Kukhala Mtumiki Woikidwa—Njira ya Mulungu!
MLENDO mwachidziŵikire akanasangalatsidwa—mwinamwake ngakhale kudabwitsidwa—ndi chimene amamva. Chochitikacho chinali msonkhano wa Mboni za Yehova. Nkhani inali kuperekedwa kwa gulu la anthu omwe anali pafupi kubatizidwa. Modabwitsa, mlankhuliyo anawuza ophunzira a ubatizo amenewo kuti: “Kukhalapo kwanu pa gulu iri la ophunzira opita ku ubatizo kumasonyeza chikhumbo chanu cha kukhala mtumiki woikidwa wa Ufumu.”
‘Kodi chimenechi chingatheke motani?’ mlendo angakhale anafunsa. ‘Kodi ubatizo suli kaamba ka anthu ovumbulutsidwa kumene ku Chikristu—ndi kaamba ka makanda? Kodi icho sichimatenga zaka za kuphunzira kokulira ndi maphunziro kukhala mtumiki woikidwa?’ Mwinamwake mungakhale munalingalirapo mofananamo. Koma chimene kwenikweni Baibulo limanena ponena za ubatizo ndi kuikidwa zingakudabwitseni.
Wina Asanabatizidwe
Choyamba, ubatizo suli kaamba ka anthu ongodziŵa kumene uthenga Wachikristu. Baibulo, pa Machitidwe 8:12, limasonyeza kuti anthu m’zana loyamba ankabatizidwa kokha pambuyo pa “kukhala wokhulupirira.” Mateyu 28:19 amasonyezanso kuti munthu ayenera kukhala ‘wophunzira’ asanabatizidwe. Kodi ndimotani mmene wina amakhalira ‘wokhulupirira,’ kapena ‘wophunzira,’ (‘wophunzitsidwa’)? Kupyolera mu phunziro losamalitsa la Baibulo! M’njira imeneyi, munthu amapeza chidziŵitso cholongosoka cha Yesu ndi Yehova Mulungu. (Yohane 17:3) Kokha pambuyo pakupeza chidziŵitso chimenechi wophunzira amakhala m’malo a kulingalira kubatizidwa. M’zana loyamba, Akristu okhazikitsidwa anapereka malangizo amenewo kwa otembenuzidwa atsopano.—Machitidwe 8:31, 35, 36.
M’mipingo ya Mboni za Yehova lerolino, makonzedwe akupangidwa mofananamo kaamba ka anthu okondwerera kusangalala ndi phunziro la Baibulo la panyumba la aliyense. Munthu wokhala ndi mtima wovomereza mwapang’onopang’ono amafikira ku kuyamikira chimene iye akuphunzira. Iye amafulumizidwa kugawana zikhulupiriro zake zongopezedwa kumenezo ndi ena. (Aroma 10:8-10) Iye amayamba kupezeka pa misonkhano ya Chikristu mokhazikika, kumene iye amapeza malangizo owonjezereka a Baibulo. (Ahebri 10:24, 25) Ndipo pambuyo pa milungu kapena miyezi ya ichi, wokhulupirira watsopanoyo amakulitsa chikhumbo chakutsatira uphungu wa Baibulo pa Aroma 12:1: “Chifukwa chake ndikupemphani inu abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.”
Chidziŵitso chokha, ngakhale kuli tero, sichimamuyeneretsa munthu kupanga kudzipereka kumeneku. Munthu amafunikira kulapa ndi “kubwerera.” (Machitidwe 3:19) Nchifukwa ninji ichi chiri tere? Mowona mtima, ena anali ndi njira ya moyo ya makhalidwe oipa asanaphunzire miyezo ya Mulungu. Ena anali okutidwa m’kulondola zinthu mwadyera. Koma kuti adzipereke iwo eni kwa Mulungu monga “oyera, olandirika,” iwo ayenera kusonyeza kuipidwa kaamba ka machitachita akale oterowo. Iwo ayenera kukhala onyansidwa chifukwa chakuti anagwiritsira ntchito moyo wawo, mphamvu zawo, ndi kuthekera kwawo m’kulondola zinthu zosakhala za m’malemba. Kuipidwa koteroko kuyenera kutsagana ndi kachitidwe koyenerera kotero kuti mowonadi “abwerere,” kapena kusintha njira yawo ya moyo.
Kuti athandize wokhulupirira wachatsopanoyo mowonjezereka, akulu Achikristu amakonzekera kukumana naye ndi kuthera nthaŵi ina kubwereramo mu ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Ichi, kaamba ka chinthu chimodzi, chimatsimikizira akuluwo kuti Mkristu woyembekezeredwayo wapeza chidziŵitso cholongosoka cha zifuno za Mulungu. Ndipo, ndithudi, kubwereramoko kumatsimikizira kukhala kothandiza koposa kwa wophunzirayo. Monga mmene kukufunikira, nkhani zina zomwe sizinamvetsetsedwe zimalongosoledwa momvekera.
Maubatizo mwachisawawa amachitidwa m’chigwirizano ndi misonkhano ya Mboni za Yehova. Pa zochitika zoterozo, nkhani yachindunji imaperekedwa kwa ophunzira oyembekezera ubatizowo. Iwo anakumbutsidwa kuti ubatizo suli chabe nkhani ya kuloŵa chipembedzo chatsopano. Yesu ananena kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW]; nanditsate ine.”—Mateyu 16:24.
Ophunzirawo amakumbutsidwanso mowonjezereka za chizindikiro chozama cha ubatizo. Lemba la pa 1 Petro 3:21 limaŵerengedwa kaŵirikaŵiri: “Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, (kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu,) mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” Pano, Petro akuyerekeza ubatizo ndi chokumana nacho cha Nowa cha kupyola madzi a Chigumula. Pamene kuli kwakuti madzi amenewo anatsimikizira kukhala odzetsa imfa kwa mtundu wa anthu oipa pa dziko lapansi, iwo anatsimikizira kukhala osunga moyo kwa Nowa popeza iwo mwachisungiko anamunyamula iye m’chingalaŵa. Mofananamo, ubatizo ‘umapulumutsa’ Akristu kuchokera ku dziko loipa iri. Pamene winawake, pamaziko a chikhulupiriro chake m’mapindu a imfa ndi chiukiriro cha Yesu Kristu, abatizidwa, munthu woteroyo ali m’mlingaliro, m’mkhalidwe wa ‘kupulumutsidwa’ pamaso pa Mulungu. Iye samalingaliridwanso monga mbali ya mbadwo woipa uwu woŵeruzidwa ku chiwonongeko.—Onani Machitidwe 2:40.
Chotero, kubatizidwa si sitepi limene liyenera kutengedwa mu mkhalidwe wa malingaliro, monga mmene zimachitikira kaŵirikaŵiri pa misonkhano yodzutsanso chikondwerero ya chipembedzo. Ikumawunikira pa ichi iri nsonga yakuti ophunzira achatsopanowo asanamizidwe, mtumiki woyang’anira pa ubatizopo amawafunsa iwo mafunso ozama aŵiri. Mayankho awo m’kuvomereza ali “chilengezo chapoyera” cha chikhulupiriro chawo mu dipo ndi chenicheni chakuti iwo modzipatulira adzipereka iwo eni kwa Yehova. (Aroma 10:9, 10) Tsopano iwo ali okonzekera kaamba ka ubatizo wa m’madzi.
Kuikidwa monga Atumiki a Ufumu
Kumizidwa kotheratu m’madzi chiri chizindikiro choyenerera cha kudzipereka kwawo kwa Mulungu. Pamene ali pansi pa madzi, kuli ngati kuti iwo afa ku njira yawo yakale ya moyo. Pa kutuluka m’madzi, kuli monga ngati kuti iwo tsopano akukhala ndi moyo ku njira yatsopano ya kudzipereka kwaumwini mu utumiki kwa Mulungu.—Yerekezani ndi Aroma 6:2-4.
Ndimotani, ngakhale kuli tero, mmene kuikidwa kumagwirizanirana ndi kachitidwe ka ubatizo? Dziŵani chimene Cyclopædia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature (1877), Volyumu VII, tsamba 411, ya M’Clintock ndi Strong ikunena: “Kuikidwa kumasonyeza kusankhidwa kapena kulozeredwa kwa munthu ku ntchito ya utumiki, kaya ndi phwando lopezekapo kapena popanda.” (Kanyenye ngwathu.) Ichi chimazindikiritsa kuti palibe chifuno cha phwando lonkitsa kapena chikalata cha kuikidwa kukhala mtumiki Wachikristu.
Koma kodi Baibulo limaphunzitsa ichi? Lingalirani Yesu Kristu. Palibe chikaikiro chirichonse chakuti iye anali mtumiki woyambirira wa Mulungu. Mosasamala kanthu za chimenecho, kodi anali ndi phwando lonkitsa la kuikidwa asanayambe ntchito yake yolalikira? Kodi iye anali ndi chikalata chomuzindikiritsa iye monga mtumiki? Mosiyana kotheratu. Chinali kokha pambuyo pa kungobatizidwa kwake m’madzi pamene Mulungu anasonyeza chivomerezo chake cha Yesu monga Mwana wake ndi kumuika iye monga mtumiki Wake.—Marko 1:9-11; Luka 4:18-21.
Bwanji ponena za Akristu a m’zana loyamba? Palibe ripoti lirilonse la kuikidwa kodzitukumula kaamba ka atumiki Achikristu oyambirira amenewo. Cholembedwa cha mu Machitidwe mobwerezabwereza chimatiuza za zochitika zopepuka za ubatizo wa okhulupirira. Ichi chinatsatiridwa ndi kugawana kwawo mokangalika mu utumiki wapoyera.—Onani Machitidwe 2:41-47; 8:36-39; 22:14-16.
Ndi umboni wotani umene atumiki oterowo anali nawo wa kuikidwa kwawo? Paulo ananena pa 2 Akorinto 3:1-3: “Kodi tirikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu? Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa m’mitima yathu, wodziŵika ndi woŵerengedwa ndi anthu onse. Popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome amiyala, koma m’magome a mitima yathupi.” Chiyambukiro cha mzimu wa Mulungu pa mitima yophunzitsidwa imeneyi chinatulutsa umunthu watsopano Wachikristu, womwe ukanaŵerengedwa ndi openyerera onse. Ichi chinali umboni wokwanira wakuti Mulungu ndithudi anaika awo ogawanamo kuphunzitsa ophunzira atsopano amenewa.
Kudzikakamiza Ife Eni mu Utumiki
Mofananamo lerolino, mtumiki amazindikiridwa ndi ntchito zake. Iye ali wofunitsitsa ‘m’kudzikakamiza iyemwini mwamphamvu’ mu utumiki wake. (Luka 13:24) Iye amawona utumiki wake monga mwaŵi waukulu kuchokera kwa Mulungu. Iye sautenga iwo mosasamala.—1 Timoteo 1:12-16.
Kulalikira Ufumu kuli thayo loyamba la atumiki oterowo. Zolondola zina zonse ziyenera kukhala ndi polekezera kotero kuti iwo ‘angakwaniritse kotheratu utumiki wawo.’ (2 Timoteo 4:2, 5) Ndithudi, iwo ayenera kusamalira kaamba ka zosowa zakuthupi za iwo eni limodzinso ndi za mabanja awo. Ngakhale kuli tero, iwo ali ‘okwaniritsidwa ndi chakudya ndi chovala.’ Iwo samalola zolondola zaumwini kapena zikhumbo zaumwini kuwacheukitsa iwo kuchoka ku utumiki. (1 Timoteo 5:8; 6:7, 8; Afilipi 2:20-22) Iwo amatsimikizira za “zinthu zofunika koposa.” (Afilipi 1:10) Iwo amakalamira kuika patsogolo pawo chitsanzo chabwino cha Yesu Kristu, amene moyo wake unazikidwa mozungulira pa kulalikira Ufumu.—Luka 4:43; Yohane 18:36, 37.
Mosasamala kanthu za chimenecho, pamene munthu wabatizidwa monga mtumiki woikidwa, iye m’chenicheni ali m’magawo oyambirira a utumiki wake kwa Mulungu. Ndithudi, iye wapeza chidziŵitso cha Kristu Yesu ndi Yehova Mulungu. Iye wapanganso masinthidwe ambiri m’moyo wake kotero kuti utumiki wake Wachikristu sungapezedwe ndi cholakwika. (2 Akorinto 6:3) Mkristu wongobatizidwa kumeneyo adakali ndi kukula kochulukira kofunikira kuti akuchite. Ubatizo wake, womwe umazindikiritsa kuikidwa kwake, uli kokha chochitika chachikulu chimodzi m’kukula kwake monga Mkristu. (Afilipi 3:16) Chotero, mtumiki aliyense woikidwa ayenera kupitirizabe kumangilira chiyamikiro cha mtima cha zinthu zauzimu. Iye amafunikira kundandalitsa nthaŵi kaamba ka phunziro laumwini. Iye ayenera kutenga mwaŵi wa makonzedwe onse kaamba ka mpingo kukumana pamodzi. Iye ayenera kugwirira ntchito pa kuwongolera mkhalidwe wa mapemphero ake, kutulukapo mu unansi waumwini wathithithi ndi Mulungu.—Luka 6:45; 1 Atesalonika 5:11; 1 Petro 4:7.
Tikulingalira kuti malingaliro a Malemba amenewa adzakuthandizani inu kumvetsetsa nchifukwa ninji digiri ya ku yunivesite siiri chiyeneretso kaamba ka awo omwe akukhumba kutumikira monga atumiki a Mulungu. Mboni za Yehova zoposa 3 miliyoni zikutumikira Mulungu mokhulupirika monga atumiki ake, kumalengeza zowonadi zondandalikidwa m’Mawu ake. Bwanji osalola mmodzi wa iwo kukuthandizani inu kupeza chidziŵitso cha Baibulo?
[Chithunzi patsamba 29]
Mogwirizana ndi Baibulo, mtumiki Wachikristu amaikidwa pa ubatizo