Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/1 tsamba 3
  • Nchifukwa Ninji Kukhala Oyamikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Kukhala Oyamikira?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mopepuka Zotengedwa Mosasamala
  • Kuyamikira Kungagonjetse Kusungulumwa
  • “Dzisonyezeni Inueni Kukhala Akuyamika”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Zifukwa Zowonjezereka za Kukhalira Oyamikira
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Sonyezani Kuyamikira Kwanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • ‘Khalani Oyamikira’
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/1 tsamba 3

Nchifukwa Ninji Kukhala Oyamikira?

YANG’ANANI pa chikuto choyambirira cha magazini ino. Ndithudi, chimatikumbutsa ife kuti pali zinthu zambiri zokongola zomwe zimaposa zonyansa ndi zowonekera zosakhala zabwino pa dzanja lirilonse.

Kodi mumayamikira kukongola kwa zinthu? Talingalirani ponena za uta waleza ndi kuwala kwake, kukhota kofeŵa kwa mitundu pambuyo pa mdima wa mkuntho. Tangolingalirani kugwa kwa madzi. Kapena yesani kuwona m’malingaliro nyama zikulumpha ndi ana awo. Lingalirani munda wa maluŵa wokongola kapena mbewu zambiri za tirigu. Inde, izi ziri zowonekera zofala kwa anthu ambiri. Koma kodi ndi chisonkhezero chotani chimene izo ziri nacho pa inu?

Mopepuka Zotengedwa Mosasamala

Kaŵirikaŵiri, mobwerezabwereza mmene chinthu chimakumanizidwira, mowonjezereka chimakhala chofala​—ndipo mopepuka koposa chimatengedwa mosasamala. Kulephera kumeneku kungawoneke kukhala kukuwonekera kwambiri m’zana loyenda mofulumira la 20. Koma kusatenga nthaŵi kusinkhasinkha kapena kuŵerenga madalitso ndi zifukwa za kuyamikirira kaŵirikaŵiri kwakhala chimodzi cha zophophonya za mtundu wa anthu opanda ungwiro.

Ku mbali ina, wamasalmo Davide, pansi pa kuwuziridwa, kaŵirikaŵiri anasonyeza chiyamiko mu nyimbo. Mawu awa otsogozedwa kwa Mulungu mu imodzi ya nyimbo za Davide ali chitsanzo choyambirira cha kuyamikira:

“Pakuwona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu,

Mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazikitsa,

Munthu ndani kuti mumkumbukira,

Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?

Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu;

Munagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake:

Nkhosa ndi ng’ombe zonsezo,

Ndi nyama za kuthengo zomwe,

Mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja,

Zopita m’njira za m’nyanja.

Yehova Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!”​—Masalmo 8:3, 4, 6-9.

Kuyamikira Kungagonjetse Kusungulumwa

Kuyamikira kwa wamasalmo kaamba ka zinthu zokongola kunathandiza kuchotsa kusungulumwa kulikonse kobweretsedwa ndi malo onyansa kapena mikhalidwe yovuta. Inunso mungakhale ndi chokumana nacho chofananacho. Motani? Mwakukalamira kuyamikira mokwanira koposa zinthu zambiri zosangalatsa zotizinga ife. Mwa njira imeneyi, inu mungawonjezere chimwemwe chanu ndi chija cha okuzungulirani.

Chotero bwanji osalola zowonekera zokongola za tsiku ndi tsiku ndi zodabwitsa kusonkhezera chiyamikiro cha mtima wonse kwa Mlengi wathu wochita ntchito yonse ya chikondi? Lingalirani tsopano zifukwa zina zowonjezereka za kukhalira oyamikira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena