Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 11/1 tsamba 3
  • Kodi Nthaŵi Zonse Padzakhala Nkhondo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nthaŵi Zonse Padzakhala Nkhondo?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbaliwali za Chiyembekezo
  • Nkhondo Yothetsa Ndhondo
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Nkhondo Nzosapeŵeka?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • N’chifukwa Chiyani Masiku Ano Sitimenya Nkhondo Ngati Mmene Ankachitira Aisiraeli?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 11/1 tsamba 3

Kodi Nthaŵi Zonse Padzakhala Nkhondo?

PA JULY 1, 1916, m’gawo labwino lolima la Picardy Kumpoto kwa France, Nkhondo Yoyamba ya somme inayambika. Pambuyo pa kuphulitsa mabomba kowopsya ndi kuwukira kwa mumlengalenga, magulu ankhondo a chiBritish ndi chiFrench anayambitsa chomwe anayembekezera kuti chikakhala chipambano chosankha cha magulu ankhondo a chiGerman okhala mmaenje omwe anayang’anizana nawo. Koma panalibe chipambano. M’malomwake, pa tsiku loyamba, asilikali achiBritish 20,000 anaphedwa. Pamene milungu inapita, nkhondo inapitiriza yopandabe chipambano. Mu October mvula yamphamvu inasintha bwalo la nkhondolo kukhala nyanja ya matope. Podzafika mkati mwa November Magulu Ogwirizanawo anali atangoyenda kokha makilomita asanu ndi atatu. Pa nthaŵiyi, miyoyo 450,000 ya chiGerman, ya chiFrench 200,000, ndi ya chiBritish 420,000 inali itatayika. Asilikali oposa miliyoni imodzi, ambiri a iwo amuna achichepere, anatha mu nkhondo imeneyo!

Iyi inali kokha mbali ya nkhondo yoyamba ya dziko. Ndipo nkhondo yoyamba ya dziko inali kokha imodzi​—yoipitsitsa kufikira pa nthaŵiyo​—ya nkhondo zosaŵerengeka zomwe zamenyedwa mkati mwa mbiri. Ndi kuwononga kopanda lingaliro kotani nanga kwa moyo wa munthu!

Nchifukwa ninji anthu amawumirira pa kuphana wina ndi mnzake mwanjira imeneyi? Pali nsonga zambiri zolowetsedwa, pakati pa zimene tingatchule dyera, chikhumbo, umbombo, limodzinso ndi kulakalaka kaamba ka mphamvu ndi kutchuka. Chochititsa china cha nkhondo chakhala utundu. Ndithudi, nkhondo inawunikira kulongosoka kwa kuyang’ana pa mbiri ya munthu kopezeka m’Baibulo: “Munthu wapweteka mnzake pa kumulamulira.”​—Mlaliki 8:9.

Chipembedzo nachonso kaŵirikaŵiri chayambitsa nkhondo. Nkhondo za chipembedzo za Mbadwo Wapakati zinamenyedwa ndi mitundu ya chipembedzo kaamba ka zifukwa za chipembedzo: kulandanso Palestine kaamba ka Chikristu cha Dziko. Mu nkhondo zonse ziŵiri za dziko za zana lino, atsogoleri achipembedzo ochokera ku zipembedzo zosiyanasiyana ayesera kulungamitsa malingaliro a chipembedzo a asilikali kukwapangitsa iwo kukhala ofunitsitsa kukpha anansi awo kumbali ina. Ndipo kwina kwa kuwombana komwe kukumenyedwa pa nthaŵi ino kwakhala mwamphamvu mbali ya chipembedzo.

Mbaliwali za Chiyembekezo

Kodi pali chiyembekezo chirichonse chakuti tsiku lina nkhondo zidzatha? Inde, chiripo. Yesu Kristu akutchedwa “Kalonga wa Mtendere.” Pamene iye anabwera ku dziko lapansi, iye anakhalira moyo ku dzina limeneli, kuphunzitsa anthu kukonda anansi awo monga iwo eni. Iye anafikira pa kuwauza iwo kukonda adani awo. (Yesaya 9:6; Mateyu 5:44; 22:39) Monga chotulukapo chake, awo amene anapereka chilabadiro ku ziphunzitso zake m’zana loyamba anakhala ubale wa mtendere, wa mitundu yonse. Chinali chosalingalirika kwa iwo kumenya nkhondo kwa wina ndi mnzake. Mwatsoka, ngakhale kuli tero, chikhulupiriro choyera cha Akristu oyambirira amenewo m’kupita kwa nthaŵi chinaipitsidwa. M’kupita kwa nthaŵi, matchalitchi anadzilowetsa mu ndale za dziko ndipo manja awo anafikira kukhala oipitsidwa ndi mwazi wa nkhondo za mitundu.

Kumapeto kwenikweni, mphepo za kusintha zinayamba kuwomba pa Europe. Chinawoneka ngati kuti mtundu wa anthu unakhala wotopa ndi nkhondo zosalekeka. Mu 1899 ndipo kachiŵirinso mu 1907, misonkhano ya mitundu yonse inachitidwa mu The Hague, Netherlands. Pa msonkhano wa 1899, chimvano chinatengedwa kaamba ka “Pacific [peaceful] Settlement of International Disputes” (Kukhazikitsa kwa Mtendere kwa Mikangano ya Mitundu Yonse). Chotero pamene zana la 20 linayambika, ambiri anayembekezera kuti dziko mwapang’onopang’ono likalekana nacho chikhumbo chake chakuyambitsa nkhondo. Ziyembekezo zoterozo, ngakhale kuli tero, zinathetsedwa ndi mfuti za nkhondo yoyamba ya dziko. Kodi ichi chinatanthauza kuti ziyembekezo za mtundu wa anthu kaamba ka mtendere sizidzakwaniritsidwa nkhomwe?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena