Kuchiritsa kwa Chikhulupiriro Nchiyani Chimene Chiri Chisonkhezero Chake?
Tchalitchi chimafuula ndi mawu a gitala, lipenga, ng’oma, lingaka, ndi nsanje zoliritsa. Amuna, akazi ndi ana amavina ndi kuimba mu mkhalidwe wa chisangalalo chopanda dongosolo. Mkhalidwewo uli wabwino kaamba ka kuchiritsako kuti kuyambike.
Wochiritsa mwa chikhulupiriro, atavala miinjiro yoyera yofutukuka, amayamba mwa kuika manja ake pa munthu wopunduka yemwe amakwawakwawa pamodzi ndi manja. Kenaka munthu wakhungu, amene magalasi ake akuda amaphimba maso ake osawonawo. “Chozizwitsa!” openyerera amafuula pamene wopunduka ayamba kuyenda ndi wakhungu ayamba kuwona . . .
ZOCHITIKA zonga izi ziri zofala m’matchalitchi ambiri ochiritsa mwa chikhulupiriro a ku Africa. Ndithudi ochiritsa mwa chikhulupiriro ali ndi atsatiri ambiri mu Africa ndi maiko ena chifukwa cha kudzinenera kwawo kuti iwo angathetse mitundu yonse ya mavuto kupyolera mwa pemphero ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Ena chotero amabwera kwa ochiritsa mwa chikhulupiriro ndi matenda a zachuma. Ndipo popeza kuti mu chitaganya cha ku Africa kukhala wopanda mwana kaŵirikaŵiri kuli chokhumudwitsa, ena amabwera kwa ochiritsa mwa chikhulupiriro kuyembekezera kaamba ka kuchiritsidwa kaamba ka kusabala.
Mavuto a zaumoyo, ngakhale kuli tero, amagwira chisamaliro cha ochiritsa mwa chikhulupiriro kuposa china chirichonse. Ngakhale kuti mankhwala ochiritsa amasefukira pa msika wadziko ndiponso zoyesayesa zamphamvu zikupangidwa m’munda wa za mankhwala kubweretsa mpumulo kwa odwala, munthu adakali kutali kwambiri kupeza yankho ku vuto la matenda. Minkhole ina ya matenda yawononga ndalama zambiri kufunafuna kuchiritsa, kokha kukumana ndi kulephera. Chotero, nchosadabwitsa, kuti mkusowa chochita, ambiri amatembenukira kwa ochiritsa mwa chikhulupiriro!
Ena amadzimva kuti kuchiritsa kwa chikhulupiriro kwagwira ntchito kwa iwo ndipo sangawone kuwombana kulikonse kwa icho ndi Chikristu. Ndithudi, popeza kuti ochiritsawo kaŵirikaŵiri amadzinenera kuti amagwira ntchito m’dzina la Yesu, sichiri chachilendo kwa otsatira awo kukhala ziwalo za ponse paŵiri chipembedzo chachikulu ndi tchalitchi chochiritsa mwachikhulupiriro. Koma kodi mlambiri wowona wa Mulungu moyenerera angadziyeneretse iyemwini kwa wochiritsa mwachikhulupiriro? (Yohane 4:23) Ndipo kodi kuchiritsa kulikonse kokwaniritsidwa ndi oterowo ndithudi kungaperekedwe kwa Mulungu?