Kukhala Ogalamuka Molimbana ndi “Mtendere ndi Chisungiko” monga Kwaganiziridwa ndi Mitundu
“Pamene angonena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’”—1 ATESALONIKA 5:3.
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji mtendere wakhala mbali yabwinopo ya nzeru? (b) Chotero, kodi madongosolo a ndale zadziko otsutsana adzagwirizana pa chiyani?
NDI KALE LONSE dziko lonse la mtundu wa anthu silinakhalepo lopanda chisungiko monga mmene liriri lerolino. Pali kudzimva kwa mantha ku nkhondo ya dziko yachitatu yokhudza mitundu yokhala ndi zida zapamwamba zomwe tsopano zikuwoneka kukhala zida zapamwamba koposa—mabomba a nyukiliya. Kuthekera kwa mitundu kwa kugwiritsira ntchito mbali zazing’ono koposa ziri zonse za maatomu mu kulondola nkhondo kwawatenga iwo kufika chifupifupi ku utali umene iwo angathe mu kupha kwa anthu kwaunyinji. Chotero, mtendere wakhala mbali yabwino koposa ya nzeru.
2 Inde, ndithudi, popeza mu nyengo yathu kugwiritsira ntchito zida zoterozo kwa nkhondo ya dziko yachitatu sikungasonyeze china chake koposa kudzipha kwa dziko lonse, anthu akuphulika kusakhala chirichonse kapena kutheratu kuchokera pa zotulukapo zotsatira za chipiyoyo cha nyukiliya. Odziŵa za ndale zadziko akawonedwe kabwino ndi atsogoleri a nkhondo mowawidwa amamva mfundo imeneyo. Iwo sakufuna kukhala ndi thayo kaamba ka tsoka lotero la dziko lonse. Chotero, madongosolo a ndale zadziko otsutsana kotheratu adzachipeza icho kukhala choyenera kufika ku kugwirizana, inde, kutsatira nzeru yaudziko ya nthanthi ya “khalani ndipo lolani kuti mukhale.”
3. Kodi ndi pachifukwa chotani pamene mitundu idzalengeza “Mtendere ndi chisungiko”?
3 Mosasamala kanthu za chimenecho, mitundu sikhulupirirana wina ndi mnzake kotheratu. Monga chenjezo, iwo amasunga makhazikidwe awo ankhondo kukhala amphamvu kwambiri. Chotero, kodi icho chidzakhala chifukwa cha kuwona mtima, chikondi chenicheni kaamba ka wina ndi mnzake monga ziwalo za banja la munthu limodzi kuti olamulira adzagwirizana m’kupanga chilengezo cha “mtendere ndi chisungiko” kaamba ka dziko lonse la mtundu wa anthu? Ayi, koma kudzakhala kufuna kuchotsa mantha olungamitsidwa a anthu.—1 Atesalonika 5:3.
Kuvomereza kwa Atsogoleri a Chipembedzo ndi Unyinji ku Chilengezo Chikudzacho
4, 5. (a) Kodi ndi chivomerezo cha unyinji chotani cha kudza kwa chilengezocho chimene tingayembekezere? (b) Mosasamala kanthu za kuchirikiza kwa atsogoleri a chipembedzo kwa chilengezo chikudzacho, kodi ndi mafunso otani amene amabukapo ponena zoti kaya Mulungu adzachichirikiza icho?
4 Pamene chilengezo chimenechi potsirizira chidzapangidwa, chivomerezo cha unyinji ku icho chidzakhala cha chiyanjo kuzungulira dziko lonse lapansi. Mosakaikira atsogoleri a chipembedzo a dziko, kuphatikizapo atsogoleri a chipembedzo a Dziko la Chipembedzo, Akatolika ndi Protestanti, adzalemekeza chisonyezero cha mitundu yonse chimenechi. Mu njira iriyonse mmene mphepo imawombela, atsogoleri a chipembedzo amapita ndi cholinga chofuna kukhalabe mu chiyanjo chotchuka ndi kukhala ndi thandizo ndi kulingaliridwa kwa ndale zadziko.
5 Komabe, kuchirikiza kwa atsogoleri a chipembedzo kwa makonzedwe olengezedwa ndi ndale zadziko sikutanthauza kuti Mulungu wa chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lathu lapansi, adzachirikiza icho. M’nyumba zawo za chipembedzo, atsogoleri a chipembedzo angapereke mapemphero a atali ndi ofuula kuti amvedwe ndi achirikizi awo a chipembedzo ndi kupempha kaamba ka dalitso laumulungu pa katengedwe kawo kochitidwa ndi mbali za ndale zadziko kaamba ka mtendere ndi chisungiko za mitundu yonse. Koma kodi mapemphero onse owona mtima oterowo, ku amene mipingo yomvetsera imapereka “Amen” wamphamvu, ali olandiridwa kwa Mulungu wa chilengedwe ichi? Kodi iye angakhale pamtendere ndi dziko logawanika mwa chipembedzo, mapemphero kaamba ka mtendere ndi chisungiko amene ali opangidwa m’chigwirizano ndi magulu ampatuko a chipembedzo osagwirizana ndi zipembedzo?
6, 7. (a) Mofanana ndi Ayuda a nthaŵi zakale, kodi ndi njira ya kachitidwe kotani imene Dziko la Chipembedzo latenga? (b) Nchiyani chimene chidzatulukapo kuchokera ku kuchirikiza kwa atsogoleri a chipembedzo kwa chilengezo cha “Mtendere ndi Chisungiko”?
6 Palibe kwina kuli konse kumene zilengezo za kuchirikiza kwa Mulungu ziri zofuula koposa kuposa mu mitundu ya Dziko la Chipembedzo. Koma Mulungu wa chilengedwe sali Mmodzi amene akulamulira Dziko la Chipembedzo. Ilo latenga njira yofanana ndi ija ya Israyeli wakale. Pamene iwo anakhala osakhutiritsidwa ndi makonzedwe a Yehova kaamba ka boma lawo ndi kuyamba kulingalira kuti makhazikitsidwe a ndale zadziko a mitundu ya kunja yowazinga iwo anali abwinoko, iwo anapita kwa mneneri wa Yehova Samueli ndi kum’funsa iye kukhazikitsa mfumu kaamba ka iwo. Samueli sanasangalatsidwe kwambiri ndipo anamva chisoni ndi ichi. Wachisoni choposerapo anali Mulungu amene iye anali mneneri wake.
7 Yehova moyenerera anadzimva kukhala wopwetekedwa pa chifunsiro chimenechi kaamba ka kuchoka ku kakhazikitsidwe kake ka teokratiki pa Israyeli. Monga mmene iye ananenera kwa mneneri wake Samueli: “Sindiwe anakukana, koma ndine anandikana.” (1 Samueli 8:4-9) Ichi chinaimira njira imene Dziko la Chipembedzo latenga mu zana lino la 20. Chotero kulemekezeka kwa mtsogolo kwa atsogoleri a chipembedzo ku chilengezo cha “Mtendere ndi chisungiko” sikudzakhala ndi chotulukapo choyanjika sichidzakhala ndi dalitso laumulungu.
Kupangitsa Mtundu wa Anthu Kukhala Wosagalamuka
8. Kodi ndi mbali yotani imene Mitundu Yogwirizana moyenerera idzachita m’chilengezo chikudzacho, ndipo nchifukwa ninji gulu limeneli likupangitsa mtundu wa anthu kukhala wosagalamuka?
8 Mitundu Yogwirizana ingakhale ikunyada chifukwa cha ziwalo 159 lerolino, kukuta chifupifupi mitundu yonse. Mosakaikira mkupita kwanthaŵi Mitundu Yogwirizana idzakhala patsogolo m’chigwirizano ndi chilengezo chikudzacho cha “Mtendere ndi chisungiko!” Chiri chachisoni kunena kuti, gulu la dziko limenelo likupangitsa mabiliyoni a mtundu wa anthu kukhala osagalamuka. Nchifukwa ninji ziri tero? Chifukwa chakuti mtendere woterowo, ngakhale kuti uli wochinjirizidwa ndi magulu onse a chipembedzo a dziko ili, kuphatikizapo aja a m’Dziko la Chipembedzo, samatanthauza mtendere ndi Mlengi wa chilengedwe, yemwe ali ndi mphamvu ya kupereka moyo ndi kuutenga iwo mogwirizana ndi kugamulapo kwake kwa nkhani zofunika kwambiri kumwamba ndi padziko lapansi.
9, 10. Kodi ndi kaimidwe kotani ka Mboni za Yehova kulinga ku “Mtendere ndi chisungiko” monga kwaganiziridwa ndi mitundu, ndipo nchifukwa ninji kali kotero?
9 Mu ulosi wa Yesaya, Mlengi momvekera bwino ananena kuti: “Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga.” (Yesaya 66:1) Mitundu pansi pano pa choikapo mapazi ake sikulilemekeza ilo ndi gulu lawo la Mitundu Yogwirizana. Iwo akuyesetsa mwa ndale zadziko kusunga mtendere wa dziko lonse ndi chisungiko ndipo motero akupangitsa Mitundu Yogwirizana kukhalapo. Mboni zodzipereka za Yehova padziko lapansi sizingagwirizane ndi dziko mu kudalira pa mapangidwe opangidwa ndi munthu omwe akutengedwa kaamba ka mtendere ndi chisungiko cha mitundu ya dziko. Iwo amatenga ku mtima mawu a Yakobo 4:4: “Akazi a chigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.”
10 Ngakhale kuti mokangalika sakutsutsa mtendere ndi chisungiko monga kwaganiziridwa ndi mitundu, Mboni za Yehova sizingavomereze icho ku mamiliyoni a anthu omwe akufunafuna malo a chisungiko pamene vuto lalikulu koposa la dziko lapansi lidzaulika ndi kufika kumapeto a dongosolo la kachitidwe ka zinthu liripoli. (Mateyu 24:21) Popeza kuti liri dongosolo la kachitidwe ka zinthu latsopano la Mulungu lomwe lidzabweretsa chisungiko cha dziko lonse pansi pa “Kalonga wa Mtendere,” Yesu Kristu.—Yesaya 9:6, 7.
11. Kodi ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo anawonera chifunsiro cha kukhazikitsa Chigwirizano cha Mitundu pambuyo pa Nkhondo ya Dziko I?
11 Mbiri yakale imachitira umboni ku kulephera kwa makonzedwe opangidwa ndi munthu kaamba ka mtendere. Timakumbukira kuti pamapeto a Nkhondo ya Dziko I mu 1918, Chigwirizano cha Mitundu chinakhazikitsidwa monga njira yochinjirizira nkhondo ya dziko. Bungwe la Chigwirizano cha Matchalitchi a Kristu mu America linalemekeza chifunsirocho ndipo linati: “Chigwirizano choterocho sichiri kokha chothandiza cha ndale zadziko; m’malo mwake icho chiri chisonyezero cha ndale zadziko cha Ufumu wa Mulungu padziko lapansi.” Koma kodi chotchedwa chisonyezero cha ndale zadziko cha ufumu wa Mulungu padziko lapansi chinabweretsa mtendere wosatha ndi chisungiko kaamba ka dziko lapansi?
12. (a) Ndimotani mmene Chivumbulutso 17:8 chakwaniritsidwira? (b) Ndi ndani amene akupitirizabe kukwera pa “chirombo chofiira” ndipo ndi kwa utali wotani?
12 Mofanana ndi “chirombo chifiira” chophiphiritsira cha Chivumbulutso mutu 17, pa chimene mkazi wachigololo wakale, “Babulo Wamkulu,” wadzikhazika iyemwini, Chigwirizano cha Mitundu chinapita “kuphompho” pa kuyambika kwa Nkhondo ya Dziko II mu 1939. Ichi chinamuyeneretsa mkazi wa chigololo wokwera pa icho kuchokapo. Pambuyo pakutha kwa Nkhondo ya Dziko II mu 1945, Mitundu Yogwirizana inakhazikitsidwa monga yolowa m’malo mwa Chigwirizano cha Mitundu chatsoka. Chiri ndi ziwalo zambiri kuposa mmene Chigwirizano chinaliri, chotero chiyenera kukhala gulu lamphamvupo ndipo loyenera kukhala lodaliridwa koposa kumbali ya dziko la mtundu wa anthu. Chotero mu 1945 “chirombo chofiira” chophiphiritsira chimenecho chinatuluka “kunja kwaphompho,” ndipo mkazi wachigololo wophiphiritsirayo, “Babulo Wamkulu,” anakweranso pa msana pake, kumene iye mopanda manyazi amakhala kufikira ku tsiku lino. (Chivumbulutso 17:3, 5, 8) Koma osati kwanthaŵi yaitali tsopano, malinga ndi chimene Chivumbulutso 17:16–18:24 chikuneneratu. Nchifukwa ninji ayi?
13. (a) Kodi Mitundu Yogwirizana nchiyani? (b) Kodi icho chinaimidwira motani nthaŵi yakale?
13 Mitundu Yogwirizana m’chenicheni iri chigwirizano cha dziko lonse motsutsana ndi Yehova Mulungu ndi Mboni zake zodzipereka za padziko lapansi. Icho m’chenicheni chiri chiwembu, chokhala ndi mitundu ya dziko ikusonkhanitsa pamodzi atsogoleri awo ndi kukonzekera zimene angachite motsutsana ndi gulu lowoneka ndi maso la Yehova Mulungu la padziko lapansi. Mkati mwa “mapeto a dongosolo ili lakale la zinthu,” chinaimiridwa ndi chiwembu cholozeredwako pa Yesaya 8:12.—Mateyu 24:3.
Yang’anani kwa Yehova Kaamba ka Mtendere ndi Chisungiko
14. Kodi nchifukwa ninji ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli unalowa m’chigwirizano ndi Syria, ndipo ndi funso lotani limene linayang’anizidwa ndi ufumu wa Yuda?
14 Isanafike nthaŵi ya Yesaya mtundu wa mafuko 12 a Israyeli unali utagawanikana pakati pa nkhani ya ufumu. Ichi chinachitika pambuyo pa ulamuliro wa ulemerero wa Mfumu Solomo. Mafuko khumi opatuka a kumpoto anakhazikitsa womwe unadzafikira kutchedwa ufumu wa Israyeli, ndi likulu lawo pa Samariya. Mafuko aŵiri otsalawo, mafuko a Yuda ndi Benjamini, anakhala omvera ku ulamuliro wa ufumu wa Mfumu Davide pa mzinda waukulu wa Yerusalemu. Ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi unatembenukira mwaudani motsutsana ndi ufumu wa Yuda wa mafuko aŵiri. Mkupita kwa nthaŵi, ufumu wa Israyeli unagwirizana ndi ufumu wa Syria, womwe unali ndi likulu lake pa Damasiko. Lingaliro lawo linali lakugwetsa ufumu wa Yuda ndi kubweretsa iwo m’chigonjero. Kodi ufumu wa Yuda chotero ukanalowa m’chigwirizano ndi mtundu wina wamphamvu ndi cholinga chofuna kulimbana ndi kukantha kwa mtundu wa Israyeli wogwirizana ndi mtundu wa chikunja wa Syria?—Yesaya 7:3-6.
15. (a) Kodi nchiyani chimene anthu ena a mu ufumu wa Yuda anakonda, ndipo kodi nchiyani chimene kachitidwe kameneka kanawononga? (b) Kodi ndimotani mmene mneneri Yesaya analankhulira motsutsana ndi kawonedwe koteroko?
15 Panalinso awo a mu ufumu waung’ono wa Yuda omwe anataya chikhulupiriro mwa Mulungu wa mtunduwo Yehova. Awa anakonda chigwirizano, kapena chiwembu, ndi ufumu wamphamvu wachikunja wa dziko ili. Kupititsa patsogolo kugwirizana kosakhulupirika kumeneku kwa ufumu wa Yehova wa Yuda ndi ufumu wa dziko lopanda umulungu, ena anali kunena kuti, “Chiwembu!” kwa awo osalingalira mu ufumu wa Yuda. Chotero iwo ananyenga kusoweka kwawo kwa chikhulupiriro ndi chidaliro mwa Mulungu amene kachisi wake anali mu Yerusalemu. Mneneri Yesaya anauzidwa kulankhula motsutsana ndi chiwembu choterocho, akumanena mu mutu 8 versi 12: “Musachinene, ‘Chiwembu!’ chiri chonse chimene anthu awa adzachinena, ‘Chiwembu!’ musawope monga kuwopa kwawo kapena musachite mantha.”
16, 17. Kodi nchiyani chimene chinatanthauza mtendere weniweni ndi chisungiko kaamba ka anthu akale a Yehova, ndipo ndimotani mmene ichi chinasonyezedwera pamene Mfumu ya Asuri Sanakeribu inawopsyeza Yerusalemu?
16 Kukhala kwa Yehova ndi anthu ake mu unansi wapangano ndi iye kunatanthauza mtendere ndi chisungiko kwa iwo. Ichi chinasonyezedwa pamene wolamulira wa Asuri Sanakeribu anatumiza komiti ya nduna zazikulu zitatu kukaitana Mfumu Hezekiya ndi anthu a ku Yerusalemu kupanga chigwirizano ndi Sanakeribu. Nduna ya ku Asuri ndi mlankhuli wake, Rabuseke, anaimirira patsogolo pa zipupa za Yerusalemu ndipo monyodola ananyoza Yehova Mulungu kotero kuti afooketse kapena kuwononga chidaliro cha Ayuda mwa iye. Omvetsedwa chisoni kaamba ka kupeputsa kwa wokhalako mmodzi ndi wowona Yehova Mulungu ndiponso moyenerera akumva tsoka lalikulu la Yerusalemu pamaso pa gulu logonjetsa loyendayenda la Asuri, Mfumu Hezekiya anapita ku kachisi ndi kuika nkhaniyo pamaso pa Yehova Mulungu. Wosangalatsidwa ndi chisonyezero cha chikhulupiriro chachikulu mwa iye ndiponso ndi kugonjera uku kwa iye kaamba ka chisonyezero cha ulamuliro wake wa dziko lonse, Yehova anapereka yankho la chiyanjo. Mneneri wake Yesaya anagwirizana nayo ndemanga yotsimikizira. Palibe yankho lirilonse limene linapatsidwa kwa kazembe wochititsa mantha wa Asuri Rabuseke, monga momwe Mfumu Hezekiya analamulira.—2 Mafumu 18:17-36; 19:14-34.
17 Mosakaikira wodabwitsidwa mokulira pa ichi, Rabuseke anabwerera ku msasa wa Sanakeribu, amene pa nthaŵiyo anali kutsira nkhondo pa Libina. (2 Mafumu 19:8) Pambuyo pa kumva ripoti la Rabuseke, Sanakeribu anatumiza makalata ochititsa mantha kwa Hezekiya, akuchenjeza kuti: “Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira ndi kuti: ‘Yerusalemu sudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asuri.’” (2 Mafumu 19:9, 10) Pambuyo pa kugwa mmdima, Yehova Mulungu analankhula iyemwini kubweza mawu kwa mlankhuli wa Asuri, Rabuseke, ndipo iye iyemwini anayankha makalata ochititsa mantha a Sanakeribu kutsimikizira kuti Iye anali wapamwamba koposa mulungu wa ufumu wa Asuri. Mapeto a mbiri ya nkhaniyi, monga mmene aperekedwera pa 2 Mafumu 19:35, amanena kuti: “Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Asuri zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu. Ndipo pouka anthu mmawa, tawonani, onsewo ndi mitembo.” Mbandakucha pamene Asuri opulumukawo, kuphatikizapo Mfumu Sanakeribu ndipo mwinamwake Rabuseke, anauka, iwo anawona chochitika chochititsa mantha pozungulirapo cha ovulala ankhondo ya Yehova Mulungu.
18. (a) Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo chake m’chigwirizano ndi Sanakeribu wonyada? (b) Kodi ndi chitsanzo chotani chimene cholembera cha mbiri yakale chimenechi chiyenera kupereka kwa Mboni za Yehova za lerolino?
18 Wogonjetsedwa mu makonzedwe ake otukumuka motsutsana ndi gulu la Yehova ndipo wochititsidwa manyazi kotheratu, Sanakeribu anabwerera mwamsanga “ndi nkhope ya manyazi” ku mzinda wa mtundu wake waukulu, Nineve, kokha kukaphedwa ndi aŵiri a ana ake amuna. (2 Mbiri 32:21; 2 Mafumu 19:36, 37) Sunabwerezenso ufumu wa Asuri kuwopsyeza gulu lowoneka ndi maso la Yehova. Pano, ndithudi, panali kuyeretsa kwapamwamba kwambiri kwa ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Mulungu Wam’mwambamwamba. Ndiponso, kusungidwa kwa Yerusalemu chiri chitsanzo chabwino koposa chosonyeza kwa uyo amene Mboni za Yehova za lerolino ziyenera kuika chidaliro chotheratu kuyang’ana kaamba ka mtendere ndi chisungiko zopitiriza, za bata—osati chiwembu cha ndale zadziko koma Yehova Mulungu.
Kukhala Ogalamuka
19. Kodi nchiyani chimene Watch Tower Society idzapitirizabe kuchita?
19 Kukuthandizani kukhala ogalamuka, Watch Tower Society idzapitirizabe kupereka mu zofalitsidwa zake machenjezo a panthaŵi yake kwa unyinji wa oŵerenga, kotero kuti inu musagwidwe osagalamuka ndi chilengezo chonyengezera chikudzacho cha “Mtendere ndi chisungiko,” monga chaganiziridwa ndi mitundu ya dongosolo ili lakale la kachitidwe ka zinthu.
20. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova mwa njira iriyonse sizidzapititsira patsogolo chidaliro pa “Mtendere ndi chisungiko,” chikudzacho, ndipo chotero tsopano iri nthaŵi ya chiyani?
20 Mboni zodzipereka za Yehova mosakaikira sizidzapititsa patsogolo chidaliro pa “Mtendere ndi chisungiko” chotsimikizirika kudzalengezedwa ndi mitundu ya dziko; ndiponso sizingayamikire olingalira a “Mtendere ndi chisungiko” a mitundu yonse oterowo, ndipo, panthaŵi imodzimodziyo, ali ndi Yehova Mulungu ndi iwo. Iwo amakhala ogalamuka motsutsana ndi kugwirizana ndi mitundu ya dongosolo ili lakale la kachitidwe ka zinthu. Iwo mosalephera amadzikumbutsa iwo eni kuti “mtundu” watsopano, wodzipatula ndi wosiyana ndi Chigwirizano cha Mitundu, unabadwa m’chaka cha pambuyo pa nkhondo mu 1919. “Mtundu” watsopano umenewu ukupitirizabe kukula ndi kufutukuka mu dziko lonse lapansi, monga momwe chinanenedweratu pa Yesaya 60:22: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” Inde, tsopano iri nthaŵi kaamba ka onse kukhala ogalamuka motsutsana ndi “Mtendere ndi chisungiko” chikudzacho monga kwaganiziridwa ndi mitundu.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchiyani chimene moyenerera chikakhala chivomerezo cha unyinji ku chilengezo cha “Mtendere ndi chisungiko”?
◻ Kodi nchiyani chimene chinaimiridwa ndi “chiwembu” cha Yesaya 8:12?
◻ Kodi ndimotani mmene UN ikupangitsira mtundu wa anthu kukhala wosagalamuka?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizidzagwidwa kukhala zosagalamuka?
[Chithunzi patsamba 18]
Mosakaikira UN idzakhala patsogolo pa chilengezo chikudzacho cha “Mtendere ndi chisungiko!”
[Chithunzi patsamba 21]
Nduna ya Asuri Rabuseke inachepetsa Mulungu wa Israyeli, koma chotulukapo chake chinasonyeza kuti mtendere weniweni ndi chisungiko zimabwera kokha kuchokera kwa Yehova Mulungu