Bukhu la Makedzana la Alexandrine
BUKHU la Makedzana la Alexandrine linali loyambirira la mamanusikripiti akulu a Baibulo kupangidwa kukhalako kwa ophunzira. Kupezedwa kwake kunatsogoza ku kusuliza komangirira kwa lemba la Baibulo la Chigriki kaamba ka phindu la atembenuzi otsatirapo a Malemba Oyera. Ndimotani ndipo ndi liti pamene ilo linabwera powonekera?
Kyrillos Loukaris, kholo la ku Alesandriya, Igupto, anali wosonkhanitsa wamkulu wa mabukhu, ndipo m’chaka cha 1621, pamene anakhala kholo mu Constantinople, Turkey, anatenga limodzi naye Bukhu la Makedzana la Alexandrinus limeneli. Ndi kusakhazikika mu Middle East, ngakhale kuli tero, ndipo ndi kuthekera kwakuti manusikripitiyo ingawonongedwe ngati inagwera m’manja mwa Asilamu, Loukaris anadzimva kuti likakhala la chisungiko koposa mu England. Mofananamo, mu 1624 iye analipereka ilo kwa kazembe woimira anthu a ku Britain mu Turkey monga mphatso kaamba ka mfumu ya Chingelezi, James I Mfumuyo inafa manusikripitiyo isanaperekedwe kwa iye, chotero inaperekedwa m’malomwake kwa m’lowa m’malo wake, Charles I, zaka zitatu pambuyo pake.
Kodi manusikripiti imeneyi inalidi ya mtengo monga mmene Kyrillos Loukaris anadzimvera kuti inali tero? Inde. Iyo iri ndi tsiku la kubwerera m’mbuyo ku mbali yoyambirira ya zana lachisanu C.E. Alembi osiyanasiyana mwachidziŵikire anagawana m’kuilemba iyo, ndipo lembalo lawongoleredwa mkati monse. Iyo inalembedwa pa chikopa, madanga aŵiri ku tsamba lirilonse, mu zirembo za uncial (zazikulu) popanda mpata uliwonse pakati pa mawu. Mbali yokulira ya Mateyu ikusoweka, monga mmene zinaliri mbali zina za Genesis, Masalmo, Yohane, ndi 2 Akorinto. Tsopano yodziŵika mwa lamulo monga Codex A, iyo iri ndi masamba 773 ndipo idakali mboni yoyambirira ya kufunika kokulira.
Mamanusikripiti ambiri a Baibulo angaikidwe m’magulu, kapena m’mabanja, chifukwa cha kufanana komwe kuli pakati pawo. Izi zinachitika pamene alembi anapanga makope awo kuchokera ku magwero amodzimodziwo kapena zitsanzo zolinganako. Ndi Bukhu la Makedzana la Alexandrine, ngakhale kuli tero, alembiwo anawoneka kukhala odera nkhaŵa ndi kubweretsa pamodzi kuŵerenga kuchokera ku mabanja osiyanasiyana kotero kuti apereke lemba labwino koposa lothekera. M’chenicheni, linatsimikizira kukhala lakaleko ndi labwinoko kuposa mamanusikripiti onse a Chigriki omwe anagwiritsiridwa ntchito monga maziko kaamba ka King James Version ya 1611.
Kuŵerenga kwa Alexandrine kwa 1 Timoteo 3:16 kunadzutsa mkangano wokulira pamene kunafalitsidwa. King James Version pano imaŵerenga kuti: “Mulungu anawonekera m’thupi,” m’kulozera kwa Kristu Yesu. Koma m’bukhu la makedzana lakale limeneli, kupangidwa kwa “Mulungu,” kopangidwa ndi malemba aŵiri a Chigriki “ΘC,” kuwoneka poyambirira kukhala kunaŵerengedwa “ΘC,” liwu kaamba ka “amene.” Mwachidziŵikire, ichi chinatanthauza kuti Kristu Yesu sanali “Mulungu.”
Chinatenga zoposa zaka 200 ndi kupezedwa kwa mamanusikripiti ena akale kuti atsimikizire kalembedwe ka “amene” kapena “chimene” kukhala kolondola. Bruce M. Metzger mu Textual Commentary on the Greek New Testament yake akumaliza kuti: “Palibe kalembedwe ka zilembo zazikulu (m’dzanja loyambirira) ka kumayambiriro kuposa zana lachisanu ndi chitatu kapena chisanu ndi chinayi . . . komwe kamachirikiza θεός [the·osʹ]; malembedwe onse akale amalingalira ὅς kapena ὅ; ndipo palibe wolemba wa zolemba za abambo a tchalitchi aliyense kumayambiriro kwa mbali yachitatu ya zana lachinayi yemwe amatsimikizira kuŵerenga kwa θεός [the·osʹ].” Lerolino, matembenuzidwe ambiri amavomereza m’kudumpha chilozero chirichonse kwa “Mulungu” m’lemba limeneli.
Mu 1757 Royal Library ya mfumuyo inakhala mbali ya British Library, ndipo bukhu la makedzana labwino limeneli lasonyezedwa mowonekera m’chipinda cha manusikripiti cha mu British Museum. Chiri chuma choyenera kuchiwona.