Lipoti la Olengeza Ufumu
“Lemba Lirilonse Adaliŵerenga Linandigwira Mtima”
“MAWU a Mulungu ali amoyo ndipo amapereka mphamvu,” anatero mtumwi Paulo. (Ahebri 4:12, NW) Izi zinatsimikizira kukhala zowona m’moyo wa mkazi wa ku Vietnam yemwe analeredwa monga Mbuda. Nayi nkhani yake.
“Makolo anga, omwe akadali m’Vietnam, ali Abuda mwadzina lokha, chotero ndinaleredwa monga Mbuda kufikira ukwati wanga pamsinkhu wazaka 22. Banja la mwamuna wanga linayesayesa kundikakamiza kubatizidwa m’Tchalitchi cha Katolika. Iwo anati apongozi anga aakazi omwe anafa ankalepheretsedwa kupita kumwamba chifukwa chakuti ndinali Mbuda! Poyamba ndinakana kuchita tero, koma pambuyo pake ndinabatizidwa kotero kuti ndiwakondweretse. Komabe, pansi pamtima wanga, ndinakumva kukhala kupusa chifukwa chakuti ndinada chinyengo cha m’Tchalitchi cha Katolika. Sichinasiyane ndi chipembedzo cha Chibuda. Nachonso chinali chodziloŵetsa m’nkhondo ndi ndale zadziko, ndipo zipembedzo zonse ziŵirizo zinalimbikitsa kulambira makolo akufa.
“Ngati nkadakhala m’Vietnam, nkadakhala ndi mwaŵi wochepa kwambiri wakuphunzira chowonadi. Ndinakula panthaŵi imene mgwedegwede wandale zadziko unadutsa Kum’mwera kwa Vietnam, ndipo ndinkakhala m’tauni yokhala pamtunda wautali kuchokera ku Saigon. Chotero linali dalitso kukhala wokhoza kuthaŵira ku Australia.
“Ndinali mmodzi wa anthu okhala ndi mwaŵi pa bwato. Ndimwana wanga wa miyezi iŵiri yakubadwa ali m’manja, ndinafunikira kuthamanga mumdima kuthaŵa apolisi ndikukakwera bwato laling’ono losodzera. Pambuyo pa masiku asanu ndi aŵiri panyanja, tinafika m’Malaysia, kumene tinakhala kwa miyezi yoŵerengeka mumsasa wa othaŵa kwawo tisanapite ku Australia.
“Pambuyo pa zaka ziŵiri ndi theka mu Australia, ndinafikiridwa ndi Mboni za Yehova ziri muutumiki wawo wa kunyumba ndi nyumba. Pakundifikira koyamba, ndinalandira phunziro Labaibulo lokhazikika chifukwa chakuti ndinaliwona kukhala mwaŵi wophunzirira Chingelezi. Koma khalidwe la Mboni imene inandipeza ndi chowonadi chimene inandiphunzitsa linandisangalatsa kwabasi. Lemba lirilonse adaliŵerenga linandigwira mtima, ndipo sindinawone chinyengo chirichonse m’gulu la Yehova. Pambuyo pophunzira Baibulo kwa chaka chimodzi ndi theka, ndinapereka moyo wanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa.
“Ndiyenera kunena kuti chowonadi chasinthiratu kawonedwe kanga ka moyo. Mwamuna wanga ngwosakhulupirira, koma Yehova wandithandiza ndikundichirikiza, pamodzi ndi banja langa laling’ono. Iye wakhala Mlangizi wanga Wamkulu ndipo wandiphunzitsa kukhala mkazi ndi mayi wabwinopo. Ndipitirizabe kumthokoza Yehova kuti wandithandiza kuwonjoka mumdima wauzimu ndikundiloŵetsa m’kuunika kwa chowonadi cha Baibulo.”
Zowonadi, Mawu a Mulungu ouziridwa anapereka mphamvu kotheratu m’chochitikachi. Kumaliphunzira Baibulo ndikugwiritsira ntchito zophunziridwazo kumapereka tanthauzo ndi chifuno m’moyo ndikutsogolera ku moyo wamuyaya m’dziko latsopano la Mulungu. Monga momwe Mulungu anauzirira Mose kunena kuti, ‘Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.’—Deuteronomo 32:47.