Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/1 tsamba 15
  • Mbiri Yabwino ya Ufumu Kuchokera Kunsi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbiri Yabwino ya Ufumu Kuchokera Kunsi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wothaŵa wa ku Vietnam
  • Munthu wa Chiaborigine Avomereza ku Chowonadi
  • Kutumiza Lamya kwa Ngozi
  • Kuvomereza Mbiri Yabwino m’Belgium
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • “Lemba Lirilonse Adaliŵerenga Linandigwira Mtima”
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Yehova Ali Wolimba Kuposa Adani Ake
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/1 tsamba 15

Ripoti la Olengeza Ufumu

Mbiri Yabwino ya Ufumu Kuchokera Kunsi

MOFANANA ndi m’maiko ena 211, mbiri yabwino ya Ufumu ikulengezedwa mwachangu ndi Mboni za Yehova cha kunsi mu Australia. Mboni zoposa 49,000 kumeneko zikusangalala ndi madalitso olemera. Anthu ambiri a mitundu yosiyanasiyana asamukira kumeneko mkati mwa zaka, kotero kuti tsopano mipingo 58 ya mafuko imachitira ripoti utumiki wa m’munda. Zokumana nazo zolimbikitsa zalongosoledwa ndi ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society.

Wothaŵa wa ku Vietnam

Wothaŵa wa ku Vietnam, yemwe tsopano akukhala mu Australia, anakula ndi kulambira makolo, Chikonfyushani, ndi Chibuda, limodzinso ndi nthanthi za Kum’mawa ndi Kumadzulo. Kufikira 1975 iye anali msilikali m’gulu lankhondo la ku South Vietnam. Mu 1979 iye anayenera kudulitsa mkono wake wa kumanzere chifukwa cha chotupa pa mfundo ya dzanja lake. Akumafuna ufulu, iye anathaŵa mu Vietnam mu 1983, limodzi ndi anthu ena 24, pa bwato laling’ono. Pambuyo pa chokumana nacho chochititsa mantha ndi mbala za pa nyanja, bwato lawo linayenda mopanda chifuno m’Nyanja ya South China kwa masiku otentha asanu ndi limodzi, kufikira pomalizira pake anafika ku Malaysia. Pambuyo pa kutha miyezi isanu mu msasa wothaŵirako, iye analoledwa kuloŵa mu Australia. Miyezi itatu pambuyo pake iye anagwirizana ndi chowonadi. Mawu a Yesu pa Yohane 8:32 anayankha kufunafuna kwake kozama kaamba ka ufulu: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” Abalewo anamusonyeza iye chikondi chochulukira. Lerolino iye ali Mboni ya Yehova ndipo ali chiwiya chogwiritsiridwa ntchito m’kuthandiza anthu ena ambiri olankhula chinenero cha ku Vietnam kuphunzira chowonadi chimene chimamasula wina.

Munthu wa Chiaborigine Avomereza ku Chowonadi

Kumpoto cha kumadzulo kwa Australia mbale wachipainiya wachichepere ndi mnzake anafikira mkazi wa Chiaborigine m’gawo la fuko lotchedwa woolshed. Pambuyo pa kumva chifukwa chimene iwo anafikira, mkaziyo anatenga mfungulo kuchokera m’khosi lake ndi kutsegula bokosi lalikulu lachitsulo. Zochulukira ku kudabwitsidwa kwawo, iwo anawona mkati pakati pa zinthu zake zochepera mabroshuwa aŵiri a Watch Tower ndi kope lakale la Baibulo. Atakhala pansi, iwo anali okhoza kuyambitsa phunziro kugwiritsira ntchito imodzi ya mabroshuwawo. Ngakhale kuti mkaziyo sanakhoze kuŵerenga kapena kulemba, iye mowonadi anawona kukhala a mtengo wake mabroshuwa amene anawapeza papitapo. Phunziro lokhazikika likutsogozedwa tsopano, ku chikondwerero chake.

Kutumiza Lamya kwa Ngozi

Mu mzinda wa Sydney, ndi chiŵerengero cha anthu cha mamiliyoni atatu, mtsikana wachichepere wa msinkhu wa zaka zitatu anali kuseŵera ndi lamya ndipo anali kuzingulutsa manambala mwa apa ndi apo. Nambalayo inachitika kukhala ija ya Mboni. Mlongo anayankha, ndipo poyamba iye analingalira kuti woitanayo anali mdzukulu wake. Kenaka iye anamva liwu la wachikulire. Ilo linali la amayi wa mtsikana wachichepereyo, yemwe anapepesa kaamba ka mwana wake wamkazi. Kukambitsirana kunayambika, mkati mwa mmene mlongo wathu anapereka umboni. Mkaziyo anafuula kuti: “Ndinali kuyembekeza kuti Mboni zikabwera ku khomo langa kachiŵirinso. Ndikufuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova!” Iye anapitiriza kunena kuti kokha miyezi iŵiri yapitayo, iye anali atachezera Peru ndipo anakondweretsedwa ndi azakhali ake ndi banja omwe anali Mboni za Yehova. Iye ananena kuti: “Ana a achibale anga anali adyerekezi aang’ono, koma tsopano iwo ali angelo aang’ono!” Makonzedwe anapangidwa kaamba ka phunziro la Baibulo, ndipo mkazi wokondweretsedwayo akupitirizabe kupanga kupita patsogolo kwabwino​—zonsezo chifukwa cha kuitanira pa lamya kwangozi kopangidwa ndi mtsikana wake wachichepere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena