Phindu la Kuimba m’Kulambira Kowona
KODI mungayerekezere dziko lopanda nyimbo? Osadzamvanso kuimba kwa chimwemwe kwa ana kapena mawu osangalatsa a mbalame zolira usiku kapena mbalame zolira ngati beru? Osadzamvanso kulira koyambukira kwa magpie kapena kusekera kum’mero kwa kookaburra? Mwachimwemwe, ichi sichidzachitika nkomwe. Koma kulingalira koteroko kumawunikira imodzi ya mphatso zambiri za Mulungu kwa munthu: mphatso ya nyimbo.
Yehova Mulungu wa Nyimbo
Nchifukwa ninji kuimba kumabweretsa chisangalalo ndi chimwemwe kwa ife? Kaamba ka chinthu chimodzi, Yehova iyemwini amasangalala ndipo amasangalatsidwa ndi nyimbo za chitamando zoimbidwa ndi zolengedwa zake. Kodi mungachitire chithunzi chochitika pamene angelo onse anafuula mwachimwemwe paukulu wa chilengedwe cha dziko lapansi cha Yehova? Kapena kodi mungalingalire za kuimirira mozizwitsa pakati pa angelo mu nthaŵi ya ngululu ya usiku wa kubadwa kwa umunthu kwa Yesu, losangalatsidwa ku kumveka kwa kuimba kwa khamu la angelo akuimba: “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba”?—Luka 2:13, 14; Yobu 38:7.
Njira imodzi imene Yehova anasonyezera kuti iye ali Mulungu wa nyimbo inali mwa kupanga kuimba kukhala mbali ya kulambira kowona mu Israyeli. Pambuyo pake, Mulungu anavumbulutsanso kugwirizana kwachindunji pakati pa kuimba ndi kulambira kowona mu Chivumbulutso cha masomphenya operekedwa kwa mtumwi Yohane. M’chochitika chimodzi cha ulosi khamu la oimba—144,000 amphamvu—likuimba nyimbo yatsopano ya chipambano pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 14:3.
Kuimba mu Nthaŵi za Chikristu Chisanakhale
Ukulu wa Mulungu ndi zochita zake zochititsa mantha zinafulumizanso atumiki ake a padziko lapansi kusangalala ndi kuimba. Imvani zisonkhezero zodzutsa maganizo zimene kuimba kunali nako pa Aisrayeli mwamsanga pambuyo pa kupulumutsidwa kwawo kozizwitsa kuchokera ku ukapolo ku Aigupto. Mitima ya Mose ndi Aisrayeli anzake inasonkhezeredwa mwa malingaliro pamene anaimba nyimbo ya chipambano kukumbukira chimene Yehova anachita kwa Farao ndi khamu lake.—Eksodo 15:1-21.
Pambuyo pake m’mbiri ya Israyeli, tsiku losangalatsa linafika pamene, pansi pa chitsogozo cha Mfumu Davide, likasa la chipangano linayenera kuikidwa mkati mwa chihema chake choikidwa mwapadera. Chinali chochitika cha m’mbiri chotani nanga! Osati kokha kuimba kowonekera komanso gulu loimba lokhala ndi zoimbira lodzutsa moyo linawonjezera ku ukulu wa tsikulo.—1 Mbiri 16:4-36.
Chikondi cha Davide kaamba ka nyimbo ndi luso lake pa zeze zinakulitsa kufunitsitsa kwake kwa kupititsa patsogolo nyimbo ndi kuimba m’kulambira kowona. Pa Masalmo 33:1, 3, timamva za kuchonderera kwake kwa chikondi kaamba ka alambiri a Yehova kuimba mokweza kwa Mulungu ndi mitima yawo yonse: “Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima . . . Muimbe mwaluso kumveketsa mawu.”
Kuimba mu Nthaŵi za Chikristu
Mu nthaŵi zoyambirira za Chikristu, kuimba kunapanganso mbali yaikulu m’kulambira kowona. Yesu ndi atumwi ake anaimba pamodzi pambuyo pa chakudya cha madzulo isanafike imfa ya Yesu. (Marko 14:26) M’ndende Paulo ndi Sila anaimba mofuula kotero kuti onse anamva. (Machitidwe 16:25) Mofanana ndi Davide mtumwi Paulo anali wotenthedwa maganizo ponena za kugwiritsira ntchito nyimbo. Nthaŵi zoposa kamodzi, iye analimbikitsa akhulupiriri anzake kuimba nyimbo za chitamando kwa Yehova.—Aefeso 5:18, 19; Akolose 3:16.
M’kulambira kwamakono kwa Chikristu, kuimba kulinso mbali yowonekera. Mu 1905 bukhu la Hymns of the Millennial Dawn linafalitsidwa. Mutu waukulu wa bukhulo unalongosola nyimbo zake 333 monga “Kusonkhanitsidwa Kosankhika kwa Masalmo ndi Nyimbo ndi Nyimbo Zauzimu Kuthandiza Anthu a Mulungu m’Kuimba ndi Kupanga Chitamando m’Mitima Yawo kwa Ambuye.”
Kenaka mu 1928 bukhu la nyimbo lokonzedwanso lokhala ndi nyimbo 337 linaperekedwa. Linali kutchedwa Songs of Praise to Jehovah, ndipo mawu ake oyamba ananena kuti: “Nyimbo izi zidzapezedwa kukhala m’chigwirizano ndi chowonadi chaumulungu chokonzekera kumveketsedwa tsopano.” Komabe, pamene zaka zinapita ndipo pamene kuwala kwa chowonadi kunawonjezeka, chinakhala chowonekera kuti zina za nyimbo zimenezi zinasonkhezeredwa ndi kulingalira kotengedwa kuchokera ku chipembedzo chonyenga. M’kuwonjezerapo, nyimbo za Ufumu zolimbikitsa kulalikira mbiri yabwino zinafunikira, pamene kulalikira kwapoyera kunawonekera koposa.—Mateyu 24:14; Ahebri 13:15.
Mu 1944 Kingdom Service Songbook inaperekedwa, yokhala ndi nyimbo 62. Zaka makumi aŵiri pambuyo pake, mu 1966, bukhu la Kuimba ndi Kutsagana ndi Nyimbo Zamalimba m’Mitima Yanu linatulutsidwa. Iyi inali ndi nyimbo za Ufumu 119 zomwe zinakwaniritsa mbali iriyonse ya mkhalidwe Wachikristu ndi kulambira, kuphatikizapo kuchitira umboni kwa ena ndi kulemekeza Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu.
Chifupifupi zaka zina makumi aŵiri zinapita, mkati mwa zimene kuwala kwa chowonadi kunapitirizabe kuwonjezereka. (Miyambo 4:18) Chifuno chinawonedwa cha kukhala ndi bukhu la nyimbo lina. Chotero mu 1984 kunabwera kutulutsidwa kwa bukhu la nyimbo lokhala ndi mutu wakuti Sing Praises to Jehovah. Iyi iri ndi nyimbo za Ufumu 225, lokhala ndi mawu ndi kaimbidwe kopangidwa kotheratu ndi atumiki odzipereka a Yehova kuchokera kumbali zonse za dziko lapansi.
Gwiritsirani Ntchito Kuimba kwa Teokratiki Mokwanira
Fanizo losonyezedwa pa pepala la masamba aŵiri kumapeto kumbuyo kwa bukhu la nyimbo laposachedwapa limeneli limatitsitsimula ife kugwiritsira ntchito kuimba kwa teokratiki mokwanira pa misonkhano ya Chikristu. Oimba ophunzitsidwa m’kachisi osonyezedwa pamenepo mwachiwonekere akukweza mitima yawo ndi mawu awo mu nyimbo kwa Mulungu.—1 Mbiri 25:7.
Ife mofananamo tingaimbe pa misonkhano yathu ya Chikristu, kutsegula pakamwa pathu ndi kuimba kuchokera m’mitima yathu. Komabe, si tonse a ife amene tingachite chimenecho. Mwinamwake kunyada kumatipangitsa ife kuphonya chimwemwe cha kuimba kwa Yehova popanda kuchititsidwa manyazi, mosasamala kanthu ndi mtundu wanji wa liwu limene tiri nalo. Tingakhale odera nkhaŵa kwambiri ndi chisonyezero chimene chikupangidwa pa ena oima pafupi nafe. Mose anali ndi vuto lofananalo—osati ndi kuimba koma ndi kulankhula. Yankho limene Yehova anampatsa iye lingatithandize ife ngati tiri ndi chikhoterero cha kusaimba chifukwa cha kusoweka kwa kuthekera. Yehova anafunsa Mose: “Anampangira munthu m’kamwa ndani? . . . Si ndine Yehova kodi?” (Eksodo 4:11) Ndithudi, Yehova mwachimwemwe adzamvetsera pamene tikugwiritsira ntchito kuthekera kulikonse kumene iye watipatsa kuimba chitamando chake mofuula!
Talingalirani, kachiŵirinso, mmene Paulo ndi Sila anaimbira mofuula pamene anali m’ndende. Panalibe kumvetsedwa manyazi pamenepo, ndipo iwo analibe zoimbira zothandizira, ndiponso analibe bukhu la nyimbo lolitsatira. Onani chithunzi cha chochitikacho: “Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Sila analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m’ndendemo analinkuwamva.” (Machitidwe 16:25) Kodi ichi chinali chifukwa chakuti kaya Paulo kapena Sila anali ataphunzira mawu oimbira? Osati kwenikweni. Chodera nkhaŵa chawo chachikulu chinali cha kuimba mofuula ndipo kuchokera mu mtima! Nchiyani chimene chiri chodera nkhaŵa chathu chachikulu pamene tiimba nyimbo za chitamando?
Tonsefe Tingawongolere
Uphungu wa woimba Davide uli woyenerera pano: “Muimbe mwaluso kumveketsa mawu.” (Masalmo 33:3) Chimenechi ndi chimene Yehova amayembekezera kwa atumiki ake onse—osati chinachake chowonjezereka, osati chinachake chochepera kuposa pa chimenecho kuti ‘tichite kuthekera kwathu.’ Ngati tingachite kokha chimenecho, tingayembekeze Yehova kudalitsa zoyesayesa zathu, ndipo ku chisangalatso chathu—ndipo nthaŵi zina kukudabwitsidwa kwathu—ife mwinamwake tidzapanga kuwongokera.a
Pano pali malingaliro ena okhoza kugwirirapo ntchito omwe angakuthandizeni inu kuwongolera mtundu wa kaimbidwe kanu: Yesani kumvetsera kaŵirikaŵiri ku makaseti a Kingdom melodies atsopano, kugwiritsira ntchito matepi a nyimbo zojambulidwa kapena marekordi kumene kuli kothekera. Kwa ena, kuimba nyimbozo pa nyumba kapena pa misonkhano yaing’ono ndi akhulupiriri anzawo kwatsimikizira kukhala kopindulitsa ndiponso kosangalatsa. Pa misonkhano ya mpingo chiri chofunika kwambiri kuti chothandizira kuimba chiseŵeredwe mofuula mokwanira kuti chimvedwe ndi awo onse amene akuimba. Ichi chimachipangitsa icho kukhala chopepuka kutsatira kaimbidwe ndi chidaliro chowonjezereka kumbali ya awo amene akuimba. Yemwe akulengeza nyimbo ayenera kutchula mutu wake, mwinamwake kuzindikira kuyenerera kwake, osati kokha nambala.
Makolo, kodi mumalimbikitsa ana anu kuimba nyimbo za Ufumu ndi kutenthedwa maganizo ndipo kuchokera m’mitima yawo? Mabanja omwe alimbikitsa achichepere awo kuimba kuchokera mu mtima, ndipo ndi kumvetsera, nthaŵi zambiri apeza kuimba koteroko kukhala thandizo labwino ku kukula kwauzimu.
Mapindu Ali Ochuluka
Pali mapindu ambiri kuchokera ku kuimba mofuula ndipo kuchokera mu mtima. Kudzilowetsamo kwathu kwaumwini m’kulambira kwapoyera kumakhala kwamphamvupo. Awo oima pafupi nafe amalimbikitsidwa kuimba mofuulirapo pamene iwo akumva kuimba kwathu kopanda manyazi. Mpingo wonse umapindulanso, popeza kuwonjezeka kwa chiunda kuli kopatsirana!
Kuwonjezerapo, kuimba kwamphamvu kumapereka umboni wabwino kwa awo opezeka pa misonkhano kwa nthaŵi yoyamba. Awo amene akudutsa pa Nyumba zathu za Ufumu, limodzinso ndi anansi okhala pafupi, amasangalatsidwa ndi kuimba kwathu kwabwino, monga mmene mosakaikira analiri andende ena omwe anamva Paulo ndi Sila. Ichi chatulukamo mu amvetseri ena kufuna kudziŵa zochulukira ponena za chowonadi.
Chofunika koposa, kuimba kwathu kowongoleredwa kudzabweretsa chilemekezo chochuluka kwa Yehova, M’yambitsi wa nyimbo ndi kuimba, mmodzi woyenera kulemekezedwa ndi nyimbo pamwamba pa ena onse.
[Mawu a M’munsi]
a Zina za nyimbo zaposachedwapa zingakhale zovutirapo pang’ono kwa ife kuziimba choyamba, koma pambuyo pa kuzoloŵerana nazo, izo zingatsimikizire kukhala zokondedwa zathu za pamtima. Mwachitsanzo, pamene bukhu la nyimbo lapapitapo linabwera, nyimbo 88, “Kuyenda mu Umphumphu,” siinakondedwe mu dziko lina, koma pambuyo pake iyo inakhala nyimbo yokondedwa kwambiri.