Satana—Kodi Iye Ali Weniweni?
KODI INU mumakhulupirira kuti Satana aliko? Ngati ndi tero, chikuwoneka kuti muli mbali yomazimiririka ya ochepa. “Pofika mu ma 1980 chikhulupiriro mwa Mdyerekezi chinazimiririka kuchotsapo kokha pakati pa Akatolika enieni, magulu opatuka kuchoka ku chiProtestanti, Aprotestanti enieni, Eastern Orthodox, Asilamu—ndi okhulupirira malaulo ochepa.” Linanena tero bukhu la Mephistopheles—The Devil in the Modern World, lolembedwa ndi Jeffrey Burton Russell.
Si aliyense, ngakhale ndi tero, amene wasiya kukhulupiririra kuti Satana ali weniweni. “Mdyerekezi adakali wamoyo ndipo adakali kugwira ntchito m’dziko,” anatero Papa John Paul II m’mawu ake a posachedwapa mu Italy.
Kodi papa ali wolondola? Ngati ndi tero, Satana ali m’malo abwino kuchita chimene afuna m’dziko. Ngati anthu sakhulupirira m’kukhalapo kwake, iwo sadzamutsutsa iye. Nchosadabwitsa kuti Cardinal Ratzinger, wolamulira wapatsogolo pa Vatican pa chiphunzitso, ananena kuti: “Mdyerekezi angatenge malo othaŵirapo mu mbali yake yokondeka koposa, kusadziŵidwa.”
Kodi Satana kwenikwendi aliko? Ngati timakhulupirira Baibulo, tiyenera kuyankha kut inde! Satana akulozeredwako nthaŵi zambiri ndi dzina m’cholembedwa chowuziridwa chimenecho. Mwachitsanzo, mlembi wa Baibulo Paulo, akumachenjeza ponena za “atumwi onyenga” ndi “ochita ochenjera” m’mathayo a mpingo Wachikristu, analemba kuti: “Kulibe kudabwa, pakuti Satana yembwe adziwonetsera ngati mngelo wakuwunika.” Paulo anawona Satana monga munthu wanzeru, wachinyengo.—2 Akorinto 11:13, 14.
Nchifukwa ninji, nanga, kuli kwakuti kukhalapo kwa Satana sikumatengedwa mosamalitsa ndi anthu ambiri lerolino? Mwachidziŵikire, kuli kuwunikira kwa mzimu wa mbadwo uno. Tikumakhala monga mmene tikuchitira mu imene ena akuitcha nyengo ya pambuyo pa Chikristu, kusakhulupirira mwa kukhalapo kwa Mulungu, kukonda zosangulutsa, kukondetsa zinthu za kuthupi, ndi chikomyunizimu zalowa m’malo chikhulupiriro cha chipembedzo m’zitaganya zambiri. Mamiliyoni a anthu samakhulupiriranso mwa Mulungu, akumawona kukhalapo kwake kukhala kosayenerera ku nthanthi zawo zaumwini. Ndipo iwo ataya Satana limodzi ndi Mulungu. Anthu ena a chipembedzo mu Chikristu cha Dziko, ngakhale kuti iwo amadzinenera kukhala okhulupirira mwa Mulungu, amadzimva kuti chikhulupiriro mwa Satana chiri chachikale m’zana lino la 20.
Chiri chofunika, ngakhale kuli tero, kuti kukana Mulungu sikuli mwa njira iriyonse kwatsopano. Zaka zina 3,000 zapitazo, wolemba ndakatulo wa Chichebri Davide analemba kuti: “Chitsiru chimati mu mtima mwake: ‘Kulibe [Yehova, NW].’ Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa.” (Salmo 14:1; 53:1) Mmalo ena analemba kuti: “Woipa monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake akuti sadzafunsira; malingaliro ake onse akuti: ‘Palibe Mulungu.’” (Salmo 10:4) Ngakhale kubwerera m’mbuyo ku nthaŵiyo, anthu anachita ngati kuti Mulungu kunlibe. Ndipo mapeto anzeru angakhale anali akuti ngati kulibe Mulungu, sikungakhalenso Satana.
Ena Amakhulupirirabe
Monga mmene chadziŵitsidwira kale, ngakhale kuli tero, ena amalandirabe chikhulupiriro mwa Mdyerekezi weniweni. Pali awo amene amakhulupirira chiphunzitso chakale cha Zoroaster chakuti chilengedwe chinalamuliridwa ndi mbali ziŵiri yabwino ndi yoipa, akumanena kuti chabwino ndi choipa. Mulungu ndi Mdyerekezi, ayenera kukhala anakhalapo nthaŵi zones kumbali ndi kumbali. Ena amafikira pa kunena kuti chabwino ndi choipa zones ziŵiri ziri mbali za mutu wa Mulungu. Ndipo padakali ambiri m’Chiristu cha Dziko ndi Chisilamu omwe amakhulupiririra m’kukhalapo kwa Satana. Ndithudi, kwa ambiri a amenewa, iye amakhalako monga mzimu wa mapiko wokhala ndi nyanga ndi m’chira yemwe amalamulira chimaliziro cha “miyoyo yosafa” yoperekedwa ku “moto wa helo,” mokulira monga mmene anasonyezedwera m’ntchito za wochitira fanizo wotchuka wa chiFrench Gustave Doré.
M’chenicheni, kwa ena, chikhulupiriro mwa Satana chimapita patalipo. Iwo amamlambira iye—kaya mwa dzina kapena kupyolera mwa miyambo ya usatana kapena ya uchiwanda. Kwa zaka zikwi zingapo, ufiti ndi matsenga zazindikiritsidwa ndi kulambira Satana. Ngakhale mu mbadwo wathu wamakono, wokaikira, Usatana ukalipobe. Chotero, tisanakambitsirane chimene Baibulo limanena ponena za Satana iyemwini, tiyeni tilingalire nsonga zina za Usatana wamakono.
[Chithunzi patsamba 3]
Kuchitira chithunzi kwa chiBuddha kwa “helo” wausatana