Kodi Miyendo Yake Inali Kuti?
“NKHOLE Yopotozedwa pa Mtanda, zofukulidwa Zotsalira Zikusonyeza.” Kodi munawonapo mutu waukulu chotero mu January 1971? Mwinamwake, popeza panali nkhani zambiri mu manyuzipepala pa “chitsimikiziro“ chatsopano ponena za imfa ya pa mtanda.
Pambuyo pa mutu wa pamwambawo, nkhaniyo inayamba: “Yerusalemu, Jan. 3 (Reuter)—odziwa za zinthu zofukulidwa pansi a ku Israel, pambuyo pa kufukula chinthu choyamba cha chitsimikiziro cha kupachikidwa pa mtanda, lero anena kuti chikusonyeza kuti Yesu Kristu ayenera kukhala anapachikidwa mu mkhalidwe wosiyana ndi uja umene umasonyezedwa pamtanda wa mwambo.”
Kodi chitsimikiziro chatsopanochi chinavumbula mmene Ayuda mu nthawi ya Yesu anali kuphedwa pamtanda kapena pamtengo? Kodi nchiyani chimene odziwa za zinthu zofotseredwa anagamulapo ponena za mkhalidwe wathupi wa nkhole? Kodi ichi chinali ndi chitsimikiziro chinachake pa imfa ya Yesu? Ndipo ndi molimba chotani, mungafunse, mmene chitsimikizirocho chinaliri?
Nsomali mu Zitendene
Kubwerera mu 1968 manda a mapanga oika anapezedwa mwatsoka pafupi ndi Yerusalemu. Mkatimo, pakati pa mafupa oikidwanso kachiwiri, panali chimene chinawonekera kukhala chopezedwa chowonekera—mafupa a ku zitendene obowoledwa ndi nsongolo wa dzimbiri. Dr. Nico Haas, katswiri wodziwa ziwalo za thupi ndiponso katswiri wodziwa mafuko a anthu wa pa Hebrew University-Hadassah Medical School, anatsogoza kufufuza kwa mafupa amenewa. Israel Exploration Journal yolemekezeka (1970, Volyumu. 20, masamba 38-59) inafalitsa matsirizidwe ake, omwe anatsogolera ku nkhani za mu manyuzipepala zodzutsa nthumanzi. Kodi nchiyani chimene chinali mamalizidwe amenewo?
lye anasimba kuti chomwe chinapezeka sichinali chirichonse koma munthu yemwe anaphedwa pamtanda mu zana loyamba. Motsimikizirika, chinawoneka kuti, zitendene ziwiri za nkholeyo zinakhomeredwa pamodzi pa mtengo Wowongoka, koma nSomaliwo unapindika pa nsOnga yake pamene unagunda mfundo ya mtengo. Pambuyo pa kufa kwa nkhole ya Chiyudayo, achibale ake anavutika kuchotsa nsomaliwo, chotero unasiyidwa mu zitendene zake pa kuikidwa. Popeza kuti nsomali umodzi unabowolamafupa onse awiri a zitendene ndipo popeza zinawoneka kuti mafupa a msongolo anaduka popindira, Dr. Haas anasimba kuti nkholeyo mwachiwonekere anaphedwa mu mkhalidwe wosonyezedwa pansipa. (Dr. Haas anadzimvanso kuti kukandika kwa fupa la kudzanja kunasonyeza kuti mikono ya munthuyo inakhome redwa pamtanda wopingasa. ) Inu mungakhale munawonapo zojambula zoterozo mu manyuzipepala kapena mu nkhani za magazini. Ambiri anali otenthedwa maganizo za chisonyezero cha mmene Yesu anafera.
Kachiwirinso, ngakhale kuti tero, mungachite bwino kufunsa: Kodi chitsimikiziro chimenecho chinali chodalirika, ndipo kodi icho m’chenichenidi chinasonyeza mkhalidwe Umene Yesu anafera?
Kutchukitsanso Zitendene
Mu zaka zochepa zotsatira, ophunzira ena otchuka, monga ngati Professor Yigal Yadin, anayamba kukaikira mapeto omwe Haas anawafikira. Pomalizira, Israel Exploration Journal (1985, Volyumu. 35, masamba 22-7) inafalitsa “Kutchukitsanso” kwa akatswiri odziwa za mafuko a anthu Joseph Zias (Israel Department of Antiquities and Museums) ndi Eliezer Sekeles (Hebrew University-Hadassah Medical School). Iwo anali ataphunzira chitsimikiziro choyambirira, zithunzithunzi, zisonyezero, ndi zithunzithunzi za pamapulasitiki za mafupawo. Mungakhale odabwitsidwa pa zina za zopeza zawo:
Nsomaliwo unali wofupikirapo kusiyana ndi mmene Haas wasimbira ndipo chotero sukanakhala wautali mokwanira kubowola mafupa a zitendene awiri ndi mtengo. Zidutswa za fupa sizinazindikiritsidwe bwino. Panalibe fupa lochokera ku chitende chachiwiri; nsomali unabowola kokha pa chitende chimodzi. Zidutswa zina za mafupa zinali zochokera kwa munthu winawake. Fupa lokandika la mkono silinali chitsimikiziro “chokhutiritsa” cha kukhomedwa pamtanda wopingasa; ‘m’chenicheni, zizindikiro ziwiri zofananazo zinawonedwa pafupa la nsongolo; palibe liri lonse la iwo limene linagwirizana ndi kupachikidwa.
Kodi ndi mapeto otani amene kusanthulanso kumeneko kunatsogolera? “Ponse pawiri kumanganso koyamba ndi komalizira kwa kupachikidwa [kwa Haas] kuli muzopangapanga ndi mu kakhalidwe ka anthu zosathekera pamene wina alingalira chitsimikiziro chatsopano . . . Sitinapeze chitsimikiziro chafupa la chitende cha kumanzere ndipo ndi kuwerengeranso kumene nsomaliwo unali wokwanira kukhomerera kokha fupa la chitende chimodzi . . . Kusoweka kwa kuvulaza kotupa ku dzanja la kutsogolo ndi zala za kumanja zikuwoneka kukhala zikulingalira kuti mikono ya munthu wokanidwayo inamangidwa osati kukhomeredwa.” Mukuwona pa tsamba lino mmene Zias ndi Sekeles akuganizira kakhalidwe ka munthuyo kaamba ka kupachikidwa.
Bwanji Ponena za Yesu?
Chotero, kodi nchiyani chimene ichi chimasonyeza ponena za mmene Yesu anaphedwera? Ndithudi, osati zambiri kwenikweni! Mwachitsanzo, monga mmene talongosolera pa tsamba 23, Yesu mwachiwonekere anaphedwa pa mtengo wowongoka popanda mtengo wina wopingasa. Palibe munthu lerolino amene angadziwe motsimikizirika kuti kaya ndi misomaii ingati imene inagwiritsiridwa ntchito mu nkhani ya Yesu. The International Standard Bible Encyclopedia (1979, Volyumu 1, tsamba 826) imachitira ndemanga kuti: “Chiwerengero chenicheni cha misomaii yogwiritsiridwa ntchito . . . yakhala nkhani ya kulingalirapo kosamalitsa. Mu zisonyezero zakale kwambiri za kupachikidwa mapazi a Yesu asonyezedwa kukhala okhomeredwa mosiyanako, koma muzaposachedwapa iwo apingasitsa ndi kukhomeredwa powongoka ndi msomali umodzi.”
Tikudziwa kuti manja ake kapena mikono sinangomangidwa kokha, popeza Tomasi pambuyo pake ananena kuti: “Ndikapanda kuwona m’manja ake chizindikiro cha misomaii.” (Yohane 20:25) Chimenecho chikanatanthauza kuti nsomali kupyola mu dzanja lirilonse, kapena pulula “misomaii” ingakhale inalozeraku zizindikiro za misomaii mu ‘manja ndi m’mapazi.’ (Onani Luka 24:39. ) Sitingathe kudziwa kwenikweni kuti ndikuti kumene misomaliyo inamubaya iye, ngakhale kuti mwachiwonekere munali m’dera la m’manja ake. Mbiri ya Malemba simapereka tsatanetsatane weniweni, ndiponso sifunikira kuchita tero. Ndipo ngati ophunzira omwe mwachindunji anafufuza mafupa opezeka pafupi ndi Yerusalemu mu 1968 sangakhale otsimikizira kuti ndimotani mmene mtembowo unakhazikitsidwira, icho m’chenicheni sichimatsimikizira mmene Yesu anakhazikitsidwira.
Ife chotero tizindikira kuti zisonyezero za imfa ya Yesu mu zofalitsidwa zathu, monga ngati zimene mukuwona pa tsamba 24, ziri kokha zisonyezero za luso zoyenerera za chochitikacho, osati ndemanga za kutsimikizirika kwa ziwalo zathupi. Zisonyezero zoterozo sizifunikira kuwunikira kusintha kapena malingaliro, owombana a ophunzira, ndipo zithunzizo mwachiwonekere zimapewa zizindikiro za chipembedzo zomwe zimachOkera ku chikunja chamakedzana.