Kukhulupirira Mizimu—Nchifukwa Ninji Pali Chikondwerero Chokulira?
FRANS ali mchirikizi wa tchalitchi cha Protestanti cha kumaloko. Ngati pali ntchito ya tchalitchi yofunika kuchita, iye ali woyambirira kupereka dzanja lothandiza. Wilhelmina analinso wowopa Mulungu. “Uyenera kupita ku tchalitchi,” iye amatero, ndipo amapita. Esther mofananamo amapezeka pa tchalitchi mokhazikika ndipo salola tsiku limodzi kupita popanda kunena mapemphero ake. Onse atatu ali ndi chinthu chimodzi chowonjezereka chofanana: Iwo alinso olankhula ndi mizimu.
Nzika zitatu zimenezi za Suriname siziri zokha. Pa dziko lonse lapansi, pali chikondwerero chomakulakula m’kukhulupirira mizimu. Talingalirani: Mu United States mokha, chifupifupi magazini 30 okhala ndi kugawiridwa kosakanizana kwa makope oposa 10,000,000 amaperekedwa ku mbali zodabwitsa zosiyanasiyana za kufufuza kwa kuthupi. Chiyerekezo cha anthu 2,000,000 mu England ali osangalatsidwa mu nkhani yofananayo. Kufufuza kwa unyinji kwaposachedwapa mu Netherlands kunasonyeza kuti okhulupirira mu kuwunika kwamphamvu zoposa za anthu amapezeka pakati pa anthu okhala mu mizinda yaikulu, anthu ophunzira kwambiri, ndi anthu achichepere. M’kuwonjezerapo, monga mmene nzika za mu Africa, Asia, ndi Latin America zingatsimikizirire, m’maiko ambiri kukhulupirira mizimu kwakhala mbali yaikulu kwambiri ya moyo wa tsiku ndi tsiku. Nchosadabwitsa kuti akonzi John Weldon ndi Clifford Wilson anamaliza mu bukhu lawo lakuti Occult Shock and Psychic Forces: “Ochitira ndemanga ambiri akuwoneka kukhala akudzimva kuti tiri mu nthaŵi yosanenedweratu ya kuyambikanso kwa matsenga.”
Inde, kukhulupirira mizimu ndi matsenga—mu mitundu ya kupenda nyenyezi, kugoneka tulo, maphunziro a zizindikiro zachilendo, kuzindikira nzeru zachilendo, matsenga, kumasulira maloto, ndi zina zowonjezereka—zikukopa anthu kuchokera kumbali zonse za moyo. Nchifukwa ninji?
Popeza chinthu chimodzi, ena a matchalitchi a Dziko la Chipembedzo amalekelera ndipo ngakhale kuvomereza kukhulupirira mizimu. Iwo amalingalira kuti kukhala m’chigwirizano ndi mizimu iri chabe njira ina yodzikokera moyandikira kwa Mulungu.
Monga chitsanzo, tengani Izaak Amelo, wamalonda wa zaka 70 wa mu Suriname. Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri iye anali chiwalo cha bungwe la tchalitchi cholemekezedwa ndipo anali wolankhula ndi mizimu wotchuka kwambiri panthaŵi imodzimodziyo. Iye akukumbukira: “Loŵeruka lirilonse bungwe lathu lonse la tchalitchi linasonkhana kunja kwa mudzi kufunsa mizimu. Tinapitiriza usiku wonse. Pamene m’mawa wotsatira udadza, dikoni anapitiriza kuyang’ana pa koloko yake, ndipo chifupifupi pa ora lachisanu, iye anatipatsa chizindikiro chakuima. Kenaka tinasamba, kusintha zovala, ndi kumapita ku tchalitchi—kokha mu nthaŵi yabwino kaamba ka kulambira kwa m’mawa kwa pa Sande. Zaka zonsezo pasitala sananenepo liwu lina lirilonse la kusavomereza.”
Pambuyo pa kuphunzira kugwirizana pakati pa okhulupirira mizimu ndi matchalitchi mu Suriname, Profresala wa chiDutch R. van Lier akutsimikizira kuti ambiri amawona kukhulupirira mizimu monga “chipembedzo chowonjezereka.” M’phunziro laposachedwapa lofalitsidwa ndi Yuniversite ya Leiden, iye anawonanso kuti kukhulupirira mizimu kukuzindikiridwa monga “mbali ya maphunziro a akulu a chipembedzo mu amene kumaima kumbali kwa Chikristu.”
Koma inu mungadabwe, ‘Kodi kuvomereza kwa kukhulupirira mizimu kwa matchalitchi a Dziko la Chipembedzo kuli chitsimikiziro chakuti kuli kovomerezedwa ndi Mulungu? Kodi kukhala wogwirizana ndi mizimu kudzakukokerani inu moyandikira kwa iye? Kodi nchiyani chimene Baibulo kwenikweni limanena ponena za kukhulupirira mizimu?’
[Chithunzi patsamba 3]
Izaak Amelo akukumbukira kutengamo mbali kwa bungwe lonse la tchalitchi mu machitachita a kukhulupirira mizimu