Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/1 tsamba 5-6
  • Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtendere ndi Chisungiko​—Kalambula Bwalo wa Chiyani?
  • Zochitika Zosonyeza Nthaŵi Zivumbulidwa
  • ‘Kulimbana’ kwa Maulamuliro Aakulu Adziko
  • Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Chiwopsezo cha Nyukliya Chichotsedwa Kotheratu!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kukhala Ogalamuka Molimbana ndi “Mtendere ndi Chisungiko” monga Kwaganiziridwa ndi Mitundu
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/1 tsamba 5-6

Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko

Anthu ambiri amangokhulupirira chowonadi chachiphamaso cha umodzi wadziko lonse ndi mtendere ndi chisungiko zimene ungabweretse. Iwo amayembekezera kuti zimenezi zingatsogolere ku dziko labwinopo. Koma Baibulo limasonyeza kuti zambiri zikuloŵetsedwamo koposa mmene zikuwonekera.

NKHANI ya mtendere ndi chisungiko iri makamaka yokondweretsa kwa Akristu chifukwa cha zimene Paulo anauziridwa kulembera mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Mawu ake analembedwa m’Baibulo pa 1 Atesalonika 5:3 (NW) kuti: “Pamene kuli kwakuti iwo akunena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ pamenepo chiwonongeko chadzidzidzi chidzaŵafikira modzidzimutsa mofanana ndi zoŵaŵa za nsautso pa mkazi wapakati; ndipo iwo mwanjira iriyonse sadzapulumuka.” Lembali limadzutsa mafunso ofunika kwambiri.

Mtendere ndi Chisungiko​—Kalambula Bwalo wa Chiyani?

Mutaŵerenga mawu apatsogolo ndi apambuyo a Paulo ogwidwa pamwambapa, mudzawona kuti amene akunena kuti “mtendere ndi chisungiko” sali Akristu ogalamuka, mmalomwake, iwo ali anthu okhala mumdima wosadziŵa zimene zikuchitika. Iwo ali mumkhalidwe woopsa komanso sakudziŵa zimenezo chifukwa chakuti akuganiza kuti zinthu ziri bwino. Komabe, ponena za Akristu, Paulo anati: ‘Koma za nthaŵizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulembereni.’ (1 Atesalonika 5:1) Inde, tiyenera kudziŵa ndandanda ya Mulungu ya nthaŵi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Paulo ananena kuti nthaŵi ya chiwonongeko chadzidzidzi, chotchedwa “tsiku la Yehova,” ikudza “mofanana kwambiri ndi mbala usiku.”​—1 Atesalonika 5:2, NW.

Kodi nkhani yonenedweratuyo ya mtendere ndi chisungiko ikuloŵetsamonji? Mwachiwonekere, siyenera kukhala nkhani wamba. Anthu akhala akulankhula za mtendere pafupifupi kwautali wonse womwe akhala akumenyana nkhondo. Mawu a Paulo ayenera kusonya ku nthaŵi pamene mitundu ikuwonekera kukhala ikupeza mtendere ndi chisungiko mwanjira yapadera. Komatu izi ziri kokha chiphamaso. Mtendere ndi chisungiko zowonekerazi zimene zimatsogolera ku chiwonongeko chadzidzidzi siziri konse mtendere weniweni kapena chisungiko chowona.

Yesu nayenso analankhula ponena za chiwonongeko chadzidzidzi chimenechi. Iye anachitcha ‘masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.’ Zaka mazana angapo Yesu asanadze, mneneri Danieli nayenso analankhula za icho, ndipo anachilongosola kukhala ‘nthaŵi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthaŵi yomwe ija.’​—Mateyu 24:21; Danieli 12:1.

Kaya chitchedwe kuti masauko aakulu kapena kuti nthaŵi ya masautso​—malinga ndi maulosiwo, icho chidzafafaniza chizindikiro chirichonse cha dongosolo lapadziko lapansi la Satana. Mmalo molandira chivomerezo chaumulungu, nkhani yoloseredwayo ya mtendere ndi chisungiko ikutsogolera ku chinthu chosiyana kotheratu!​—Yerekezerani ndi Zefaniya 3:8.

Zochitika Zosonyeza Nthaŵi Zivumbulidwa

Kodi zochitika zowonekera kusonya ku umodzi wokulirapo wa dziko ndi ziyembekezo zotsatirapo za mtendere ndi chisungiko ndizo kukwaniritsidwa kwa chenjezo laulosi la Paulo? Eya, monga momwe magazini ano asonyezera mobwerezabwereza, chiyambire 1914 tawona kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo ambiri okhudza kukhalapo kwa Yesu kumwamba muulamuliro wa Ufumu. (Mateyu, mitu 24, 25; 2 Timoteo 3:1-5; Chibvumbulutso 6:1-8) Yesu anasonyeza kuti tsiku la Yehova, pamene chiwonongeko chadzidzidzi chidzabwera pa anthu oipa, lidzafika ziŵalo zina za mbadwo wa anthu amene anawona kuyambika kwa nthaŵi imeneyi zidakali zamoyo.​—Luka 21:29-33.

Mtumwi Paulo nayenso anapereka chochitika chodziŵitsa nthaŵi. Iye anati: “Pamene akunena za mtendere ndi chisungiko, panthaŵi imodzi yomweyo tsoka lidzawafikira.” Kumasulira kumeneku kwa The New English Bible kwa mawu a Paulo kumasonyeza mowonekeratu kuti chisautso chachikulu chimenecho chikuchitika “pamene akunena.” Mofanana ndi mbala usiku​—chiwonongeko​—chosawonedweratu chidzakantha pamene sakuchiyembekezera mpang’ono pomwe, pamene chisamaliro cha anthu ambiri chiri chosumikidwa pa mtendere ndi chisungiko zoyembekezeredwazo. Chotero, ngakhale kuti pakali pano sitingagamule motsimikiza kuti mkhalidwe ulipowu wa mtendere ndi chisungiko ukukwaniritsa mawu a Paulo​—kapena kuti ndi kumlingo wotani umene kulankhula za mtendere ndi chisungiko kuyenera kukulabe​—chenicheni chakuti kulankhula koteroko tsopano kukumvedwa pa mlingo waukulu kuposa ndi kale lonse chimachenjeza Akristu kufunika kwakukhala maso panthaŵi iriyonse.

‘Kulimbana’ kwa Maulamuliro Aakulu Adziko

Pamene analankhula za nthaŵi ya masautso, mneneri Danieli anaperekanso chochitika chodziŵitsa nthaŵi. Iye anasonyeza kuti nthaŵi ya masautso ikakhalapo kumapeto a kulimbana kwanthaŵi yaitali kwa maulamuliro aakulu aŵiri, wina wotchedwa “mfumu ya kumpoto” ndi winawo, ‘mfumu ya kumwera.’ (Danieli 11:5-43) Chiyambire mapeto a Nkhondo Yadziko ya II, maulamuliro aakulu ameneŵa aimiridwa ndi ‘mfumu ya kumwera’ yachikapitolizimu ndi “mfumu ya kumpoto” yachisosholizimu.

Danieli ananeneratu kuti chidani chachikulu chokhala pakati pa maulamuliro aŵiri aakulu ameneŵa, monga momwe chawonedwera mkati mwa zaka 45 zapitazo, chikakhala ‘kulimbana,’ mofanana ndi opingana ndale aŵiri akukalamira kuti apambane. Posachedwapa, kulimbanako kwaonekera kuti kwazimiririka. Mwachitsanzo, m’May chaka chatha, nduna yowona nkhani zakunja kwa Soviet Union inalengeza kutha kwa Nkhondo Yoputana ndi Mawu. M’June, magazini a Time anasonya ku msonkhano wa atsogoleri aboma a United States ndi Soviet Union kuti: “Zivomerezano zina za kuchepetsa zida zankhondo ndi kuchepetsa kuyesa zida za nyukiliya zawonekera kukhala chipambano chodabwitsa m’zaka zingapo zapitazo. Komano, ngati zonse zipendedwa, zimawonekera kukhala zosafika pachimake.”

Kaya ngati ubwenzi wowonekerawu pakati pa maulamuliro aakulu aŵiriwo uli wakanthaŵi kapena wokhalitsa, zidzadziŵika m’kupita kwa nthaŵi. Komabe, chinthu chimodzi nchowonekeratu. Nyengo yanthaŵi yotchulidwa ndi Yesu yafika patali. Ndipo zinthu zochitika m’dziko zikusonyeza kuti tiri pafupi ndi zochitika zonenedweratu ndi mtumwi Paulo ndi mneneri Danieli. Ngakhale kuti zochitika za ndale zadziko zaposachedwapa kumlingo winawake zachititsidwa ndi chisonkhezero cha matchalitchi a Chikristu Chadziko, izo sizidzatsogolera ku mtendere wokhalitsa. Umboni ukusonyeza kuti izo zidzatsogolera mitundu ya dziko lino ku chosiyana kotheratu.

[Zithunzi patsamba 6]

Zidzadziŵika m’kupita kwa nthaŵi kuti ubwenzi wowonekera kukhala pakati pa maulamuliro aakulu aŵiri udzakhala kwa utali wotani

[Mawu a Chithunzi]

USSR Mission to the UN

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena