Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/15 tsamba 3
  • Yesu Kristu—Mulungu, Munthu, kapena Nthano?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Kristu—Mulungu, Munthu, kapena Nthano?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Dziwani Zoona Zake za Yesu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Kristu, Mwana wa Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Yesu Kristu Ndi Ndani?
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/15 tsamba 3

Yesu Kristu​—Mulungu, Munthu, kapena Nthano?

NYIMBO ya rock yomwe inatsegulidwa pa Broadway mu Mzinda wa New York mu 1971 inatsimikizira kukhala yodzutsa mkangano, ikumachita monga mmene inachitira ndi nkhani ya chipembedzo. Koma mwinamwake nkhaniyo sinali yodzutsa mkangano kuposa mmene chinaliri chizindikiritso cha munthu wake wotchuka.

Imodzi ya nyimbo zotchuka za nyimbozo inafunsa kuti: “Yesu Kristu Nyenyezi Yowala, kodi ukuganiza kuti uli amene iwo amanena kuti uli?” Ndani amene anthu kubwerera m’mbuyo m’zana loyamba ananena kuti Yesu anali? Yesu iyemwini anafunsa ophunzira ake funso limenelo ndi kulandira mayankho ambiri osiyanasiyana. (Mateyu 16:13, 14) Lerolino, chifupifupi zaka 2,000 pambuyo pake, chizindikiritso cha Yesu Kristu chidakali chodzutsa mkangano.

Kodi icho chiridi n’kanthu amene Yesu anali? Ndi chotulukapo chotani chimene chizindikiritso chake chingakhale nacho pa ife? Chabwino, anthu otchuka a masiku apita anapanga mbiri ya dziko, mwakutero kuyambukira tonsefe, ngati kokha osati mwachindunji. Koma lerolino iwo ali akufa. Chotero, ngakhale kuti iwo atiyambukira ife ndi zimene anachita, m’njira iriyonse iwo sangatiyambukire ife ndi zimene akuchita.

M’nkhani ya Yesu Kristu, ngakhale kuli tero, mkhalidwewo uli wosiyana kotheratu. Mamiliyoni amakhulupirira, ndipo ali ndi umboni wokwanira kaamba ka chikhulupiriro choterocho, kuti Yesu alidi wamoyo lerolino, osati monga munthu pa dziko lapansi koma monga mzimu wamphamvu kumwamba. Chimene Yesu wakhala akuchita, makamaka m’zana lino la 20, chakhala ndi chiyambukiro champhamvu pa anthu onse. M’kuwonjezerapo, chiyambukiro cha Yesu pa miyoyo yathu sichiri ndi malire pa chimene iye anachita kalelo. Icho chimafutukuka kuphatikiza chimene iye akuchita pa nthaŵi ino ndipo, mwachimwemwe, chimene iye adzachita mtsogolo.

Kubwerera ku mutu wathu: Yesu Kristu​—Mulungu, munthu, kapena nthano? Nchiyani chimene mukuganiza? Yesu Kristu wa nthano akatanthauza kuti iye sanali Mulungu kapenanso munthu, kupangitsa kulingalira kowonjezereka kukhala kopanda phindu. Ku mbali ina, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuphunzira ponena za Yesu yemwe ali ndi moyo ndi amene wapatsidwa mphamvu ndi Mulungu kubweretsa mapindu osatha ku mtundu wa anthu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena