Kodi Ndimotani Mmene Makamu Anamverera Yesu?
UTHENGA wabwino wa Mateyu umasimba kuti pa chochitika chimodzi Yesu Kristu “analowa m’ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pa mtunda. Ndipo iye anawauzira zinthu zambiri m’mafanizo.” (Mateyu 13:1-35; Marko 4:1-9) M’bukhu lawo Come See the Place: The Holy Land Jesus Knew, Robert J. Bull ndi B. Cobbey Crisler akudzutsa mafunso ena osangalatsa onena za chochitikachi. Iwo akufunsa kuti: “Ndimotani mmene wina akanamvedwera ndi ‘khamu lalikulu’ popanda phindu la mtundu wina uliwonse wa chokuzira mawu? Ndipo kodi icho chiri chothekera kupeza malo a ku gombe la nyanja okhala ndi zinthu zokhoza kukuza mawu zomwe zikatulutsa kukuza mawu koteroko?” Mwinamwake mungakhale munadabwapo ponena za ichi.
Chabwino, dziŵani yankho lawo: “Pakati pa malo a zidikha ambiri pafupi ndi Kapernao, pali amodzi omwe posachedwapa apezedwa kukhala ndi zizindikiro za mawu zoterozo za bwalo la zamaseŵera lozungulira la chilengedwe. Kuyesa kwa kukuza mawu kunachitidwa m’malo amenewa kusonyeza kuti ‘khamu lalikulu’ la anthu zikwi zisanu kufika ku zikwi zisanu ndi ziŵiri, atasonkhana pamenepo, ndithudi iwo ponse paŵiri akanawona ndi kumva momvekera bwino munthu wolankhula kuchokera pa ngalawa yokhala pa malo a pafupi ndi pakati pa malo a chidikhawo.” Ndipo ndimotani mmene kuyesa kumeneku kwa kukweza mawu kunachitidwira? Virginia Bortin, mlembi wa nkhani za zinthu zofotseredwa kale, akulongosola mu The San Juan Star, nyuzipepala ya mu Puerto Rico.
Molingana ndi Bortin, katswiri wa zinthu zofotseredwa kale B. Cobbey Crisler, mlembi mnzake wa bukhu lotchulidwa pamwambali, ndi injiniya wa kubwezedwa kwa mawu Mark Myles anachita mayesowo “pafupi ndi Tell Hum, malo a Kapernao wakale.” Kumeneko “dziko limatsetsereka pang’ono kukwera pang’ono kuchokera M’nyanja ya Galileya ku msewu wamakono womwe uli pa mtunda wa utali kuposa bwalo loseŵerera mpira.” Crisler anasambira kupita m’malo a chidikhawo ndi kuima pa mwala waukulu kumeneko. Kenaka iye anapopa zibaluni za mlingo wofanana kuti zitulutse liwu lofanana ndi kuziphulitsa izo pa utali woyesedwa wa nthaŵi. Myles, akugwiritsira ntchito mita yolinga chiunda ya electronic, anaŵerengera mlingo waukulu wa kufuula pamene iye anakwera kulinga ku msewuwo. Crisler kenaka anabwera ku gombe ndi kubwereza kuphulitsa kwa zibaluniko kumeneko. Chotulukapo? Mphamvu ya mawu inali yokulira kuchokera ku thanthwe mkati mwa chidikha kuposa kuchokera pa gombe! Mosangalatsa, pamene Crisler anali kunja mu chidikhacho, unyinji wa magalimoto a alendo anaima pa msewuwo pamwamba pake. Iye anamva bwino lomwe pamene munthu mmodzi anafunsa kuti: “Kodi akuchita chiyani mmenemo?” Wina anayankha kuti, “Sindikudziŵa. Iye wangoima pamenepo atagwira zibaluni zofiira.”
Mwachiwonekere, pamene anthu aima kapena kukhala pansi pa mlingo wofanana, kumvekera kwa mawu otulutsidwa kumamwerera ndi matupi, tsitsi, zovala, zomera, ndi malo. Ngakhale kuli tero, ngati iwo ali pa phiri kapena malo otsetsereka monga ngati pafupi ndi Kapernao, mlankhuli, pa mtunda woyenerera pansi ndi kutali kwa iwo, angamvedwe, liwu lake limakulitsidwa mokulira. Ndithudi, losafunika kunyalanyazidwa liri bata, kumvetsera kwa chisamaliro koperekedwa ndi khamu pa nthaŵiyo ndi kusoŵeka kwa phokoso la kumbuyo lamakono kuchokera ku ndege za jeti, magalimoto, magalimoto akulu, ndi zina zotero.
Koma bwanji ponena za zochitika zina pamene Baibulo limasimba kuti Yesu analankhula kwa makamu akulu? Crisler ndi Myles akupereka nthanthi yakuti Yesu ndi anthu ena a m’nthaŵi za Baibulo omwe analankhula kwa khamu lalikulu mwadala “anasankha malo otseguka odziŵika kaamba ka zinthu zawo za chilengedwe zokulitsira mawu ndi kugwiritsira ntchito izo kaamba ka kulankhula kofika patali.”
Crisler ndi Myles afufuzanso “kuti agamulepo kuti ndi anthu angati omwe mwachiwonekere akanawona Yesu tsiku limene analankhula pamenepo.” Akumayerekeza kuti linali tsiku lowala, lopanda mitambo, iwo anayerekezera kuti “khamu la 5,000 ndi 7,000 likanamva ndi kuwona Yesu akulankhula kuchokera pa gombe.” Ichi chinapangitsa wolemba nyuzipepala Bortin kumaliza kuti “ichi chimachirikiza mbiri ya Uthenga wabwino ya makamu a akulu kuchokera mu Palestine omwe anapita ku Galileya kukachitira umboni wochiritsa wozizwitsa pamene iye analankhula kwa iwo m’mafanizo. Malo a ku Kapernao okhala ndi bwalo la maseŵera lozungulira lachilengedwe longa mbale ndithudi linatheketsa aliyense kumuwona iye mowonekera bwino.”
Ndithudi, icho sichinganenedwe mogamulapo kuti Crisler ndi Myles apeza malo enieni a nkhani ya pa gombe la nyanja ya Yesu. Komabe, chiri chosangalatsa kudziŵa kuti malo oyerekezedwawo ali malo kumene zitsamba ndi miyala ziri zambiri, ndi maluwa achikasu a mpilu akumakula pakati pawo. Kuwonetsera kwawo kwa Yesu m’mafanizo ake kungakhale kunawonjezera ku kuphunzitsa kwake. M’malo okhala ndi kubweza mawu koteroko, lamulo la Yesu lakuti “kumvetsera” lingakhalenso linali loyenerera koposa. (Marko 4:3) Mofananamo, kugwiritsira ntchito kwake kwa liwu la “makutu” ndi mitundu ina ya verebu la “kumvetsera” kungakhale kunayamikiridwa mopepuka ndi amvetseri ake onse m’malo oterowo. Inde, onse omwe analipo pamenepo “m’malo a zamaseŵera ozungulira a chilengedwe” sakanamva kokha ndi kuwona Yesu mowonekera bwino komanso akanagwira nsonga yeniyeni ya mafanizo ake kokha mwakungoyang’ana pa malo owazungulira.
[Mapu patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Malo a:
1. Kapernao
2. Chigwa cha Gennesaret
3. Tiberiya
4. Potulukira pa Mtsinje wa Yordano kum’mwera
5. Phiri la Tabor
Nyanja ya Galileya
Galileya
[Mawu a Chithunzi]
Based on a map copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel
[Chithunzi patsamba 24]
Kuyang’ana kumpoto cha kum’mawa m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya kumka ku Kapernao; yowonedwa kuchokera ku mphepete kwa Chigwa cha Gennesaret
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 26]
Ngodya ya kumpoto cha kumadzulo kwa Nyanja ya Galileya. Mwinamwake, panali pafupi ndi Kapernao pamene Yesu analankhula ku khamu ali m’ngalawa
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.