Chifukwa Chimene Ena Asinthira Chipembedzo Chawo
KWA munthu kuti atenge sitepi la mwamsanga chotere monga la kusintha chipembedzo chake, iye motsimikizirika akufunikira kukhala ndi zifukwa zabwino. Mapindu adzafunikira kupambana zophophonya zirizonse.
Kodi mungalingalire za kufuna kudziŵa Mlengi wanu ndi kukulitsa unansi ndi iye kukhala chifukwa chabwino? Chakhala tero kwa ambiri. Kuti tikulitse unansi ndi winawake, tifunikira kumdziŵa munthuyo bwino lomwe. Mwachitsanzo, mwana wachichepere amakhala wa mantha kugwirana dzanja ndi mlendo kufikira atamdziŵa iye. Motero ndi ifenso, timafunikira kumdziŵa Mulungu tisanayambe kumukhulupirira iye. Zowona, zipembedzo zambiri ziri ndi mbali yokulira yomwe zimalambira monga Mulungu. Koma kodi sichirinso chowona kuti kwa anthu ambiri Mulungu sali weniweni ndipo wosakhala pafupi wopanda umunthu wolongosoledwa bwino? Chotero ndimotani mmene tingamudziŵire iye?
Pamene tiyang’ana pa zinthu zotizungulira, timazizwitsidwa ndi zimene timawona. Timawona kukongola, luntha, ndi mphamvu. Chiyambi cha zonsezi chimazizwitsa ambiri, koma pali bukhu limene limalongosola icho momvekera bwino. Ilo liri Baibulo. Kupyolera m’masamba ake, timaphunzira kuti zozizwitsa zimenezi zinayambidwa ndi Mlengi yemwe ali ndi dzina ndi umunthu. Pamene tiphunzira Baibulo mosamalitsa, umunthu wa Mulungu umakhala wowonekera bwino kwambiri kwa ife. Timamuwona iye monga Mulungu wachikondi ndi wosamalira. “Mulungu ndiye chikondi,” limatero Baibulo. (1 Yohane 4:8) Timakokeredwa ku umunthu wodabwitsa umenewu, wolinganizika mwangwiro m’chikondi, nzeru, chilungamo ndi mphamvu. Unansi wathithithi umatsatira.
Misae anapita kokha m’chokumana nacho choterocho cha kukokeredwa kwa Yehova. Iye analongosola kuti: ‘Monga mwana, ndinaphunzitsidwa kuti milungu yambiri inaliko. Panali mulungu wa madzi, mulungu wa mitengo, ndi mmodzi wa nyumba. Ngakhale kuti ndinakaikira kukhalapo kwawo, ndinakhulupirira kuti pafunikira kukhala Mulungu mmodzi wowona. Kaleredwe kanga kosamalitsa ka chiBuddha-Shinto kanandipangitsa ine kulingalira za Mulungu kukhala wowopsya, winawake yemwe anadzetsa chilango kaamba ka kuchita zoipa. Ngakhale kuti ndinali ndi chikhumbo cha kupita ku tchalitchi ndi kuphunzira ponena za Mulungu wa Chikristu, chiyambi changa cha chiBuddha chinandiletsa ine. Kenaka mtsikana anadza kunyumba yanga ndi kudzipereka kuphunzira Baibulo ndi ine. Kupyolera mu phunziro limenelo, ndinaphunzira kuti Mulungu ali ndi dzina, Yehova. Ndinasangalatsidwa kudziŵa kuti sanali Mulungu wowopedwa koma wokonda, wotiyang’anira ife nthaŵi zonse, osati kuti atilange, koma kutithandiza. Ndinafuna kutumikira Mulungu ameneyo, ndipo chotero ndinasintha chipembedzo changa.’ Iye wakhala akusangalala ndi unansi wokhutiritsa ndi Mulungu kwa zaka 29.
Unansi Umene Umapereka Ufulu ndi Chiyembekezo
Pali phindu lapambali lomwe ambiri alandira kupyolera mu kukulitsa unansi ndi Mulungu. Pamene maunansi ena ayamba kuchepetsa kufunika kwake mu miyoyo yawo, ambiri apeza ufulu kuchokera ku ukapolo wa mantha a munthu ndi miyambo yotsendereza yopanda tanthauzo lenileni ndi phindu. Chotero, iwo atulutsidwa ku zotaika zolemetsa za kusungirira kawonekedwe ndi miyambo, yomwe imasunga mabanja ambiri mu ngongole zokhazikika. “Kuwopa anthu kutchera msampha,” limachenjeza tero Baibulo, likumawonjezera chitsimikiziro chakuti, “Koma okhulupirira Yehova adzapulumuka.”—Miyambo 29:25.
Ufulu wina wopezedwa uli ufulu wa kuwopa imfa. Misae wogwidwa mawu pamwambapo wanena kuti: “Pamene ndinali wa zaka 22, ndinayambukiridwa ndi malungo a typhoid. Pamene ndinali pansi pamenepo wokomoka, ndinamva mabwenzi ndi ziwalo za banja akulankhula ponena za ine monga ngati ankandiyembekezera kufa. Koma ndinkawopa imfa. Lingaliro langa lokha linali lakuti ndifuna kukhala ndi moyo, ndipo mwamwaŵi ndinachira. Kupyolera mu phunziro langa la pambuyo pake la Baibulo, ndinamasulidwa ku mantha amenewa a imfa. Ndinaphunzira kuti imfa iri kokha kusakhalapo.” Baibulo limanena kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5, 10) Ngati winawake wafa, pali chiyembekezo chabwino kwambiri cha kuwukitsidwa chifukwa chakuti Mulungu amasunga akufa kukhala amoyo m’chikumbukiro chake.—Yohane 5:28, 29.
Ambiri ena omwe amaphunzira Baibulo mofananamo apeza kuti zinthu zimene aphunzira zapatsa moyo wawo tanthauzo lenileni ndi chiyembekezo. Ichi ndi chifukwa chimodzi chimene Baibulo linalembedwera, kuti “tikakhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Chibuddha sichimaphunzitsa chirichonse ponena za Mlengi kapena Mulungu. Chanenedwa kuti kuipa ndi kuvutika kumakhalapo kwa nthaŵi zonse ndipo kudzapitirizabe kosatha kupyola mu zungulirezungulire wosatha wa kubadwanso. Zipembedzo zambiri za Kumadzulo zimaphunzitsa kuti abwino adzapita kumwamba, malo osatha, koma ponena za chimene adzachita kumeneko, iwo sali otsimikiza kwenikweni. Mosiyana ndi nthanthi za chipembedzo zimenezi zimene zimapatsa chiyembekezo chochepera kapena tanthauzo ku miyoyo yawo, Baibulo limaphunzitsa kuti munthu anapangidwira kusangalala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi monga wolisamalira. (Genesis 2:15-17; Yesaya 45:18) Ife chotero tingakhoze kuzindikira kuti moyo ufunikira kuwonongedwa osati kokha m’kusonkhanitsa chuma ndi kutumikira mwini komanso kutumikira Mulungu ndi ena m’njira yopanda dyera.—Mlaliki 12:13; Mateyu 22:37-39.
Kupeza Chowonadi ndi Mabwenzi Owona
Ena akakamizika kusintha chipembedzo chawo kaamba ka zifukwa zina. Pakati pa izo pali chikhumbo cha kufunafuna chowonadi cha chipembedzo. Ndithudi, anthu ambiri amadzimva kuti palibe chinthu choterocho chonga chowonadi chenicheni ndipo, monga mmene Baibulo limanenera, ‘safunsira.’—Masalmo 10:4.
Koma pali aja omwe amapanga kufunsira koteroko. Sakae, yemwe amakhala cha pakati pa Japan, anapita kuchokera ku mpatuko wa chiBuddha wina ndi unzake kwa zaka 25 kuti apeze chowonadi. Iye sanali wokhutiritsidwa ndi pang’ono pomwe. Pamene anakwera ku malo a thayo m’gulu lirilonse, iye nthaŵi zonse anawona zinthu zomwe zinamukhumudwitsa, zonga ngati kuchita malonda, chisembwere, ndi kudyerana masuku pamutu. Iye anakhoza ngakhale kupita ku India kukafunafuna maziko a chiBuddha a mbiri yakale kumene a Buddha anakhala ndi kuphunzitsidwa. Iye anagwiritsidwa mwala mokulira kupeza zikondwerero zochepera mu chiBuddha m’dziko la chiHindu limeneli. Kenaka m’kukambitsirana kwake ndi Mboni za Yehova, iye anawuzidwa kuti si zipembedzo zonse zomwe zimachokera kwa Mulungu koma ziri zochokera kwa mdani wake, Satana Mdyerekezi.—1 Akorinto 10:20.
Ichi chinazizwitsa Sakae, koma chinampangitsa iye kulingalira ndi kufufuza. Iye anaŵerenga bukhu lakuti What Has Religion Done for Mankind?a ndi zofalitsidwa zina za Baibulo. Iye anayamba kuwona kuti pamene kuli kwakuti chiBuddha, monga mmene chinachitidwira mu Japan, chinapita kupyola masinthidwe ambiri mkati mwa zaka, Baibulo lakhala losasinthidwa kwa zaka mazana angapo. Potsirizira pake kufufuza kwake kunakhala kophula kanthu. Iye anapeza chowonadi chomwe ankachifunafuna. Chimwemwe chake chinali chonga chimwemwe cha munthu m’fanizo la Yesu yemwe anapeza chuma chobisika m’munda: “M’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.”—Mateyu 13:44.
Awo omwe apeza chowonadi cha chipembedzo amasonyeza “kuchitirana chifundo” kaamba ka ena omwe akuchifuna icho. (1 Petro 3:8) M’chenicheni, kutentha kwawo ndi chikondi chenicheni poyambirirapo chimakokera ambiri ku phunziro la Baibulo. “Adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake,” anatero Yesu. (Yohane 13:35) Kodi ndi kuti kumene tingapeze mkhalidwe wa chikondi woterewo lerolino? Kazuhiko Nagoya, akumalemba m’danga lake la Daily Yomiuri ya ku Tokyo, anachitira ndemanga pa njira yotentha imene iye anachitidwira pamene anachezera malo osonkhanira a Mboni za Yehova. “Njira mu imene amwetulira,” anatero Nagoya, “chinawoneka monga ngati kuti anandidziŵa ine pa msonkhano wa papitapo ndipo anali achimwemwe kundiwonanso.” Koma ichi sichinali tero. “Ndinayang’anitsitsa pa nkhope zawo ndipo ndinapeza kuti iwo anali alendo kotheratu.” Pamene anthu ena aŵiri anamwetulira, “Ndinadzimva wachimwemwe kwambiri,” akukumbukira Nagoya. “Imeneyo ndi njira imene anthuwo amamwetulira kwa mlendo, pamene amuwona pa iriyonse ya misonkhano yawo.”
Kutentha ndi chikondi sizimatuluka kuchokera ku kudziŵana kwa anthu wina ndi mnzake bwino lomwe chifukwa cha kusonkhana pamodzi pa maziko okhazikika. M’malomwake, izi zimatulukapo kuchokera ku kuphunzira Baibulo kokhazikika ndi kugwiritsira ntchito malamulo ake m’miyoyo yawo. Anthu ambiri oitanidwa kukapezeka ku Msonkhano Wachigawo wa “Osunga Umphumphu” wa mu 1985-86 wa Mboni za Yehova m’maiko achilendo anakhudzidwa mozama ndi chikondi ndi kuolowa manja kosonyezedwa kwa iwo ndi owaitanawo. Okwatirana achichepere ochokera ku Japan omwe anapezeka pa msonkhano mu Philippines anachitira ndemanga kuti: “Pamene tonsefe tigwirizana pamodzi kaamba ka nyimbo yothera, aliyense akumaimba m’chinenero chake, tinayambukiridwa mokulira. Tinamva nthaŵi yoyamba chimene chimatanthauza kukhala mbali ya ubale wa mitundu yonse mowonadi.”
Potsirizira, ambiri adzakuuzani inu za kusintha kokulira kumene ayenera kupanga m’miyoyo yawo monga chotulukapo cha kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsira ntchito ilo. Anthu okhala ndi maumunthu osiyana kumbuyoko monga mmene nkhosa ziriri zosiyana ndi mimbulu akukhalira limodzi mwamtendere m’nyumba zosonkhanira Zachikristu. (Yesaya 11:6) Ena anali oipa ndi opanda ubwenzi, okwiya msanga ndipo ngakhale owopsya. Ena anali ndi mavuto ndi kupsyinjika. Ndiponso ena anali aliwuma ndi odzitukumula. Ena anali ndi zizoloŵezi zoipa zofunikira kuzilaka. Koma ndi kuyesayesa kwamphamvu, limodzi ndi chikhumbo cha kufuna kukondweretsa Mulungu, iwo anali okhoza kupanga masinthidwe mwamsanga.
Bwanji ponena za inu? Kodi chirichonse cha zifukwa zomwe ziri pamwambazo zopangira masinthidwe zikukukhudzani inu? Ngati ndi tero, tikulimbikitsani kupanga kuphunzira kosamalitsa kwa Baibulo. Baibulo limasonyeza kuti zipembedzo za bodza zonse ziri pa njira yowombana ndi Mulungu wa Baibulo. Monga woyendetsa ndege wotchulidwa m’nkhani yapitayo, inu mungafune kupanga kasinthidwe ka mwamsanga kupulumutsa moyo wanu ndi miyoyo ya okondedwa anu. “Chipata chiri chachikulu ndi njira ya kumuka nayo ku kuwonongeka iri yotakata,” anatero Yesu, “ndipo ali ambiri amene alowa pa icho; pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo ya kumuka nayo kumoyo.” (Mateyu 7:13, 14) Inde, ngati mukuyenda pa njira imeneyo “yaikulu,” pali chifukwa chabwino cha kusinthira chipembedzo chanu!
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 5]
Kuleledwa kwanga kosamalitsa kwa chiBuddha-Shinto kunandipangitsa ine kulingalira za Mulungu monga wowopsya
[Chithunzi patsamba 7]
‘Ichepetsa njirayo ya kunka nayo kumoyo’