Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 1/15 tsamba 21-23
  • Kodi Munayamba Mwayanjanapo ndi Gulu la Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Munayamba Mwayanjanapo ndi Gulu la Yehova?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakhumudwitsidwa?
  • Kodi Simunavomerezane Ndi Chiphunzitso?
  • Bwererani Tsopano
  • Athandizeni Kubwerera Mwamsanga
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kulandiridwa Mwachikondi kwa Obwerawo
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • “Yehova, Mulungu Wachifundo ndi Wachisomo”
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Khalani Otetezereka m’Gulu Lolinganizidwa la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 1/15 tsamba 21-23

Kodi Munayamba Mwayanjanapo ndi Gulu la Yehova?

MWAMUNA wachichepereyo anadzimva wamanyazi ndi wokanidwa kotheratu. Zovala zake, zansanza ndi zong’ambika, zinasonyeza zizindikiro zakuti poyamba zinali zovala za kawonekedwe kabwino. Tsopano sizinasiye chikaikiro chakuti iye anali atagwera m’nthaŵi zovuta. Pamene malingaliro ake anabwerera ku dziko lake la kutali, iye anayamba kumva kuipsyidwa kaamba ka moyo wosakaza umene anakhala ndi njira imene iye anawonongera cholowa chimene anaumirira kuchitenga asanakule. Mimba yake ya njala inawonjezera ku kusauka kwake, ndipo iye anakhumba kunyumba. Nkulekelanji, popeza kuti ngakhale akapolo a atate wake kumudzi anali bwino kuposa mmene iye analiri! Eya, ndimotani nanga mmene iye anakondera kukhala m’mkhalidwe wawo!

Koma kodi ndi kulandiridwa kotani kumene iye akayembekezera kuchoka kwa atate wake ngati iye abwererako tsopano? Iye sangayerekeze nkomwe kulonjeredwa motentha kapena ngakhale kuloledwa kulowa m’nyumba pambuyo pa njira yochititsa manyazi imene iye anawonongera kukoma mtima kwa atate wake. Mosasamala kanthu za chimenecho, lingaliro lozama linalamulira maganizo ndi mtima wake: Iye ayenera kupita kunyumba.

Ndi mochepera chotani nanga mmene mwamuna wachichepere ameneyu anamvetsetsera malingaliro a atate wake kaamba ka iye! Ndi chinthu chodabwitsa chotani nanga chimene chinamuyembekezera iye pamene anali kufika pafupi ndi nyumba yake yakale! M’chenicheni, “pakudza iye kutali, atate wake anamuwona, nagwidwa chifundo, namuthamangira, namkupatira pakhosi pake nampsompsonetsa.”​—Luka 15:20.

Mofanana ndi mwana wolowerera, kodi mwachoka kunyumba yanu? Kodi mwatengeka kuchoka kwa Atate wanu, Yehova, ndi gulu lake? Kodi tsopano mumakhumbanso ‘kubwerera kunyumba’?

M’nkhani zambiri, awo amene atengeka kuchoka ku gulu la Yehova sanakhale ofanana kwambiri ndi mwana wolowerera. Kwa ambiri, inali kokha njira ya pang’onopang’ono, yosawona kwambiri, ya kutengeka​—monga bwato laling’ono, lotengeka ndipo pang’onopang’ono likumayandama kupita kutali kuchoka ku mtunda. Ena alemetsedwa koposa ndi mavuto a za chuma kapena mavuto a banja, ndi matenda kapena ngakhale “kupita patsogolo” m’dziko, kotero kuti zinthu zauzimu zatsekerezedwa. Ena adzilola iwo eni kukhumudwitsidwa ndi anthu amene amayanjana ndi mpingo Wachikristu kapena achoka chifukwa chakuti sanavomereze kumvetsetsa kwinakwake kumene gulu la Yehova linali nako pa nsonga ya Malemba. Komabe ena adzilola iwo eni kukhala okhumudwitsidwa ndi kusiya pamene dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu silinathe panthaŵi imene iwo anaiyembekezera.

Ngati inu muli mmodzi wa amene sakuyanjananso mokangalika ndi gulu la Yehova, mwachiwonekere chimodzi kapena zifukwa zambiri za izi zidzagwirizana ndi mkhalidwe wanu. Koma mosasamala kanthu za chochititsa, kodi ino si nthaŵi tsopano ya kulingalira za kubwerera?​—Mateyu 18:12-14.

Kodi Mwakhumudwitsidwa?

Kumalingalira ndi ku utali wotani kumene mtundu wa anthu wagwera kuchoka ku ungwiro, wina angayembekezere kuwombana kwa umunthu kuchitika ku nthaŵi ndi nthaŵi. Ichi chatsogolera kukukhumudwitsa ena. Ena akhumudwitsidwa pamene wina amene anamlemekeza kwambiri mwadzidzidzi achita zinthu m’njira yothamangira kapena m’njira yosakhala ya Chikristu kapena kulowetsedwa m’kachitidwe koipa.

Kodi ichi chachitika kwa inu? Mosasamala kanthu za chimene chinakukhumudwitsani, ndithudi sanali Yehova amene anapangitsa kukhumudwitsako. (Yerekezani ndi Agalatiya 5:7, 8) Chotero kodi palidi nsonga yeniyeni ya kuthetsera unansi wathu ndi iye chifukwa chakuti winawake anachita icho? M’malomwake, kodi ife sitiyenera kupitiriza kumtumikira iye mokhulupirika, tikumakhulupirira kuti Yehova amadziŵa chimene chikuchitika ndipo adzachita ndi ife m’njira ya chikondi?​—Akolose 3:23-25.

Ndi kupita kwanthaŵi, ena apeza kuti chimene poyambirira chinawakhumudwitsa sichikuwoneka kukhala chofunika kwambiri tsopano kapena sichingakhalepo nkomwe. Kapena m’mkhalidwe wodekha wa nkhaniyo, iwo tsopano angafikire mapeto akuti anali iwo amene analakwa. Ichi kaŵirikaŵiri chimakhala chowona pamene munthu sanagwirizane ndipo anakhumudwitsidwa pa uphungu wina kapena chilango chopatsidwa kwa iye. M’kubwereramonso m’zochitika zakale, iye angazindikire kuti chilango chimenecho chinapatsidwa m’chikondi chowona ndi kaamba ka ubwino wake. (Ahebri 12:5-11) Chiri choyenerera chotani, nanga, kugwirira ntchito pa uphungu wa mtumwi Paulo! Iye analemba kuti: “Limbitsani manja anu ogooka, ndi mawondo olobodoka, ndipo yendetsani mapazi anu molunjika. Ndipo mwendo wopunduka sudzapatulidwa, koma udzapezanso mphamvu yake yakale.”​—Ahebri 12:12, 13, The New English Bible.

Kodi Simunavomerezane Ndi Chiphunzitso?

Chingakhale chakuti munasiya gulu la Yehova chifukwa munali ndi kamvetsetsedwe kosiyana pa nsonga ina ya Malemba. Mofanana ndi mmene Aisrayeli opulumutsidwa kuchokera ku Aigupto mwamsanga “anaiwala ntchito [za Mulungu]” m’malo mwawo ndipo “sanayembekeze kaamba ka uphungu wake,” inu mwinamwake mungakhale munamaliza mwamsanga kuti popeza gulu silinayanje kawonedwe kamene munakalingalira kukhala kabwino, mudzathetsa kugwirizana kwanu ndi ilo. (Masalmo 106:13) Mwinamwake nsongayo kuyambira pamenepo inamveketsedwa, kaya mwakusinthidwa kapena kukhazikitsidwanso ndi kufufuza Malemba kopitiriza pansi pa chitsogozo cha mzimu wa Mulungu. Kodi sichikanakhala chabwino kungokhala m’gululo, kuyembekezera pa Yehova?

Chiri chabwino kukumbukira kuti Yehova nthaŵi zonse wagwira ntchito kupyolera mwa gulu limodzi lokha. M’tsiku lathu, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akugawira chakudya chauzimu “panthaŵi yake.” Dziŵani kuti kapolo ameneyu anayenera ‘kupezeka akuchita tero pamene Mbuye wake afika.’ (Mateyu 24:45-47) Ndithudi, ndi ndani lerolino amene amazindikira kuti Mbuyeyo wafika kale? Ndipo kodi ndani amene ali otanganitsidwa ndi ntchito yosonyezedwayo? Kokha awo amene amayanjana ndi gulu la Yehova la mboni za Chikristu!

Pamene ena anamsiya Yesu, mtumwi Petro ananena kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” Petro anadziŵa popanda chikaikiro chirichonse kuti Yesu anali Mesiya. Chotero pamene ophunzira ena anapeza ena a mawu a Yesu kukhala odabwitsa, Petro anazindikira kuti chikakhala chopanda nzeru kusiya magwero a “mawu a moyo wosatha.” M’kupita kwanthaŵi chikaikiro chirichonse kapena kusamvetsetsa kukamveketsedwa. (Yohane 6:51-68; yerekezani ndi Luka 24:27, 32.) Iyi idakali nkhani lerolino, pamene Yehova mopita patsogolo akutsogolera atumiki ake m’njira ya chowonadi.​—Miyambo 4:18.

Bwererani Tsopano

“Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova,” anachonderera tero mneneri Yeremiya. (Maliro 3:40) Komabe, ena angakhale akukaikakaikabe, mwinamwake akumawopa kulandiridwa koipa ndi awo amene ali mu mpingo. Koma kodi nchiyani chimene chinali chivomerezo pamene mwana wolowerera anabwerera kunyumba? “Koma kudayenera kuti tisangalale,” analongosola tateyo, “chifukwa m’ng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo, anataika ndipo wapezeka.” (Luka 15:32) Kulandiridwa kwabwino kofananako kumadikira awo amene ‘abwerera kwa Yehova’ ndi chikhumbo chowona mtima cha kuchita chifuniro chake.​—Yerekezani ndi Luka 15:7.

Koma mpingo Wachikristu siukungokhala chabe ndi kudikira kulandira oterowo pamene asankha ‘kubwerera kunyumba.’ M’fanizo la Yesu, tateyo anathamanga kukumana ndi mwana wake pamene “anali kudza kutali.” Mofananamo, Mboni za Yehova zimachilingalira icho kukhala thayo laumwini kufunafuna awo amene poyamba anayanjana ndi kuwathandiza iwo kubwerera ku gulu la Yehova.

Koma bwanji ngati wina anakhala ndi liwongo la mkhalidwe woipa kwambiri pamene anapatulidwa ku gulu la Yehova? Kapena bwanji ngati wina analetsedwa kuyanjana ndi anthu a Mulungu chifukwa cha choipa chachikulu koma tsopano wasiya kudzilowetsa mu mkhalidwe wosakhalala wachikristu? Akulu adzadziŵa mmene angathandizire iye m’njira yachifundo ndi yachikondi kotero kuti alungamitse zinthu ndi Yehova. Chotero aliyense amene tsopano akukhumba kubwerera ndi kukhala m’chigwirizano ndi chifuno cha Mulungu ayenera kupanga chikhumbo chimenechi kudziŵika kwa akulu. “‘Bwerani, tsono, anthu inu, ndipo lolani tilungamitse zinthu pakati pathu,’ atero Yehova. ‘Ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala.’”​—Yesaya 1:18, NW.

Ndi wachifundo, wokoma mtima, ndi wachikondi chotani nanga Atate wathu wa kumwamba! Ndipo iye ali woleza mtima chotani nanga ndi wokondweretsedwa mwa aliyense wa ife mwaumwini! Ndithudi, iye safuna kuti tiwonongedwe ndi dongosolo loipa la kachitidwe ka zinthu iri. (2 Petro 3:9) Anali Yehova amene anafulumiza anthu ake amakedzana kuti: “Bwererani kwa ine, ndipo ndidzabwerera kwa inu.” Chiitano chimodzimodzicho chidakalipo lerolino.​—Malaki 3:7.

Nthaŵi irinkutha, chotero musachedwe. Limodzi ndi anthu a Yehova, sangalalaninso ndi ‘mtendere wambiri womwe uli ndi awo okonda chilamulo cha Mulungu.’ “Ndipo alibe chokhumudwitsa,” anatero wamasalmo. (Masalmo 119:165) Mkati mwa mtima wanu, kodi mumakonda lamulo la Yehova? Ngati muli mtumiki wodzipereka wa Mulungu, ichi ndicho chifukwa chimene munadziperekera kwa iye. Palibe china chirichonse​—inde, palibe n’chimodzi chomwe​—chimene chingakhale chofunika kuposa kubwezeretsa unansi wathu ndi Yehova. Musamutembenukire iye. Lingalirani za nkhaniyo mosamalitsa ndipo mwapemphero. Ngati mwakhala mukusowa umodzi ndi ubwino wa anthu a Yehova, sikuli kuchedwa kwambiri kubwerera ku gulu la Yehova. Chitani tero mosachedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena