Bwanamkubwa Wonyada Alandidwa Ufumu
“MFUMU Belisazara anakonzera anthu ake akulu chikwi chimodzi madyerero akulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho,” analemba motero mneneri Danieli. Komabe, pamene madyererowo anali mkati, “padasandulika pankhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m’chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.” Usiku womwewo, “Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa. Ndipo Dariyo Mmedi analandira ufumuwo.”—Danieli 5:1, 6, 30, 31.
Kodi Belisazara anali yani? Kodi ndi motani mmene iye anatchedwera “mfumu ya Akasidi”? Kodi iye anali ndi udindo wanji kwenikweni mu Ufumu Watsopano wa Babulo? Nanga zinatani kuti alandidwe ufumuwo?
Bwanamkubwa Kapena Mfumu?
Danieli anafotokoza kuti Nebukadinezara anali atate wake wa Belisazara. (Danieli 5:2, 11, 18, 22) Komabe, ubale umenewu sudziŵika bwino. Buku lakuti Nabonidus and Belshazzar (Nabonidus ndi Belisazara), lolembedwa ndi Raymond P. Dougherty, likufotokoza kuti mwina Nebukadinezara anali agogo wake kudzera mwa amayi wake, Nitocris. Nkuthekanso kuti Nebukadinezara anali “atate” wake wa Belisazara chifukwa chakuti Belisazarayo analoŵa m’malo mwake monga mfumu. (Yerekezerani ndi Genesis 28:10, 13.) Mulimonse mmene zinalili, malemba angapo ozokotedwa padongo omwe anapezeka kummwera kwa Iraq m’zaka za zana la 19 amati Belisazara anali mwana wamkulu wa Nabonidus, mfumu ya Babulo.
Popeza kuti nkhani ya m’chaputala 5 cha Danieli ikufotokoza zomwe zinachitika pausiku umene Babulo anagwa mu 539 B.C.E., iyo sifotokoza mmene Belisazara anayambira kulamulira. Koma zinthu zofukulidwa m’mabwinja zimasimba za ubale wa pakati pa Nabonidus ndi Belisazara. “Mabuku a ku Babulo amati Nabonidus anali wolamulira woyendayenda,” anatero Alan Millard, wofukula za m’mabwinja ndiponso wodziŵa za zinenero za Asemiti. Millard anawonjezera kuti: “Ngakhale kuti sanafune kusiya kulambira milungu ya Babulo, iye . . . anachirikizanso mulungu mwezi m’mizinda inanso iŵiri ya Uri ndi Harana. Pazaka zingapo za ulamuliro wake, Nabonidus sanakhaleko nkomwe m’Babulo; m’malo mwake, iye ankakhala kumalo achonde otchedwa Teima [kapena kuti Tema] kumpoto kwa Arabia.” Mwachionekere, Nabonidus analamulira nthaŵi yaitali ali kunja kwa mzinda wa Babulo. Panthaŵi imene iye kunalibe, Belisazara ndiye anapatsidwa ulamuliro wonse.
Pofotokoza bwino za udindo weniweni wa Belisazara, malemba ena ozokotedwa omwe amanenedwa kuti ndiwo “Nkhani ya Moyo wa Nabonidus” amati: “Iye [Nabonidus] anapereka ‘Gulu [lankhondo]’ kwa (mwana) wake wamkulu, woyamba kubadwa, ndipo asilikali a m’dzikolo anali mu (ulamuliro) wa ameneyo. Iye anapereka (ulamuliro wonse), anapereka ufumuwo kwa iye.” Choncho, Belisazara anali bwanamkubwa.
Komabe, kodi bwanamkubwa angatchedwe mfumu? Chiboliboli cha wolamulira wakale chomwe chinapezeka kumpoto kwa dziko la Syria cha m’ma 1970 chimasonyeza kuti zinali zofala kutchula wolamulira aliyense kuti mfumu, ngakhale ngati anali ndi udindo wotsikirapo. Chibolibolicho chinali cha wolamulira wa Gozan ndipo analembapo mawu a m’chinenero cha Asuri ndi m’Chialamu. Malemba a m’chinenero cha Asuri anatcha munthuyo kuti bwanamkubwa wa Gozan, koma malemba ena a m’Chialamuwo anamutcha mfumu. Choncho, nzosadabwitsa kwenikweni kuona kuti m’malemba aboma a ku Babulo, Belisazara anatchedwa kalonga wa ufumu pamene kuli kwakuti iye anatchedwa mfumu m’malemba a Danieli a m’Chialamu.
Nabonidus ndi Belisazara analamulira mothandizana mpaka chakumapeto kwa Ufumu Watsopano wa Babulo. Nchifukwa chake, pausiku womwewo wa kugwa kwa Babulo, Belisazara analonjeza kuti adzaika Danieli monga wolamulira wachitatu mu ufumuwo, osati wachiŵiri.—Danieli 5:16.
Bwanamkubwa Wodzidalira Mopambanitsa Ndiponso Wonyada
Zochitika kumapeto kwa ulamuliro wa Belisazara zimasonyeza kuti kalongayo anali wodzidalira mopambanitsa ndiponso wonyada. Pamene mapeto a ulamuliro wake anadza pa October 5, 539 B.C.E., Nabonidus anabisala ku Borsippa, atagonjetsedwa ndi ankhondo a Amedi ndi Aperisi. Babulo weniweniyo anazingidwa ndi magulu ankhondo. Koma Belisazara anadzimva kukhala wotetezeredwa kwambiri mumzinda wozingidwa ndi makoma aakulu koposa, kotero kuti usiku womwewo, anakonzera “anthu ake akulu chikwi chimodzi madyerero akulu.” Herodotus, wolemba mbiri wachigiriki wa m’zaka za zana lachisanu B.C.E., anati mkati mwa mzindawo, anthu “anali kuvina panthaŵiyo, ndipo anali pachikondwerero.”
Komabe, kunja kwa makoma a Babulo, ankhondo a Amedi ndi Aperisi anali kuchita zinthu mokangalika. Motsogozedwa ndi Koresi, iwo anapambutsa madzi a Mtsinje wa Firate, umene unkadutsa pakati pa mzindawo. Mitima ili m’malere, ankhondo ake anali okonzekera kuyenda khuvukhuvu mumtsinjewo madziwo atangophwera. Anakonzeka zokwezeka ndi kuloŵa mumzindamo pazitseko zamkuwa zotseguka zomwe zinali pakhoma la m’gombe la mtsinjewo.
Chikhala kuti Belisazara anadziŵa zimene zinali kuchitika kunja kwa mzindawo, iye akanatseka zipata zamkuwazo, ndipo akanauza amuna ake amphamvu kuti akwere makoma a m’gombe la mtsinjewo nagwire adaniwo. M’malo mwake, ataledzera ndi vinyo, Belisazara wodzigangirayo anaitanitsa zotengera za m’kachisi wa Yehova. Kenaka, iye, alendo ake, akazi ake, ndiponso adzakazi ake anamwera m’zikhozo monyozera Yehova akumatamanda milungu yachibabulo. Mwadzidzidzi ndiponso modabwitsa, panaoneka dzanja lomwe linayamba kulemba pakhoma la nyumba yachifumuyo. Atachita mantha, Belisazara anaitana amuna ake anzeru kuti amasulire uthengawo. Koma iwo “sanakhoza kuŵerenga lembalo, kapena kudziŵitsa mfumu kumasulira kwake.” Pomalizira pake, Danieli ‘analoŵa naye kwa mfumu.’ Mouziridwa ndi Mulungu, mneneri wolimba mtimayo wa Yehova anavumbula tanthauzo la uthenga wodabwitsawo, kuneneratu za kugwetsa Babulo kwa Amedi ndi Aperisi.—Danieli 5:2-28.
Amedi ndi Aperisi analanda mzindawo mosavuta, ndipo Belisazara sanakhalenso ndi moyo usikuwo. Iye ataphedwa, ndiponso Nabonidus atagonja kwa Koresi, Ufumu Watsopano wa Babulo unathera pomwepo.
[Chithunzi patsamba 8]
Danieli amasulira uthenga wa chiwonongeko cha Ufumu wa Babulo