Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Popeza Danieli ananena kuti sakalandira mphatso kuchokera kwa Mfumu Belisazara kaamba ka kumasulira kulembedwa kwa pa khoma, nchifukwa ninji iye anapezedwa akuvala chibakuwacho ndi unyolo wa m’khosiwo pambuyo pake?
Nthaŵi pang’ono Amedi ndi Aperisiya asanagwetse Babulo, Mfumu Belisazara ndi mabwalo ake anali pakati pa phwando. Mkati mwa phwandolo, iye anatenga ziŵiya zomwe zinali zochokera ku kachisi wa Yehova ndi kugwiritsira ntchito izi kaamba ka kumweramo vinyo, akumatamanda milungu ya Chibabulo. Koma phwandolo linasokonezedwa mwamsanga pamene dzanja losakhala la munthu linalemba zinthu zachilendo pa khoma.—Danieli 5:1-5.
Anthu anzeru ndi openda nyenyezi a ku Babulo anali osakhoza kulongosola kalembedweko, ngakhale kuti Belisazara anawalonjeza kuwapatsa unyolo wa golidi wa m’khosi ndi malo otchuka a boma kwa aliyense yemwe akakhoza kulongosola kalembedwe kachilendoko.—Danieli 5:7-9.
Pamene Mhebri wotchedwa Danieli potsirizira pake anabweretsedwa, mfumu inabwereza chopereka chake—kuveka Danieli ndi chibakuwa, kuika unyolo wagolidi wa m’khosi pa iye, ndi kumpanga iye kukhala wolamulira wachitatu mu ufumu. Mneneriyo anayankha mwaulemu kuti: “Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphoto zanu mupatse wina; koma ndidzaŵerengera mfumu lembalo, ndi kumudziŵitsa kumasulira kwake.”—Danieli 5:17.
Chotero Danieli sanafunikire kupatsidwa chiphuphu kapena kulipiridwa kuti apereke kumasulira. Mfumu ikakhoza kusunga mphatso zake kapena kuzipereka izo kwa winawake. Danieli akapereka kulongosolako, osati kaamba ka mphatso, koma chifukwa chakuti anapatsidwa mphamvu kchita tero ndi Yehova, Mulungu wowona, amene chiweruzo chake pa Babulo chinali kubwera.
Pamene tiŵerenga pa Danieli 5:29, pambuyo pakuti Danieli waŵerenga ndi kulongosola mawuwo monga mmene iye ananenera kuti akachita mfumu inalamulira kuti mphatsozo ziperekedwe kwa Danieli ngakhale ndi tero. Danieli iyemwini sanaike chovalacho ndi unyolo wa m’khosiwo. Izo zinaikidwa pa iye mwalamulo la mfumu yolamulira, Mfumu Belisazara. Koma ichi sichikusepemphana ndi Danieli 5:17, pamene mneneriyo anachipangitsa icho kukhala chowonekera kuti cholinga chake sichinali chadyera.
Yesu pambuyo pake ananena kuti “iye wakulandira mneneri padziko la mneneri adzalandira mphotho ya mneneri.” (Mateyu 10:41) Zimenezo sizinagwire ntchito mpang’ono pomwe kwa Belisazara, popeza kuti sanali kuchita ndi Danieli mwachifundo kapena mwaulemu chifukwa chakuti analemekeza mwamuna wachikulupiriro ameneyu monga mneneri wa Mulungu wowona. Mfumu Belisazara anali wofunitsitsa kupatsa mphatso zofananazo kwa aliyense wokhoza kuthetsa chinsinsi cha kalembedweko, ngakhale openda nyenyezi akunja. Mfumu inapeza mphatso yoyenera, imene inali yogwirizana ndi kalembedwe ka ulosi pa khoma: “Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Akasidi inaphedwa. Ndipo Dariyo Mmedi analandira ufumuwo.”—Danieli 5: 30, 31.