linali lokumbukirika, kachiwirinso, kaamba ka chokumana nacho chaubale wadziko lonse wotentha. Mboni za Yehova ziri mbali ya ubale wadziko lonse lapansi, ndipo ichi chinatsimikiziridwa ndi alendo omwe anabwera kuchokera ku maiko akutali monga ngati ku Australia, United States, Canada, Britain, ndi Taiwan, ndiponso kuchokera ku Papua New Guinea, Samoa, ndi zisumbu zina za ku South Pacific. Materegramu anabwera kuchokera kwa ambiri omwe sakanatha kufikapo mwaumwini, kuphatikizapo moni wochokera ku Bungwe Lolamulira, ziwalo za banja la pa Beteli ku Brooklyn, ndi kalasi la 82 la amishonale a sukulu ya Gileadi. Indedi, chinali cholimbikitsa chikhulupiriro kukhala ozindikira za chikondwerero cha abale ochuluka chotero m’maiko ambiri m’kuperekedwa kwa zipangizo za nthambi za mu New Zealand.

Maziko Okhazikitsidwa ndi Mboni Zokhulupirika

Kukumbutsidwa za mbiri yaitali ya ntchito yolalikira mu New Zealand kumene kunatsogoza ku kumangidwa kwa zipangizo zatsopano za nthambi zimenezi kunali kosangaiatsa ndipo kunapanganso tsikulo kukhala lokumbukirika. (Yerekezani ndi Ahebri 10:32. ) Monga mmene mlankhuli m’modzi ananenera: “Kufunika koteroko monga mmene aliri maziko a kuthupi a nyumba ya Beteli yatsopano imeneyi, apadera kwambiri ali maziko ophiphiritsira okhazikitsidwa ndi abale ndi alongo okhulupirika, odzipereka mwaumwini kubwerera m’mbuyo kuchiyambi kwa zanali.”

Ichi chinatsatiridwa ndi kufunsidwa kwa amuna ndi akazi okhulupirika 11 omwe anali ndi chiwonkhetso cha zaka 680 za utumiki wodzipereka. Iwo analankhula ponena za misonkhano yakale kwambiri mu New Zealand, mu 1913. Iwo anakumbukira kuvuta kwa upainiya mu South Island mu ma-1930, zovuta za zaka za Nkhondo ya Dziko II pa mene gulu linaletsedwa, kupangidwa kwa nthambi ya New Zealand mu 1947, kufika kwa amishonale a Gileadi oyambirira, ndi kumangidwa kwa Nyumba ya Ufumu yoyamba mu dzikomo mu 1950. Lingaliro lofala la awo ofunsidwa linali: ‘Tiri oyamikira chotani nanga kukhala pano ndi kuwona chitsimikiziro cha kuwonjezeka kumene, m’masiku oyambirira, sitikanalota nkomwe!’

Dalitso la Yehova

Mwinamwake chinthu chenicheni chimene chinapangitsa tsikulo kukhala losaiwalika chinali kuzindikira kuti dalitso la Yehova linali litatsogolera ntchito yomanga ndi kubweretsa iyo kukhala yopatsa chipatso. Moyenerera, mbali imodzi ya programu ya tsikulo inali ndi mutu wakuti:“Dzanja Lokoma la Mulungu Wathu Lotikhalira.”​—Nehemiya 2:8, NW.

Dzanja lokoma la Yehova linawonedwa m’kuthandiza ndi kugwirizana kwa anthu a malonda a kumaloko ndi olamulira, limodzinso ndi mikhalidwe Yachikristu yosonyezedwa ndi ogwira ntchito iwo eni pamalowo. Wamalonda m’modzi, akuchezera ku malo omanga, anazindikira: “Sindinayambe ndawonapo kwina kuli konse kudzimva kwa mtendere ndibata lomwe ndiri nalo pamene ndiri pano.”

Dalitso la Yehova linawonedwa m’kukoma mtima kwa Mboni wamba zozungulira m’dzikolo zomwe zinachirikiza projekitiyo mwa ndalama. Linawonedwanso m’kufunitsitsa kwa awo omwe anadzipereka iwo eni kuchita ntchito yomanga yeniyeniyo. Onse pamodzi, 1, 237 anadzaza mapepala ofunsira kupereka kwaufulu mautumiki awo, ena akuyenda ku malowo kuchokera ku maiko akutali ndipo kudzilipirira iwo eni kuthera milungu ingapo kapena miyezi kuthandiza ndi ntchito yomanga. Anatero mbaie m’modzi: “Kuthandizira pa malowa panali posinthira m’moyo wanga.”

Monga mmene Mbale Barr anatchulira mu nkhani yopereka, zipangizo za nthambi zatsopanozo ziyenera kuwonedwa monga “chisonyezero chakunja, chokhudzika cha Ufumu Waumesiya wa Mulungu wokhazikitsidwa tsopano.” Inde, iio linalidi tsiku lokumbukirika mu New Zealand. Pamapeto, panali chivomerezo chochokera mu mtima kumbali ya onse opezekapo kuchimango cholumbirira “chirikizo lotheratu ku gulu la Yehova monga likuimiridwa ndi nthambi yathu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena