Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 8/1 tsamba 6-7
  • Chiwopsezo cha Nyukliya Chichotsedwa Kotheratu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiwopsezo cha Nyukliya Chichotsedwa Kotheratu!
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mtendere ndi Chisungiko”​—Chinyengo
  • Mtendere ndi Chisungiko​—Zenizeni
  • Potsiriza Pake Tsogolo Lopanda Choopsa!
    Galamukani!—1999
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Kuopa Nyukiliya Kwatha?
    Galamukani!—1999
  • Kuopa Nyukiliya—Sikunathe Ngakhale Pang’ono
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 8/1 tsamba 6-7

Chiwopsezo cha Nyukliya Chichotsedwa Kotheratu!

MULUNGU samafuna kuti anthu akhale m’mantha oipa. Monga “Mulungu wachimwemwe,” amafuna kuti iwo asangalale ndi mtendere ndi kukhala ndi moyo m’chisungiko​—mwachidule, kukhala achimwemwe. (1 Timoteo 1:11, NW) Mwachionekere, zimenezi nzosatheka m’dziko lodzala ndi ziwopsezo za nyukliya.

“Mtendere ndi Chisungiko”​—Chinyengo

Kuyenera kukhala kwachionekere kuti chiwopsezo cha nyukliya sichinathe konse. Komabe, mosasamala kanthu za kusakhazikika kwa ndale zadziko, chuma, ndi chitaganya, maiko ambiri akuonekera kukhala ndi chiyembekezo. Kuyesayesa kwapang’onopang’ono kwa kuletsa ngozi kwakhala koonekera chiyambire pa kulengezedwa kwa International Year of Peace ya Mitundu Yogwirizana mu 1986.

The Bulletin of the Atomic Scientists m’zaka khumi zapitazo yabwezera kumbuyo koloko yake ya tsiku lachiweruzo​—njira yake yosonyezera kuthekera kwa nkhondo ya nyukliya​—kuchokera pa mphindi 3 pakati pausiku pasanafike kuibwezera kumphindi 17 pakati pa usiku pasanafike. Mu 1989 Stockholm International Peace Research Institute inanena kuti “chiyembekezo chothetsera mikangano mwamtendere chinali ndi maziko abwino kwambiri koposa m’chaka china chilichonse chiyambire kutha kwa Nkhondo Yadziko II.”

M’zaka zaposachedwapa Mitundu Yogwirizana yalimbitsidwa kuchitapo kanthu kumalo a mavuto padziko lonse. Chipambano chake, pamene kuli kwakuti sichili chotheratu, chakhala chokwanira kuchirikizira mzimu wa anthu onse wa chiyembekezo. Mwachionekere mtsogolo mudzabweretsa zipambano zina zowonjezereka. Mfuu za “mtendere ndi [chisungiko, NW]” mwinamwake zidzakhala zomveka mowonjezereka ndi zazikulu kwambiri. Zingadzafikire pa kukhulupiridwadi.

Koma chenjerani! “Pamene angonena, Mtendere ndi chisungiko,” Baibulo limachenjeza motero, “pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” Motero, mfuu za “mtendere ndi chisungiko” zidzasonyeza nthaŵi ya Mulungu ya “kuwononga iwo [amene kupyolera mwa kuipitsa, kwa nyukliya ndi njira zina] akuwononga dziko.”​—1 Atesalonika 5:3, 4; Chivumbulutso 11:18.

Onani kuti Baibulo silimanena kuti mitundu idzadzipezera “mtendere ndi chisungiko.” Mwachionekere idzakhala ikulankhula za izo m’njira yapadera, ikumasonyeza chiyembekezo ndi chikhutiro chimene sichinamvedwe papitapo. Mipata yopezera mtendere ndi chisungiko idzaonekera kukhala ili pafupi kwambiri koposa ndi kale lonse. Mosasamala kanthu za kupitiriza kwa chiwopsezo cha nyukliya, mitunduyo idzakopedwa ndi lingaliro lonyenga la chisungiko.

Komabe, Akristu owona sadzanyengedwa. Pokhala ndi chidwi chachikulu adzayembekezera kanthu kena kabwino kwambiri koposa mtendere ndi chisungiko za anthu!

Mtendere ndi Chisungiko​—Zenizeni

Malinga ndi kunena kwa Salmo 4:8, mtendere woona ndi chisungiko ziyenera kupezedwa m’makonzedwe a Yehova Mulungu okha: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.” Mfuu iliyonse ya “mtendere ndi chisungiko” yosonyezedwa kunja kwa makonzedwe a Ufumu wa Yehova ingangokhala yachinyengo. Singathe kupeza kanthu kalikonse kofunika kokhalitsa.

Ufumu wa Mulungu pansi pa Kristu suli wokhutiritsidwa ndi zothetsera mavuto zakanthaŵi. Boma la Mulungu lidzachita zambiri koposa kuchepetsa chiŵerengero cha zida za nyukliya; lizadzichotseratu limodzi ndi zida zina zonse zankhondo. Salmo 46:9 limalonjeza kuti: “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.”

Mofananamo, ziwopsezo za nyukliya zokhalapo chifukwa cha makina otulutsira mphamvu ya nyukliya osagwira bwino ntchito kapena chifukwa cha zotayidwa za radiation zidzakhala zinthu zakale. Zitapanda kutero mawuwo angadzakhale abodza: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Mulungu sanganame. Tilibe chifukwa chokayikirira mawu ake.​—Mika 4:4; Tito 1:2.

Kodi mungakonde kukhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo m’dziko limene chiwopsezo cha nyukliya chachotsedwa kotheratu? Mungathe kutero, pakuti Mawu a Mulungu amafotokoza momvekera bwino zofunika zake. Mwa kuziphunzira ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nazo, tsiku lina inu mungadzakhale ndi chimwemwe cha kunena ndi mpumulo kuti: “Chiwopsezo cha nyukliya​—chatha tsopano!”

[Chithunzi patsamba 7]

Mtendere udzafunga m’dziko latsopano la Mulungu popanda chiwopsezo chilichonse cha nyukliya

[Mawu a Chithunzi]

M. Thonig/​H. Armstrong Roberts

[Mawu a Chithunzi patsamba 6]

Chithunzi cha U.S. National Archives

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena