Zifukwa Zowonjezereka za Kukhalira Oyamikira
ANTHU a Israyeli wakale anali ndi zifukwa zambiri kuposa ena za kusonyezera chiyamikiro kwa Mlengi. Nchifukwa ninji tinganene ichi?
Chabwino, mofanana ndi anthu ena onse, Aisrayeli anali ndi chifukwa cha kukhalira oyamikira kaamba ka zinthu zokongola ndi zosangalatsa zolengedwa ndi Mulungu. Koma iwo anali ndi chifukwa chowonjezereka cha kukhalira oyamikira chifukwa Wamphamvuyonseyo anawasankha iwo kukhala anthu ake apadera ndi kutenga chisamaliro chapadera cha iwo. (Amosi 3:1, 2) Lingalirani zina za zifukwa zawo zowonekera kaamba ka kuyamikira.
Kupulumuka Kuŵiri Kuchokera ku Imfa
Ndi moyamikira chotani nanga mmene makolo onse a Chiisrayeli anakhalira pa usiku wa Nisani 14, 1513 B.C.E.! Pa usiku wowopsya umenewo, mngelo wa Mulungu anabweretsa imfa kwa “woyamba kubadwa yense m’dziko la Aigupto, kuchokera kwa munthu kufika ku nyama.” Koma iye anapitirira panyumba za Aisrayeli pamene mwazi wa nyama za Paskha unawazidwa pa mphuthu ndi m’mbali. Bata linaswedwa pamene “kunali kulira kwakukulu m’Aigupto, pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m’menemo.” Komabe nyumba iriyonse ya Chiisrayeli inalidi ndi mwana wake woyamba kubadwa wokondeka ali wamoyo ndipo waubwino.—Eksodo 12:12, 21-24, 30.
Osati kwa nthaŵi yaitali pambuyo pake, kuyamikira kuyenera kukhala kunakula m’mitima ya Aisrayeli pamene anachitira umboni kulowereramo kozizwitsa kwa Yehova pamene iwo anawoneka kukhala atagwidwa m’magombe a Nyanja Yofiira, ndi gulu lankhondo la Farao wa Igupto m’kulondola kwake kotentha. Choyamba, iwo anawona mtambo uja womwe unawatsogolera iwo ukupita kumbuyo kwawo, mokhutiritsa ukumachedwetsa olondolawo. Kenaka Aisrayeli anawona Mose akufutukula dzanja lake pa nyanja, ndipo anayang’ana ndi kuzizwitsidwa pamene Mulungu anapangitsa mphepo yamphamvu ya kum’mawa kuwomba usiku wonse, kugawanitsa madzi ndi kupanga nyanja kukhala malo owuma. Aisrayeli anafunikira kufulumizidwa kochepa kuti afulumire kudutsa malo opulumukira operekedwa mwaumulungu amenewa.
Tsopano, ngakhale kuli tero, chopangitsa chatsopano cha kudabwa! Aigupto analowa m’gombe la nyanja, ndi chidaliro cha kuwapeza Aisrayeli. Koma tawonani! Pamene Aigupto onse anali m’njira yokhala ndi khoma la madziyo, magundumu anayamba kuchoka ku magareta awo, ndipo mwamsanga panali msokonezo. Kenaka, ndi Aisrayeli onse achisungiko ku gombe lina, Yehova kachiŵirinso anauza Mose kutambasula dzanja lake, “popeza nyanja inabwerera m’mayendedwe ake mbanda kucha.” Chotulukapo chake? Osati ngakhale limodzi la gulu lankhondo lonyadiridwa la Farao linapulumuka kumizidwa, ndipo sanatero wolamulira wonyada iyemwiniyo. (Eksodo 14:19-28; Masalmo 136:15) Kodi mungalingalire mmene analiri oyamikira kwa Yehova Aisrayeli opulumutsidwawo?
Njira Zomenyera Zowonekera za Mulungu
Ngakhale kuti anali oyamikira kaamba ka chipulumutso chawo kuchokera ku Igupto ndi kudutsa kwawo kosaiwalika kupyola Nyanja Yofiira, Aisrayeli anayenera kuyang’anizana ndi zokumana nazo zowopsya zambiri asanafike ku Dziko Lolonjezedwa. Koma chokumana nacho chirichonse mkati mwa kuyenda kwawo kwa zaka 40 m’chipululu chinayenera kukhala chifukwa chowonjezereka kaamba ka chiyamikiro chapadera kwa Yehova.
Pomalizira, Aisrayeli anawoloka Mtsinje wa Yordano ndipo anali m’dziko limene Mulungu anawapatsa iwo. Iwo mwamsanga anachitira umboni chitsanzo cha njira zomenyera zowonekera za Yehova m’malo mwawo. Motani? Nkulekelanji, mwakulanda ndi kuwononga kozizwitsa kwa mzinda woyamba wa Chikanani umene anafikako—Yeriko! (Yoswa, mutu 6) Inali yachilendo chotani nanga njira yotsogozedwa ndi Mulungu ya kuyenda kuzungulira Yeriko atanyamula likasa la chipangano! Kwa masiku asanu ndi limodzi otsatizana, iwo anayenda kuzungulira linga kamodzi tsiku lirilonse. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, iwo anayenda kuzungulira lingalo nthaŵi zisanu ndi ziŵiri. Pamene ansembe anaimba malipenga awo, Aisrayeli anadzaza mpweya ndi “mfuu ya nkhondo,” ndipo “malinga anayamba kugwa pansi”! (Versi 20) Kokha nyumba ya Rahabi ndi mbali ya linga pansi pake inakhalabe yoimirira. Linga la mzinda wowoneka wosakhoza kulowereredwawo linagwa popanda kufunika kwa Yoswa ndi gulu lake lankhondo kuponya uta umodzi! Ndithudi, chokumana nacho chimenecho pa Yeriko chinali chifukwa chowonjezereka chowonekera cha kuyamikirira Mulungu.
Pa chochitika china, panali chisonyezero chowonjezereka chowonekera cha njira zomenyera zowonekera za Yehova. Pamene anthu a Gibeoni anapanga mtendere ndi Aisrayeli, mafumu asanu a chiAmori analengeza nkhondo pa Agibeoni. Yoswa anabwera ku thandizo lawo, ndipo dzanja lozizwitsa la Yehova linasonyezedwa mobwerezabwereza m’kamenyedwe ka nkhondoyo. Mulungu anasokoneza a Amori, ndipo “pakuthaŵa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo.” Ambiri anakumanizana ndi imfa kuchokera ku miyala yamatalala imeneyo kuposa amene anaphedwa ndi Aisrayeli ndi lupanga.—Yoswa 10:1-11.
“Pamaso pa ana a Israyeli,” Yoswa kenaka analankhula kwa Yehova ndi kunena: “Dzuŵa iwe, linda pa Gibeoni ndi, mwezi iwe, m’chigwa cha Ajalo.” Chotulukapo chake? “Momwemodi,” ikutero mbiriyo, “dzuŵa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani awo.”—Yoswa 10:12, 13.
Ndi zochitika zozizwitsa zotani nanga! Ndipo ndi zifukwa zowonjezereka zowonekera zotani nanga za kukhalira oyamikira ku mbali ya anthu a Yehova!
Kuyamikira kwa Kanthaŵi Kochepa
Pambuyo pa chiwonetsero cha kulowereramo kulikonse kwa Yehova, Aisrayeli anadzazidwa ndi chiyamikiro. Mwachiwonekere, M’israyeli aliyense ananena mu mtima mwake kuti iye sadzaiwala zinthu zimene anawona. Komabe, kuyamikira koteroko kunali mosakhulupiririka kwa kanthaŵi kochepa. Nthaŵi ndi nthaŵi, Aisrayeli anasonyeza mkhalidwe wosayamikira. Chotero, Mulungu “anawapereka m’manja mwa amitundu, ndipo odana nawo anachita ufumu pa iwo.”—Masalmo 106:41.
Komabe, Yehova anasonyeza mzimu wake wopirira wa kukhululukira pamene Aisrayeli analowa m’vuto, nalapa za kachitidwe kawo kolakwa ndi njira ya kusayamikira, ndi kuitana kwa iye kaamba ka thandizo. “Koma anapenya nsautso yawo, pakumva kufuula kwawo. Ndipo anakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.” (Masalmo 106:44, 45) Nthaŵi ndi nthaŵi, Mulungu wawo wokhululukira anawamasula iwo kuchokera kwa owatsendereza ndi kuwatenga iwo kubwerera m’chiyanjo chake.
Mosasamala kanthu za kupirira kwa Mulungu ndi kutumiza kwake aneneri mobwerezabwereza kukawongolera kulingalira kwawo, Aisrayeli anatsimikizira kukhala osalamulirika. Potsirizira, kuleza mtima kwa Yehova kunatha, ndipo iye analola mtundu wa Yuda kugonjetsedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. Awo amene sanaphedwe ndi magulu ankhondo a Mfumu Nebukadinezara anatengedwa andende ku Babulo.
Ndi mapeto ochititsa tsoka chotani nanga a kusayamikira kobwerezabwereza ndi kukhala osakhulupirika kwa Mulungu! Ndipo ichi chinachitika mosasamala kanthu za kuchuluka kwa zifukwa za kukhalira oyamikira.
Ndimotani mmene Akristu lerolino angapewere kupanga cholakwa chimodzimodzicho cha kulephera kusonyeza chiyamikiro kaamba ka zonse zimene Yehova Mulungu wakhala akuchita kaamba ka iwo, kupitirira ndi pamwamba pa kachitidwe kake ka ubwino kulinga kwa mtundu wa anthu mwachisawawa? Ichi tikuchisiya kaamba ka kulingalira m’nkhani yotsatira.