Kodi Mukanena Chiyani kwa Mbuda?
1 M’mayiko ena anthu oposa theka la anthu amene akubatizidwa ndi Abuda. Kodi n’chiyani chimene chikukopera anthu amenewa ku choonadi? Mungalalikire bwanji uthenga wabwino kwa Mbuda?
2 Sonyezani Nkhaŵa Yeniyeni: Ambiri amene kale anali Abuda anena kuti si kuya kwa chidziŵitso komwe kunawakopera ku choonadi. Komano, anakhudzidwa ndi nkhaŵa yeniyeni imene inasonyezedwa kwa iwo. Mmwenye wina wamkazi amene akukhala ku United States anachita chidwi kwambiri ndi ubwenzi wa mlongo wina amene anam’fikira moti anavomera zoti aziphunzira naye. Mkaziyu sankalankhula bwino Chingelezi, koma mlongoyo anali woleza. Pamene mkaziyu watopa kapena kuti saphunzira, mlongoyo amangobwera ndi kucheza naye kenako n’kupangana za phunziro la ulendo wotsatira. Pomalizira pake, mkaziyu, ana ake aamuna aŵiri, ndi mayi ake okalamba anabatizidwa. Anabwerera kudziko la kwawo ndipo anathandiza ambiri kuphunzira choonadi. Mmodzi mwa ana ake aamuna akutumikira pa ofesi ya nthambi. Si dalitso lake limene linadza mwa kusonyeza “kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu” zimene Yehova amasonyeza.—Tito 3:4.
3 Zimene Abuda Amakhulupirira: Abuda ambiri amalolera zikhulupiriro za ena, koma samakuona kukhala kofunika kutsatira chiphunzitso chapaderadera. Choncho zokhulupirira za aliyense payekha zimasiyanasiyana. Koma nkhani yofala pa chiphunzitso china cha Abuda ndi yakuti moyo ndi wodzaza ndi mavuto okhaokha, koma mwa kugonjetsa zilakolako ndi kuipa, munthu angathetse mchitidwe womapitirira wobadwanso komanso moyo wosasangalatsa. Amati, kuti munthu amasulidwe ku mchitidwe umenewu, ayenera kuloŵa m’Nirvana, mkhalidwe umene sungafotokozedwe chifukwa si malo kapena chochitika koma, malere komwe kulibe zopweteka ndi zoipa. Kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti kukambirana ndi anthu za filosofi ya Abuda n’kopanda phindu. M’malo mwake, kambiranani mavuto amene amakhudza tonse.
4 Gogomezerani Zimene Zimakhudza Tonse: Popeza Abuda amaona moyo wapadziko pano kuti n’kuvutika, lingaliro la moyo wosatha padziko lapansi lingakhale lopanda pake. Komabe, tonsefe timakhumba kusangalala ndi moyo wabanja wachimwemwe, kuona kuvutika kutachotsedwa, ndi kudziŵa tanthauzo la moyo. Onani mmene mungagogomezere zimene zimatikhudza tonsefe.
5 Mungayese mawu oyamba awa:
◼ “Lerolino tikukhala m’dziko limene anthu ambiri osalakwa akuvutika. Kodi mumakhulupirira kuti pafunika chiyani kuti zopweteka ndi mavuto zithe kwa onse? [Yembekezerani yankho.] Pali lonjezo lakale kwambiri limene limanditonthoza zedi. [Werengani Chivumbulutso 21:4.] N’zoona, nthaŵi imeneyo sinafike, koma ikadzafika, tidzafuna kuona, kodi si choncho?” Ndiyeno gaŵirani buku limene limafotokoza mmene kuvutika kudzathera.
6 Kwa munthu wachikulire, munganene kuti:
◼ “Mwinamwake muli ndi nkhaŵa ngati ine chifukwa cha kuwonjezereka kwa malingaliro oipa amene alipowa komanso mmene akukhudzira ana athu. N’chifukwa chiyani chisembwere chikuwonjezereka pa achinyamata? [Yembekezerani yankho.] Kodi mukudziŵa kuti zimenezi zinanenedweratu m’buku limene linalembedwa kale kwambiri zipembedzo za Chisilamu, Chikristu, ndi Chihindu kulibe? [Werengani 2 Timoteo 3:1-3.] Onani kuti mikhalidwe imeneyi ikupitirira mosasamala kanthu za kuwonjezereka kwa maphunziro. [Werengani vesi 7.] Buku ili linandithandiza kumvetsa choonadi chimene anthu ambiri sanaphunzirepo. Kodi mungakonde kuliŵerenga?” Gaŵirani buku kapena bolosha loyenerera.
7 Abuda amalemekeza Baibulo monga malembo opatulika. Choncho ŵerengani mmenemo mwachindunji. (Aheb. 4:12) Ngati munthuyo akuopa kutengera chikhalidwe cha Kumadzulo, muuzeni kuti olemba Baibulo onse anali a ku Asia.
8 ndi Zofalitsa Ziti Zimene Zimagwira Ntchito Kwambiri? Ofalitsa ambiri agwiritsa ntchito bwino mabuku otsatirawa: buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene amathandiza; komanso bolosha la“Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” ndi Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?; ndiponso ngati udakalipo, Uthenga wa Ufumu Na. 35, Kodi Anthu Onse Adzakondanapo? Abuda ambiri amene tsopano akuphunzira choonadi choyamba amaphunzira bolosha la Mulungu Amafunanji ndiyeno kenako buku la Chidziŵitso.
9 Ngakhale amati amishonale achibuda anafika ku Atene kale kwambiri zaka pafupifupi 400 Paulo asanalalikireko, sizidziŵika ngati anakumanako ndi munthu wamaganizo achibuda. Komabe, tikudziŵa mmene Paulo anamvera ponena za kuchitira umboni kwa anthu amitundu yonse. Anadziloŵetsa yekha “ukapolo kwa onse” kuti ‘paliponse akapulumutse ena.’ (1 Akor. 9:19-23) Pochitira umboni kwa aliyense amene tikumana naye, tingachite chimodzimodzi mwa kusonyeza chidwi mwa anthu komanso kugogomezera zinthu zimene tonsefe timafuna.