Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 9/1 tsamba 4-6
  • Kukhulupirira Mizimu—Kumawonedwa Motani ndi Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhulupirira Mizimu—Kumawonedwa Motani ndi Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maula, Kuvutitsidwa, ndi Imfa
  • Kukhulupirira Mizimu ndi “Ntchito za Thupi”
  • Kukhulupirira Mizimu Kumatsogolera ku Imfa
  • Labadirani Chenjezo la Yesaya
  • Mapindu Osatha
  • Kukhulupirira Mizimu—Nchifukwa Ninji Pali Chikondwerero Chokulira?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • N’chifukwa Chiyani Kukonda Kukhulupirira Mizimu Kwafala Motere?
    Galamukani!—2000
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupewa Zamizimu?
    Galamukani!—2008
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Polimbana ndi Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 9/1 tsamba 4-6

Kukhulupirira Mizimu​—Kumawonedwa Motani ndi Mulungu?

“KUKONDA ndi kusakonda zinthu zimodzimodzi, ichi ndi chimene chimapangitsa ubwenzi wolimba,” anatero wophunzira mbiri yakale wa Chiroma Sallust. Indedi, bwenzi ali mmodzi amene muli naye zinthu zambiri zofanana naye, munthu amene mungadalire. Mofananamo, Mulungu amawona pa ife monga mabwenzi ndi kutilola kudzikokera kufupi ndi iye ngati tikonda ndi kusakonda zinthu zimodzimodzi zimene iye amatero. Ichi chimatanthauza kuti tiri okokeredwa ku mikhalidwe yoteroyo ya Mulungu monga chikondi, mtendere, kukoma mtima, ndi ubwino, ndipo kuti tikupanga kuyesayesa kofunikira kutsanzira zikhoterero zimenezi m’moyo wathu.​—Agalatiya 5:22, 23.

Kuti tipeze ngati kukhulupirira mizimu kuli kovomerezedwa ndi Mulungu, choyamba tingasanthule zipatso zake. (Mateyu 7:17, 18) Kodi kumatithandiza ife kukulitsa mikhalidwe yosangalatsa ya umulungu? Kuti tipeze, tiyeni tiwone zitsanzo ziŵiri zenizeni za moyo.

Maula, Kuvutitsidwa, ndi Imfa

Asamaja Amelia, mkazi wa zaka za pakatikati mu Suriname, anali wa zaka 17 pamene iye poyamba anakhala wogwirizana ndi maula, mtundu wa kukhulupirira mizimu. Popeza zolosera zake zinakhala zowona ndipo ofunsa ake anapindula kuchokera ku thandizo lake, iye anakondedwa kwambiri m’mudzi wake. (Yerekezani ndi Machitidwe 16:16.) Koma chinthu chimodzi chidamuvuta iye.

“Mizimu imene inalankhula kupyolera mwa ine inali ya chifundo kwa awo amene anafuna thandizo lawo,” iye akutero, “koma panthaŵi imodzimodziyo inapanga moyo wanga kukhala wachisoni. Pambuyo pa kukhala pansi kuli konse, ndinali kudzimva kukhala womenyedwa kwambiri ndiponso sindikanatha kuyenda nkomwe. Pamene usiku unafika, ndinayembekezera kaamba ka mpumulo wina, koma mizimu siinandisiye ndekha. Iyo inapitiriza kundivutitsa ine, kulankhula kwa ine ndi kundipangitsa ine kukhala wa maso. Ndipo zinthu zimene inali kunena!” Iye akuusa moyo ndi kuyang’ana pansi, akupukusa mutu wake m’kukhumudwitsidwa. “Inakonda kulankhula kwa iye ponena za nkhani ya kugonana ndipo inaumirira pa kugonana ndi ine. Chinali chinthu chochititsa manyazi. Ndinali wokwatiwa. Sindinafune kukhala wosakhulupirika ndipo ndinaiuza tero. Icho sichinathandize. Kamodzi mphamvu yosawoneka inandiposa mphamvu, kundikhudza ndi kupanikiza thupi langa, ndipo ngakhale kundimenya. Ndinadzimva kukhala wotopa.”

‘Mizimu kulimbikitsa mkhalidwe woipa wa kugonana? Limenelo liri bodza lamkunkhuniza!’ inu mungafuule tero. Kodi mizimu imeneyo iridi kwenikweni yoipitsidwa motero?

“Iri ngakhale yoipirapo!” akutero Izaak, wotchulidwa poyambirirapo. “Usiku umodzi tinaitanidwa kukathandiza mkazi wodwala wovutitsidwa ndi mizimu. Mtsogoleri wa gululo​—wolankhula ndi mzimu wamphamvu koposa​—anayesa kuthamangitsa mzimu umenewo. Kwa tsiku lonse tinali kuchonderera kaamba ka thandizo la mzimu wake. Tinavina ndi kusewera ng’oma, ndipo mwapang’onopang’ono mkaziyo anawongokera. Iye analamulira mzimu wake kutuluka, ndipo ichi chinathandiza. ‘Tinapeza chipambano,’ anasangalala tero mtsogoleriyo. Kenaka tinakhala pansi ndi kupumula.”

Manja olankhula a Izaak anapuma kwa kanthaŵi pamene iye anapumula mwatanthauzo. Kenaka iye akupitiriza: “Kwakanthaŵi zonse zinawonekera bwino, koma kenaka kulira kunathetsa batalo. Tinathamangira ku nyumba kumene kulirako kunachokera ndi kuwona mkazi wa mtsogoleriyo. Iye anali kulira ndi kunjenjemera. Mkati mwa nyumba, tinapeza mwana wake wamkazi wamng’ono​—mutu wake unali kuyang’ana chakumbuyo! Mphamvu ina inapotola ndi kuthyola khosi lake, kumupha iye ngati nkhuku​—mwachiwonekere, kubwezera kwa mzimu wotulutsidwawo. Chomvetsa chisoni! Mizimu imeneyi iri yakupha anthu mopanda chifundo.”

Kukhulupirira Mizimu ndi “Ntchito za Thupi”

Uve, mkhalidwe woipa wa kugonana, ndi kupha​—monga zaperekedwera mu zokumana nazo ziŵiri zimenezi za kukhulupirira mizimu​—ziri zikhoterero zotsutsana kotheratu ndi umunthu wa Mulungu. Ndipo chimenechi chimathandiza kuzindikira ndi ndani amene mizimu imeneyo mowonadi ili. Iyo ingayerekeze kukhala athenga a Mulungu, koma ntchito zawo zoipa ndi zakupha zimawapatutsa iwo kukhala monga otsanzira a mdani wa Mulungu ndipo wakupha woyamba m’mbiri, Satana Mdyerekezi. (Yohane 8:44) Iye ali mtsogoleri wawo. Iwo ali athandizi ake​—angelo oipa, kapena ziwanda.​—Luka 11:15-20.

Koma inu mungafunse: ‘Kodi zikhoterero zausatana zimenezi zimasonyezedwa mu kukhulupirira mizimu kokha pa mikhalidwe yosawonekawoneka? Kodi kukhulupirira mizimu monga lamulo kungandiyike ine m’chigwirizano ndi mizimu yabwino yomwe ingathandize kundibweretsa kufupi ndi Mulungu?’ Ayi, Baibulo limandandalitsa “kachitidwe ka kukhulupirira mizimu” limodzi ndi “ntchito zina zathupi” zomwe ziri mwachindunji zotsutsana ndi mikhalidwe Yachikristu.​—Agalatiya 5:19-21.

Pa Chivumbulutso 21:8, NW “awo okhulupirira mizimu” (“awo olankhula ndi ziwanda,” The Living Bible) amayikidwa m’mbali imodzimodzi ndi “awo opanda chikhulupiriro ndi awo amene ali onyansa ndi ambanda, ndi achigololo . . . ndi olambira mafano, ndi onama.” Kodi ndimotani mmene Yehova amawonera onama mwadala, achigololo, akupha, ndi okhulupirira mizimu? Iye amada ntchito zawo!​—Miyambo 6:16-19.

Kufufuza kukhulupirira mizimu, chotero, kumafanana ndi kukonda zimene Yehova Mulungu amada. Chiri chofanana ndi kukana Yehova, kukhala mu msasa wa Satana, ndi kukhala kumbali imodzi ya mdani wamkulu wa Mulungu ndi athandizi ake. Tsopano lingalirani ichi: Kodi mungakonde kukhala woyandikana ndi munthu amene amatenga mbali ndi mdani wanu? Ndithudi ayi. M’malo mwake, mungakhale odzipatula kotheratu ndi munthu woteroyo. Mwachiwonekere, chotero, tingayembekezere kachitidwe kamodzimodziko kuchokera kwa Yehova Mulungu. Ikutero Miyambo 15:29, “Yehova atalikira oipa.”​—Onaninso Masalmo 5:4.

Kukhulupirira Mizimu Kumatsogolera ku Imfa

Kusewera ndi kukhulupirira mizimu kulinso kuwopsyeza moyo. Mulungu anakuwona iko monga chifukwa cha chilango chachikulu cha imfa pakati pa anthu ake mu Israyeli wakale. (Levitiko 20:27; Deuteronomo 18:9-12) Chotero icho sichiyenera kukhala monga chozizwitsa kuti okhulupirira mizimu “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:20, 21) M’malo mwake, “gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka ndi moto,” yomwe imaimira “imfayachiŵiri,” kapena chiwonongeko chotheratu. (Chivumbulutso 21:8) Zowona, lerolino ena a matchalitchi a Dziko la Chipembedzo angalekelere kukhulupirira mizimu, koma lingaliro la Baibulo silinasinthe.

Bwanji ngati inu munatenga kale masitepi oyamba panjira yopita ku kukhulupirira mizimu? Chotero mudzachita bwino kuleka mwamsanga ndi kutembenuka. Tsatirani uphungu wouziridwa mwaumulungu umene mneneri wa Mulungu Yesaya anapereka kwa Aisrayeli akale. Mkhalidwe wawo unafanana ndi uja wa anthu lerolino omwe amadzilowetsa m’machitachita onyansa koma amalingalira kuti akulambira Mulungu panthaŵi imodzimodziyo. Chotero, pali ziphunzitso zofunika koposa mu chokumana nacho chawo. Maphunziro otani?

Labadirani Chenjezo la Yesaya

Kuyang’ana pa mutu woyamba wa Yesaya kumasonyeza kuti Aisrayeli “anali atasiya Yehova” ndipo anali “atabwerera m’mbuyo.” (Versi 4) Ngakhale kuti iwo anali atatayika, iwo anapitirizabe kupereka nsembe, kusunga zikumbukiro za chipembedzo, ndi kupereka mapemphero. Koma popanda phindu! Popeza iwo anasowa chikhumbo cha mkatikati cha kusangalatsa Mlengi wawo, Yehova anati: “Ndidzakubisirani maso anga. Inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva.” Aisrayeli amenewo anali anaukira motsutsana ndi iye mwakutenga machitachita onyansa, ngakhale ku nsonga ya ‘kudzaza manja awo ndi mwazi.’​—Maversi 11-15.

Pansi pa mikhalidwe yotero kodi Yehova angawalandire iwonso? Onani ziyeneretso zotchulidwa pa Yesaya 1:16. Iye akuti: “Sambani; dziyeretseni.” Chotero ngati ife titenga uphungu umenewo mosamalitsa, tidzasiya kapena kuchoka ku machitachita onyansa, kuphatikizapo kukhulupirira mizimu, imodzi ya “ntchito zathupi.” Popeza tikudziŵa kuti lingaliro loipa kumbuyo kwa kukhulupirira mizimu liri lija la Satana Mdyerekezi, tidzakulitsa chidani kaamba ka iko.

Kenaka tidzafuna kuchotsa zinthu zonse zogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Izaak anachita tero. Iye akunena kuti: “Tsiku limodzi ndinasonkhanitsa zinthu zanga zonse za mizimu patsogolo panyumba yanga, kutenga nkhwangwa, ndi kuzidula izo zonse kukhala zidutswa. Mnansi wanga analira kuti ndidzamva chisoni ndi zimene ndinachita. Pamene iye anali adakalira, ndinathira parafini pa zidutswazo ndi kutentha chimodzi ndi chimodzi chirichonse. Palibe chirichonse chimene chinasiyidwa.”

Zimenezo zinali zaka 28 zapita. Kodi Izaak anamva chisoni ndi kachitidwe kake? Mosiyanako. Lerolino, iye akutumikira Yehova mwachimwemwe monga minisitala Wachikristu mu umodzi wa mipingo ya Mboni za Yehova.

Yesaya 1:17 amapereka uphungu wowonjezereka: “Phunzirani kuchita zabwino.” Chimenecho chimafunikira kuphunzira Mawu a Yehova, Baibulo, kotero kuti mupeze chimene chiri “chifuno cha Mulungu, chabwino ndi chokondweretsa ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Ndipo kugwiritsira ntchito chidziŵitso chopezeka chatsopano chimenecho kudzatsogolera ku madalitso odzetsa mpumulo. Chimenecho ndi chimene Asamaja anapeza.

Mosasamala kanthu za chitsutso chowopsya kuchokera kwa achibale ndi anansi, Asamaja molimba mtima anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo mwamsanga pambuyo pake anasiyana ndi kukhulupirira mizimu. Kenaka iye anapereka moyo wake kwa Yehova Mulungu ndipo anabatizidwa mkati mwa msonkhano. Tsopano, zaka zina 12 pambuyo pake, iye akunena moyamikira: “Kuyambira pa ubatizo wanga, sindinavutitsidweponso ndi mizimu.” Ndipo iye akukumbukira ndi kumwetulira: “Usiku pambuyo pa ubatizo wanga, tulo tanga tinali tozama ndipo tosavutitsidwa kotero kuti ndinachedwa m’mawa wotsatira kaamba ka programu ya msonkhano.”

Mapindu Osatha

Lerolino, onse aŵiri Izaak ndi Asamaja anganene motenthedwa maganizo ndi wamasalmo Asafu: “Kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.” (Masalmo 73:28) Ndithudi, kuyandikira pafupi kwa Yehova kunabweretsa kwa iwo mapindu a kuthupi ndi malingaliro. Koma choposa zonse, chinapatsa iwo mtendere wa mkatikati ndi unansi wathithithi ndi Yehova.

Madalitso oterewo amaposa mokulira kupweteka ndi kulimbana kofunikira kuchotsa goli la kukhulupirira mizimu. Kulekana nayo, ngakhale kuli tero, kungakhale kovuta. Lintina van Geenen, mkazi wa mu Suriname, ali ndi chokumana nacho choterocho. Kenaka, tidzawona mmene iye analimbanirana nayo kwa zaka zingapo koma pomalizira anapambana.

[Chithunzi patsamba 5]

Asamaja Amelia akulongosola kuti: “Mizimu . . . inapangitsa moyo wanga kukhala wachisoni . . . Ndipo zinthu zimene inakamba!”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena