Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 6/15 tsamba 27
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chochiritsa Chokha
  • Chapadera cha Dziko Lonse
  • “Nthenda Yeniyeni”
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Dziko Likumka Limera Imvi
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 6/15 tsamba 27

Chidziŵitso pa Nyuzi

Chochiritsa Chokha

Pamene ambiri a akatswiri a dziko pa ukalamba anakumana chaka chatha pa New York’s Mount Sinai Medical Center kukambitsirana sayansi ya za ukalamba, nsonga imodzi inali yowonekeratu​—palibe wina aliyense amene angavomereze pa chifukwa chimene munthu amakalambira ndi kufa. Akatswiri ena apereka nthanthi yakuti “ukalamba uli ‘woikidwiratu’ mu zinthu zimene zimapanga ziwalo za thupi, mofanana ndi masitepi ena a moyo,” inasimba tero Newsweek on Science & Technology. Ngakhale kuli tero, nkhaniyo ikuwonjezera kuti “chiri chovuta kudziŵa nchifukwa ninji chilengedwe chingasinthe gene ya ukalamba.” Nthanthi imodzi yoperekedwa ndi Leonard Hayflick, katswiri wa za ukalamba wa pa Yunivesite ya Florida, inali yakuti “magene ena angakhale anasinthika kupangitsa anthu kukhala a umoyo ndi kugwira ntchito kufikira pamene iwo angabale.” Hayflick anamaliza kuti podzafika pa nthaŵi imene munthu afika 30 kapena kuposerapo, magene a moyo wa utali amenewo amayamba kutha. Chenicheni chiri chakuti, avereji ya chiyembekezo cha moyo kaamba ka anthu a ku America chiri choposera pang’ono pa zaka 74 “kaamba ka dongosolo la kakhazikitsidwe ka lerolino,” ndipo “ngakhale kuchiritsa kaamba ka matenda a ukalamba​—kansa, arthritis, Alzheimer​—zidzachita zochepa kufutukula malire a kunja,” inadziŵitsa tero nkhaniyo.

Ngakhale kuti asayansi apeza kuchiritsa kaamba ka ukalamba kukhala kothetsa nzeru mofanana ndi choyambitsa chake, ophunzira osamalitsa a Mawu a Mulungu satero. Chifukwa chimene munthu amakalambira ndi kufa chinalongosoledwa pa Aroma 5:12: “Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” Chochiritsa chokha kaamba ka ziyambukiro za chimo la cholowa chidzabwera kupyolera mwa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. “Mulungu anatuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Pansi pa ulamuliro wa Ufumu wake, “sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro kapena kulira kapena chowawitsa.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Chapadera cha Dziko Lonse

Pamene atsogoleri a mphamvu zadziko ziŵiri anakumana pamodzi pa December 8, 1987, kusaina pangano la kuchepetsako zida za nkhondo, chinalongosoledwa monga chochitika chomwe chiri “m’chenicheni chapadera” kaamba ka mtundu wa anthu. Nchifukwa ninji? Chifukwa “iri nthaŵi yoyamba chiyambire kucha kwa Mbadwo wa Atomic kuti mphamvu zazikulu zavomereza osati kokha kuchepetsako zida za nyukliya koma kuchotsa madongosolo onse,” ikusimba tero New York Daily News. Ikuchitira ndemanga ponse paŵiri pa pangano lenilenilo ndi chiŵerengero chochepetsedwa cha zida za nkhondo, News inawonjezera kuti: “Ngati kalongosoledwe kawo ndi maprinsipulo zingafutukulidwe, mbiri yakale kotheratu ingalembe izo monga chochitika choyamba chofunika koposa m’chitsanzo cha mtendere ndi chisungiko cha mitundu yonse m’dziko Lapansi.”

Zowona, zifunsiro zaposachedwapa kulinga ku mtendere ndi chisungiko ziri zapadera. Ngakhale kuli tero, chapadera cha dziko lonse chachikulu kwambiri chidzakhala nthaŵi m’mbiri ya dziko pamene atsogoleri a dziko adzafuula mtendere ndi chisungiko m’njira yomvekera kwambiri kuposa ndi kale lonse. Mphindi idzabwera pamene kufuula kwawo kudzatsimikizira kukhala kosiyana kuchokera ku zoyesayesa zambiri za mtendere zomwe zakhala zikupangidwa kufikira pa nthaŵi imeneyo. Nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira? Chifukwa chakuti kale kwambiri mtumwi Paulo ananeneratu kuti “pamene angonena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera . . . ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:3, NW) Mtendere weniweni ndi chisungiko kenaka zidzatsatira pansi pa ulamuliro wangwiro wa Kristu Yesu, “Kalonga wa Mtendere.”​—Yesaya 9:6, 7.

“Nthenda Yeniyeni”

“AIDS siiri ngozi ya mwatsoka kapenanso yachilengedwe yosapeweka. Kufalikira kwake kokulira kuli chotulukapo cha kupusa kwathu kwenikweni. . . . Tiribe wina aliyense koma ife eni oyenera kudzipatsa mlandu,” anatero katswiri wodziŵa za kubala ndi matenda a akazi wa ku Denver, W. M. Merrick Thomas. Akumalongosola chifukwa cha kawonedwe kake mu nyuzipepala ya Rocky Mountain News, iye anadziŵitsa kuti: “AIDS siiri nthenda ya kugonana kwa ofanana ziwalo. Iyo iri nthenda ya kuyanjana ndi kugonana kosasankha. . . . Nthenda ya kugonana kosasankha idzayambukira mwachindunji awo onse omwe amagonana mosasankha.” Chotero, monga momwe Thomas anawonera, “mkhalidwe wathu uli nthenda yeniyeni.”

Ali a panthaŵi yake chotani nanga mawu a Paulo, yemwe, pamene anali kulongosola mkhalidwe wosakhululukidwa wa anthu omwe amadzinenera kudziŵa Mulungu, ananena kuti: “Chifukwa chake Mulungu, anawapereka iwo m’zilakolako za mitima yawo, kuzonyansa, . . . ku zilakolako za manyazi, . . . omachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphoto ya kuyenera kulakwa kwawo”! (Aroma 1:24-27) Kakhalidwe koyera m’chigwirizano ndi miyezo ya Baibulo kaŵirikaŵiri kamatumikira monga chinjirizo molimbana ndi zovuta zomwe zimakantha mtundu wa anthu lerolino.​—Masalmo 19:7-11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena