Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ M’chiyang’aniro cha mawu a Yesu pa Yohane 15:15, kodi Akristu ayenera kudziwona iwo eni monga “akapolo” ake, kapena kodi tingadzilingalire ife eni kukhala “mabwenzi” ake?
Tingatero ndipo tiyenera kukhala zonse ziŵiri. Kuti tiwone nchifukwa ninji, tiyeni tidziwe chimene Yesu pamenepo ananena kwa atumwi ake okhulupirika pa usiku wake womalizira ndi iwo:
“Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu. Sinditchanso inu akapolo, chifukwa kapolo sadziŵa chimene mbuye wake achita. Koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate anga ndakudziŵitsani.”—Yohane 15:13-15.
Choyamba, nchiyani chimene Yesu anatanthauza mwa kunena kuti ophunzira ake okhulupirika anali akapolo? Iye sanatanthauze akapolo mu lingaliro lakuti mbadwa zonse zaumunthu za Adamu zinabadwa zopanda ungwiro, mwakutero kugulitsidwa kapena kuloŵetsedwa mu ukapolo ku uchimo. (Yohane 8:34; Aroma 5:18, 19; 6:16; 7:14) Mofanana ndi Akristu kuyambira nthaŵi imeneyo, atumwi nawonso anali mu ukapolo m’njira imeneyo, koma nsembe ya Yesu ikapereka njira ya kuwamasula, kapena kuwaombola, iwo. (1 Petro 1:18, 19; Agalatiya 4:5) Komabe, iwo sanakhale omasuka kotheratu pa nthaŵi imeneyo. Monga mmene mtumwi Paulo pambuyo pake analembera, iwo “anagulidwa ndi mtengo,” mwazi wa Yesu, chotero anakhala akapolo a Mulungu ndi a Kristu.—1 Akorinto 6:20; 7:22, 23.
Pa Yohane 15:15 Yesu sanali kulingalira kuti atumwi okhulupirika omwe mwamsanga akalandira mzimu woyera ndi kukhala Akristu odzozedwa sanalinso akapolo. (Yerekezani ndi Yohane 15:20.) Ndithudi, kutumikira Mulungu kupyolera mwa Kristu sikuli kotsendereza ndi kodzetsa imfa. Kuli kwachikondi ndi kosunga moyo. (2 Timoteo 4:8; Tito 1:1, 2) Mkristu yemwe mwachimwemwe amalandira mtengo wa mwazi wa Kristu ndi kukhala kapolo wa Mulungu adzayang’anizana ndi imfa yotheratu kokha ngati iye pambuyo pake akana nsembe imeneyo ndi kudzipereka iyemwini kubwerera ku uchimo, kukhala kapolo wa ilo kachiŵirinso. (Agalatiya 1:10; 4:8, 9; Ahebri 6:4-6) Chotero, ophunzira a Yesu akapitiriza kukhala akapolo a Mulungu ndi a Kristu, koma iwo ali oposa akapolo. Nchifukwa ninji?
Yesu ndi atumwi anamvetsetsa kuti kubwerera m’mbuyo ku nthaŵi imeneyo, mu unansi wachibadwa kapena wa nthaŵi zonse wa mbuye ndi kapolo, ‘kapolo sakanadziŵa chimene mbuye akuchita.’ Mwachibadwa, mbuye waumunthu sangakambitsirane ndi kapolo wake wogulidwa, ndiponso sangavumbule kwa iye malingaliro achinsinsi ndi maganizo.
Tingawone kuchokera ku mawu a Yesu, ngakhale kuli tero, kuti chinali chosiyana ndi atumwi. Iye ananena kuti: “Ndatcha inu abwenzi, chifukwa zonse ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.” (Yohane 15:15) Inde, monga mmene chiriri chofala pakati pa mabwenzi okondana, Yesu anavumbula kwa iwo tsatanetsatane ndi kumvetsetsa komwe kunali kwa chinsinsi. (Mateyu 13:10-12; 1 Akorinto 2:14-16) Ngakhale kuti iwo anali atumiki, kapena akapolo, kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu, atumwiwo anasangalala ndi chiyanjo chathithithi chomwe chinawazindikiritsa iwo kukhalanso mabwenzi okhulupiriridwa. (Yerekezani ndi Masalmo 25:14.) Chimenecho chingakhale ndipo chiyenera kukhala chowona kwa ifenso. Ndi mwaŵi wotani nanga kukhala ndi monga Ambuye kumwamba Awo omwe amatitenga ife monga mabwenzi okhulupiriridwa, ndi olemekezedwa odaliridwa!