Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/15 tsamba 5-7
  • Mbali Yowongoleredwa ya Akazi Dalitso Losakanizika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbali Yowongoleredwa ya Akazi Dalitso Losakanizika?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chotulukapo pa Ukwati ndi Banja
  • Zotulukapo Zoipa
  • Makhalidwe Abwino a m’Baibulo Ngwofutukulika?
  • Mtsogolo Mokhutiritsa​—Motani?
  • Mbali Yowongoleredwa ya Akazi mu Nthawi Zamakono
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • ‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chipani cha Akazi—Nchiyani Chimene Chachitika ku Icho?
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/15 tsamba 5-7

Mbali Yowongoleredwa ya Akazi Dalitso Losakanizika?

”MWAUNYINJI, akazi a mu zaka za m’makumi asanu ndi zitatu ali ophunzira bwino, a umoyo wabwino, ndi moyo wachikwanekwane, wautali.” Ndi mawu amenewa, magazini inamaliza nkhani yake yakuti: “Njira Imene Tinali; Njira Imene Tiri Tsopano.” Koma kodi chinganenedwe kuti mbali yowongoleredwa ya akazi yakhala kwenikweni dalitso losakanizika chifukwa cha zotulukapo zake zapadera?

Chotulukapo pa Ukwati ndi Banja

Mwachitsanzo, pali kuwombana kofala pakati pa umoyo wabwino wa banja ndi kulondola ntchito. Ripoti limodzi linanena kuti: “Oyang’anira achikazi mwachiwonekere ali osakhoza kupereka ku moyo wawo wa kunyumba malo oyambirira kuposa anzawo achimuna, ndipo iwo mwachiwonekere ali oyenera kuthamangitsidwa mu banja kuwirikiza kawiri.” Mungadabwe nchifukwa ninji. Profesala wodziwa zolinganiza zinthu pa California State University akulongosola: “Amuna amayang’ana pa mkhalidwe wa nyumba yawo monga dongosolo lochirikiza, pamene akazi amayiwona iyo monga cholemetsa. Amuna amabwera kunyumba ndi kupumula; ndicho chifukwa chake iye akugwirira ntchito. Koma kwa akazi chimaimira ntchito yowonjezereka.”

Ichi sichimagwira ntchito kwa akulu oyang’anira okha. Akazi a Chirussia akhala akugwira ntchito kwa mbadwo wotalikirapo kusiyana ndi mmene akhalira akazi a ku maiko a Kumadzulo. Iwo amapezabe kusamalira ntchito ndi banja kukhala cholemetsa. Mkonzi wa Chirussia wa Working Woman ananena kuti: “Akazi ali mtima wa banja ndipo ayenera kukhala otentha kuti apange mkhalidwe wotizinga wotentha ndi wachikondi.” Chotero iwo amayang’anizana ndi ntchito ziwiri, pamene amuna ambiri amalephera kugawanamo mu ntchito za m’nyumba.

Magwero ena akuwombana achitiridwa chitsanzo ndi mmodzi wa akazi achipambano kwambiri a mu Wall Street. Iye akunyada kuti: “Ntchito kwa ine iri chosangulutsa,” ndipo akuwonjezera, “Ndimakonda chimene ndikuchita, ndipo ndimapanga kuvomereza kochepa kwambiri”​—ngakhale kaamba ka banja lake. Ubwino wake umadalira pa mwamuna wake amene amayang’anira ana awo awiri, ngakhale kuti iye ali mwamuna wa bizinesi. Oyanjana nawo anzake akulongosola chikondwerero chake chosakaza monga “mwachiwonekere choipa kaamba ka maunsi abanja.”

Chiri chofanana ndi mmodzi wa nduna za boma zamakono. Banja lake silinapeze chisamaliro chambiri chifukwa cha zonulirapo zake za ndale zadziko. Pamene anali kukula, ana ake kawirikawiri anali kukhala ku nyumba ndi amalume awo chifukwa, tikuwuzidwa kuti, “chimodzi cha zinthu zomwe [anakonda] kwambiri chinali kungokhala pansi ndi kudya monga banja, china chake chimene sichinakonzedwe mokhweka” kunyumba.

Mkufufuza kwaposachedwa kwa oyang’anira achikazi anayi apamwamba mu Europe, mmodzi anavumbula kuti mwana wake wa mkazi wa zaka 12 anali kuleledwa mokulira kotheratu ndi mwamuna wake. Woyang’anira wina ananena kuti kokha pakutha kwa mlungu iye anali wokhoza kusamalira ana ake. Malinga ndi maripoti a nyuzi, khamu linawona kuti atatu a akazi amenewa anakhoterera ku kusoweka kwa chiyanjo chaumunthu.

Ndithudi, akazi ena ali ndi ntchito zakuthupi kokha chifukwa cha kufuna, mwinamwake chifukwa amuna awo anafa kapena anachoka panyumba. Chotero kwa akazi oterowo, kukhala okhoza kupeza ntchito kungakhale dalitso, koma kaya amafuna kapena ayi, iwo ayenera kupikisana ndi mbali zoipa.

Zotulukapo Zoipa

Kunena kuti kusinthidwa kwa mbali ya akazi kwakhala dalitso losakanizika chikuwonekera bwino koposa kuchokera ku zotulukapo zofala pamene akazi apambana amuna awo mu mphamvu ya kulandira ndalama kapena malo apamwamba antchito. Malingana ndi asing’anga odziwa zoyanjanitsa anthu, chikhoterero chimenechi “chikukhala chodziwika ndi magwero apadera a mavuto mu maukwati ambiri. Kudandaula kwa mwamuna mmodzi kuli kofala: “Ndimadziwa mwanzeru kuti ndimamuyamikira iye chifukwa cha chipambano chake. Koma mwamaganizo ndimadzimva moipa. Ndimadzimva kukhala wosiyidwa. Ndipo ndimadzimva kukhala wa mlandu chifukwa ndiri wokhumudwitsidwa koposa.” Ngati okwatirana onse awiri a Chikristu panthawi ina ayenera kugwira ntchito, kukambitsirana kwachikondi ndi kulingalira kungathandize kuchepetsa maganizo ndi zotulukapo zoipa zimenezo.​—1 Petro 4:8.

Nsonga ina yosonyeza kuti kupita patsogolo kopangidwa ndi akazi kuli dalitso losakanizika iri chigogomezero chimene opititsa patsogolo zikondwerero za akazi ambiri amaika pa zimene kwenikweni ziri kaamba ka ubwino wawo. The Coming Matriarchy inaloza kunthawi pamene dziko lidzatsogozedwa ndi akazi omwe ali odzikonda iwo eni ndi omwe akafunsa, “Nchiyani chimene chiripo kaamba ka ine?” Mosangalatsa, mkazi wa chipambano wogwira ntchito zandalama yemwe walongosoledwa papitapo amachiika icho chifupifupi mu njira imeneyo; iye sanali wosangalatsidwa m’kuthandiza ena kugwirizana kokha ngati iye anali pamalo akupeza phindu

ndi icho. Iye anavomereza kuti: “Malingaliro anga ali ozikidwa pa kupeza phindu lokulira.” Kodi ndi chanzeru chotani, m’chiyang’aniro cha uphungu wanzeru wa Yesu? Mu ulaliki wa pa Phiri iye anati: “Muyenera kuchita ndi anthu ena monga mufunira iwo kuchita ndi inu.” “Musadere nkhawa ponena za mawa, pakuti mawa lidzakhala ndi zodera nkhawa za ilo leni.” (Mateyu 7:12; 6:34, American Translation) Mwachidziwikire, akazi Achikristu amakalamira kusunga kayang’anidwe ka Yesu pa nkhani zoterozo.

Makhalidwe Abwino a m’Baibulo Ngwofutukulika?

Mosakaikira mbali yoipa kwambiri ya kusinthidwa kwa mbali ya akazi kuli kutayika kwa makhalidwe abwino. Zilozero zopangidwa ndi awo opititsa patsogolo zikondwerero za akazi kwa Mulungu ndi chipembedzo ziri zosawonekawoneka ndipo kawirikawiri zoipa kwambiri. Akazi amene amaleka mabanja chifukwa cha ntchito yawo kawirikawiri amachipanga kuti ukwati siuli woyenerera asanagonane.

Chikhoterero choipa cha machitachita akupititsa patsogolo zikondwerero za akazi chiri kuchirikiza kwake kwa kugonana kwa akazi okhaokha. Mu 1971 msonkhano wapachaka wa NOW (National Organization of Women) (National Organization of Women) unagamula: ”Kuti NOW ikuzindikira mphamvu ya ulamuliro wa mbali ziwiri wa akazi omwe amagonana akazi okhaokha, Kuti kuyenera kwa mkazi ku umunthu wake kumaphatikizapo kuyenera kwa kuika malire ndi kulongosola mkhalidwe wake wa kugonana ndi kusankha njira ya moyo imene angafune, Kuti NOW imazindikira kugwira ntchito kwa akazi ogonana okhaokha monga chodera nkhawa chokhazikitsidwa mwalamulo cha kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi.” Ngakhale kuli tero, yerekezani, chiweruzo cha Mulungu chopezeka pa Aroma 1:26, 27. Kawirikawiri chopitira pamodzi ndi kawonedwe ka opititsa patsogolo zikondwerero za akazi za kugonana kwa akazi okhaokha kuli kukhulupirira kwa kulamulira kuchotsa mimba. Profesala Billups Percy wa lamulo wa Tulane University anachikhazikitsa bwino icho: uKulingalira kuwonongedwa kwa kamwana komakula m’mimba monga ngati njira zina za mankhwala kuli kunyalanyaza mazana a maphunziro a upandu, maphunziro achipembedzo, ndi nthanthi ya makhalidwe abwino.”

Ripoti limodzi limanena kuti mu zaka khumi zapita upandu woipa kwambiri ku mbali ya akazi wawonjezeka mokulira kuposa umene uli pakati pa amuna. Pakati pa 1974 ndi 1979, chiwerengero cha akazi omangidwa mu United States kaamba ka kunyengeza chinawonjezereka chifupifupi ndi 50 peresenti, koma kuwonjezekako kunali kokha 13 peresenti pa amuna. Kuba ndalama za kampani kochitidwa ndi akazi kunawonjezereka mofananamo chifupifupi ndi 50 peresenti koma kokha ndi 1. 5 peresenti kwa amuna. Kumangidwa pakati pa akazi chifukwa cha kusaina maina a anzawo ndi kulemba manambala abodza pa malisiti kunawonjezeka ndi 27. 7 peresenti koma kunatsika ndi 10 peresenti pakati pa amuna. Mwachiwonekere mbali yosinthidwa ya akazi sinatulukepo mu kukhutiritsa kokwanira.

Kugwiritsira ntchito kwa fodya kwawonjezekanso pakati pa akazi. Kansa ya m’mapapo chifukwa cha kusuta ikulowa m’malo a kansa ya mabere monga chochititsa choyamba cha imfa pakati pa akazi. Mu chaka chimodzi chaposachedwa chinawerengera 25 peresenti ya imfa za kansa zonse pakati pa akazi ndi kuwonjezeka kwa liwiro la 7 peresenti chaka chirichonse.

Mtsogolo Mokhutiritsa​—Motani?

Kodi ntchito yodzilemba kapena yolembedwa imapatsa akazi ambiri chikhutiritso chathuthu mu moyo? Mwachiwonekere ayi, monga mmene ochulukira akuchipezera icho. Hilary Cosell, mkonzi wa Woman on a Seesaw: The Ups and Downs of Making It, anakamba vuto limeneli mu nkhani, akufunsa: “Ngati akazi analakwa pasadakhale kumbali ya ukwati ndi umayi ndi mkazi wa panyumba, kodi iwo angakhale akulakwanso kachiwiri kumbali ya ntchito yolembedwa, ntchito ndi chipambano?” Iye anafunsanso: “Kodi ife kwenikwenidi tingachite chirichonse chimene amayi athu anachita, ndipo chirichonse chimene atate athu anapanga?”

Mofananamo, mu The Cost of Loving, Megan Marshall anavumbula kuti “chinyengo cha kudziwa bwino ntchito mopambana kwambiri chinabisa pang’ono mabala a mwamseri: chikondi chogwiritsidwa mwala, mkhalidwe wa kugonana kokakamiza, kuyesera kwa kugonana kwa akazi okhaokha, kuchotsa mimba, kudula ukwati ndi kusungulumwa.” Iye akukamba mmene machitachita a akazi abafira “Nthanthi ya Ku- dziimira pa Okha,” koma kwa ambiri, ichi sichikugwira ntchito.

Marshall akumaliza kuti “tiyenera kukhulupirira mu chikondi cha nthawi yaitali kuti ukwati wabwino umachinjiriza,” kuti “munthu samadziyimira payekha,” ndi kuti “tiyenera kupeza ena oyenera kuwasamalira, ndi wina amene ayenera kutisamalira.” Ichi chimaitanira ku maganizo mawu a Mphunzitsi wamkulu koposa pa dziko lapansi, Yesu Kristu. “Muli chimwemwe chambiri mkupatsa koposa mkulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Ndithudi, anthu ali ndi chikhoterero cha kupita ku malekezero awa ndi aja. Chakuti mbali yowongoleredwa yamakono ya akazi siiri dalitso losakanizika chikumveketsedwa bwino ndi mawu a mneneri Yeremiya: “Sichiri kwa munthu woyenda kutsogoza mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Akazi Achikristu, mwakudziwa ndi masinthidwe otani amene awonekapo (otsagana ndi madalitso ndi mavuto) angachite bwino kuyamikira kufunika kwa kutsatira uphungu wa Mulungu. Zokumana nazo zasonyeza kuti “uyenera kukondedwa koposa golidi.” ‘Mkuusunga iwo pali mfupo yaikulu.​_masalmo19:7-11

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena