Mutu 1
Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
1. Kodi ndimikhalidwe yotani imene imapangitsa mtendere weniweni ndi chisungiko kukhala zokhumbika kwambiri?
NDITHUDI inu, mofanana ndi anthu ambiri, mumafuna mtendere ndi chisungiko. Anthu kulikonse atopa ndi upandu, chiwawa, nkhondo, ndi mkhalidwe wochititsa mantha wa nyukliya umene ukuwopseza. Ndiponso, ochuluka sali pantchito zotsimikizirika, alibe nyumba zokwanira, kapena chakudya chokwanira. Ha kukanakhala kosangalatsa chotani nanga ngati mavuto oterewa akanathetsedwa ndipo dziko lino lapansi nalikhala malo okhalamo okondweretsa, ndi osungika kaamba ka okhalapo ake!
2, 3. (a) Ngati mtendere weniweni ndi chisungiko zayandikiradi, kodi ndimafunso otani amene ayenera kufunsidwa? (b) Kodi ndimotani mmene chochita cha Mitundu Yogwirizana chimawonekera kukhala chogwirizana ndi chikhumbo cha mtendere ndi chisungiko?
2 Modabwitsa, pali chifukwa chabwino chokhulupiririra kuti mpumulo wolakalakidwa kwanthawi yaitaliwo wayandikira, kuti mtendere ndi chisungiko padziko lonse lapansi ziri pafupi kukwaniritsidwa! Koma kodi ndani amene adzazidzetsa? Kodi mitundu ya dziko lino idzathetsa mikangano yawo kuti iwupeze?
3 Ulosi wokondweretsa Wabaibulo unanena kuti nthawi ikafika pamene atsogoleri a dziko akaperekadi chilengezo cha “mtendere ndi chisungiko!”a Ndithudi, pamene Mitundu Yogwirizana inalengeza 1986 kukhala “Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse” inapempha kuti magulu kuli konse apange kuyesayesa kwapadera kuyambira chakacho kumkabe mtsogolo kupanga chonulirapo cha “mtendere, chisungiko cha mitundu yonse ndi chigwirizano.”1
4. Ngati kakonzedwe kalikonse ka mtendere ndi chisungiko kati kakupindulitseni, kodi ndimavuto ati amene kayenera kuthetsa?
4 Koma kodi umenewu ungakhale ‘mtendere weniweni ndi chisungiko’? Kodi ungafike kwanuko ndi m’banja mwanu ndi kuthetsa mavuto amene amakuyambukirani mwachindunji? Kodi ungathetse mavuto a upandu wowonjezerekawonjezereka ndi kumwerekera ndi mankhwala, kukwera mitengo kwa zakudya, ndi kukwera kwa misonkho, kuipitsa kofalikira, ndi kunyonyosoka kwa zomangira zabanja komakwera mosalekezako? Malinga ngati uliwonse wa mikhalidwe imeneyi upitirizabe, iyo ikuwopseza mtendere wanu ndi chisungiko.
5, 6. Pamaziko a chokumana nacho cha moyo wanu, kodi mukhulupirira kuti anthu adzathetsa mavuto amenewo?
5 Nzowona kuti, anthu akuyembekezera kuti angagonjetse mavuto amenewa. Iwo amanena kuti, atamasulidwa ku akatundu olemera a zandalama zankhondo, iwo angathe kulunjikitsa chuma chonsecho, kufufuza, ndi antchito kukuthetsa mavuto otero.
6 Kodi mumakhulupiriradi zimenezo? Kodi pali umboni wamphamvu wosonyeza kuti anthu angadzetse zothetsera mavuto zirizonse zosatha? Kodi mbiri imasonyezanji? Ndithudi, Kodi chokumana nacho cha inumwini m’moyo chimakuuzani chiyani?
7, 8. (a) Kodi tingayang’anenso kuti kaamba ka chothetsera mavuto? (b) Kodi Baibulo liri bukhu lotchuka motani?
7 ‘Koma ngati anthu alibe zothetsera, kodi pamatsala chiyani?’ inu mungafunse. Eya, pali umboni wosatsutsika wakuti dziko lapansi ndi zinthu za moyo pa iro zimasonyeza mpangidwe wanzeru. (Ahebri 3:4) Kodi kuli kotheka kuti Uyo amene akuchititsa zinthuzi akuphatikizidwa m’nkhaniyi? Kodi iye adzalowerera m’zochitika za anthu? Baibulo lokha limapereka mayankho a mafunso amenewa.
8 Pamenepa, polingalira chimene chiri paupandu, kodi sikuli kokupindulitsani kupenda chimene Baibulo limanena ponena za nkhani imeneyi? Inu mungazindikire kuti ndilo bukhu lotembenuzidwa ndi kufalitsidwa mofala kopambana pa dziko lapansi. Makope mabiliyoni ambiri agawiridwa m’zinenero zoposa 1 800 liri lathunthu kapena mbali yake.2 Koma kodi munadziwa kuti bukhu lakale limeneli limanena nkhani zenizenizo zimene ziri zofunika kopambana kwa ife m’zaka zino za zana la20?
9, 10 (a) Kodi Baibulo limanena chiyani ponena za mtsogolo, ndi ponena za maboma a anthu? (b) Kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani, ndipo ndiliti pamene udzatenga ulamuliro ku maboma onse a lero lino?
9 Ochuluka amadziŵa kuti Baibulo limaneneratu za ‘chimaliziro cha dziko.’ Koma ngoŵerengeka amene amadziŵa chimene limanena ponena zakuti ndiliti pamene chimenecho chidzabwera, kapena mmene moyo padziko lapansi udzakhalira pambuyo pake. (Mateyu 24:21, 22; 2 Petro 3:11-13) Iwo angapempheredi Pemphero la Ambuye, kumene amapempherera ‘ufumu wa Mulungu kuti udze.’ (Mateyu 6:9, 10) Koma ngoŵerengeka amene amazindikira kuti ufumu wa Mulungu uli boma lenileni limene lidzaloŵa m’malo madongosolo alipowa a ndale za dziko. Monga mmene mneneri Danieli anafotokozera kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthawi zonse. . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
10 Mokondweretsa, ulosi wa Baibulo wonena za “mtendere ndi chisungiko” wotchulidwa pachiyambi umaphatikizapo mbali izi: “Pamene kuli kwakuti iwo anena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ pamenepo chiwonongeko cha mwadzidzidzi chidzawafikira modzidzimutsa.” (1 Atesalonika 5:3, NW) Chotero mwachiwonekere ziri zonse zimene zidzakhala mtendere ndi chisungiko zimene atsogoleri aumunthu adzalengeza zidzakhala zakanthawi. Pakuti maulosi amasonyeza kuti mofulumira pambuyo pa nthawiyo maulamuliro onse a anthu adzaphwanyidwa psiti, kuti alowedwe m’malo ndi boma limodzi kaamba ka dziko lonse lapansi—Ufumu wa Mulungu.
11, 12. Kodi pali kusiyana kwina kotani pakati pa zimene Baibulo limanena kuti Ufumu wa Mulungu udzachita ndi zimene atsogoleri a anthu akuyesa kuchita?
11 Ndiponso, Baibulo limavumbula kusiyana kochuluka pakati pa mtendere ndi chisungiko zimene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa ndi zimene atsogoleri a anthu amalonjeza. Lerolino anthu akunena mogwirizana ndi kuchepetsedwa kwa zida zankhondo mwa mapangano. Baibulo, mosiyana ndi zimenezo, limanena kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa kotheratu zida zonse zankhondo ndipo adzachotsa zoyambitsa nkhondo. (Salmo 46:9; Yesaya 2:2-4) Ndipo chisungiko chimene Mulungu akulonjeza sichiri kokha ku nkhondo zapakati pa mitundu. Chiri kwa adani a mtundu uliwonse, kotero kuti palibe aliyense amene adzafunikira kuchitanso mantha—usana kapena usiku. (Mika 4:3, 4) Ndiponso, anthu tsopano akudera nkhawa ndi kuletsa upandu, koma chifuno cholengezedwa cha Mulungu ndicho kuchotsa malingaliro ndi mikhalidwe imene imayambitsa upandu.—Salmo 37:8-11; Agalatiya 5:19-21.
12 Mitundu imanyadiranso kupita kwawo patsogolo m’kufufuza mankhwala ndi kusamalidwa kopitisidwa patsogolo kwa odwala ndi okalamba. Koma Baibulo limalongosola mmene boma la Mulungu lidzabweretsera thanzi lokwanira ndi losatha, ngakhale kulaka mavuto aukalamba ndi imfa! (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndiponso, mu Ufumu wa Mulungu ntchito ya munthu idzakhaladi yopereka tanthauzo, ikumabweretsa chikhutiro chenicheni. Pakuti kodi mungakhale okondwa motani ngati ntchito yanu iri yogwiritsa mwala kapena simabweretsa lingaliro lenileni la kuchita kanthu?—Yesaya 65:21-23; Aroma 8:19-21.
13. Kodi ndimafunso otani amene kukakhala kopindulitsa kuti ife tiwapende?
13 Kodi nchiti chimene mukhulupirira kuti chimapereka mtundu wa mtendere ndi chisungiko zimene zidzawongolera mbali iriyonse ya moyo wanu—malonjezo a anthu, kapena malonjezo a Mulungu okwaniritsidwa ndi boma lake la Ufumu? Mwa kutsatira chimene dziko lonse limapereka, kodi mwapeza kwenikweni chimene mumafuna m’moyo? Bwanji ngati mudzilola kutengedwa ndi zimene zingakhale zofala patsopano lino, ndiyeno nkudzazindikira kuti mwatengeka ndi malonjezo osokeretsa, kukumakusiyani wopanda mtendere wowona ndi chisungiko? Kumbali ina, kodi mungakhale ndi chidaliro kuti zimene Baibulo limalonjeza ziri zokhoza kukhulupirika, zopindulitsa, ndi zothandiza? Ndithudi, mayankho a mafunso otere ngofunikira kupenda mosamalitsa.
[Mawu a M’munsi]
[Chithunzi chachikulu patsamba 4]
[Chithunzi patsamba 9]
Palibe munthu amene adzakhalanso m’mantha—usana kapena usiku