Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/03 tsamba 6
  • Kuimba Kwathu Kutamande Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuimba Kwathu Kutamande Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Imbirani Yehova Zitamando
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Phindu la Kuimba m’Kulambira Kowona
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Tiziimba Mosangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Malo a Nyimbo Pakulambira Kwamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 12/03 tsamba 6

Kuimba Kwathu Kutamande Yehova

1 Akristu odzipatulira amasangalala kumva anthu ambiri akuimba zotamanda Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi. Inde, njira yabwino kwambiri yogwiritsa ntchito mawu ndiyo kutamanda Amene anapangitsa kuti anthu azitha kuimba ndi kupeka nyimbo.

2 Kuimba pagulu kunalitu mbali ya kulambira pa kachisi ku Yerusalemu. M’buku la Ezara ndi Nehemiya amatchula za kuimba malo oposa makumi aŵiri kusonyeza kuti kuimba kunali kofunika kwambiri pa utumiki wa pakachisi. M’buku la Masalmo, limene kwenikweni lili ndi nyimbo, timapezamo malo pafupifupi 130 onena za kuimba ndiponso nyimbo, ndipo m’Malemba otsalawo amatchulanso za nyimbo maulendo 130. Ndipo kodi buku la Masalmo si limene lili lalikulu pa mabuku 66 a m’Baibulo?

3 Yesu ndi atumwi ake atamaliza kudya Mgonero woyamba wa Ambuye, timaŵerenga kuti anaimba nyimbo zotamanda ndiyeno anapita kumunda wa Getsemani. (Mat. 26:30) Pamalangizo amene mtumwi Paulo anapatsa Akristu ku Kolose, tikhoza kuona kuti mtumwiyu anazindikira kufunika koti Akristu aziimba nyimbo. Iye anati: “Mawu a Kristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha (“kulangizana wina ndi mnzake,” NW) ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo.” (Akol. 3:16) Nyimbo zimene anthu a Yehova amaimba pamisonkhano yawo sikuti zangokhala mawu omveka bwino koma kuti zili ndi zitsanzo za m’Malemba zotamanda Mulungu ndiponso malangizo ofunika. Mwa kuimba mokweza mawu abwino kwambiri a m’nyimbo zimenezi ‘timalangizana wina ndi mnzake,’ osati tokha basi.

4 Kuimba pampingo ndi mbali yofunika kwambiri ya kulambira koyera kwa atumiki achikristu a Yehova ndipo anthu onse opezekapo afunika kuimba nawo ndi mtima wonse. Popeza kuimba ndi mbali ya kulambira Yehova ndiponso njira imodzi imene tingalangizire ena komanso tingadzilangizire tokha, tiyenera kuimba nyimbo mosamala ndi mosonyeza chidwi, monga timachitira ndi pemphero. Pamene pemphero lili m’kati pamsonkhano wa anthu a Yehova, sitiganiza zina kapena kunyamula zinthu zina m’manja, koma timaimirira n’kukhala chete ndi kutchera khutu, kuti maganizo athu onse akhale pa pempherolo. N’chimodzimodzinso ndi nyimbo zathu pamisonkhano yampingo, timaika maganizo athu onse pa nyimboyo mwa kuimba nawo ndi mtima wonse.

5 Chaka chino pamisonkhano yachigawo abale ndi alongo anachita bwino kwambiri pankhani yoimba motsatira nyimbo za pakaseti. Mwachionekere izi zili chonchi chifukwa chakuti abale m’mipingo ina amayamba kuimba madododo asanayimbe mawu ake. M’madera ena ndi kofunikabe kuti mipingo ikhale ndi mbale wotsogolera nyimbo. Mbale ameneyu ayenera kuyesetsa kuzidziŵa bwino nyimbo, komanso liŵiro la nyimbozo, kuti mpingo usamavutike kwenikweni poimba motsatira makaseti pamisonkhano yadera ndi yachigawo.

6 Mpingo ukakhala ulibe makaseti a nyimbo ndipo ulibenso mbale wodziŵa bwino nyimbo amene angatsogolere nyimbo, zomwe ndi zosachitikachitika, akulu amene amachititsa msonkhano angasankhe nyimbo ina imene abale angaimbe bwino, m’malo mwa nyimbo imene anthu sakuidziŵa yotchulidwa mu Nsanja ya Olonda kapena mu Utumiki Wathu wa Ufumu kuti iimbidwe pamsonkhanowo. Ndiyeno ndi bwino kusankhiratu nyimbo ina yogwirizana ndi mfundo ya nyimboyo pa “Chisonyezero cha Nyimbo” kumapeto kwa buku la nyimbo. Mwachitsanzo, ngati nyimbo imene sikudziŵikayo ndi yokamba za ubale, akulu angapeze nyimbo yofanana ndi imeneyo imene abale amaidziŵa pamutu wakuti “Ubale Wachikristu.” Kusintha nyimbo mwa njira imeneyi kuzichitika kamodzikamodzi basi ndiponso pofunikadi kutero ngati palibe mwina mochitira mu mpingo umene abale alibe makaseti a nyimbo ndipo mulibe mbale wotsogolera nyimbo amene amazidziŵa bwino nyimbozo. Mipingo isakhale ndi chizoloŵezi chosintha nyimbo zimene zotchulidwa kuti ziimbidwe pamsonkhano. Cholinga chawo chikhale kuphunzira nyimbo zonse.

7 Chotero, tiyeni tonse tiziimba ndi mtima wonse nyimbo za Ufumu pamisonkhano yathu ya kulambira. Tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova Mulungu amasangalala kumva atumiki ake apadziko lapansi akum’tamanda ndi nyimbo, ndiponso sitingamutamande mokwanira pa zonse zimene watichitira. Choncho tiyeni tisanyalanyaze njira yosonyezera kutamanda ndi kuthokoza imeneyi. Komanso kumbukirani mmene timapindulira poimbira pamodzi nyimbo zotamanda, ngakhale kuti panthaŵiyo tingakhale tisakufuna kuimba. Mwina tingakhale titatopa, koma ngati tiimba nawo mmene tingathere zidzatithandiza kupeza mphamvu mwakuthupi ndi mwauzimu.

8 Ndi bwinonso kukumbukira kuti chofunika si kukula kwa mpingo kapena luso la kuimba. Chofunika ndi kuimba nawo ndi mtima wonse, maganizo athu ali pa zimene tikuimbazo, monga mmene timachitira ndi pemphero. Kuimba kumeneku n’kumene kumatamanda Yehova, komanso kumabweretsa madalitso kwa amene amaimba nawo. Choncho tiyeni titamande Yehova mwa kuimba kwathu, tichite zimenezi mwanjira imene ingapangitse iye kulemekezedwa ndiponso kumene kungatipezetse madalitso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena