Kupeza Chigwirizano Chaufuko mu South Africa Yovutitsidwa
Monga momwe yasimbidwira ndi Merlyn Mehl
INE ndine wa ku South Africa, kapena, monga zimalongosoledwera mofala m’dziko lino, nzika ya mu South Africa mwa mtundu. Ndinenso profesa pa Yunivesiti ya Western Cape, yunivesiti yaikulu koposa ya anthu akuda m’dzikoli. Ndiri ndi ukatswiri m’maphunziro a physics (sayansi ya zopangapanga zocholowanacholowana). Kwa zaka 20 zapitazo, ndakhalanso mmodzi wa Mboni za Yehova. Chotero ndi uti wa mikhalidwe iŵiri imeneyi wandithandiza ine kukumana ndi chigwirizano chaufuko m’dziko limeneli la kupikisana ndi kukangana?
Kukulira mu South Africa
Cape Town, kothera kwenikweni kwa kum’mwera kwa Africa, yalongosoledwa kukhala ‘Cape [Nsonga ya dziko] yabwino koposa m’dziko lonse lapansi.’ Kuyang’ana pa nyenyezi pa usiku wowala mu Cape Town kuli chokumana nacho chochititsa chidwi. Nthaŵi ina, pamene ndinkachita tero, ndikumbukira kukhala ndikunena kwa bwenzi kuti: “Kodi ndi nsonga yanji ya zonsezi? Ndithudi chiyenera kutanthauza chinachake; komabe, pansi pano zinthu ziri zopanda pake kwenikweni. Ndimotani mmene anthu angadzipatulana mokulira chotero motsutsana ndi ena? Nchifukwa ninji zinthu ziri zoipa chotero?”
Kubadwira mu South Africa kulinso kukhala wozindikira za kupatulana pa msinkhu wauchichepere. Mavuto afuko akuwoneka kukhala paliponse nthaŵi zonse. Kuyambira ku msinkhu woyambirira wauchichepere, anthu amakhala olekanitsidwa ndi ozindikiritsidwa ndi fuko. Banja lathu limazindikiritsidwa kukhala “akaladi” ndi malamulo a ku South Africa. Monga ana, ife tinaphunzitsidwa kuti oyera anali opondereza pamene ife tinali pakati pa oponderezedwa. Ndipo popeza kuti, pamene tinali kukula, kuyanjana kwa mafuko pa sukulu kapena mwamayanjano panaliberetu, chiri chomvetsetseka kuti anthu a fuko lina anali kuwonedwa ndi chikaikiro. Kwa ife chinawoneka kuti oyera anali ndi zabwino za chinthu chirichonse—kuphatikizapo nyumba, zogwiritsira ntchito, ndi sukulu. “Apartheid” (tsankho la khungu), kulekanitsidwa kwa lamulo kwa mafuko, linadzakhala liwu lodedwa koposa mu mpambo wathu wa mawu.
Ndisanamalize sukulu ya pulaimale, banja lathu linakakamizika kuchoka m’nyumba mu unansi wosanganizana mwa ufuko kumene mlongo wanga ndi ine tinabadwira. Chifukwa ninji? Chifukwa cha Lamulo la Malo a Gulu, lomwe linalola malo olunjikitsidwa kulinganizidwa kaamba ka gulu la fuko limodzi lokha. Tinasamukira ku malo ena, komwe tinakhala kwa zaka zoŵerengeka kufikira analengezedwanso kukhala “malo a oyera.” Kenaka, tinasamukanso.
Chifukwa cha kusalongosoka kotsimikizirika, makolo anga limodzinso ndi aphunzitsi athu anatisonkhezera kuphunzira zolimba pa sukulu. Uthengawo unali wakuti, “Inu muyenera kumusonyeza munthu woyera kuti muli abwinopo kuposa iye.” Ichi chinayambukira mkhalidwe wanga kulinga ku sukulu. Ngakhale kuti ndinali wamanyazi kwambiri, ndinakonda kuphunzira. Kuŵerenga chirichonse ndi zirizonse kunatenga nthaŵi yanga yochulukira. Chotero, ndinamaliza sukulu ndikukhala pakati pa ophunzira apamwamba m’dzikolo. Chotero chinali chachibadwa kuti ndinayenera kupita ku yunivesiti. Chifukwa chakuti ndinakonda sayansi ndi masamu, chinali chopepuka kugamulapo kumenyera digiri mu sayansi, ndi physics limodzi ndi masamu monga maphunziro aakulu.
Chiyambire 1960 (chaka chenicheni chomwe ndinayamba pa yunivesiti) Lamulo la Mayunivesiti Opatulidwa linayamba kugwira ntchito, ndinapangitsidwa kukapezeka ku yunivesiti ya gulu la fuko langa. Panali kufalitsa kochulukira konena za ophunzira pa mayunivesiti opatulidwa amenewa. Ndinamaliza maphunziro chaka chirichonse ndi chipambano chapamwamba ndipo pomalizira ndinapeza digiri ya Master of Science (Katswiri wa Sayansi) mu physics ya nyukliya, ndipo chimenecho chinakoka chisamaliro chochulukira, makamaka popeza kuti kenaka ndinaikidwa ku nthambi ya maphunziro ya Yunivesiti ya Western Cape—wophunzira wachikaladi woyamba kuikidwa chotero.
Komabe, pa nthaŵi imeneyi ndinadzimva wokhumudwitsidwa kwambiri. Ndinasowa yankho ku funso lofunikira la moyo: Kodi nchiyani chomwe chiri chifuno chake? Ndemangayo kwa bwenzi langa, yotchulidwa poyambirirapo, inapangidwa chifupifupi pa nthaŵi imeneyi.
Mafunso Anga Ayankhidwa
Kudzafika pa nthaŵi imeneyi, chipembedzo chinachita mbali yochepera kwambiri m’moyo wanga. Monga mwana, ndinali kupita ku Tchalitchi cha Anglican ndipo ndinavomerezedwa pa msinkhu wa 16. Koma sikunali mayankho aliwonse ku mafunso anga. Chotero pamene ndinali kukula, kupezeka ku tchalitchi kwanga kunachepekera ndipo pomalizira ndinaleka.
Kenaka tsiku lina ndinachezera nyumba ya mnzanga wa pa yunivesiti. Mkazi wake, Julia, anagwiritsira ntchito Baibulo kusonyeza kuti panali yankho ku mavuto a ndale zadziko ndi aufuko osati kokha a South Africa komanso a dziko lonse. Ndinadabwitsidwa ndi kukaikira. Koma ndinalandira kabukhu kakuti Basis for Belief in a New World, ndinapita kunyumba, ndi kuyamba kukaŵerenga iko kokha chifukwa chofuna kudziŵa.
Pa ora lachiŵiri m’mawa wotsatira, ndinali ndidakaŵerengabe! Mmenemo munali makambitsirano olingaliridwa ponena za chifukwa chimene Baibulo liriri lowona, chifukwa chimene maulosi ake ali odalirika, chifukwa chimene mtundu wa anthu uli m’vuto lokulira chotero, chifukwa chimene 1914 iri deti lofunika chotero, ndi chifukwa chimene tingayembekezere kaamba ka dongosolo la kachitidwe latsopano lolungama pano pa dziko lapansi. Ichi motsimikizirika chiyenera kukhala chowonadi!
Tsiku lotsatira ndinabwerera kunyumba ya mnzanga. “Kodi muli ndi mabukhu owonjezereka onga limeneli?” ndinafunsa mkazi wake. Ndinachokapo ndi mulu wa mabukhu ochita ndi ziphunzitso zazikulu za Baibulo, malongosoledwe a maulosi a Danieli ndi Chibvumbulutso, mkhalidwe wa masiku asanu ndi limodzi a chilengedwe, ndi zochulukira, zowonjezereka. Chofunika kwambiri chinali chakuti, anasonyeza kuti kulibe paliponse m’Baibulo pamene pali kulungamitsidwa kwa kupatulana kwaufuko, popeza kuti “Mulungu alibe tsankho.” (Machitidwe 10:34) Ndinawatha mabukhu onsewo. Pano panali mayankho ku mafunso omwe nthaŵi zonse anandikantha ine. Pambuyo pa chifupifupi chaka chimodzi chodzazidwa ndi phunziro la Baibulo la khama, ndinabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Pamenepo panali pa November 21, 1967.
Monga gulu, Mboni za Yehova ziridi zopanda tsankho laufuko ndipo siziri za ndale zadziko. Iwo amapereka kumamatira kwawo ku boma limodzi, Ufumu wa Mulungu. Kwa iwo magawano a zamayanjano monenetsadi sali ofunikira. Koma mu South Africa, nthaŵi zonse pali mavuto okhudza nkhani zaufuko. Chifukwa cha Lamulo la Malo a Gulu, mipingo imawunikira makhazikitsidwe a ufuko a malo amene iyo iri. Chotero mu Mpingo wa Claremont womwe ndinkapezekako, anthu ambiri anali akaladi. Anthu oyera oŵerengeka omwe anapezekako anali amishonale kapena amuna okhala m’malo a chiyang’aniro.
Ndimakumbukirabe, pambuyo pa zaka zonse zimenezi, zochitika ziŵiri zomwe zimasonyeza mmene chiriri chovuta kudzichotsera iwemwini mikhalidwe yaufuko. Pa misonkhano, oyera opezekapo ankapita kutsogolo kwa mizera ya kafiteria, kutenga zakudya zawo, ndi kupita kukadya modzipatula, pamene kuli kwakuti otsalafe tinaimirira tikumadikirira. Chimenecho chinandikhwethemula. Mboni zachiyera zinalinso ndi chizoloŵezi cha kudziŵikitsa akazi awo m’njira iyi: “Wokondedwa wanga, uyu ndi Merlyn. Iye akuphunzira Baibulo.” “Merlyn, uyu ndi mkazi wanga, Mlongo Uje.” Iwo anandiitana ine ndi dzina langa loyambirira, koma ine ndinafunikira kugwiritsira ntchito “Mlongo” kapena “Mbale.” Ndinakwiyitsidwa!
Koma kenaka ndinayamba kuwunikira. Vuto liri lakuti nthaŵi zonse mumadzimva kuti ali munthu wina yemwe ali wa tsankho laufuko. Ndipo komabe chitaganya chogawanika mwaufuko monga South Africa chiyenera kuyambukira munthu aliyense yemwe akhala mmenemo. Zowona, Mboni zachiyera zina zinafunikira kugwirira ntchito pa maunansi awo ndi anthu ena a khungu losiyana. Koma kenaka, inenso ndinafunikira kutero. Pa nsonga imeneyi Baibulo limapereka uphungu wabwino uwu: “Usafulumire kusonyeza mkwiyo; pakuti mkwiyo umasungidwa ndi zitsiru.” (Mlaliki 7:9, The New English Bible) Inde, ndinafunikira kugwirira ntchito pa kusakhala wozindikira mopambanitsa ndi kusawona zikhoterero zozindikiziridwa m’nkhani yaufuko.
Ndifunikiranso kutchula kuti mkhalidwe wachisawawa m’dzikoli wasintha m’njira ina yake chiyambire nthaŵiyo. M’zaka zapapita, kokha chiŵerengero chokhala ndi polekezereka cha anthu achiyera analoledwa kupezeka pa kusonkhana kwa chipembedzo kwa mafuko ena, ndipo anafunikira kudya paokha. Ichi sichirinso tero.
Chofunika koposa, ngakhale ndi tero, pano panali gulu la anthu omwe anasanganizana mwaufulu, omwe analandiridwa m’nyumba ya wina ndi mnzake, ndi omwe anaitanana wina ndi mnzake mbale ndi mlongo ndipo anatanthauzadi chimenecho! Zitsimikizo zimenezi zinasungiliridwa zolimba ndipo zinazikidwa pa maprinsipulo a Baibulo. Chotero pamene zochita zaufuko zibuka—ndipo mu South Africa ziri chifupifupi zosapeŵeka—kuwunikira pa zenizeni zimenezi nthaŵi zonse kumavutitsa kudzimva kwanga. Pamene zaka zikupita, ndimaphunzira kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo mwabwinopo ndipo chotero kukhala ndi mtendere wochulukira mwa inemwini pa nkhani zaufuko. Koma wina afunikira kugwirira ntchito pa icho!
Utumiki wa Nthaŵi Zonse
Mwamsanga pambuyo pa ubatizo wanga, ndinachimva chifuno cha kuwonjezera utumiki wanga. Ndinali mbeta ndipo ndinali ndi mathayo oŵerengeka, chotero pa October 1, 1968, ndinayamba monga mpainiya wokhazikika. Chimenechi chinachititsa kuzizwitsa kwenikweni, popeza kuti chinatanthauza kuchoka kwanga pa yunivesiti ndi kuleka chomwe ambiri anachilingalira kukhala ntchito yonyezimira. Nkhani ya m’nyuzipepala yonena za kachitidwe kanga inali ndi mutu wakuti: “Wasayansi Wapamwamba Apita Kukaseŵera ndi Baibulo.” Mwamsanga ndinali kutsogoza maphunziro a Baibulo khumi kapena kuposerapo ndi anthu osiyanasiyana kapena mabanja. Pa msonkhano wina aŵiri a anthu amenewa anabatizidwa, pa wotsatira, anayi; kenaka asanu ndi aŵiri, ndi kupitirizabe.
Pa September 17, 1969, ndinakwatira Julia, Mboni yomwe inadziŵitsa chowonadi kwa ine. Iye anapeza chisudzulo pa maziko a lamulo ndi a M’malemba nthaŵi ina tisanakwatirane. Chimenechi chinatanthauza kuti ine ndinakhala ndi choloŵa cha banja la panthaŵi yomweyo, popeza kuti anali ndi anyamata aŵiri, John ndi Leon. Tinagamulapo kupitiriza mu utumiki wa upainiya kwa utali wothekera, chomwe chinatsimikizira kukhala maziko abwino kaamba ka anyamatawo ndi kundithandiza ine kupanga chipambano cha banja lathu lopeza.
Kuchiyambi kwa ma 70 kunali nthaŵi yosangalatsa kwambiri kukhala mu utumiki wa nthaŵi zonse, monga momwe zokumana nazo izi zikusonyezera. Polalikira ku nyumba ndi nyumba, tinakumana ndi mayi wotchedwa Annabel. Iye mwamsanga analandira bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi Baibulo. (Tinaphunzira pambuyo pake kuti iye analipira kaamba ka mabukhuwo ndi ndalama zotsirizira zomwe iye anali nazo—wogulitsa mkaka anafunikira kubwerera mlungu wotsatira kaamba ka ndalama zake!) Kuchokera pa chiyambi, mayiyo anakonzekera bwino kaamba ka phunziro lake la Baibulo la mlungu ndi mlungu mosasamala kanthu za khanda losapatsa mpumulo. Iye anayambanso kuwuza banja lake chomwe anali kuphunzira. Mwamsanga mwamuna wake, Billy, anatsagana naye ku misonkhano. Makolo a Annabel anapatsa ana awo asanu maina motsatira mpambo wa mawu wa alufabeti. Mng’ono wake Beattie anayamba kuphunzira. Charlie ndi mkazi wake sakanasiidwa kunja. Daphne nayenso anasonyeza chikondwerero, ndipo Edna ndi mwamuna wake anadziloŵetsamonso. Lerolino banja lonse limenelo lakhala likutumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri. Amunawo ali akulu kapena atumiki otumikira, ndipo ambiri a akaziwo akhala akutumikira monga apainiya.
Ndipo palinso Stanley. Tinakumana naye mu ntchito ya kunyumba ndi nyumba, kufikira komalizira pa masana ozizira pa Lolemba. Koma kunali kulandiridwa kotani nanga! Mkazi wake anatiitanira ife mkati, ndipo chinali chowonekeratu kuti tinali kuchita ndi munthu waulemu. M’chenicheni, iye anali atangopemphera kaamba ka thandizo la kumvetsetsa Baibulo. Kukambitsirana kwathu koyamba kunazikidwa pa chiphunzitso cha Utatu. Pambuyo pa kukambitsirana kwa ora limodzi, iye anawonekera wokhutiritsidwa. Mlungu wotsatira, iye anatilandira ife ndi mawu awa: “Anthu inu muli olondola. Ndaŵerenga ‘Chipangano Chatsopano’ chonse, ndipo mulibe Utatu. Ndinapita kukawonana ndi minisitala kukamufunsa chifukwa chimene iye anali kundisokeretsa ine. Iye anakana kundiwona, chotero ndinabweza maenivulupu a zosonkhanitsidwa omwe ndinkagwiritsira ntchito kusonkhetsa ndalama kuchokera ku ziŵalo zina za tchalitchi.” Ndipo zonsezi popanda kulandira chofalitsidwa chirichonse kuchokera kwa ife! Iye anakhumba kupezeka pa misonkhano, ndipo tinalonjeza kukamtenga iye. Koma Sande imeneyo tinabwera mphindi zisanu mochedwera ndi mmene tinalonjezera. Tinakumana naye akupalasa njinga yake kupita ku msonkhano! “Ndinaganiza kuti munandiiwala ine,” iye anatero. Tinaphunzira katatu pa mlungu, ndipo iye anabatizidwa miyezi itatu pambuyo pa kukumana kwathu koyamba. Stanley watumikira kwa zaka zambiri ndi changu chimodzimodzi chomwe anali nacho poyamba.
Julia ndi ine tinaŵerengera kuti kwa zaka zingapo, takhala ndi mwaŵi wa kuthandiza anthu 50 kukhala Mboni za Yehova.
Kubwerera ku Ntchito Yakuthupi
Pambuyo pa zaka zinayi mu utumiki wa upainiya, ndalama zathu zinali pafupi kutha. Mtengo wa kakhalidwe unakwera, ndipo anyamatawo anali kukula. Chotero, mowawitsidwa ndipo mozengereza, tinagamulapo kusiya utumiki wa nthaŵi zonse. Mmenemo munali mu September 1972. Chotsatirapo nchiyani? Kokha pambuyo pa choposa chaka chimodzi, pa January 1, 1974, ndinabwerera ku ntchito yophunzitsa pa yunivesitiyo pamene malo anapezeka mu physics. Ichi chinatanthauza kusintha kolingalirika ndiponso kudzichinjiriza molimbana ndi kukhala wolefuka. Koma ndi chirikizo lolimba kuchokera kwa Julia, ndinakhoza kupanga masinthidwe. Iko kunatsimikizira kukhala kwathandizo kwambiri kukhalabe wokangalika koposa mu utumiki ndi mu mpingo—m’chenicheni kupitirizabe ‘kufuna ufumu choyamba.’—Mateyu 6:33.
Popeza kuti alangizi onse a pa yunivesiti amayembekezeredwa kufufuza, funso la kubwereranso ku physics ya nyukliya linabuka. Ndinachipeza icho kukhala chovuta kwenikweni kulingalira kuchita kufufuza kwapandekha kumeneku pamene kuli kwakuti nthaŵi yanga kunja kwa yunivesiti inatheredwa m’kuyesera kuphunzitsa anthu chowonadi chochokera m’Baibulo. Chinawoneka kukhala chosaphula kanthu kudziloŵetsa m’kufufuza kokha kaamba ka chifukwa chake. Ndipo, ndithudi, kufufuza kwa physics ya nyukliya mothekera kukakhala ndi kugwiritsira ntchito kwa zankhondo, ndipo chimenechi chikabweretsa mavuto kulinga ku uchete Wachikristu.—Yesaya 2:2-4.
Mu South Africa yunivesiti yonga ngati ija ya Western Cape iri ndi ophunzira ambiri omwe akutchedwa “osowa mwaŵi.” Iwo amabwera ku yunivesiti osakonzekeretsedwa mokwanira chifukwa cha kuchepekera kwa maphunziro ndi zinthu zina za mikhalidwe ya zandalama. M’zochitika zambiri iwo samasowa kuthekera—iwo analibe kokha mwaŵiwo. Kwa zaka 13 zapita, monga mbali ya ntchito yanga ya pa yunivesiti, ndakhala ndikufufuza mavuto a kuphunzira kwa ophunzira oterowo ndi kukonzekera njira zosiyanako za kuphunzitsa. Kufufuza kumeneku kwandibweretsera ukatswiri wa maphunziro mu physics ndi kuthera m’kukwezedwa kwanga ku uprofesa. Maprogramu a kufufuza kwa zigwirizano tsopano akuchitidwa ndi mayunivesiti mu United States ndi Israyeli. Chiri chokondweretsa kuyerekeza zopezedwa m’kufufuza kumeneku ndi njira zophunzitsira za Mboni za Yehova.
Nthanthi yokulitsidwa ndi Profesa Reuven Feuerstein ndi ogwira ntchito anzake mu Israyeli ikutchedwa Mediated Learning Experience (Luso la Kuphunzira la Mkhala Pakati). Nsonga ya nthanthi imeneyo iri yakuti ana amakulitsa kuthekera kwa kuganiza osati kokha kuchokera ku chochititsa chakunja chowafikira iwo kupyolera m’nzeru zawo komanso kuchokera mwa mkhala pakati waumunthu akumamasulira zakunjazo kwa iwo. Ngati chimenechi sichinachitidwe, ana samakulitsa kuthekera kwawo kwa kuganiza kwakukulu monga mmene angakhozere.
Mboni za Yehova zimaika chigogomezero champhamvu pa thayo la kholo monga mlangizi woyambirira wa mwana. Makolo omwe ali Mboni amathera maora ambiri akumasanthula zothandiza za phunziro la Baibulo zokhala ndi zitsanzo ndi ana awo, akumawafunsa iwo ponena za zimene akuwona ndi kuwathandiza iwo kumvetsetsa kufunika kwa nkhani za m’Baibulo. Iwo amagogomezera kufunika osati kokha kwa phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu komanso kaamba ka chilangizo chokhazikika, makamaka m’maprinsipulo a Baibulo. (Deuteronomo 6:6-8) Kufufuza kwapamwambako kumawoneka kusonyeza kuti m’kuchita tero, makolo kwenikweni akukulitsa luntha la ana awo.
Constructivism (kumangilira) kuli nthanthi ina yomwe imasungilira kuti kuphunzitsa sikuli kokha kusamutsa chidziŵitso kopepuka kuchokera ku maganizo a mlangizi kupita ku maganizo a wophunzira. M’malomwake, munthu aliyense amapanga kumangilira kwa iyemwini kuchokera ku chimene achiwona kapena kumva kapena kukumana nacho. Chimenecho ndicho chifukwa chake anthu aŵiri angamvetsere ku chidziŵitso chimodzimodzi ndi kupezapo kumaliza kosiyana. Kuti anthu aphunzire mokhutiritsa, iwo afunikira kuchita ndi chidziŵitsocho iwo eni.
Misonkhano ya Mboni za Yehova imalimbikitsa kwenikweni chimenechi. Aliyense amayembekezeredwa kukonzekera pasadakhale chidziŵitso chodzakambitsiridwacho kuchokera ku mabukhu omwe alipo. Mkati mwa msonkhano weniweniwo, ndemanga zimatengedwa kuchokera ku gulu pa nkhani zokonzekeredwa. Mwanjira imeneyi anthu amalimbikitsidwa osati kokha kulongosola chimene iwo achiphunzira komanso kupindula kuchokera ku kukonzekera komwe ena akupanga.
Kubwera kwa maphunziro ozikidwa pa kompyuta kwatamandidwa kukhala njira yopangitsira chilangizo kugwira ntchito pa chokha. Komabe, ntchito ya phunziro la Baibulo imene Mboni zatsatira kwa zaka zambiri m’nyumba za anthu yapambana pa chimenecho! Mlangizi mmodzi amathandiza munthu mmodzi, aŵiri, kapena atatu (m’nthaŵi zoŵerengeka oposerapo) kulingalira nkhani zosindikizidwa pa nkhani ya Baibulo imene wophunzirayo wabwereramo m’kukonzekera. Wophunzirayo amalimbikitsidwa kulongosola chimene iye wachimvetsetsa, ndime ndi ndime, ndipo kenaka chimenechi chimakambitsiridwa—mowonadi phunziro la Baibulo laumwini. Atapatsidwa kugwira ntchito kwa maprinsipulo abwino a chilangizo oterowo, nchosadabwitsa kuti Mboni za Yehova zimachuluka monga momwe zikuchitira. Ndithudi, iwo safunikira kuphunzira maprinsipulo amenewa kuchokera ku yunivesiti. Iwo amawapeza iwo kuchokera ku magwero apamwamba—Baibulo.—Mateyu 28:19, 20; Yohane 6:45.
Chigwirizano Chaufuko Chiloŵa M’malo Kukwinjika Kwaufuko
Zaka zoposa 20 zapita chiyambire pamene ndinakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. John ndi Leon, ana anga aamuna opeza, tsopano aakulu, onse aŵiri ali obatizidwa ndipo akutumikira mokhulupirika. Mu 1976 mwana wathu wamwamuna Graeme anabadwa. Uli mwaŵi kumuleranso iye m’njira ya chowonadi. Banja lathu ladalitsidwa chifukwa chakuti Julia ali wokhozanso kuchita upainiya, pamene ine ndikuchita upainiya wothandizira mosachepera pa nthaŵi zitatu pa chaka. Mozungulira ife mu South Africa, pakhala kuwonjezeka kwakukulu m’kukwinjika kwaufuko. Aliyense amakhoza kukuwona iko kolembedwa pa zimango ndi kukumva iko m’mphepo. Komabe, pakati pa kugawanika kwaufuko konse, chozizwitsa chamakono chikuchitika. Ndi kufeŵetsedwa kochitidwa ndi Boma pa malamulo a mayanjano, Mboni za Yehova tsopano ziri zokhoza kukumana chapamodzi mwaufulu, makamaka pa misonkhano yaikulu. Ine ndakhala ndi mwaŵi wa kutengamo mbali m’kulinganiza ina ya misonkhano imeneyi kaamba ka magulu onse a fuko. Kumeneko timawona kusasankhana kwaufuko kukugwira ntchito, anthu ophunzitsidwa ndi miyezo yapamwamba ya Baibulo kukhala mowonadi osawona mtundu! Pano pali anthu amene amawona chimene ena ali mkatikati, osati kokha mtundu wa khungu lawo.
Mboni za Yehova lerolino zimapanga ubale wowona wokha wachiwunda chonse wa mtundu wa anthu. Posachedwapa, mu dongosolo lake latsopano la kachitidwe ka zinthu, Yehova “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” Limodzi ndi mamiliyoni a abale anga ndi alongo dziko lonse, ndikuyang’ana kutsogolo ku dziko latsopano limenelo losangalatsa, lolungama, lopanda kusankhana kwaufuko.—Chibvumbulutso 21:3-5.