Angelo—Nthaŵi Zakale ndi Zamakono
“Iwo amachitiridwa chitsanzo m’nthaŵi za Krisimasi mu zokometsera zomwe timapachika pa mtengo, kapena kuwonekera pa makadi a Krisimasi—zidoli za golidi zokhala ndi nkhope zokongola, kuliza zeze kapena organi ya tchalitchi kapena kunyamula makandulo. Iwo ali ndi mapiko osongoka onga aja a mbalame zazing’ono. Mu liwu limodzi lokha, iwo ali ochenjera.”—The Sunday Denver Post.
“ANGELO amanyalanyazidwa mwachisawawa m’sukulu zophunzirira za chipembedzo, kutchulidwa pang’ono pa sukulu ya Sande, ndipo sakutchulidwa nkomwe mu zolozera za National Catechetical Directory, bukhu lolangiza la maphunziro a chipembedzo Achikatolika mu America.”
Analengeza tero Charles W. Bell, mkonzi wa chipembedzo. Iye anadziwa kuti akatswiri ena ophunzitsa za chipembedzo, makamaka kuchokera ku matchalitchi akulu Achiprotestanti, amadzimva “osakhazikika ndi osatsimikizira ponena za angelo.” New Catholic Encyclopedia yawona kuti olingalira amakono amanena kuti “kukhulupirira konse kwa kukhalapo kwa angelo kufunikira kukanidwa.”
Ichi sichinakhale tero nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, mu zana la 13, ophunzira omwe anaphunzira za ungelo, nthambi ya maphunziro a za chipembedzo ochita ndi angelo, ananenedwa kukhala osangalatsidwa ndi malingaliro onena za “chibadwa, luntha, ndi kudzifunira” kwa angelo. Kwa mazana angapo, mapemphero ankaperekedwa kwa “angelo osunga.” Koma, monga momwe kwadziŵidwira pamwambapo, mkhalidwe wasintha kuyambira pamenepo.
Kulingana ndi New Catholic Encyclopedia, “m’malingaliro amakono angelo . . . akunyalanyazidwa mokulira kumlingo wa kukhala chabe mbiri, kokha nthano, ndi zosangalatsa ana.” Ndithudi, podzafika pakati pa zana la 19, m’malingaliro mwa anthu ambiri angelo anadzakhala ogwirizana mochepera ndi chipembedzo ndipo kuwagwirizanitsa mokulira ndi malingaliro achikondi chakunja. Lerolino, ngakhale anthu ochulukirapo amawalingalira iwo kukhala zotulukapo za kuyerekezera; chotero anthu oterowo amakana kukhalapo kwa angelo.
Angelo mu Zipembedzo Zina
Komabe, angelo adakali ndi malo mu zimpembedzo zina. Mwachitsanzo, tchalitchi cha Roma Katolika “chimalimbikitsa okhulupirika kukonda, kulemekeza, ndi kuitanira pa angelo.” Mchenicheni, Chikatolika chakweza atatu omwe chimawalingalira kukhala angelo—Mikayeli, Gabriyeli, ndi Rafayeli—kukhala oyera. Rafayeli amawonekera kokha mu bukhu la Apocryphal (mabukhu okhala ndi ziphunzitso za Baibulo zokaikiridwa)ndipo osati mu Baibulo lovomerezedwa.
Mu matchalitchi a Eastern Orthodox, angelo ali ofunika mu litany, mtundu wa pemphero mu umene zifunsiro kapena zopempha zimapangidwa ndi kuyankha kwa mpingo. Angelo alinso ndi malo mu Chisilamu, chikhulupiriro mwa angelo kukhala imodzi ya mbali ya chikhulupiriro mu maphunziro achipembedzo Achisilamu.
Chikhalirechobe, palibe kukaikira kuti m’nthaŵi yathu kukhulupirira m’kukhalapo kwa angelo kukuzimiririka.
Kodi Mumakhulupirira mwa Angelo?
Ponena za kukhulupirira mwa angelo, New Catholic Encyclopedia yanena kuti: “Mwapang’onopang’ono . . . m’njira ya kupita patsogolo kwakutali ndi kuyengedwa . . . kupyolera mu ziganizo zogwiriridwapo ntchito za ziphunzitso zopezedwa m’Malemba Oyera, panadzatuluka maphunziro aungelo amene, ndi mlingo wosiyanasiyana wa kutsimikizirika, akhala chiphunzitso cha tchalitchi.” [Kanyenye ngwathu.] Kodi ndi chikhulupiriro cholimba chotani mwa angelo chimene inu mukakhala nacho ngati mukadadziŵa kuti chikhulupiriro chanu chinazikidwa pa “ziganizo zogwiriridwapo ntchito”?
Mokondweretsa, mipatuko ya malingaliro pa nkhaniyi imakhalako ngakhale mkati mwa Tchalitchi cha Chikatolika. Ponena za ndiliti pamene angelo analengedwa, Enciclopedia de la Religión Católica yalongosola kuti: “Mu lingaliro la abambo Achigriki, angelo analengedwa lisanadze dziko lowoneka ndi maso, koma lingaliro la chisawawa la abambo Achilatini liri lakuti iwo analengedwa pambuyo pake. Mosasamala kanthu za icho, lingaliro limene liri ndi ochirikiza ambiri liri lakuti iwo analengedwa pa nthaŵi imodzi ndi dziko.” Kusatsimikizirika koteroko kumapanga chisokonezo m’malingaliro a anthu ndipo kumathandizira kusonkhezera chikhoterero kulinga ku kusakhulupirira lerolino.
Wa nthanthi wa Chiyuda, Philo, anagogomezera kuti angelo anali kokha “zowonekera ndi mphamvu za chilengedwe.” Mkati mwa zaka, ophunzira za chipembedzo akambitsirana nkhani zopanda pake ponena za chilengedwe ndi chizindikiritso cha angelo, zonga ngati funso lopusa lakuti, kodi ndi angelo angati omwe angaimirire pa nsonga ya singano? Kodi chingakhale chodabwitsa kuti anthu ambiri mu mbadwo wathu wamakono asankha kusakhulupirira mwa angelo?
M’chiyang’aniro cha zikhulupiriro zotsutsana zonsezi, nchifukwa ninji osasanthula chimene Baibulo lenilenilo limanena ponena za angelo? Ichi chidzatithandiza kupeza mayankho okhazikika onena za mafunso onga ngati: Kodi angelo ali enieni? Ngati ndi tero, Kodi iwo akhala ndi kale lonse akulowereramo mu zochita za anthu? Ndipo, chofunika koposa, kodi angelo angayambukire moyo wanu?