“Zothandiza Monga Zitsogozo ku Moyo wa Tsiku ndi Tsiku”
CHIMENECHO ndi chimene mkazi wina wochokera ku Toronto, Canada, anatcha zofalitsidwa za Watch Tower Bible and Tract Society. “Ndimasangalala kuŵerenga izo ndi kupeza nkhanizo kukhala zachidziŵitso, zotonthoza mtima, ndipo pamwamba pa zonse, zothandiza koposa monga zitsogozo ku moyo wa tsiku ndi tsiku.”
Iye anawonjezera kuti: “Ndine womaliza maphunziro pa yunivesite, ndipo ndiyenera kuvomereza modabwitsa kuti ndaphunzira zambiri koposa kupyolera m’zofalitsidwa zanu kuposa zaka zanga zonse za maphunziro. Ndinasangalala mwapadera ndi bukhu lanu Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Palibe zofalitsidwa zina zirizonse zomwe zakhoza kukhala ndi chisonkhezero chabwino choterocho pa moyo wanga monga mmene zachitira zanu—izo zandithandiza ine mokulira; ndipo kaamba ka ichi ndikuyamikirani mowonadi.”
Bukhu lotchulidwa pamwambalo, Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, limapereka malingaliro achindunji omwe amathandiza kuthetsa mavuto ndi kupangitsa ukwati kukhala chosangalatsa monga mmene Mlengi anafunira iwo kukhala. Kaamba ka kope lanu, dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka limodzi ndi chopereka cha K8.00.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Ndatsekeramo K8.00 (Zambia).