Ripoti la Olengeza Ufumu
Chowonadi cha Ufumu Chiphuka mu Sri Lanka
SRI LANKA, kutanthauza “Dziko Lowala,” liri dzina lakale lobwezeretsedwa ku chisumbu chokondeka chimenechi lodziŵikabe kwa ambiri ndi dzina lake la olamulira akale, “Ceylon.” Chifukwa cha kukhala kwake m’Nyanja ya India, imatchedwanso kuti Misozi ya India; koma misozi yonse sinakhale ija ya chisangalalo popeza m’nthawi za posachedwapa chiwawa cha magulu a fuko chabuka, chikumapanga mitu ya nkhani kuzungulira dziko lonse.
Komabe, kuno nakonso chowonadi cha Ufumu chikuphuka. Abuddha, Ahindu, Asilamu, Aparsi, ndi Akristu wamba akuphunzitsidwa kuti kokha Ufumu wa Yehova mwa Kristu Yesu ungabweretse kuchiritsa kosatha ku mabala a ufuko ndi andale zadziko ogawanitsa midzi. Chokumana nacho chotsatirachi chimasonyeza kuphuka kwa chowonadi cha Ufumu “M’dziko Lowala” limeneli.
◻ Salimoon analeredwa akumakhulupirira kuti Qurʼan ali Mawu a Mulungu. Koma iye sanakhoze kuvomereza kotheratu kuti Mulungu wachifundo chonse angakhoze kuzunza anthu m’helo wotentha. Tsiku lina Mboni za Yehova zinamuitana iye ku msonkhano. Akumazindikira chowonadi mwamsanga, iye sanalefukepo, ndipo iye tsopano akutumikira mwachimwemwe monga mkulu mu mpingo Wachikristu.
◻ Harry, m’Buddha wa nthaŵi yaitali yemwe wasonyeza chikhulupiriro cha chipembedzo chake mwa kuyenda pa makala otentha, anali wosakhoza kutsatira malamulo opezeka m’chiphunzitso cha chiBuddha cha njira ya mbali zisanu ndi zitatu: (1) kumvetsetsa kolondola; (2) malingaliro olondola; (3) malankhulidwe olondola; (4) kachitidwe kolondola; (5) umoyo wolondola; (6) kuyesayesa kolondola; (7) kulingalira kolondola; ndi (8) kusumika kolondola. Izi zifunikira kudzaza mbali iriyonse ya moyo wa munthu. Ngakhale kuti anadzilingalira iyemwini kukhala m’Buddha wabwino, kusutsa fodya kwake, kumwa, ndi mikhalidwe ina yoipa inapanga mavuto ndi banja lake. Potsirizira pake, iye anagamulapo kuphunzira Baibulo. Komabe, palibe aliyense yemwe anadzipereka kuphunzira ndi iye. Iye anamva kuti Mboni za Yehova zingakhale zofunitsitsa, chotero iye anapezeka pa msonkhano pa Nyumba ya Ufumu, ndipo phunziro linakonzekeretsedwa. Mmodzi wa Mboni wa chiyambi cha Chisilamu anamthandiza iye kuphunzira chimene Baibulo limaphunzitsa. Tsopano, potsirizira pake, wapeza mphamvu kuchokera kwa Yehova ya kutsatira mopita patsogolo njira ya malamulo abwino. Iye akusangalala kutumikira monga mtumiki wotumikira ndipo akupanga makonzedwe akulowa mu utumiki wa upainiya.
Chotero chowonadi cha Ufumu chikuphuka mu Sri Lanka, ndipo tsopano pali Mboni 1,086 m’dziko lokongolali. Kufutukuka kumeneku kumatanthauza kuti ziwiya zokulira za nthambi zikufunika, ndipo malo kaamba ka ichi akufufuzidwa. Abale akumanganso Nyumba za Ufumu zatsopano. Mu Puttalam mpingo wokhala ndi mabanja khumi unagamulapo kumanga Nyumba ya Ufumu ndi kuimanga iyo yokulira mokwanira kugwiritsira ntchito kaamba ka msonkhano wadera. Nyumbayo inatsirizidwa m’nthaŵi yake kaamba ka msonkhano wadera, kumene 107 anapezekako. Tsopano mpingowo wachuluka chifupifupi kuwirikiza kaŵiri, wokhala ndi opezekapo oposa pa 75 pa msonkhano wochitidwa ponse paŵiri mu Tamil ndi Sinhalese. Ndiponso pali chonde chokulira kaamba ka kukula kowonjezereka.
Maulosi a Baibulo okwaniritsidwa amaloza ku chenicheni chakuti mwamsanga kwenikweni misozi iriyonse ya chisoni idzapukutidwa kuchoka m’maso onse monga mmene Mulungu walonjezera. Ngakhale malingaliro a chiwawa cha ufuko sadzabweranso kumtima. (Chivumbulutso 21:4; Yesaya 65:17) Ndipo mu “misozi” yokondeka ya chisumbuchi, misozi ya chimwemwe idzatulutsidwa pamene chiyambukiro cha zipatso za mtendere za Ufumu wa Mulungu zipitiriza kusangalalidwa ku nthaŵi zosatha.